-
Yehova, Wochita Zinthu ZodabwitsaNsanja ya Olonda—1992 | December 15
-
-
Ubwino wa Yehova
8. Kodi ndikuzoloŵerana kotani kumene tingakhale nako ndi Yehova, ndipo kodi iye wasonyeza motani ubwino wake?
8 Davide akupereka pemphero lina lochonderera kuti: “Inu, O Yehova, ndinu wabwino ndi wokhululuka msanga; ndi wachifundo chochuluka kwa onse oitanira pa inu. Tcherani khutu, O Yehova, kupemphero langa; ndipo mvetserani mawu a mapembedzero anga. M’tsiku la nsautso yanga ndidzaitana pa inu, pakuti mudzandiyankha.” (Salmo 86:5-7, NW) “O Yehova”—mobwerezabwereza tikuchita chidwi chotani nanga ndi mawu osonyeza kuzoloŵerana amenewa! Ndiko kuzoloŵerana kumene kungakulitsidwe mosalekeza kupyolera mwa pemphero. Davide anapemphera panyengo ina kuti: “Musakumbukire zolakwa zaubwana wanga kapena zopikisana nanu: mundikumbukire monga mwachifundo chanu, chifukwa chaubwino wanu, Yehova.” (Salmo 25:7) Yehova ndiye chitsanzo chenicheni chaubwino—m’kupereka dipo la Yesu, m’kusonyeza chifundo kwa ochimwa olapa, ndi m’kusonyeza kukoma mtima kwachikondi kwa Mboni zake zokhulupirika ndi zoyamikira.—Salmo 100:3-5; Malaki 3:10.
-
-
Yehova, Wochita Zinthu ZodabwitsaNsanja ya Olonda—1992 | December 15
-
-
10. Kodi ndiulemu wotani umene bukhu la Masalmo limapereka pa kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova?
10 Bukhu la Masalmo limatchula ‘kukoma mtima kwa chikondi’ kwa Yehova nthaŵi zoposa zana. Kukoma mtima kwachikondi kotero nkochulukadi! M’mavesi ake anayi oyamba, Salmo 118 limapempha atumiki a Mulungu kuyamika Yehova, likumabwereza nthaŵi zinayi kuti “pakuti chifundo chake chachikondi chiri kunthaŵi zosadziŵika, (NW).” Salmo la 136 limagogomezera mkhalidwe wabwino koposawo wa ‘kukoma mtima kwake kwachikondi’ nthaŵi 26. Mulimonse mmene tingachimwire—ndipo monga momwe Yakobo 3:2 akunenera, “timakhumudwa tonse pazinthu zambiri”—tikhaletu okonzekera kufunafuna chikhululukiro cha Yehova, tiri ndi chidaliro cha chifundo chake ndi kukoma mtima kwachikondi. Kukoma mtima kwake kwachikondi ndiko chisonyezero chachikondi chake chokhulupirika kwa ife. Ngati ife tipitirizabe mokhulupirika kuchita chifuniro chake, iye adzasonyeza chikondi chake chokhulupirika mwakutilimbikitsa kuti tigonjetse chiyeso chirichonse.—1 Akorinto 10:13.
-