Mtendere wa Dziko Lonse—Kodi Udzatanthauzanjidi?
MTENDERE wa dziko lonse umene Mulungu alinawo m’maganizo udzaloŵetsamo zoposa kuleka nkhondo kwa chiwunda chonse kapena kuimitsa zida za nyukliya. Izi zikuwoneka mwa njira imene Baibulo limagwiritsirira ntchito liwu lakuti “mtendere.”
Mwachitsanzo, m’Malemba Achihebri (“Chipangano Chakale”) liwu lotembenuzidwa mtendere ndilo Sha·lohmʹ. Liwu la mtundu umenewu lagwiritsiridwa ntchito pa Genesis 37:14, pamene kholo Yakobo akuwuza mwana wake Yosefe kuti: “Nukawone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta ziri bwino, nundibwezere ine mawu.”a Sha·lohmʹ lagwiritsiridwanso ntchito pa Genesis 41:16, pamene latembenuzidwa “mwamtendere.”
Motero, m’lingaliro Labaibulo, mtendere weniweni umaloŵetsamo osati kuleka nkhalwe kokha komanso thanzi laumoyo, chisungiko, ndi khalidwe labwino. Kope lathu lapita linasonyeza kuti anthu sali okhoza kuyankha funso la mmene angabweretsere mtendere. Yesu Kristu yekha, “Kalonga wa mtendere,” adzagwirizanitsa pamodzi zidutswa zonse ndi kubweretsa mtendere weniweni pa dziko lapansi. (Yesaya 9:6, 7) Mwachitsanzo, lingalirani zimene Baibulo likulosera pa Salmo 72:7, 8 ponena za ulamuliro wa ameneyo: “Masiku ake wolungama adzakhazikika; Ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi. Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.” Tangolingalirani—thanzi laumoyo, chisungiko, ndi khalidwe labwino pa mlingo wa dziko lonse! Palibe pangano la ndale zadziko limene lingakwaniritse zimenezo. Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo ungathe, ndipo udzakwaniritsabe zoposapo. Baibulo limatipatsa unyinji wa zowoneratu zaulosi zochititsa chidwi m’dziko lamtendere lamtsogolo limeneli. Tiyeni tilingalire zina za izo.
Kuchotsapo Zida kwa Chiwunda Chonse—Njira ya Mulungu!
Salmo 46:8, 9 limati: “Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa pa dziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; Athyola uta, nadula nthungo; Atentha magareta ndi moto.” Mawu akuti “uta,” “nthungo,” ndi ‘gareta,’ ali ziphiphiritso za mtundu uliwonse wa chida chankhondo kapena makina a nkhondo. Motero Yehova amafika patali kupyola pa kuchepetsa zida kapena kupyoladi pa kuchotsa kotheratu. Iye akuchotsapo kotheratu zida zanyukliya, mfuti zazikulu, akasinja, zoponyera mamisaelo, maguluneti, mabomba apulasitiki, mfuti za laifo, mfuti zakumanja—chirichonse chimene chingawopsyeze mtendere wa chiwunda chonse!
Komabe, zida mwa izo zokha sizimachititsa nkhondo. Kaŵirikaŵiri, nkhondo imakhala ndi mizu yake mu mkhalidwe waudani, waumbombo, kapena wachiwawa wa anthu opanda ungwiro. (Yerekezerani ndi Yakobo 4:1-3.) Chotero Ufumu wa Mulungu udzaukira muzu wa nkhondo umenewu mwakuchotsapo mikhalidwe yoipa yaumunthu yoteroyo mwa anthu. Motani? Mwaprogramu ya maphunziro a dziko lonse. “Dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.
Chotero pokhala “ophunzitsidwa ndi [Yehova, NW],” mtundu wa anthu sudzaonanso kusiyana kwa mafuko monga maziko a kukangana, chidani, kapena kunyada. (Yohane 6:45) “Mulungu alibe tsankhu,” ndipo nzika za dziko lapansi zidzaunikira kupanda tsankhu kwake. (Machitidwe 10:34) Ufumuwo udzachotsanso kuthekera kulikonse kwa kulimbanira dziko mwa kuchotsapo malire adziko alionse. ‘Kuchokera ku nyanja mpaka kunyanja kufikira malekezero a dziko lapansi,’ onse adzalumbira kufunitsitsa kwawo ndi chigonjero chawo chachiyamikiro ku ulamuliro wa Kristu.—Salmo 72:8.
Kuti mtendere umenewo ukhalitse, Ufumuwo udzachotsaponso mphamvu yopatula koposa m’mbiri ya munthu: chipembedzo chonyenga. (Zefaniya 2:11) Mtundu wa anthu udzagwirizana m’kulambira kwawo kwa Mulungu yekha wowona. (Yesaya 2:2, 3) Padzakhala ubale wa dziko lonse!
Mtendere Panyumba
Komabe, kodi mtendere wa dziko lonse ungakhale waphindu lanji ngati nyumba zinali mabwalo ankhondo kumene nthaŵi zonse kumakhala kunyozana, mawu oputana, ndi ziwopsyezo. Ndimo mmene ziliri m’mabanja ambiri lerolino. Mabanja ena amabisa udani waukulu mwakukhala chete kwa mpeni kumphasa.
Chotero mtendere weniweni uyenera kuphatikizapo chisangalalo chapanyumba. Pansi pa programu ya maphunziro a Ufumu, amuna ndi akazi adzaphunzitsidwa kuchitirana mwachikondi ndi ulemu. (Akolose 3:18, 19) Ana adzaphunzitsidwa ‘kumvera makolo awo m’zonse.’ (Akolose 3:20) Sipadzakhala azaka zapakati pa 13 ndi 19 opanduka kudodometsa ndi kudetsa nkhaŵa makolo awo. Chimvero chidzangokhala mkhalidwe, chigwirizano chidzakhala lamulo lake. Ana adzakhala osangalatsa kuwaona ndi chikondwerero kukhala nawo.
Lerolino, mavuto azachuma amakulitsirako mikangano yam’banja, pamene makolo onse aŵiri kaŵirikaŵiri amakakamizika kukhala ndi mtolo wolemera wa ntchito yakuthupi. Koma pansi pa kulamulira kwa Kristu, mabanja adzamasulidwa ku mavuto a zachuma osakaza—malendi okwezedwa, malipiro a chikole chogula nyumba omakwera, misonkho yomakwera, kusoŵa ntchito. Ntchito yokhutiritsa, yachipambano idzakhala yambiri. Ndipo palibe amene adzafunikira kukhala wopanda nyumba. Onani mmene ulosi pa Yesaya 65:21-23 ukugogomezera nsongazi: “Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo . . . sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; . . . Osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa awo adzakhala pamodzi ndi iwo.”
Tangolingalirani kukhala m’malo amene sakukuipizani ndi zowonawona, phokoso, ndi mfungo za zoola zam’matauni! Tangolingalirani kukhala pa nthaka yobiriŵira—nthaka yanu—yolimidwa bwino, kubzalidwa maluŵa, ndi kusalazidwa mokongola. Tangolingalirani kupuma mpweya wabwino ndi woyera wosangalatsa; kumvetsera, osati ku mawu a phokoso a kutsungula kwamakono, koma mawu achibadwa, okoma kumvetsera. Zowonadi, anthu ena amwaŵi akusangalala kale ndi mlingo wa zina za zinthu zimenezi. Koma pansi pa Ufumu wa Mulungu, mikhalidwe ya moyo yamtendere idzasangalalidwa ndi onse. Kudzakhala kulibe osauka, kulibe anjala, kulibe osoŵa mwaŵi uliwonse.—Salmo 72:13, 14, 16.
Baibulo limalonjezanso kuti “koma oipa adzalikhidwa.” (Miyambo 2:22) Zimenezo zikutanthauza kuthetsedwa kwa upandu. Mwana wanu wang’ono pa onse atapita kukaseŵera, simudzafunikira kuda nkhaŵa za oipsya ana kapena akuba ana obisala m’mdima, magalimoto oyendetsedwa mosasamala ndi oyendetsa oledzera, kapena magulu a achichepere omayendayenda openga ndi mankhwala ogodomalitsa. Mwana wanu adzaseŵera m’chitetezo ndi m’chisungiko chotheratu.
Mtendere ndi Khalidwe Labwino Laumwini
Chomalizira, pali mbali ya khalidwe labwino laumwini. Ngakhale mikhalidwe ya Paradaiso siimapha ululu wa kansa kapena kupweteka m’mfundo zathupi. Chotero mtendere weniweni uyenera kuphatikizapo kuchotsedwa kwa matenda, kudwala, ndi imfa. Kodi chinthu choterocho nchotheka? Pamene anali pa dziko lapansi, Yesu Kristu mobwerezabwereza anawonetsa ukulu wake pa zovutitsa zaumunthu. (Mateyu 8:14-17) Alikumwamba pamalo ake okwezeka, Kristu adzakhoza kuchita zozizwitsa pa dziko lonse lapansi! “Pamenepo,” likulonjeza Baibulo, “maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzayimba.”—Yesaya 33:24; 35:5, 6.
Komabe, ndawala ya Kristu motsutsana ndi tsoka laumunthu siidzaimira pamenepo. Mtumwi Paulo akufotokoza ponena za ufumu wa Kristu kuti: “Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.” (1 Akorinto 15:25, 26) Izi zikutanthauza kukonzanso chivulazo chonse chimene imfa yachititsa pa mtundu wa anthu kuyambira pa chiyambi penipeni. Monga mmene Yesu Kristu iyemwini analongosolera kuti: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [a Kristu] nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Chotero mamiliyoni osaŵerengeka amene akhala ndi moyo ndi kufa m’tsoka adzakhala ndi mwaŵi wokhala ndi phande m’mtendere wa dziko lonse ukudzawo.
Kodi inu mudzakhalamo ndi phande? Mboni za Yehova zikukufulumizani kuphunzira zowonjezereka zimene Baibulo limaphunzitsa kulinga ku zimenezi.b Chiyembekezo cha mtendere wa dziko lonse nchochititsadi chidwi, chenichenidi chosati nkunyalanyazidwa. Khalani wotsimikiziridwa kuti ngati muchita mwamphamvu kuphunzira ndi kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu, “Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu”—kwamuyaya!—Afilipi 4:9.
[Mawu a M’munsi]
a M’lingaliro lenileni, “Nukawone mtendere wa abale ako ndi mtendere wa zoweta.”
b Phunziro la Baibulo lapanyumba laulere lingakonzedwe mwakulembera ofalitsa a magazine ano.
[Chithunzi patsamba 5]
Yehova adzaleketsa nkhondo kufikira “ku malekezero a dziko lapansi”
[Mawu a Chithunzi]
USAF Official Photo
[Chithunzi patsamba 6
Amuna ndi akazi adzaphunzitsidwa kuchitirana mwamtendere