Kodi Mumakumbukira?
Kodi mwapereka chisamaliro chachikulu ku makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati mwatero, mwinamwake mudzakupeza kukhala kokondweretsa kukumbukira zotsatirazi:
▫ Kodi nchiyani chimene chili “chizindikiro chotanthauza ubwino” chimene Yehova amachitira otsatira mapazi a Yesu? (Salmo 86:17, NW)
Chinali “chisangalalo cha mzimu woyera” chimene chinalimbikitsa Akristu oyamba kupirira mitundu yosiyanasiyana ya zizunzo zimene zinawagwera. (1 Atesalonika 1:6) Zili zofanana lerolino, ndipo Yehova, Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro,” amakondwera ‘kupatsa mzimu woyera kwa iwo akumpempha iye.’ (Yakobo 1:17; Luka 11:13) Chotero chili chisangalalo cha mzimu woyera chimene chili “chizindikiro chotanthauza ubwino” kwa otsatira a Yesu.—12/15, masamba 18-19.
▫ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti ife tivomereze lingaliro la Mulungu lonena za kunama?
Salmo 5:6 limanena kuti Mulungu ‘adzawononga iwo akunena bodza.’ Chivumbulutso 21:8 chimanenanso kuti choikidwiratu cha abodza onse ndicho “imfa yachiŵiri.” Chifukwa chake, kuvomereza lingaliro la Mulungu lonena za kunama kumatipatsa chifukwa champhamvu cha kulankhulira chowonadi ndipo chotero kulandira mphatso yake ya moyo.—12/15, tsamba 23.
▫ Kodi nchiyani chimene chinali mpangidwe wakulambira wa Asamariya? (Yohane 4:20)
Asamariya, m’kulambira kwawo kosanganikira, anavomereza monga Malemba mabuku asanu okha oyamba a Mose, Pentateuch. Pafupifupi zaka za zana lachinayi B.C.E., iwo anamanga kachisi pa phiri la Gerizimu, mopikisana ndi kachisi wa Mulungu m’Yerusalemu. Ngakhale kuti kachisi wa Asamariya anawonongedwa, kufikira lerolino iwo amachitira phwando lachaka ndi chaka la Paskha pa Gerizimu.—1/1, tsamba 25.
▫ Kodi Akristu amafunikira kupititsa patsogolo zolinganiza za kuletsa kuipitsidwa kwa malo kapena kuyeretsa?
Pamene anali padziko lapansi, Yesu sanayese kuthetsa mavuto onse a anthu m’tsiku lake. Pamene Yehova kupyolera mwa Ufumu wake Waumesiya achilikiza malamulo ake amkhalidwe olungama pamlingo wadziko lonse, mavuto a malo okhala adzathetsedwa kwachikhalire. Chifukwa chake, Mboni za Yehova zimakhala ndi lingaliro lachikatikati. Kukonda mnansi kumazisonkhezera kusonyeza ulemu pa chuma cha ena, koma moyenerera iwo amaika kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu patsogolo. (Mateyu 6:33)—1/1, tsamba 31.
▫ Kodi ndi m’njira yotani mmene Yesu anatumikira monga wonyamula kuunika? (Yohane 8:12)
Yesu anadzipereka ku kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43; Yohane 18:37) Iye anavumbulanso mabodza achipembedzo ndipo chotero anapereka ufulu wauzimu kwa awo ogwidwa ukapolo wachipembedzo. (Mateyu 15:3-9) Iye anatsimikizira mwapadera, kukhala kuunika kwa dziko mwakupereka moyo wake waumunthu wangwiro monga dipo. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16)—1/15, masamba 10-11.
▫ Kodi nzifukwa zina ziti zimene tiyenera kukhalira ogonjera kwa Yehova Mulungu?
Yehova ali Mfumu ya Chilengedwe, ndipo pachifukwa chimenechi ali ndi kuyenera kwakuti ife timgonjere. Ndiponso, popeza kuti Yehova ngwamphamvu yonse, palibe aliyense amene mwachipambano angatsutsane naye, chotero sitingathe kunyalanyaza chigonjero chathu kwa iye. Zolengedwa zonse za luntha zinalengedwa kutumikira chifuno cha Mpangi wawo, ndipo izi zikuika onse kukhala ndi thayo lakudzigonjetsera kwa Mulungu m’mbali zonse.—2/1, masamba 10-11.
▫ Kodi nchiyani chinathandiza Yosefe kukana kuchita dama ndi mkazi wa Potifara?
Yosefe anali ndi nyonga yamphamvu yosonkhezera maganizo ake. Iye anali kuzindikira unansi wake ndi Yehova ndipo anazindikira kuti kuchita dama kukakhala kuchimwira osati mwamuna wa mkazi yekhayo, koma chowopsa kwambiri, kuchimwira Mulungu.—2/15, tsamba 21.
▫ Kodi Yesu anatanthauzanji pamene anati: “Ndine . . . chowonadi”? (Yohane 14:6)
Yesu sanalankhule kokha ndi kuphunzitsa chowonadi; iye anachikhalira moyo nakhala chitsanzo chake. Chotero, Chikristu sichili kokha lingaliro; chili njira ya moyo.—3/1, tsamba 15.
▫ Kodi ndiphunziro lotonthoza lotani limene lili m’Salmo 51?
Salmo limeneli limatithandiza kuzindikira kuti ngati tikhumudwa muuchimo koma tili olapadi, Atate wathu wachikondi wakumwamba adzamva mfuu yathu yopempha chifundo ndipo adzatipulumutsa kukutaya mtima. Komabe, kwakukulukulu tiyenera kukhala odera nkhaŵa ndi chitonzo chilichonse choikidwa pa dzina la Yehova.—3/15, tsamba 18.
▫ Kodi nchiyani chimene chimaphiphiritsidwa ndi ubatizo wa m’madzi?
Ubatizo ndiwo chisonyezero chakunja chakudzipatulira kwa munthuwe kwa Yehova Mulungu. Kuviikidwa m’madzi kumasonyeza kuti obatizidwawo akufa kunjira ya moyo yakudzidalira iwo eni. Kuvuulidwa m’madzi kumachitira chizindikiro kuti iwo tsopano akukhalira moyo kuchita chifuniro cha Mulungu, kuchiika poyamba m’miyoyo yawo. (Mateyu 16:24)—4/1, masamba 5-6.