Kulemera Kungayese Chikhulupiriro Chanu
KULEMERA kungayese chikhulupiriro cha munthu wolungama. Kukalimirira kulemera kwakuthupi kungataitse wina chikhulupiriro. (1 Timoteo 6:9, 10) Koma kulemera kungayesenso chikhulupiriro mwanjira ina. Pamene munthu wolungama awona kuti anthu ambiri osalungama akulemera mwa zinthu zakuthupi pamene iye akusauka, angayesedwe kufuna kulondola njira yosakhala yaumulungu. Eya, ichi chachititsa ngakhale ena a atumiki a Yehova kukayikira phindu la kulondola moyo wa mtima wolungama!
Zimenezi zinachitika kwa woimba nyimbo Wachilevi Asafu mkati mwa kulamulira kwa Davide, mfumu ya Israyeli. Asafu anapeka masalmo amene anagwiritsiridwa ntchito m’kulambira kwapoyera. Limodzi ndi Hemani ndi Yedutuni, iye ananeneranso, akumatamanda ndi kuyamikira Yehova Mulungu ndi nyimbo zamalimba. (1 Mbiri 25:1; 2 Mbiri 29:30) Chinkana kuti Asafu anali ndi mwaŵi waukulu, Salmo 73 limasonyeza kuti kulemera kwa anthu oipa kunakhaladi chiyeso chachikulu pa chikhulupiriro chake.
Mkhalidwe Wamaganizo Waupandu wa Asafu
“Indedi Mulungu achitira Israyeli zabwino, iwo a mtima wa mbe. Koma ine, ndikadagwa; mapazi anga akadaterereka.” (Salmo 73:1, 2) Mwa mawuŵa, Asafu anazindikira kuti Yehova anali wabwino kwa mtundu wa Israyeli. Anali wotero makamaka kwa awo “a mtima wa mbe,” popeza kuti chinali chikhumbo chawo kudzipereka kotheratu kwa Mulungu ndi kuthandizira kuyeretsa dzina lake loyera. Ngati tikhala ndi mkhalidwe wa maganizo wofananawo, tidzadalitsa Yehova mwakulankhula zabwino ponena za iye ngakhale ngati tikuyesedwa ndi kulemera kwa anthu oipa kapena mkhalidwe wina uliwonse.—Salmo 145:1, 2.
Ngakhale kuti Asafu anali kudziŵa za ubwino wa Yehova, mapazi ake anatsala pang’ono kuterereka panjira yolungama. Kunali ngati kuti anali kuterereka panjira yamatope pochita makani othamanga mtunda wautali. Kodi nchifukwa ninji chikhulupiriro chake chinafooka motero? Iye analongosola kuti: “Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa. Pakuti palibe zomangira pakufa iwo: ndi mphamvu yawo njolimba. Savutika monga anthu ena; sasautsika monga anthu ena.”—Salmo 73:3-5.
Kulemera ndi zinthu zakuthupi kwa anthu osalungama kunachititsa nsanje Asafu. Iwo anawoneka kukhala ndi moyo wamtendere, ngakhale kuti anapeza chuma chawo mwanjira zosayenera. (Yerekezerani ndi Salmo 37:1.) Mosasamala kanthu za ntchito zawo zoipa, mwamawonekedwe akunja iwo anali achisungiko. Eya, anawonekera kumafa imfa yabwinopo! Iwo nthaŵi zina anafa mwamtendere ndi otsimikizirika mumtima, popanda kuzindikira kusoŵa kwawo kwauzimu. (Mateyu 5:3) Kumbali ina, ena a atumiki a Mulungu amavutika ndi matenda ozunza ndi kufa imfa yoŵaŵitsa, koma iye amawachilikiza, ndipo ali ndi chiyembekezo chabwino koposa cha chiukiriro.—Salmo 43:1-3; Yohane 5:28, 29.
Anthu oipa ambiri alibe mavuto athanzi amene angawaletse kusangalala ndi zakudya zawo zambiri. “Mphamvu yawo njolimba,” ndipo mimba zawo zichita khweve! Ndiponso, iwo “savutika monga anthu ena,” pakuti mosiyana ndi anthu ambiri, iwo savutika kuti apeze zofunika za moyo. Asafu anatsimikiza kuti oipa “sasautsika monga anthu ena.” Iwo makamaka samakhala ndi ziyeso zimene anthu opembedza amakumana nazo chifukwa chakuti opembedzawo amamamatira pa miyezo yolungama ya Yehova m’dziko loipa la Satana.—1 Yohane 5:19.
Chifukwa cha kulemera kwa oipa, Asafu anapitiriza kumati za iwo: “Chifukwa chake kudzikuza kunga unyolo pakhosi pawo; achivala chiwawa ngati malaya. Kunenepa kwawo kutuzulitsa maso awo: malingaliro a mitima yawo asefukira. Achita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa: alankhula modzitama. Pakamwa pawo anena zam’mwamba, ndipo lilime lawo liyendayenda m’dziko lapansi.”—Salmo 73:6-9.
Oipa amavala kudzikuza monga “unyolo pakhosi pawo,” ndipo ntchito zawo zachiwawa nzochuluka moti ‘azivala ngati malaya.’ Pofuna kutsatira njira yawoyawo, amalankhula moipa za ena. Maso a oipa samagobeka chifukwa cha kuwonda koma ‘amatudzuka chifukwa cha kunenepetsa,’ akumatong’oka chifukwa cha kunenepetsa kochititsidwa ndi madyaidya. (Miyambo 23:20) Ziwembu zawo nzopambana kwambiri kwakuti zimaposadi ‘malingaliro a mitima yawo.’ Amalankhula za chinyengo chawo monyada ndi “modzitama.” Eya, ‘pakamwa pawo palankhula za m’mwamba, ndipo lilime lawo liyendayenda m’dziko lapansi’! Pokhala opanda ulemu kwa aliyense m’mwamba ndi padziko lapansi, amachitira mwano Mulungu ndi kuchitira dumbo anthu.
Mwachiwonekere, sanali Asafu yekha amene anakhudzidwa moipa ndi zimene anawona. Iye anati: “Chifukwa chake anthu ake amabwera kudza kuno: ndipo chikho chodzala ndi madzi achigugudiza. Namati, Akachidziŵa bwanji Mulungu? Kodi Wam’mwambamwamba ali nayo nzeru?” (Salmo 73:10, 11) Lemba Lachihebri lingakhale likutanthauza kuti chifukwa chakuti oipa akuwonekera kukhala akulemera, ena mwa anthu a Mulungu amakhala ndi kawonedwe kolakwa nakhala mumkhalidwe wofanana ndi osayeruzikawo, akumanena kuti: ‘Mulungu sakudziŵa zimene zikuchitika ndipo sadzachitapo kanthu motsutsana ndi osayeruzikawo.’ Kumbali ina, kuwona anthu oipa akuchita kusayeruzika namawonekera kusakumana ndi chilango kumafanana ndi kumwa mankhwala oŵaŵa, kumene kumachititsa wolungama kufunsa kuti: ‘Kodi Mulungu akuloleranji zinthu zimenezi? Kodi sakuwona zimene zikuchitika?’
Atayerekezera mikhalidwe yake ndi ija ya anthu oipa, Asafu anati: “Tapenyani, oipa ndi awa; ndipo pokhazikika chikhazikikire awonjezerapo pa chuma chawo. Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe, ndipo ndinasamba m’manja mosalakwa; popeza andisautsa tsiku lonse, nandilanga mamaŵa monse.” (Salmo 73:12-14) Asafu analingalira kuti kunali kopanda pake kukhala ndi moyo wolungama. Anthu oipa analemera, mwachiwonekere ‘akumawonjezera chuma chawo’ mwanjira zosalungama. Iwo anawonekera kumapulumuka chilango pa zochita zawo zoipitsitsa, koma Asafu anavutika ‘tsiku lonse’—kuchokera pouka m’maŵa mpaka pokagona usiku. Anawona ngati kuti Yehova anali kumuwongolera m’maŵa uliwonse. Popeza kuti zimenezi sizinawoneke kukhala chilungamo, zinayesa chikhulupiriro cha Asafu.
Kuwongolera Kalingaliridwe
Potsirizira pake atazindikira kuti kalingaliridwe kake kanali kolakwa, Asafu anati: “Ndikadati, ndidzafotokozera chotere, Taonani, ndikadachita chosakhulupirika ndi mbadwo wa ana ako. Pamene ndinayesa kudziŵitsa ichi, ndinavutika nacho; mpaka ndinaloŵa m’zoyera za Mulungu, ndi kulingalira chitsiriziro chawo. Indedi muwaika poterera: muwagwetsa kuti muwaononge. Ha! m’kamphindi ayesedwa bwinja; athedwa konse ndi zowopsa. Monga anthu atauka, apepula loto; momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa chithunzithunzi chawo.”—Salmo 73:15-20.
Zinali bwino kuti Asafu sanatchule mawu oŵiringula, popeza kuti mwakunena poyera kuti kutumikira Yehova kunali kopanda pake, akanalefula ziŵalo za banja lake la olambira kapena kudodometsa chikhulupiriro chawo. Nkwabwinopo chotani nanga kukhala chete ndi kuchita mofanana ndi Asafu! Kuti awone chifukwa chake oipa anawonekera kupulumuka chilango ndi ntchito zawo zoipa pamene olungama anavutika, iye anapita ku malo opatulika a Mulungu. Mkhalidwe wa malowo unalola Asafu kusinkhasinkha modekha ali pakati pa alambiri a Yehova, ndipo kalingaliridwe kake kanawongokera. Chotero lerolino, ngati tivutitsidwa ndi zimene tawona, mofananamo tifune mayankho pamafunso athu mwakuyanjana ndi anthu a Mulungu m’malo mwakudzilekanitsa tokha.—Miyambo 18:1.
Asafu anafika pakuzindikira kuti Mulungu anaika oipa “poterera.” Chifukwa chakuti miyoyo yawo inasumikidwa pa zinthu zakuthupi, iwo ali paupandu wakuyang’anizana ndi kugwa kwadzidzidzi. Potsirizira pake, imfa idzawapeza paukalamba, ndipo chuma chawo chopezedwa mosayenera sichidzawatalikitsira moyo wawo. (Salmo 49:6-12) Kulemera kwawo kudzakhala ngati loto losakhalitsa. Chiweruzo cholungama chikhozanso kuwapeza asanakalambe kuti atute zimene anafesa. (Agalatiya 6:7) Popeza kuti afulatira dala Uyo yekha amene akhoza kuwathandiza, iwo ali osoŵa chochita, opanda chiyembekezo. Pamene Yehova achitapo kanthu motsutsana nawo, adzanyansidwa ndi “chithunzithunzi chawo”—kutchuka kwawo ndi malo awo.
Samalani ndi Mmene Muchitira
Popeza kuti sanachite bwino pazimene anawona, Asafu anavomereza kuti: “Pakuti mtima wanga udaŵaŵa, ndipo ndinalaswa m’impso zanga; ndinali wam’thengo, wosadziŵa kanthu; ndinali ngati nyama pamaso panu. Koma ndikhala ndi Inu chikhalire: mwandigwira dzanja langa la manja. Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira m’ulemerero.”—Salmo 73:21-24.
Kusumika maganizo pakulemera kwakuthupi kwa anthu oipa ndi pakuvutika kwa anthu olungama kungaŵaŵitse mtima wa munthu kapena kumkwiitsa. Mkati mwake—mu impso zake—kuvutika kwa Asafu pamkhalidwe umenewo kunamchititsa kupweteka kwakukulu. Kwa Yehova, iye anakhala ngati nyama yosalingalira ikumachita malinga ndi kupsa mtima. Komabe, Asafu ‘anali ndi Mulungu nthaŵi zonse, amene anamgwira dzanja lake lamanja.’ Ngati tilakwa m’kalingaliridwe kathu koma tifunafuna uphungu wa Yehova monga momwe Asafu anachitira, Mulungu adzatigwira dzanja lathu lamanja, kutigwirizira ndi kutitsogolera. (Yerekezerani ndi Yeremiya 10:23.) Ifeyo tingatsogoleredwe mtsogolo mwachimwemwe kokha pamene tigwiritsira ntchito uphungu wake. Tingachititsidwe manyazi kwa nthaŵi yakutiyakuti, koma Yehova adzasanduliza zinthu, ‘kutipatsa ulemerero,’ kapena ulemu.
Pozindikira kufunika kwa kudalira pa Yehova, Asafu anawonjezera kuti: “Ndili ndi yani kumwamba, koma Inu? Ndipo padziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu. Likatha thupi langa ndi mtima wanga: Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha. Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzawonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu. Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu: ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.”—Salmo 73:25-28.
Mofanana ndi Asafu, tilibe aliyense koma Yehova amene tiyenera kumdalira kaamba ka chitetezo chowona ndi chitonthozo. (2 Akorinto 1:3, 4) Chotero, m’malo mwakusirira chuma cha wina cha padziko lapansi, tiyeni titumikire Mulungu ndi kusungira chuma chathu kumwamba. (Mateyu 6:19, 20) Kukhala ndi kaimidwe kovomerezedwa pamaso pa Yehova kuyenera kukhala chisangalalo chathu chachikulu koposa. Ngakhale ngati thupi lathu ndi mtima zingalephere, iye adzatilimbitsa ndi kutipatsa kukhazikika kwa mtima kuti tisataye chiyembekezo ndi kulimbika kwathu pakati pa adani. Unansi wathu wathithithi ndi Yehova uli chuma cha mtengo wapatali koposa. Kuulola kutaika kukatanthauza tsoka kwa ife limodzi ndi ena onse amene amamsiya iye. Chotero mofanana ndi Asafu, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi kumsenzetsa nkhaŵa zathu zonse. (1 Petro 5:6, 7) Zimenezi zimachilikiza ubwino wathu wauzimu ndi kutisonkhezera kuuza ena ponena za ntchito zodabwitsa za Yehova.
Khalanibe Wokhulupirika kwa Yehova
Asafu anavutika mtima chifukwa cha kuwona anthu oipa akulemera m’Israyeli, dziko lakelake. Pakati pa atumiki okhulupirika a Yehova, panali “anthu oipa” odzitama, odzikweza, achiwawa, otonza, ndi apyuta, ndi amene analingalira kuti Mulungu sanadziŵe zimene anali kuchita. (Salmo 73:1-11) Ha, limenelo ndichenjezo lotani nanga! Kuti tikondweretse Yehova Mulungu, tiyenera kuleka kusonyeza mikhalidwe yoteroyo monga kunyada, chiwawa, kunyodola, ndi kusawona mtima. Mofanana ndi Asafu, atumiki a Yehova onse ‘aloŵetu m’zoyera za Mulungu’ mwakusonkhana mokhazikika ndi alambiri Ake okhulupirika. Indedi, okonda Yehova onse ‘ayandikire kwa Mulungu,’ akumadalira pa iye kuti awachilikize pakati pa mavuto, mosasamala kanthu ndi zimene ena anganene kapena kuchita.—Salmo 73:12-28; 3 Yohane 1-10.
Zowona, kulemera kwakuthupi kwa anthu oipa kungayese chikhulupiriro chathu, monga mmene kunayesera cha Asafu. Komabe, tikhoza kupirira chiyeso chimenechi ngati tisumika moyo wathu pa utumiki wa Yehova. Tidzafupidwa mwakuchita chimenechi chifukwa chakuti ‘Mulungu sali wosalungama kotero kuti aiŵale ntchito zathu ndi chikondi chimene tichisonyeza pa dzina lake.’ (Ahebri 6:10) Ziyeso zathu zidzakhala ‘zakanthaŵi ndi zofeŵa’ poziyerekezera ndi mphotho yathu. (2 Akorinto 4:17) Ngakhale zaka 70 kapena 80 zakuvutika zimapita msanga ngati mpweya chabe wa mluzu pamilomo pathu pamene tiziyerekezera izo ndi moyo wachimwemwe wamuyaya umene Yehova walonjeza atumiki ake okhulupirika.—Salmo 90:9, 10.
Tisalole konse kulemera kwa anthu oipa pamene ife tikuvutika chifukwa cha chilungamo kuti kutiletse kusonyeza chikhulupiriro chimene chili chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23; 1 Petro 3:13, 14) Satana adzakondwera ngati tifanana ndi anthu oipa, amene kaŵirikaŵiri amalemera chifukwa cha kusawona mtima. M’malo mwake, tiyeni tilemekeze dzina la Yehova mwakukaniza ziyeso zakuleka miyezo yake yolungama. (Zefaniya 2:3) Tisavutike mtima konse ndi chipambano cha ochita zoipa, popeza kuti, zoposa zimene angapeze ndizo kokha chuma chakuthupi. Ndipo kodi chimenecho nchaphindu lotani? Sichingayerekezeredwe konse ndi kulemera kwauzimu kumene kuli ndi awo osonyeza chikhulupiriro mwa Ambuye Mfumu Yehova.