Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 12/15 tsamba 14-19
  • Kuyenda ndi Mtima Umodzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyenda ndi Mtima Umodzi
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mantha Oyenerera
  • Kukoma Mtima Kwachikondi kwa Yehova
  • “Chizindikiro Chotanthauza Ubwino”
  • Yehova, Wochita Zinthu Zodabwitsa
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Yehova Ndiye Chitsanzo Chachikulu Pankhani Yosonyeza Ubwino
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Pitirizani Kuchita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Ndipatseni Mtima Wosagawanika Kuti Ndiope Dzina Lanu”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 12/15 tsamba 14-19

Kuyenda ndi Mtima Umodzi

“Mundilangize, O Yehova . . . Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliwope dzina lanu.”​—SALMO 86:11, NW.

1. Kodi Yehova amafupa motani okhulupirika ake?

‘O YEHOVA, ndinu Mulungu, ndinu nokha.’ (Salmo 86:8, 10) Davide anatamanda Mulungu kuchokera mumtima wosefukira ndi chiyamikiro. Ngakhale Davide asanakhale mfumu pa Israyeli yense, Yehova anali atamulanditsa kwa Sauli ndi kwa Afilisti. Chifukwa chake, anakhoza kuimba kuti: ‘Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi mpulumutsi wanga. Kwa wokhulupirika mudzachita mokhulupirika.’ (2 Samueli 22:2,  26) Yehova anali atatetezera mtumiki wake wokhulupirika kupyola ziyeso zambiri. Davide anakhoza kuika chidaliro chake ndi chikhulupiriro mwa Mulungu wake wokhulupirika, koma iye anafunikira chitsogozo chopitirizabe. Tsopano Davide anapempha Mulungu kuti: “Mundilangize, O Yehova, njira yanu.”​—Salmo 86:11, NW.

2. Kodi Yehova wapanga bwanji makonzedwe akuphunzitsidwa kwathu ndi iye?

2 Davide sanafune kuphatikizidwa ndi malingaliro audziko kapena nthanthi. Iye anafuna ‘kuphunzitsidwa ndi Yehova,’ monga momwe mneneri wa Mulungu ananenera pambuyo pake. (Yesaya 54:13) Mwachiwonekere, Davide anakhoza kusinkhasinkha m’mabukhu asanu ndi anayi okha a Baibulo amene analipo m’tsiku lake. Komabe, malangizo amenewo ochokera kwa Yehova anali amtengo wapatali kwa iye! Pophunzitsidwa lerolino, ife tingathe kusangalala ndi mabukhu onse 66 a Baibulo, kuphatikizapo mabukhu ofotokoza Ufumu ambirimbiri ogaŵiridwa kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Mofanana ndi Davide, tiyeni tiitanire pa Yehova, kuti mzimu wake utithandize kusanthula ‘zinthu zimene Mulungu anakonzeratu iwo akumkonda iye, . . . zakuya za Mulungu zomwe.’​—1 Akorinto 2:9, 10.

3. Kodi ndim’njira zotani zimene chilangizo cha Baibulo chimatipindulitsa?

3 Baibulo liri ndi yankho la funso lirilonse ndi vuto zimene zingabuke m’miyoyo yathu. “Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Kulandira malangizo ochokera kwa Yehova kudzatilimbikitsa kupirira mazunzo, kutitsitsimula m’nthaŵi zakuchita tondovi, ndi kuchititsa chiyembekezo cha Ufumu kuŵala m’mitima yathu. Tipezetu chikondwerero m’kuŵerenga Mawu a Mulungu ndi m’kusinkhasinkhamo “usana ndi usiku,” pakuti nzeru yochokera m’Baibulo imakhala “mtengo wamoyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala.”​—Salmo 1:1-3; Miyambo 3:13-18; wonaninso Yohane 17:3.

4. Ponena za zochita zathu, kodi nchitsanzo chotani chimene Yesu anapereka kwa ife?

4 Mwana wa Mulungu, Yesu, wotchedwanso “Mwana wa Davide,” nthaŵi zonse anayang’ana kwa Yehova kupeza chilangizo. (Mateyu 9:27)a Iye anati: “Sakhoza Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene awona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo.” “Sindichita kanthu kwa ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.” (Yohane 5:19; 8:28) Yesu anatisiyira chitsanzo kuti ‘titsatire mapazi ake mosamalitsa.’ (1 Petro 2:21) Tangolingalirani! Ngati tiphunzira monga momwe Yesu ayenera kukhala atachitira, mumkhalidwe uliwonse tidzakhoza kuchita monga momwe Yehova angafunire kuti tichite. Nthaŵi zonse njira ya Yehova njolungama.

5. Kodi “chowonadi” nchiyani?

5 Kenako Davide akulengeza kuti: “Ndidzayenda m’chowonadi chanu.” (Salmo 86:11) Zaka chikwi chimodzi pambuyo pake, Pilato, polankhula ndi Mwana wa Davide, Yesu, anafunsa kuti: “Chowonadi nchiyani?” Koma Yesu anali atangoyankha kumene funsolo, akumauza Pilato kuti “Ufumu wake suli wadziko lino lapansi,” anawonjezera kuti: “Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi chowonadi.” (Yohane 18:33-38) Chotero Yesu panopa anadziŵikitsa kuti chowonadi ndicho Ufumu Waumesiya. Ndithudi, mutu wankhani wa Baibulo lathunthu ndiwo kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova kupyolera mu Ufumuwo.​—Ezekieli 38:23; Mateyu 6:9, 10; Chivumbulutso 11:15.

6. Poyenda m’chowonadi, kodi tiyenera kukhala osamala za chiyani?

6 Kodi kuyenda m’chowonadi kumatanthauzanji? Kumatanthauza kupanga chiyembekezo cha Ufumu kukhala mbali yaikulu ya miyoyo yathu. Tiyenera kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chowonadi cha Ufumu. Tiyenera kukhala osagaŵanika m’kuika zabwino za Ufumu pachiyambi, achangu mogwirizana ndi mwaŵi wathu m’kuchitira umboni chowonadi cha Ufumu, molondola chitsanzo cha Yesu. (Mateyu 6:33; Yohane 18:37) Sitingathe kuyenda nthaŵi ina m’chowonadi, tikumapereka utumiki wachiphamaso ndiyeno pamenenso tikudzikondweretsa mwakuyamba kupatuka kukaphatikizidwa m’kusanguluka kopambanitsa kapena kuloŵa ntchito yodzisankhira yodya nthaŵi kapena ‘kukhala akapolo . . . Achuma.’ (Mateyu 6:24) Tingakhoze kusochera pa amodzi a malo opatulikapo amenewo, tiri osakhoza konse kupeza njira yobwererera pa ‘njira yopapatiza yakumka kumoyo.’ Tisasocheretu panjirayo! (Mateyu 7:13, 14) Mlangizi Wathu Wamkulu, Yehova, kupyolera mwa Mawu ake ndi gulu, akuunikira njirayo, akumati: “Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu kulamanja ndi potembenukira kulamanzere.”​—Yesaya 30:21.

Mantha Oyenerera

7. Kodi “tingagwirizanitse” motani mitima yathu?

7 Pemphero la Davide likupitirizabe m’vesi 11 kuti: “Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliwope dzina lanu.” Mofanana ndi Davide, tiyenera kufuna mitima yathu kukhala yosagaŵanika, yamphumphu, pochita chifuniro cha Mulungu. Zimenezi ziri zogwirizana ndi uphungu wa Mose wakuti: “Ndipo tsopano, Israyeli, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziwopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m’njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu?” (Deuteronomo 10:12, 13) Ndithudi, kuli chifukwa cha ubwino wathu kuti titsanulire mtima ndi moyo wathu m’kutumikira Yehova. Chotero timasonyeza mantha oyenera a dzina lake laulemerero. Dzina la Yehova kwenikweni limatanthauza “Iye achititsa kukhalako,” makamaka ponena za kuchititsa zifuno zake zazikulu kukwaniritsidwa. Limaimiranso ulamuliro wake waukulu pa chilengedwe chonse. Kutumikira mowopa ukulu wa Yehova, sitidzadodometsedwa ndi kuwopa munthu wokhoza kufa. Mitima yathu sidzakhala yogaŵanika. Mmalomwake, tidzawopa kuchita kanthu kalikonse kamene kadzakwiitsa Yehova, Woweruza Wamkulukulu ndi Ambuye Mfumu, amene miyoyo yathu yeniyeniyo iri m’dzanja lake.​—Yesaya 12:2; 33:22.

8, 9. (a) Kodi kumatanthauzanji ‘kusakhala mbali yadziko’? (b) Kodi ndinjira zotani zimene tiyenera kutenga chifukwa chakukhala kwathu chowonetsedwa “kudziko lapansi”?

8 Ngakhale poyang’anizana ndi mtonzo ndi chizunzo, tidzatsatira chitsanzo chopanda mantha cha Yesu m’kusakhala mbali yadziko loipa lotizinga. (Yohane 15:17-21) Zimenezi sizitanthauza kuti ophunzira a Yesu ayenera kukhala monga anthu obindikiritsidwa kapena obisidwa m’nyumba ya avirigo. Yesu anati m’pemphero kwa Atate wake: “Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Siali a dziko lapansi monga ine sindiri wa dziko lapansi. Patulani iwo m’chowonadi; mawu anu ndi chowonadi. Monga momwe munandituma ine ku dziko lapansi, inenso ndinatuma iwo ku dziko lapansi.” (Yohane 17:15-18) Mofanana ndi Yesu, tatumidwa kukalalikira chowonadi cha Ufumu. Yesu anali wofikirika. Anthu anapeza mpumulo mwanjira yake yakuphunzitsa. (Yerekezerani ndi Mateyu 7:28, 29; 11:28, 29; Yohane 7:46.) Ziyenera kukhala zofananazo ndi ife.

9 Mkhalidwe wathu waubwenzi, kapesedwe kathu ndi kawonekedwe kathu kabwino, makambitsirano okoma mtima ndi abwino, ziyenera kutipanga ife ndi uthenga wathu kukhala olandirika kwa anthu a mitima yowongoka. Sitiyenera kukhala anyankhalala, ovala mosadekha, amayanjano amene angatsogolere kukuphatikizidwa m’zinthu zadziko, ndi njira yakusadziletsa, yosalamulirika zimene timawona m’dziko lotizinga. Popeza kuti takhala “chowonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu,” tiri pantchito kwa maola 24 tsiku lirilonse kutumikira ndi kukhala ndi moyo monga Akristu achitsanzo chabwino. (1 Akorinto 4:9; Aefeso 5:1-4; Afilipi 4:8, 9; Akolose 4:5, 6) Tiyenera kukhala ndi mtima umodzi m’mbali zonsezi.

10. Kodi Yehova amakumbukira motani awo amene ali ndi mtima umodzi mu utumiki wopatulika?

10 Ife amene tiri ndi mtima umodzi m’kuwopa dzina la Yehova, tikumasinkhasinkha pa zifuno zake zazikulu ndi kudzaza miyoyo yathu ndi utumiki wopatulika, tidzakumbukiridwa ndi Yehova. “Pakuti maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudziwonetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi iye.” (2 Mbiri 16:9) Akumasonya molosera ku tsiku lathu, Malaki 3:16 amati: “Pamenepo iwo akuwopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi bukhu la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.” Tikhaletu ndi mtima umodzi m’kuwopa Yehova kwabwino kumeneko!

Kukoma Mtima Kwachikondi kwa Yehova

11. Kodi kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova kudzasonyezedwa motani kwa okhulupirikawo?

11 Pemphero la Davide nlosonyeza khama chotani nanga! Iye akupitirizabe kuti: “Ndikuyamikani, O Yehova Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse, ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthaŵi yosadziŵika, pakuti kukoma mtima kwachikondi kwanu kuli kwakukulu kwa ine, ndipo munalanditsa moyo wanga m’Sheoli, malo ake otsika koposa.” (Salmo 86:12, 13, NW) Kwanthaŵi yachiŵiri m’salmo limeneli, Davide akutamanda Yehova kaamba ka kukoma mtima kwachikondi Kwake​—chikondi Chake chokhulupirika. Chikondi chimenechi chiri chachikulu kwambiri kotero kuti chingathe kupulumutsa ngakhale m’mikhalidwe yowonekera kukhala yosatheka. Pamene Sauli anali kumsaka m’chipululu, Davide angakhale atamva kuti mwenzi akanafika pamalo ena ndi kufa. Kunali ngati kuti anali kuyang’anizana maso ndi maso ndi kunsi kwa Sheoli​—malo akunsi kwamanda. Koma Yehova anamlanditsa! Mofananamo, kaŵirikaŵiri Yehova wadzetsa mpumulo kwa atumiki ake amakono mwanjira zozizŵitsa, ndiponso iye walimbikitsa osunga umphumphu amene apirira mokhulupirika ngakhale kufikira imfa. Okhulupirika onse adzalandira mphotho zawo, ngakhale mwachiukiriro ngati kuli kofunika.​—Yerekezerani ndi Yobu 1:6-12; 2:1-6, 9, 10; 27:5; 42:10; Miyambo 27:11; Mateyu 24:9, 13; Chivumbulutso 2:10.b

12. Kodi atsogoleri achipembedzo akhala odzikuza ndi ankhalwe motani, ndipo kodi mphotho yawo idzakhala chiyani?

12 Polankhula za ozunzawo Davide akufuula kuti: “O Mulungu, odzikuza andiukira; ndi msonkhano wa anthu owopsa ufunafuna moyo wanga, ndipo sanaika inu pamaso pawo.” (Salmo 86:14, NW) Lerolino, ozunzawo aphatikizapo atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko. Amenewa amadzinenera kulambira Mulungu koma padzina lake loyeralo amalowetsapo dzina laulemu lakuti “Ambuye” ndipo amamlalikira monga Utatu wachinsinsi umene kwenikweni sukutchulidwa kulikonse m’Baibulo. Nkupanda ulemu kotani nanga! Kuwonjezera apa, iwo amayesayesa kunyengerera olamulira andale zadziko kuti aletse mwalamulo ndi kuika m’ndende Mboni za Yehova, monga momwe kukali kuchitidwabe m’chiŵerengero chachikulu modabwitsa cha maiko apadziko lapansi. Ochitira mwano dzina la Mulungu ovala miinjiro amenewa adzatuta mphotho yawo, limodzi ndi mbali zonse zonga mahule za Babulo Wamkulu.​—Chivumbulutso 17:1, 2, 15-18; 19:1-3.

13. Kodi ndimikhalidwe yotani imene Yehova amasonyeza podziŵitsa ubwino wake?

13 M’kusiyana kokondweretsa, pemphero la Davide likupitirizabe kuti: “Koma inu, O Yehova, ndinu Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosafulumira kukwiya ndi wochuluka m’kukoma mtima kwachikondi ndi chowonadi.” (Salmo 86:15, NW) Ndithudi, imeneyi iri mikhalidwe yabwino koposa ya Mulungu wathu. Mawu amenewa akutibwezera kumbuyo pa Phiri la Sinayi pamene Mose anapempha kuti awone ulemerero wa Yehova. Yehova anayankha kuti: “Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzatchula dzina la Yehova pamaso pako.” Koma iye anachenjeza Mose kuti: “Sungathe kuwona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiwona ine ndikukhala ndi moyo.” Pambuyo pake, Yehova anatsika m’thambo, akumafuula kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi waukoma mtima wochuluka ndi wachowonadi.” (Eksodo 33:18-20; 34:5, 6) Davide anagwira mawu amenewa m’pemphero lake. Mikhalidwe yotero ya Yehova imatanthauza zambiri kwa ife kuposa mawonekedwe akuthupi aliwonse! Kuchokera m’zimene takumana nazo, kodi sitikuyamikira ubwino wa Yehova monga momwe wachitidwira chitsanzo m’mikhalidwe yabwino kwambiri imeneyi?

“Chizindikiro Chotanthauza Ubwino”

14, 15. Kodi Yehova amachitira motani atumiki ake “chizindikiro chotanthauza ubwino”?

14 Kachiŵirinso Davide akupempha dalitso la Yehova akumati: “Tembenukirani kwa ine ndi kundisonyeza chiyanjo. Patsani mtumiki wanu nyonga yanu, ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu. Mundichitire chizindikiro chotanthauza ubwino, kuti ondida achiwone nachite manyazi. Pakuti inu mwininu, O Yehova, mwandithandiza ndi kunditonthoza.” (Salmo 86:16, 17, NW) Davide akuzindikira kuti monga ‘mwana wa mdzakazi wa Yehova,’ iye ayeneranso kukhala wa Yehova. Chomwechonso ife tonse lerolino amene tapatulira miyoyo yathu kwa Yehova ndi kuvutikira mu utumiki wake. Timafunikira nyonga yopulumutsa ya Yehova kupyolera mwa mzimu wake woyera. Chifukwa chake, timapempha Mulungu wathu kutichitira “chizindikiro chotanthauza ubwino.” Ubwino wa Yehova umaphatikizapo mikhalidwe yabwino imene tangokambitsirana kumene. Pamaziko amenewa, kodi nchizindikiro, kapena chisonyezero, chotani chimene tingayembekezere Yehova kutipatsa?

15 Yehova ali Mpatsi wa ‘mphatso iriyonse yabwino ndi yangwiro’ ndipo ngwowolowa manja, monga momwe Yesu akutitsimikizirira, amapatsa “mzimu woyera kwa iwo akumpempha iye.” (Yakobo 1:17; Luka 11:13) Mzimu woyera​—ndi mphatso yamtengo wapatali chotani nanga yochokera kwa Yehova! Kupyolera mwa mzimu woyera, Yehova amapereka chisangalalo cha mtima, ngakhale m’nthaŵi ya chizunzo. Chotero, atumwi a Yesu, pamene anali kuzengedwa mlandu kuti akaphedwe, anali okhoza kufuula mwachisangalalo kuti Mulungu amapereka mzimu woyera kwa omvera iye monga wolamulira. (Machitidwe 5:27-32) Chisangalalo cha mzimu woyera chinapitirizabe kugwira ntchito kwa iwo monga “chizindikiro chotanthauza ubwino.”​—Aroma 14:17, 18.

16, 17. (a) Kodi nchizindikiro chaubwino wake chotani chimene Yehova anapereka kwa Paulo ndi Barnaba? (b) Kodi nchizindikiro chotani chimene chinaperekedwa kwa Atesalonika ozunzidwawo?

16 Mkati mwa nthaŵi ya ulendo wawo waumishonale ali mu Asia Minor, Paulo ndi Barnaba anakumana ndi mavuto, ngakhale chizunzo chadzawoneni. Pamene analalikira mu Antiokeya wa ku Pisidiya, Ayuda anakana uthenga wawo. Chifukwa chake, iwo anatembenukira kwa amitundu. Chinatulukapo nchiyani? “Pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza mawu a Mulungu; ndipo anakhulupira onse amene anaikidwiratu ku moyo wosatha.” Koma Ayuda anachititsa chipolowe, kotero kuti amishonale amenewo anatulutsidwa kunja kwa dzikolo. Kodi iwo ndi okhulupirira atsopano anachita tondovi nzimenezi? Kutalitali! Mmalomwake, “akuphunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndi mzimu woyera.” (Machitidwe 13:48, 52) Yehova anawapatsa chizindikiro chimenecho cha ubwino wake.

17 Pambuyo pake, mpingo watsopano mu Tesalonika unayamba kuzunzidwa. Zimenezi zinachititsa mtumwi Paulo kulemba kalata yachitonthozo, akumayamikira chipiriro chawo posautsidwa. Iwo anali “kulandira mawuwo m’chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha mzimu woyera.” (1 Atesalonika 1:6) “Chimwemwe cha mzimu woyera” chinapitirizabe kuwalimbikitsa monga chizindikiro chaumboni chochokera kwa Mulungu amene ali wachifundo ndi wachisomo, wosafulumira kukwiya, ndi wochuluka m’kukoma mtima kwachikondi ndi chowonadi.

18. Kodi abale athu Kummaŵa kwa Yuropu asonyeza chiyamikiro motani kaamba ka ubwino wa Yehova?

18 M’nthaŵi zaposachedwapa, Yehova wasonyeza ubwino wake kwa abale athu okhulupirika a Kummaŵa kwa Yuropu, akumachititsa manyazi awo amene anawada​—amene poyamba anali owazunza. Ngakhale kuti posachedwapa amasulidwa kuchitsenderezo cha zaka makumi ambiri, abale okondedwa amenewa afunikirabe kupirira, pakuti ambiri akuyang’anizana ndi mavuto adzawoneni achuma. Komabe, ‘chimwemwe chawo cha mzimu woyera’ chimawatonthoza. Kodi nchisangalalo chachikulu kwambiri chotani chimene angakhale nacho kuposa kugwiritsira ntchito ufulu wawo wopezedwa chatsopano m’kufutukula umboniwo? Anthu ambiri akuwamvetsera, monga momwe malipoti osimba misonkhano yaikulu ndi maubatizo akusonyezera.​—Yerekezerani ndi Machitidwe 9:31.

19. Kodi ife tingapange bwanji mawu a Salmo 86:11 kukhala athuathu?

19 Zonse zimene zakambitsiridwa m’nkhani ino ndi m’nkhani yapita zikubwereza pemphero losonyeza khama la Davide kwa Yehova lakuti: “Mundilangize, O Yehova . . . Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliwope dzina lanu.” (Salmo 86:11, NW) Tipangetu mawu amenewo a lemba la chaka chathu cha 1993 kukhala athuathu pamene tikugwira ntchito mwamtima wonse mochirikiza zabwino za Ufumu ndi m’kusonyeza chiyamikiro chaubwino wosatha wa Mulungu wathu mmodzi, Ambuye Mfumu Yehova.

[Mawu a M’munsi]

a Monga “mbewu” yonenedweratuyo, Yesu anali woloŵa nyumba mu ufumu wa Davide ndipo chotero anali “Mwana wa Davide” ponse paŵiri m’lingaliro lenileni ndi m’lingaliro lauzimu.​—Genesis 3:15; Salmo 89:29, 34-37.

b Kuti muwone zitsanzo zamakono, wonani Yearbook of Jehovah’s Witnesses, m’kope la 1974, tsamba 113-212; la 1985, tsamba 194-7; la 1986, tsamba 237-8; la 1988, tsamba 182-5; la 1990, tsamba 171-2; la 1992, tsamba 174-81

Kodi Mukayankha Bwanji?

◻ Kodi timatanthauzanji mwakupemphera kuti, “Mundilangize, O Yehova”?

◻ Kodi kumatanthauzanji kukhala ndi mtima umodzi kuti uliwope dzina la Yehova?

◻ Kodi Yehova adzasonyeza motani kukoma mtima kwachikondi kwa okhulupirika onse?

◻ Kodi Yehova amatichitira motani “chizindikiro chaubwino?”

[Bokosi patsamba 16]

Lemba lachaka cha 1993: “Mundilangize, O Yehova . . . Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliwope dzina lanu.”​—Salmo 86:11, NW.

[Chithunzi patsamba 15]

Yehova ndiye thanthwe ndi ngaka kwa awo oyenda mowongoka m’chowonadi

[Chithunzi patsamba 18]

Pamsonkhano wa Mitundu Yonse wa “Onyamula Kuunika” wa Mboni za Yehova mu St. Petersburg, Russia, mu June, 46,214 anafikapo ndipo 3,256 anabatizidwa. Nkokondweretsa chotani nanga kuti amenewa akupindula ndi ubwino wa Yehova, mwa “chimwemwe cha mzimu woyera”!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena