-
Kodi Cholinga cha Mulungu Ndi Choti Tikhale Ndi Moyo Wotani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
PHUNZIRO 25
Kodi Cholinga cha Mulungu Ndi Choti Tikhale Ndi Moyo Wotani?
Baibulo limanena kuti munthu “amakhala ndi moyo waufupi, wodzaza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Kodi Mulungu amafuna kuti tizikhala ndi moyo woterewu? Ngati si choncho, nanga cholinga chake ndi chotani? Kodi cholinga chakechi chidzakwaniritsidwa? Baibulo lili ndi mayankho otonthoza a mafunso amenewa. Tiyeni tiwaone.
1. Kodi Yehova amafuna kuti tizikhala ndi moyo wotani?
Yehova amafuna kuti tizikhala moyo wabwino kwambiri. Iye atalenga Adamu ndi Hava omwe ndi anthu oyambirira, anawaika m’Paradaiso wokongola, wotchedwa munda wa Edeni. Kenako “Mulungu anawadalitsa n’kuwauza kuti: ‘Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.’” (Genesis 1:28) Yehova ankafuna kuti iwo abereke ana, asamalire dziko lonse lapansi kuti likhale paradaiso ndiponso kuti azisamalira zinyama. Cholinga chake chinali chakuti anthu onse akhale ndi thanzi labwino n’kukhala ndi moyo mpaka kalekale.
Ngakhale kuti masiku ano anthu sitikukhala ndi moyo umene Mulungu ankafunawu,a cholinga chake sichinasinthe. (Yesaya 46:10, 11) Mulungu amafunabe kuti anthu amene amamumvera adzakhale ndi moyo wopanda mavuto mpaka kalekale.—Werengani Chivumbulutso 21:3, 4.
2. Tingatani kuti tizisangalala ndi moyo panopa?
Yehova anatilenga m’njira yakuti tizitha kuzindikira “zosowa zathu za uzimu,” kutanthauza kuti timakhala ndi mtima wofuna kumudziwa ndi kumulambira. (Werengani Mateyu 5:3-6.) Iye amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba, ‘tiziyenda m’njira zake zonse, kumukonda’ komanso kumutumikira ‘ndi mtima wathu wonse.’ (Deuteronomo 10:12; Salimo 25:14) Zimenezi zingatithandize kuti tizisangalala ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto. Tikamatumikira Yehova timakhala ndi moyo watanthauzo chifukwa chakuti timachita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza chikondi chachikulu chimene Yehova anasonyeza pamene ankalenga dzikoli kuti anthufe tikhalemo komanso zimene Mawu ake amanena zokhudza cholinga cha moyo.
3. Yehova amafuna kuti anthu azikhala moyo wabwino kwambiri
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani Mulungu analenga dziko lapansi lokongola chonchi?
Werengani Mlaliki 3:11, kenako mukambirane funso ili:
Malinga ndi lembali, mwaphunzira zotani zokhudza Yehova?
4. Cholinga cha Yehova sichinasinthe
Werengani Salimo 37:11, 29 ndi Yesaya 55:11, kenako mukambirane funso ili:
Kodi timadziwa bwanji kuti cholinga cha Yehova chokhudza anthufe sichinasinthe?
Nyumba yomwe yawonongeka ikhoza kukonzedwanso. N’chimodzimodzi ndi dzikoli. Anthu aliwononga kwambiri koma Mulungu adzalikonza kuti anthu amene iye amawakonda azidzakhalamo
5. Tikamalambira Yehova timakhala ndi moyo wosangalala
Kudziwa cholinga cha moyo, kumatithandiza kuti tizikhala mosangalala. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Kodi kudziwa kuti moyo uli ndi cholinga kunathandiza bwanji Terumi?
Werengani Mlaliki 12:13, kenako mukambirane funso ili:
Tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova pa zinthu zabwino zambiri zimene watichitira?
MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?”
Mungamuyankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yehova amafuna kuti tizikhala moyo wabwino kwambiri wopanda mavuto padziko pano. Tikamamulambira ndi mtima wonse timakhala ndi moyo wosangalala kwambiri ngakhale panopa.
Kubwereza
Kodi Yehova ankafuna kuti Adamu ndi Hava azikhala moyo wotani?
Kodi timadziwa bwanji kuti cholinga cha Mulungu chokhudza anthu sichinasinthe?
Mungatani kuti muzikhaladi moyo wosangalala?
ONANI ZINANSO
Onani umboni wosonyeza kuti munda wa Edeni unalipodi.
“Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?” (Nsanja ya Olonda, January 1, 2011)
Onani chifukwa chake sitikayikira kuti dzikoli lidzakhalapo mpaka kalekale.
Onani mmene Baibulo lingakuthandizireni kudziwa cholinga cha moyo.
Munthu yemwe ankaganiza kuti ali ndi chilichonse pa moyo anazindikira kuti ankasowekera chinachake. Onani chimene chinamuthandiza kudziwa cholinga cha moyo.
a M’phunziro lotsatira, mudzaphunzira chifukwa chake masiku ano anthufe timakumana ndi mavuto.
-
-
Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
2. Kodi ndi ndani akulamulira ndi Yesu?
Yesu sakulamulira yekha. Anthu ochokera “mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse . . . adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.” (Chivumbulutso 5:9, 10) Ndi anthu angati amene adzalamulire ndi Khristu? Kungoyambira pamene Yesu anabwera padziko lapansi, anthu ambiri akhala otsatira ake ndipo panopa alipo mamiliyoni ambiri. Koma ndi anthu okwana 144,000 okha amene adzapite kumwamba kukalamulira ndi Yesu. (Werengani Chivumbulutso 14:1-4.) Koma Akhristu ena onse adzakhala padziko lapansi ndipo azidzalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu.—Salimo 37:29.
-
-
Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?
Ufumu wa Mulungu unayamba kale kulamulira. Posachedwapa Ufumuwu ubweretsa madalitso ambiri padzikoli. Tiyeni tione ena mwa madalitso amene tidzasangalale nawo Ufumuwu ukadzayamba kulamulira dziko lonse lapansi.
1. Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita chiyani kuti ubweretse mtendere ndi chilungamo padzikoli?
Yesu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzawononga anthu oipa ndi maboma onse a anthu pa nkhondo ya Aramagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Pa nthawi imeneyo, tidzaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la m’Baibulo ili: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso.” (Salimo 37:10) Yesu adzagwiritsa ntchito Ufumuwu pobweretsa mtendere komanso chilungamo padziko lonse lapansi.—Werengani Yesaya 11:4.
2. Kodi moyo udzakhala wotani chifuniro cha Mulungu chikadzachitika padziko lapansi?
Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira dzikoli, “olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kuona kuti aliyense padzikoli ndi wolungama ndipo akukonda Yehova ndi anthu ena. Palibe aliyense amene azidzadwala ndipo anthu onse adzakhala ndi moyo mpaka kalekale.
3. Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani anthu oipa akadzawonongedwa?
Anthu oipa akadzawonongedwa, Yesu adzalamulira monga Mfumu kwa zaka 1,000. Pa nthawiyi, Yesu ndi olamulira anzake okwana 144,000, adzathandiza anthu onse padzikoli kuti akhale angwiro. Pofika kumapeto kwa zaka 1,000, dziko lonse lidzakhala paradaiso ndipo anthu azidzakhala mosangalala chifukwa chomvera malamulo a Yehova. Kenako Yesu adzabwezera Ufumu kwa Atate wake Yehova. Pa nthawi imeneyo, dzina la Yehova ‘lidzayeretsedwa’ kusiyana ndi kale lonse. (Mateyu 6:9, 10) Aliyense adzadziwa kuti Yehova ndi wolamulira wabwino kwambiri yemwe amaganizira atumiki ake. Kenako Yehova adzawononga Satana, ziwanda ndi anthu onse amene adzasonyeze kuti sakufuna kumvera ulamuliro wake. (Chivumbulutso 20:7-10) Zimenezi zikadzachitika, madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse padzikoli adzakhalapo mpaka kalekale.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake sitikayikira kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pokwaniritsa malonjezo onse amene ali m’Baibulo.
4. Mulungu adzathetsa maboma onse a anthu
Baibulo limati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pothetsa zinthu zonse zopanda chilungamo zimene anthu amachitira anzawo.
Werengani Danieli 2:44 ndi 2 Atesalonika 1:6-8, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Yehova komanso mwana wake Yesu, adzachita chiyani ndi maboma a anthu komanso anthu amene amawatsatira?
Kodi zimene mwaphunzira zokhudza Yehova ndi Yesu zikukutsimikizirani bwanji kuti azidzachita zinthu mwachilungamo?
5. Yesu ndi Mfumu yabwino kwambiri
Monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzachitira anthu zinthu zabwino kwambiri padzikoli. Onerani VIDIYO kuti muone umboni wosonyeza kuti Yesu ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu komanso kuti Mulungu anamupatsa mphamvu zochitira zimenezo.
Zimene Yesu ankachita ali padzikoli, zinasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu padzikoli. Pa madalitso amene ali m’munsiwa, ndi dalitso liti limene inuyo mukuliyembekezera kwambiri? Werengani malemba amene ali kutsogolo kwa dalitso lililonse.
ALI PADZIKOLI, YESU . . .
ALI KUMWAMBA, YESU . . .
anathetsa chimphepo chamkuntho.—Maliko 4:36-41.
adzakonza zinthu zonse zimene zawonongedwa padzikoli.—Yesaya 35:1, 2.
anadyetsa anthu ambiri modabwitsa.—Mateyu 14:17-21.
adzathetsa njala padziko lonse.—Salimo 72:16.
anachiritsa anthu ambiri.—Luka 18:35-43.
adzathetsa matenda onse.—Yesaya 33:24.
anaukitsa anthu amene anamwalira.—Luka 8:49-55.
adzathetsa imfa.—Chivumbulutso 21:3, 4.
6. Madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse
Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti anthu azikhala moyo wabwino ngati mmene Yehova ankafunira poyamba. Anthu adzakhala ndi moyo m’paradaiso padzikoli mpaka kalekale. Onerani VIDIYO kuti muone mmene Yehova akukwaniritsira cholinga chake pogwiritsa ntchito Mwana wake Yesu.
Werengani Salimo 145:16, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mumamva bwanji mukaganizira kuti Yehova ‘adzakhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse’?
ZIMENE ENA AMANENA: “Ngati titamachita zinthu mogwirizana, tikhoza kuthetsa mavuto apadziko lonse.”
Kodi Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto ati amene maboma a anthu alephera kuwathetsa?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa cholinga chimene Mulungu anali nacho poyamba. Udzachititsa dzikoli kuti likhale paradaiso, momwe mudzakhale anthu abwino omwe azidzalambira Yehova mpaka kalekale.
Kubwereza
Kodi Ufumu wa Mulungu udzachititsa bwanji kuti dzina la Yehova liyeretsedwe?
N’chifukwa chiyani timakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa zonse zimene Baibulo linalonjeza?
Pa madalitso onse amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse, ndi dalitso liti limene inuyo mukuliyembekezera kwambiri?
ONANI ZINANSO
Fufuzani kuti mudziwe zimene nkhondo ya Aramagedo imatanthauza.
“Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?” (Nkhani yapawebusaiti)
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zomwe zidzachitike pa nthawi imene Yesu anaitchula kuti “chisautso chachikulu.”—Mateyu 24:21.
“Kodi Chisautso Chachikulu N’chiyani?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani zimene zingathandize mabanja kuyerekezera kuti ali m’Paradaiso.
Munkhani yakuti, “Ndinali Ndi Mafunso Ambiri Omwe Ankandisowetsa Mtendere,” onani zimene zinathandiza munthu wina woukira boma kupeza mayankho a mafunso omwe ankamusowetsa mtendere.
“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, January 1, 2012)
-