Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 5/15 tsamba 32
  • ‘Ndidzathaŵira kwa Mulungu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Ndidzathaŵira kwa Mulungu’
  • Nsanja ya Olonda—1997
Nsanja ya Olonda—1997
w97 5/15 tsamba 32

‘Ndidzathaŵira kwa Mulungu’

MU “Nthawi zoŵaŵitsa” zino, ziyeso ndiponso zosonkhezera kuchita zoipa zikunka nzichuluka. Mwachitsanzo, kuona mtima kwathu, kungayesedwe ku ntchito. Chiyero chathu chingayesedwe pakati pa anzathu akusukulu. Ndipo kusunga umphumphu kwathu kaŵirikaŵiri kumayesedwa ndi dziko la makhalidwe oipali.​—2 Timoteo 3:1-5.

Mlembi wa Baibulo Asafu nayenso analiko panthaŵi imene kuipa kunali kutafalikira. Ena a m’nthaŵi yake anafika ngakhale pakudzitama chifukwa cha khalidwe lawo losaopa Mulungu. “Kudzikuza kunga unyolo pakhosi pawo” analemba motero Asafu. “Achivala chiwawa ngati malaya. Achita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa: alankhula modzitama.”​—(Salmo 73:6, 8) Kodi khalidwe ili likuoneka kukhala lozoloŵereka?

Kwa amene amafuna kumachita zabwino, khalidwe lotereli nlosautsa kwambiri, ngakhale lokhumudwitsa. “Andisautsa tsiku lonse,” Asafu anadandaula. “Ndinavutika nacho.” (Salmo 73:14, 16) Inu mungamve mofananamo, koma musataye mtima! Asafu anatha kulimbana ndi kuipa kwa m’tsiku lake, ndipo inunso mungachite mofananamo. Koma motani?

Asafu anafikira pozindikira kuti sikwapafupi kuti chilungamo chenicheni chikhalepo muulamuliro wopanda ungwiro wa munthu. (Salmo 146:3, 4; Miyambo 17:23) Choncho, m’malo motaya nthaŵi yake yofunikayo, mphamvu, ndi chuma kulimbana ndi kuipa komzungulira, anaika maso pa ubwenzi wake ndi Mulungu. Asafu anati: “Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu: ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine.”​—Salmo 73:28.

Lero, amene amachita katangale m’malonda kaŵirikaŵiri amasangalala ndi chuma. Ambiri angafike ngakhale podzitama chifukwa cha kunyalanyaza kwawo malamulo a makhalidwe abwino a Mulungu. Koma sikuti adzazichita zimenezi kwamuyaya. “Indedi muwaika poterera,” anatero Asafu. “Muwagwetsa kuti muwawononge.”​—Salmo 73:18.

Inde, panthaŵi yake Mulungu adzathetsa, ukathyali, chiwawa, ndi ukatangale, kuphatikizapo machitidwe onse a kusaopa Mulungu amene Akristu oona ayenera kupewa. Baibulo limalonjeza kuti: “Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.” (Salmo 37:9) Pakali pano, tibwerezetu mawu a wamasalmo yemwe anati: “Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira iye [“ndidzathaŵira kwa iye,” NW].”​—Salmo 18:2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena