Chifundo cha Yehova Chimatipulumutsa Kukugwiritsidwa Mwala
‘Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga.’—SALMO 51:1.
1, 2. Kodi ndimotani mmene mmodzi wa atumiki a Yehova angayambukidwire ndi tchimo lalikulu?
LAMULO la Yehova silingaswedwe mwaufulu popanda chilango. Zimenezo zimakhala zachiwonekere chotani nanga ngati tachimwira Mulungu tchimo lomvetsa chisoni! Ngakhale kuti tingakhale titatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri, kuswa lamulo lake kungachititse nkhaŵa yaikulu kapena kuchita tondovi kwakukulu. Tingalingalire kuti Yehova watisiya ndi kuti sitirinso oyenerera kumtumikira. Tchimo lathu lingawonekere kukhala ngati thambo la mdima wokhuthala lotsekereza kuunika kwa chiyanjo cha Mulungu.
2 Mfumu Davide wa Israyeli wakale nthaŵi zina anakhala mumkhalidwe wotero. Kodi mkhalidwewo unabuka motani?
Zophophonya Zingatsogolere ku Tchimo Lalikulu
3, 4. Kodi nchiyani chimene chinachitikira mfumu Davide mkati mwa nyengo yakulemera?
3 Davide anakonda Mulungu koma anatenga njira zolakwa zimene zinatsogolera ku machimo aakulu. (Yerekezerani ndi Agalatiya 6:1.) Zimenezi zingachitike kwa munthu aliyense wopanda ungwiro, makamaka ngati iye ali ndi ulamuliro pa ena. Monga mfumu yolemera, Davide anali ndi ulemu ndi mphamvu. Kodi ndani amene akanayesa kukaikira mawu ake? Amuna oyeneretsedwa anali okonzeka ndi ofunitsitsa kumtumikira, ndipo anthu anachita mofunitsitsa zimene anawapempha kuchita. Komabe, Davide analakwa mwakudzichulukitsira akazi ndi kuŵerenga anthu.—Deuteronomo 17:14-20; 1 Mbiri 21:1.
4 Mkati mwa nyengo imeneyi ya kulemera m’zinthu zakuthupi, Davide anapalamula machimo aakulu motsutsana ndi Mulungu ndi munthu. Eya, tchimo limodzi linatsogolera kulinzake mofanana ndi nkhosi zolukanalukana za nsalu zolinganizidwa ndi Satana! Pamene Aisrayeli anzake anali kumenyana nkhondo ndi Aamoni, ali patsindwi pa nyumba yake Davide anawonerera mkazi wokongola wa Uriya, Bateseba, akusamba. Popeza Uriya anali kunkhondo, mfumuyo inaitanitsa mkaziyo kunyumba yake yachifumu ndi kuchita naye chigololo. Tayerekezerani kuvutika kwake maganizo atamva pambuyo pake kuti mkaziyo anali ndi pakati! Davide anaitanitsa Uriya, akumayembekezera kuti akagona usiku ndi Bateseba ndipo akalingalira mimbayo kukhala yake. Ngakhale kuti Davide anamledzeretsa, Uriya anakana kugona ndi mkaziyo. Tsopano atathedwa nzeru, Davide mobisa anatumiza malangizo kwa kazembe wankhondo Yoabu kuti aike Uriya m’mizera yakutsogolo kumene akatsimikizira kuti akaphedwa. Uriya anaphedwa m’nkhondo, mkazi wake wamasiye anachita mwambo wakulira maliro, ndipo Davide anamkwatira anthu asanazindikire kuti ali ndi mimba.—2 Samueli 11:1-27.
5. Kodi chinachitika nchiyani Davide atachimwa ndi Bateseba, ndipo kodi machimo ake anali ndi chiyambukiro chotani pa iye?
5 Kupyolera mwa mneneri Natani, Mulungu anaulula machimo a Davide ndipo anati: “Ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m’nyumba yako ya iwe wekha.” Chotero, mwana wobadwa kwa Bateseba anafa. (2 Samueli 12:1-23) Mwana wamwamuna wachisamba wa Davide, Amnoni, anagwirira chigololo Tamara mlongo wake mwa amayi ena ndipo Amnoni anaphedwa mwambanda ndi mlongo wa Tamara wa mimba imodzi. (2 Samueli 13:1-33) Abisalomu mwana wamwamuna wa mfumu, anayesa kulanda mwachiwembu mpando wachifumu ndipo anachititsa manyazi atate wake mwakugona ndi adzakazi a Davide. (2 Samueli 15:1–16:22) Nkhondo yachiweniweni inachititsa imfa ya Abisalomu ndi chisoni chowonjezereka kwa Davide. (2 Samueli 18:1-33) Komabe, machimo a Davide anamchititsa kukhala wodzichepetsa ndi kumpangitsa kuzindikira kufunika kwa kukhala pafupi ndi Mulungu wake wachifundo. Ngati tingachimwe, tiyeni modzichepetsa tilape ndi kuyandikira kwa Yehova.—Yerekezerani ndi Yakobo 4:8.
6. Kodi nchifukwa ninji Mfumu Davide anali waliwongo mwapadera?
6 Davide anali kwakukulukulu waliwongo chifukwa chakuti anali wolamulira Wachiisrayeli wozindikira kotheratu Chilamulo cha Yehova. (Deuteronomo 17:18-20) Iye sanali farao wa Igupto kapena mfumu ya ku Babulo imene inalibe chidziŵitso chotero ndi imene mwachizoloŵezi ingachite zinthu zosavomerezedwa ndi Mulungu. (Yerekezerani ndi Aefeso 2:12; 4:18.) Monga chiŵalo cha mtundu wodzipatulira kwa Yehova, Davide anazindikira kuti chigololo ndi kupha mwambanda ndizo machimo aakulu. (Eksodo 20:13, 14) Akristu amadziŵanso lamulo la Mulungu. Komabe, mofanana ndi Davide, ena a iwo amaliswa chifukwa cha mkhalidwe wa uchimo wa choloŵa, chifooko chaumunthu, ndi chiyeso chosalamuliridwa. Ngati zimenezo zingachitikire aliyense wa ife, sitifunikira kukhala mumkhalidwe wopanda chiyembekezo umene umadodometsa lingaliro lathu lauzimu ndi kutiloŵetsa m’kugwiritsidwa mwala kwakukulukulu.
Kuulula Kumadzetsa Mpumulo
7, 8. (a) Kodi chinachitikira Davide nchiyani pamene anayesa kubisa machimo ake? (b) Kodi nchifukwa ninji munthuwe uyenera kuulula ndi kusiya tchimo lako?
7 Ngati tiri ndi liwongo la machimo aakulu a lamulo la Mulungu, tingakupeze kukhala kovuta kuulula machimo athu, ngakhale kwa Yehova. Kodi chingachitike nchiyani m’mikhalidwe yotero? Mu Salmo 32, Davide anavomereza kuti: ‘Pamene ndinakhala chete [mmalo mwakuulula] mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu [la Yehova] linandilemera ine; Uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.’ (Vesi 3, 4) Kuyesa kubisa tchimo lake ndi kukanikiza chikumbumtima cha liwongo kunatopetsa Davide wochimwayo. Nkhaŵa inathetsa nyonga yake kwambiri kotero kuti anali wofanana ndi mtengo wa m’chilala wopanda madzi opatsa moyo. M’chenicheni, angakhale atakhala ndi ziyambukiro zovulaza mwa maganizo ndi mwakuthupi. Ndiiko komwe, iye anataya chisangalalo chake. Ngati aliyense wa ife agwera mumkhalidwe wofananawo, kodi tiyenera kuchitanji?
8 Kuulula kwa Mulungu kungabweretse chikhululukiro ndi mpumulo. ‘Ndinavomera choipa changa kwa inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa,’ anaimba motero Davide. ‘Ndinati, ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.’ (Salmo 32:5) Kodi ndinu watondovi chifukwa cha tchimo lobisidwa? Kodi sikukakhala bwino koposa kuliulula ndi kulisiya kotero kuti mulandire chifundo cha Mulungu? Kodi mulekeranji kuitana akulu ampingo ndi kufunafuna kuchiritsidwa kwauzimu? (Miyambo 28:13; Yakobo 5:13-20) Mzimu wanu wakulapa udzavomerezedwa, ndipo m’kupita kwanthaŵi chisangalalo chanu Chachikristu chingabwezeretsedwe. ‘Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake,’ anatero Davide. ‘Wodala munthuyo Yehova samuŵerengera mphulupulu zake; ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo.’—Salmo 32:1, 2.
9. Kodi ndiliti pamene Salmo 51 linalembedwa, ndipo chifukwa ninji?
9 Davide ndi Bateseba anali oŵerengeredwa mlandu kwa Yehova Mulungu wa cholakwa chawo. Ngakhale kuti iwo akanaphedwa chifukwa cha machimo awo, Mulungu anawachitira chifundo. Iye anali wachifundo kwa Davide makamaka chifukwa cha pangano la Ufumu. (2 Samueli 7:11-16) Mkhalidwe wakulapa wa Davide machimo ake ophatikizapo Bateseba ukuwonekera mu Salmo 51. Salmo lomvetsa chisoni limeneli linalembedwa ndi mfumu yolapa pambuyo pakuti Natani anatsitsimula chikumbumtima chake kuwona mlingo waukulu wa machimo ake kulamulo la Mulungu. Panafunikira kulimba mtima kuti Natani asonyeze Davide machimo ake, monga momwedi akulu Achikristu oikidwa ayenera kukhalira olimba mtima kuti achite zinthu zofananazo lerolino. Mmalo mwakulandula chinenezocho ndi kulamula kuti Natani aphedwe, mfumuyo modzichepetsa inavomereza machimowo. (2 Samueli 12:1-14) Salmo 51 limasonyeza zimene ananena kwa Mulungu m’pemphero ponena za zochita zake zochititsa manyazi ndipo nloyenerera kukhala kusinkhasinkha kwa pemphero, makamaka ngati tachimwa ndipo tikulakalaka kupeza chifundo cha Yehova.
Tiri Oŵerengeredwa Mlandu kwa Mulungu
10. Kodi ndimotani mmene Davide akanachirira mwauzimu?
10 Davide sanafunefune kudzikhululukira tchimo lake koma anapempha kuti: ‘Mundichitire ine chifundo Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwaunyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga.’ (Salmo 51:1) Mwa kuchimwa, Davide anali atalumpha malire a Chilamulo cha Mulungu. Komabe, panali chiyembekezo cha kuchira kwake kwauzimu, ngati Mulungu anamsonyeza chiyanjo mogwirizana ndi kukoma mtima kwachifundo Kwake, kapena chikondi chokhulupirika. Kuchuluka kwa nsoni za Mulungu zapitazo kunapatsa mfumu yolapayo maziko akukhulupiririra kuti Mlengi wake akafafaniza machimo ake.
11. Kodi nchiyani chimene chinali nsembe zovomerezedwa pa Tsiku Lachitetezo, ndipo kodi lerolino pamafunika chiyani kuti mupeze chipulumutso?
11 Kupyolera mwa mithunzi yolosera ya nsembe za Tsiku Lachitetezo, Yehova anasonyeza kuti anali ndi njira yakuyeretsera anthu olapa machimo awo. Tsopano tikudziŵa kuti chifundo chake ndi chikhululukiro zimaperekedwa kwa ife pa maziko akukhulupirira kwathu nsembe ya dipo la Yesu Kristu. Ngati Davide, wokhala kokha ndi zitsanzo ndi mithunzi ya nsembe imeneyi m’maganizo, anali wokhoza kudalira kukoma mtima kwachikondi ndi zinsoni za Yehova, koposa kotani atumiki amakono a Mulungu ayenera kusonyeza chikhulupiriro m’dipo loperekedwera chipulumutso chawo!—Aroma 5:8; Ahebri 10:1.
12. Kodi kuchimwa kumatanthauza chiyani, ndipo kodi Davide anamva bwanji ponena za cholakwa chake?
12 Pochonderera kwa Mulungu, Davide anawonjezera: ‘Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa. Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chiri pamaso panga chikhalire.’ (Salmo 51:2, 3) Kuchimwa ndiko kuphonya chandamale cha miyezo ya Yehova. Davide anali atachitadi motero. Komabe, iye sanali wofanana ndi wakupha mwambanda kapena wachigololo amene ali wosadera nkhaŵa za tchimo lake, wongovutika maganizo chifukwa cha chilango chake kapena kuthekera kwa kutenga nthenda. Monga wokonda Yehova, Davide anada choipa. (Salmo 97:10) Iye ananyansidwa ndi tchimo lake lenilenilo ndipo anafuna Mulungu kumyeretsa kotheratu. Davide anali kuzindikira bwino lomwe machimo ake ndipo anali wachisoni kwambiri kuti anali atalola chikhumbo chake cha uchimo kumposa mphamvu. Tchimo lake linali pamaso pake chikhalire, chifukwa chakuti chikumbumtima cha liwongo cha munthu wowopa Mulungu sichimapuma kufikira pakhale kulapa, kuulula, ndi chikhululukiro cha Yehova.
13. Kodi nchifukwa ninji Davide akananena kuti anachimwira Mulungu yekha?
13 Kuvomereza kuŵerengeredwa mlandu kwake kwa Yehova, Davide anati: “Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachita choipacho pamaso panu: kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pakuweruza kwanu.” (Salmo 51:4) Davide anali ataswa malamulo a Mulungu, analuluza malo antchito aufumu, ndipo “mosakaikira anachitira Yehova mwano,” akumapereka mtonzo pa Iye. (2 Samueli 12:14, NW; Eksodo 20:13, 14, 17) Zochita zauchimo za Davide zinalinso kuchimwira chitaganya cha Israyeli ndi ziŵalo za banja lake, monga momwedi wochimwa wobatizidwa lerolino amachititsira chisoni kapena nsautso mumpingo Wachikristu ndi pakati pa okondedwawo. Ngakhale kuti mfumu yolapayo inadziŵa kuti inachimwira anthu anzakewo monga Uriya, iye anazindikira thayo lalikulu kwambiri kwa Yehova. (Yerekezerani ndi Genesis 39:7-9.) Davide anazindikira kuti chiŵeruzo cha Yehova chikakhala cholungama. (Aroma 3:4) Akristu amene achimwa afunikira kukhala ndi lingaliro lofananalo.
Mikhalidwe Yochititsa
14. Kodi ndimikhalidwe yochititsa iti imene inatchulidwa ndi Davide?
14 Ngakhale kuti Davide sanayese kudzilungamitsa, adanena kuti: “Tawonani! Ndinabadwa ndi tchimo ndi zoŵawa za pakubala, ndipo mu uchimo mayi ŵanga anandikhalira ine pakati.” (Salmo 51:5, NW) Davide anabadwira m’cholakwa, ndipo amake anali ndi zoŵawa zapakubala chifukwa cha mkhalidwe wauchimo wa choloŵa. (Genesis 3:16; Aroma 5:12) Mawu ake samatanthauza kuti maunansi aukwati oyenerera, kutenga mimba, ndi kubadwa nzauchimo, chifukwa chakuti Mulungu anapereka ukwati ndi kubala ana; ndiponso Davide sanali kulankhula za tchimo lenileni lirilonse la amake. Amake anali ndi pathupi pake mu uchimo chifukwa chakuti makolo akewo anali auchimo mofanana ndi anthu onse opanda ungwiro.—Yobu 14:4.
15. Ngakhale kuti Mulungu angapende mikhalidwe yochititsayo, kodi nchiyani chimene sitiyenera kuchita?
15 Ngati ife tachimwa, tingathe kutchula m’pemphero kwa Mulungu mikhalidwe iriyonse yochititsa imene ingakhale itasonkhezera kuchita kwathu cholakwa. Koma sitiyenera kusanduliza kukoma mtima kwapadera kwa Mulungu kukhala chodzikhululukira kuchitira kusadziletsa kapena kugwiritsira ntchito mkhalidwe wauchimo wobadwa nawo kukhala chotchinga chakubisalako kuti tisakhale ndi thayo la uchimo wathu. (Yuda 3, 4) Davide anavomereza thayo lakulola malingaliro odetsedwa ndi kugonjera ku chiyeso. Tiyeni tipemphere kuti tisaloledwe kuloŵa m’chiyeso ndiyeno tichitepo kanthu mogwirizana ndi pempherolo.—Mateyu 6:13.
Pempho la Kuyeretsedwa
16. Kodi ndimkhalidwe wotani umene Mulungu amakondwerera, ndipo kodi zimenezo ziyenera kuyambukira motani khalidwe lathu?
16 Anthu angawonekere kukhala anthu abwino odzipereka kwa Mulungu, koma Mulungu amayang’ana zakuya ndipo amawona chimene iwo ali mkati. Davide anati: ‘Wonani, Inu [Yehova] mukondwera ndi zowonadi mmalo a m’katimo; ndipo mmalo a m’tseri mudzandidziŵitsa nzeru.’ (Salmo 51:6) Davide anali ndi liwongo la kunama ndi lakuchita chiwembu polinganiza imfa ya Uriya ndi kuyesa kubisa maumboni onena za kutenga mimba kwa Bateseba. Komabe, iye anadziŵa kuti Mulungu amakondwera ndi chowonadi ndi chiyero. Zimenezi ziyenera kuyambukira khalidwe lathu mwanjira yabwino, pakuti Yehova akatitsutsa ngati tinali achiwembu. (Miyambo 3:32) Davide anazindikiranso kuti ngati Mulungu anati ‘amchititse kudziŵa nzeru,’ monga mfumu yolapa, akakhoza kuchita mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu m’mbali yonse yathunthu ya moyo wake.
17. Kodi nchiyani chimene chinali tanthauzo la kupempherera kuyeretsedwa ndi hisope?
17 Chifukwa chakuti wamasalmo anawona kufunikira kwake chithandizo cha Mulungu pogonjetsa zikhoterero za uchimo, iye anawonjezera kuchonderera kuti: “Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera: munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala.” (Salmo 51:7) Pakati pa zinthu zina, chomera cha hisope (mwinamwake marjoram, kapena Origanum maru) chinagwiritsidwa ntchito m’dzoma lakuyeretsa anthu amene kale anali ogwidwa ndi matenda akhate. (Levitiko 14:2-7) Chotero kunali koyenerera kuti Davide ayenera kupemphera kuti ayeretsedwe tchimolo ndi hisope. Lingaliro lachiyero liri logwirizanitsidwanso ndi pempho lake lakuti Yehova amtsuke kuti akhale wosadetsedwa kotheratu, woyera mbu kuposadi chipale chopanda mwaye kapena zinyalala zina. (Yesaya 1:18) Ngati aliyense wa ife tsopano akuvutika ndi zoŵawa za chikumbumtima chifukwa cha cholakwa chirichonse, tiyeni tikhale ndi chikhulupiriro chakuti ngati molapa tifunafuna chikhululukiro cha Mulungu, iye angathe kutiyeretsa ndi kutitsuka pa maziko a nsembe ya dipo ya Yesu.
Pempho la Kubwezeretsedwa
18. Kodi mkhalidwe wa Davide asanalape ndi kuulula machimo unali wotani, ndipo kodi kuzindikira zimenezi kungakhale kothandiza motani lerolino?
18 Mkristu aliyense amene anakanthidwapo ndi chikumbumtima cha liwongo angazindikire mawu a Davide akuti: “Mundimvetse chimwemwe [Yehova] ndi kusekera: kuti mafupawo munawatyola akondwere.” (Salmo 51:8) Davide asanalape ndi kuulula machimo ake, chikumbumtima chake chovutitsidwa chinamsautsa. Iye sanapezedi chisangalalo m’nyimbo zakukondwera ndi kusangalala zoimbidwa ndi oimba nyimbo abwino ndi oimba ndi zoimbira aluso. Chotero ululu wa Davide wochimwayo unali waukulu kwambiri chifukwa cha kupanda chivomerezo cha Mulungu kotero kuti anali ngati munthu amene mafupa ake anaphwanyidwa momvetsa ululu. Iye analakalaka kukhululukidwa, kuchira kwauzimu, ndi kubwezeretsedwera chisangalalo chimene anali nacho poyamba. Wochita cholakwa wolapa lerolino afunikiranso chikhululukiro cha Yehova kotero kuti apezenso chisangalalo chimene anali nacho poyamba asanachite chinthu chirichonse chimene chimaika pachiswe unansi wake ndi Mulungu. Kubwezeretsedwa kwa ‘chisangalalo cha mzimu woyera’ kwa munthu wolapa kumasonyeza kuti Yehova wamkhululukira ndipo amamkonda. (1 Atesalonika 1:6) Zimenezo zimabweretsa chitonthozo chotani nanga!
19. Kodi ndimotani mmene Davide akamverera ngati Mulungu anafafaniza mphulupulu zake zonse?
19 Ndiponso Davide anapemphera kuti: “Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga, ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.” (Salmo 51:9) Yehova sakanayembekezeredwa kuyang’ana pa uchimo movomereza. Chifukwa chake, iye anapemphedwa kubisa nkhope yake pa machimo a Davide. Mfumuyo inapemphanso kuti Mulungu afafanize mphulupulu zake zonse, achotse chisalungamo chake chonse. Ngati kokha Yehova akanachita zimenezo nanga! Kukatsitsimula mikhalidwe ya Davide kuchotsa mtolo wa chikumbumtima chovutitsidwa, ndi kulola mfumu imene tsopano inalapa kudziŵa kuti inakhululukiridwa ndi Mulungu wake wachikondi.
Bwanji Ngati Mwachimwa?
20. Kodi chikuvomerezedwa nchiyani kuti Mkristu aliyense amene wachita tchimo lalikulu achite?
20 Salmo 51 limasonyeza kuti alionse a atumiki odzipatulira a Yehova amene achita tchimo lalikulu koma amene ali olapa angampemphe mwachidaliro kuti awasonyeze chiyanjo ndi kuwatsuka tchimo lawo. Ngati inu muli Mkristu amene walakwa mwanjira yotero, kodi mulekeranji kufunafuna chikhululukiro cha Atate wathu wakumwamba m’pemphero lodzichepetsa? Vomerezani kufunikira kwanu chithandizo cha Mulungu kotero kuti mukhale ovomerezedwa pamaso pake, ndipo pemphani kuti abwezeretse chisangalalo chanu choyamba. Akristu olapa angapite kwa Yehova mwachidaliro m’pemphero ndi mapempho otero, pakuti “adzakhululukira koposa.” (Yesaya 55:7; Salmo 103:10-14) Ndithudi akulu ampingo ayenera kuitanidwa kotero kuti akhoze kupereka chithandizo chauzimu chofunikacho.—Yakobo 5:13:15.
21. Kodi tidzapenda chiyani chotsatira?
21 Chifundo cha Yehova chimapulumutsa anthu ake kukugwiritsidwa mwala. Koma tiyeni tipende mapempho ena ochokera pansi pa mtima a Davide wolapayo mu Salmo 51. Phunziro lathu lidzasonyeza kuti Yehova samapeputsa mtima wosweka.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi nchiyambukiro chotani chimene tchimo lalikulu lingakhale nacho pa mmodzi wa atumiki a Yehova?
◻ Kodi ndimotani mmene Davide anayambukiridwira pamene anayesa kubisa tchimo lake?
◻ Kodi nchifukwa ninji Davide ananena kuti anachimwira Mulungu yekha?
◻ Ngakhale kuti Mulungu angapende mikhalidwe yochititsayo ngati tichimwa, kodi sitiyenera kuchita chiyani?
◻ Kodi Mkristu ayenera kuchitanji ngati wachita tchimo lalikulu?