Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 189
  • Kodi M’Baibulo Mungapezeke Mawu Omwe Angandilimbikitse?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi M’Baibulo Mungapezeke Mawu Omwe Angandilimbikitse?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Mavuto
  • Imfa ya munthu amene tinkamukonda
  • Kudziimba mlandu
  • Kukhumudwa
  • Kudwala
  • Nkhawa komanso kuvutika maganizo
  • Nkhondo
  • Kudera nkhawa zam’tsogolo
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Baibulo Lingathandize Amuna Amene Ali Ndi Nkhawa
    Nkhani Zina
  • Kodi Baibulo Lingandithandize Kuti Ndisiye Kudziimba Mlandu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Muzimutulira Yehova Nkhawa Zanu Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 189
Mzimayi akuwerenga Baibulo mosangalala.

Kodi M’Baibulo Mungapezeke Mawu Omwe Angandilimbikitse?

Yankho la m’Baibulo

Inde. (Aroma 15:4) Mwachitsanzo, taonani mfundo za m’Baibulo zomwe zili m’munsimu zomwe zathandiza anthu ambiri omwe akulimbana ndi mavuto komanso nkhawa zosiyanasiyana.

Zimene zili munkhaniyi

  • Mavuto

  • Imfa ya munthu amene tinkamukonda

  • Kudziimba mlandu

  • Kukhumudwa

  • Kudwala

  • Nkhawa komanso kuvutika maganizo

  • Nkhondo

  • Kudera nkhawa zam’tsogolo

Mavuto

Salimo 23:4: “Ngakhale ndikuyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani, sindikuopa kanthu, pakuti inu muli ndi ine.”

Mfundo yake: Tikamapemphera kwa Mulungu komanso kudalira Mawu ake opezeka m’Baibulo kuti atitsogolere, tikhoza kulimbana ndi mavuto athu.

Afilipi 4:13: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”

Mfundo yake: Mulungu akhoza kutipatsa mphamvu kuti tilimbane ndi vuto lililonse.

Kuti mudziwe mmene Baibulo lingakuthandizireni kuthana ndi mavuto okhalitsa, werengani nkhani yakuti “Vuto Limene Limakhalapo: Zinthu Zina Simungazisinthe.”

Imfa ya munthu amene tinkamukonda

Mlaliki 9:10: “Kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda kumene ukupitako.”

Mfundo yake: Anthu omwe anamwalira sakuvutika ndipo sangativulaze chifukwa sadziwa chilichonse.

Machitidwe 24:15: “Kudzakhala kuuka.”

Mfundo yake: Mulungu ali ndi mphamvu zodzaukitsa omwe anamwalira kuti adzakhalenso ndi moyo.

Kuti mudziwe mmene Baibulo lingakuthandizireni kuthana chisoni ngati mutaferedwa munthu amene munkamukonda kwambiri, werengani nkhani yakuti “Zimene Zingakuthandizeni Mukaferedwa—Zimene Mungachite Panopa.”

Kudziimba mlandu

Salimo 86:5: “Inu Yehova a ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka. Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.”

Mfundo yake: Mulungu amakhululukira anthu omwe amadzimvera chisoni chifukwa cha zinthu zomwe analakwitsa ndiponso omwe ndi ofunitsitsa kuti asadzabwerezenso zomwe anachita.

Salimo 103:12: “Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.”

Mfundo yake: Mulungu akatikhululukira, amatiikira kutali machimo athu. Ndipo sakhalira kutikumbutsa zomwe tinalakwa ndi cholinga chofuna kutiimba mlandu kapena kutilanga.

Kuti mudziwe mmene Baibulo lingakuthandizireni ngati mukulimbana ndi vuto lodziimba mlandu, werengani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Lingandithandize Kuti Ndisiye Kudziimba Mlandu?”

Kukhumudwa

Salimo 31:7: “Mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwera.”

Mfundo yake: Mulungu akudziwa bwino za mavuto omwe mukudutsamo. Amadziwanso bwino mmene mavutowo amakukhudzirani mumtima ngakhale pamene anthu ena sakuona zimenezo.

Salimo 34:18: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”

Mfundo yake: Mulungu akulonjeza kuti ndi wokonzeka kukuthandizani pamene muli wokhumudwa. Iye angathe kukupatsani mphamvu kuti mupirire.

Kuti mudziwe mmene Baibulo lingakuthandizireni mukakhala wokhumudwa, onerani vidiyo yakuti Zimene Mungachite Kuti Muyambirenso Kusangalala.

Kudwala

Salimo 41:3: “Yehova adzachirikiza wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.”

Mfundo yake: Mulungu akhoza kukuthandizani pamene mukudwala kwambiri. Angachite zimenezi pokupatsani mtendere wamumtima, mphamvu zoti muthe kupirira komanso nzeru kuti mukwanitse kusankha bwino zoti muchite.

Yesaya 33:24: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”

Mfundo yake: Mulungu analonjeza kuti m’tsogolomu anthu onse adzakhala ndi moyo wathanzi.

Kuti mudziwe mmene Baibulo lingakuthandizireni pa nthawi yomwe mukudwala, werengani nkhani yakuti “Zimene Zingakuthandizeni Ngati Mwayamba Kudwala Mwadzidzidzi.”

Nkhawa komanso kuvutika maganizo

Salimo 94:19 “Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”

Mfundo yake: Tikamadalira Yehova pamene tili ndi nkhawa, Iye angatithandize kuti tikhazikitse maganizo athu m’malo.

1 Petulo 5:7: ‘Mutulireni nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’

Mfundo yake: Mulungu amatidera nkhawa tikamavutika. Iye amatilimbikitsa kuti tizipemphera kwa iye n’kumuuza zomwe zikutidetsa nkhawa.

Kuti mudziwe mmene Baibulo lingakuthandizireni kuthana ndi nkhawa, werengani nkhani yakuti “Mungatani Kuti Muchepetse Nkhawa?”

Nkhondo

Salimo 46:9: “Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”

Mfundo yake: Posachedwa, Ufumu wa Mulungu udzathetsa nkhondo zonse.

Salimo 37:11, 29: “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka. . . . Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”

Mfundo yake: Anthu abwino adzakhala mwamtendere padziko lapansi mpaka kalekale.

Kuti mudziwe chifukwa chake tikutsimikiza kuti Ufumu wa Mulungu ufika posachedwa, werengani nkhani yakuti, “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulira Dzikoli?”

Kudera nkhawa zam’tsogolo

Yeremiya 29:11: “Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watero Yehova.”

Mfundo yake: Mulungu akutsimikizira anthu ake kuti adzawapatsa tsogolo labwino kwambiri.

Chivumbulutso 21:4: “Adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”

Mfundo yake: Mulungu akulonjeza kuti adzachotsa zinthu zonse zoipa zomwe timaziona komanso kukumana nazo masiku ano.

Kuti mudziwe zambiri zomwe Baibulo limaphunzitsa ponena zam’tsogolo, werengani nkhani yakuti, “Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo.”

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti, “Kodi Yehova Ndi Ndani?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena