Armagedo—Liti?
“TIKUIMA pa Armagedo ndipo tikumenyera nkhondo Ambuye. Ndi mawu amenewo, purezidenti wapapitapo wa U.S. Theodore Roosevelt anagwiritsira ntchito liwuli “Armagedo” kunkhondo yandale zadziko mu imene iye anaphatikizidwamo. Chotero, kodi tiyenera kufunafuna Armagedo m’bwalo la ndale zadziko?
Zaka zoŵerengeka zapitazo, magazine a ku Canada Business Life anali ndi mutu wankhani wakuti “Armagedo ya Zachuma.” Mutu wake waung’ono unafunsa kuti: “Kodi kulephera kulipira ngongole kwa Maiko Osatukuka kumene kungadzetse kugwa kwa chuma chathu?” Koma kodi tiyenera kulingalira Armagedo monga tsoka la zachuma?
Malinga ndikunena kwa magazini a Newsweek, mapeto adziko anakhala mutu wankhani pamsonkhano wokambirana za masankho a purezidenti wochitidwa mu 1984. Pachochitikacho, purezidenti wapanthaŵiyo wa U.S. Ronald Reagan “anafunsidwa ngati amakhulupiriradi kuti dziko likunka ku ‘Armagedo yanyukliya.’ Reagan anavomereza ‘makambitsirano otsimikizirika’ onena za kuchitikira panthaŵi yofanana ya zochitika zamakono ndi zizindikiro za m’Baibulo zozindikiritsa masiku otsiriza, koma kazembe wamkulu wa gulu lankhondo anaumirira kuti iye sananenepo kuti ‘tiyenera kukonzekera mogwirizana ndi Armagedo.’” Komabe, kodi kufufuza kwathu tanthauzo la Armagedo kuyenera kuzikidwa pakachitidwe ka gulu lankhondo kamene kakuwopseza kubweretsa chipiyoyo cha nyukliya?
Anthu ambiri achipembedzo amati Armagedo ndinkhondo. Koma kuchiyambiyambi kwa zaka za zana la 19, katswiri wa Baibulo Adam Clarke analemba kuti: “Ha kuyerekezera kwa anthu kwakhala kopanda pake chotani nanga pa mfundoyi! Mogwirizana ndi olosera athu onyenga ndi odzitcha kukhala aneneri, m’zaka makumi aŵiri zapitazo nkhondoyi inamenyedwa m’madera osiyanasiyana! Panthaŵi imodzi iyo inkatchedwa Austerlitz, panthaŵi ina Moscow, pa inanso Leipsic, ndipo tsopano ikutchedwa Waterloo! Ndipo motero iwo apitirizabe, ndipo adzapitirizabe, kugubuduza ndi kugubuduzidwa.
Mwachiwonekere kufufuza tanthauzo la Armagedo kumadzetsa mafunso ofunika kwambiri. Kodi Armagedo nchiyani? Ngati iri nkhondo, kodi ndani amene adzakhalamo ndi phande? Kodi idzamenyedweranji? Kodi iyo idzachitikira kuti? Ndipo kodi Armagedo idzachitika liti?
Kodi Armagedo Nchiyani?
Liwu lakuti “Armagedo” lachokera ku liwu lopezeka m’buku la Baibulo la Chivumbulutso, lodziŵika kaamba ka chinenero chophiphiritsira. Mmenemo mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndipo ndinawona motuluka mkamwa mwa chinjoka, ndi m’kamwa mwa chilombo, ndi mkamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati achule; pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kumka kwa mafumu adziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse. . . . Ndipo anawasonkhanitsira kumalo otchedwa m’Chihebri Harmagedo.”—Chivumbulutso 16:13-16.
Armagedo, kapena Harmagedo, ndiko kulembedwa kwa masupelo a chinenero china kwa liwu Lachigriki lofanana ndi Lachihebri lakuti Har Meghid·dohnʹ kutanthauza “Phiri la Megido,” kapena “Phiri la Magulu Ankhondo Osonkhana.” Ilo lagwirizanitsidwa ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” Motero Armagedo sindiyo nkhondo wamba ya ndale zadziko, tsoka lazachuma, chipiyoyo cha nyukliya, kapena nkhondo ya anthu. Mmalo mwake, Armagedo ndiyo nkhondo ya Mulungu.
Kodi Ndani Amene Adzakhalamo ndi Phande?
Mizimu itatu yonyansa ngati achule inatuluka m’kamwa mwa chinjoka (Satana Mdierekezi), chirombo (makonzedwe ake andale zadziko a padziko lapansi), ndi mneneri wonyenga wa Mgwirizano wa Angelezi ndi Amereka. Mizimu imeneyi youziridwa ndi ziwanda, kapena angelo oipa, ikusonkhanitsa mafumu apadziko lapansi, kapena olamulira, ku Harmagedo.—onani mutu 32 wa bukhu la Revelation—Its Grand Climax At Hand! lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kumbali ya Yehova m’nkhondo ya Armagedo kuli gulu lankhondo lalikulu la makamu auzimu osawoneka otsogozedwa ndi Mfumu Yesu Kristu. Mtumwi Yohane anasimba kuti: “Ndipo ndinawona mutatseguka m’mwamba; ndipo tawonani, kavalo woyera, ndi iye wakumkwera wotchedwa wokhulupirika ndi wowona; ndipo [Yesu] aweruza nachita nkhondo molungama. . . . Ndipo magulu ankhondo okhala m’mwamba anamtsata iye. . . . Ndipo mkamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wamkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse. Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pantchafu yake dzina lolembedwa, Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye.” (Chivumbulutso 19:11-16) Lupanga lakuthwa lalitalilo limaimira mphamvu za Kristu za kulamulira kuphedwa kwa onse okana kuchilikiza Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 1:16; 2:16) Magulu ankhondo aakulu osawoneka ngokonzekeretsedwa kaamba ka nkhondo ya Armagedo.
Otsutsana nawo ndiwo Satana, makamu ake a ziwanda, ndi mafumu adziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu. Komatu sitiyenera kuganizira kokha za olamulira a dziko okhala m’malo owonekawo, pakuti anthu amene iwo akuwalamulira akuphatikizidwamonso. Kunanenedweratu kuti: “Pakuti Yehova akwiyira amitundu onse, nachitira ukali khamu lawo lonse.”—Yesaya 34:2.
Kodi Idzamenyedweranji?
Armagedo idzamenyedwa chifukwa chakuti Mulungu ngwolungama ndipo sadzalekererabe kuipa. (Salmo 11:7) Chotero gulu la Satana Mdierekezi, lophatikizapo ponse paŵiri ziwanda ndi anthu opanduka, omwe achititsa kuipa ndi masoka a m’zaka zikwi zambiri, ayenera kuwonongedwa. (Yerekezerani ndi Genesis 3:15.) Ulamuliro wa Yehova wa chilengedwe cha ponseponse udzachirikizidwa pa Armagedo, ndipo nkhondo imeneyo idzachotsa chitonzo chowunjikidwa padzina lake kwa zaka mazana ambiri. Monga mmene Mulungu analengezera kudzera mwa mneneri wake Ezekieli kuti: ‘Sindidzalola dzina langa loyera alidetse; ndipo amitundu adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.”—Ezekiel 39:7.
Kwenikweni nkhondo ya Mulungu ya Armagedo idzatchinjiriza kuwonongedwa kwa anthu onse. Yehova analenga dziko lapansi kuti likhalidwe, osati kuwonongedwa ndi nkhondo ya anthu yoŵaula ya nyukliya kapena kuchititsidwa kukhala losayenerera chamoyo. (Yesaya 45:18) Iye “adzawononga owononga dziko.” (Chivumbulutso 11:18) Koma wamasalmo analengeza kuti: “Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe lakhazikika [Chihebri, te·velʹ; dziko lapansi, monga lachonde ndi lokhala anthu, chiunda chokhoza kukhalidwa] kuti silingagwedezeke.”—Salmo 96:10.
Chimene Mulungu adzachita pa Armagedo chidzakhala chogwirizana ndendende ndi mikhalidwe yake yaikulu ya chilungamo, nzeru, mphamvu, ndi chikondi. (Deuteronomo 32:4; Yobu 12:13; Yesaya 40:26; 1 Yohane 4:8) Iye adzachitapo kanthu motsutsana ndi “ochimwa osapembedza,” osati motsutsana ndi owongoka. (Yuda 14, 15) ‘Oipa okha ndiwo adzawonongedwa ndi lupanga.’ (Yeremiya 25:31) Ichi chidzalambula njira ya kubwezeretsedwa kwa Paradaiso, kukwaniritsa chifuno chaumulungu kaamba ka dziko lapansi ndi anthu.—Luka 23:43.
Kodi Idzachitikira Kuti?
Popeza kuti liwu lakuti “Armagedo” limachokera kuliwu Lachihebri lotanthauza “Phiri la Megido,” ena anganene kuti nkhondo imeneyi idzamenyedwera pamalo apamwamba otchuka okhala ndi dzina limenelo. Komabe, kunalibeko phiri lotchedwa Megido. Makilomita 100 chakumpoto kumadzulo kwa Yerusalemu kunali tauni yokhala pakaphiri, kapena mzinda, wotchedwa Megido, komatu tsopano ndichiunda chokha chachitali mamita 20 pamalo amenewo.—Yoswa 17:11.
Mzinda wakalekale umenewu unali cha pamtunda pa “chigwa cha Megido.” (2 Mbiri 35:22) Kugwirizanitsa Armagedo (kapena Harmagedo) ndi malo amenewo nkoyenerera chifukwa chakuti anali malo a bwalo la nkhondo ya kamuthemuthe. Mwachitsanzo, kumeneko Mulungu anatheketsa Woweruza Baraki kupha mfumu ya Kanani Yabini ndi magulu ake ankhondo olamuliridwa ndi Sisera. (Oweruza 4:12-24; 5:19, 20) Pamalo amenewo Gedeoni ndi gulu lake la anthu oŵerengeka anakhaulitsa Amidyani. (Oweruza 7:1–8:35) Ndiko kumenenso Mfumu Ahazi ndi Mfumu Yosiya anaphedwera.—2 Mafumu 9:27; 23:29, 30.
Komabe, tiyenera kudziŵa kuti, chigwa chimenechi, chotchedwanso Chigwa cha Esdraelon, nchautali wa makilomita 32 okha ndi makilomita 29 chambwambi mwake kumalire ake akummaŵa. Mafumu adziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu ndi magulu awo ankhondo sakakhoza konse kukwanira m’dera lailong’ono loterolo. Ndiponso, chiundacho (pamulu wa Megido) kapenanso chigwa sichiri phiri. Motero, mwachiwonekere, Armagedo sidzalekezera m’dera lakutilakuti lamapiri m’Middle East. Mmalo mwake, Armagedo (kapena Harmagedo) ndiwo mkhalidwe wadziko lonse wophiphiritsira, ngakhale kuti zina za zizindikiro zake zikutengedwa kuchokera ku Megido ndi zimene zinachitikira m’dera limenelo.
Kodi Armagedo Idzachitika Liti?
Popeza kuti Megido anali m’dziko la anthu akale a Mulungu, chimene chidzachitika pa Armagedo chikukhudza Mboni za Yehova “m’nthaŵi ino ya mapeto.” (Daniel 12:4) Harmagedo imasonya “malo” kumene olamulira andale zadziko asonkhanitsidwako motsutsana ndi Yehova ndi Ufumu wake mwa Yesu Kristu. (Chivumbulutso 16:14, 16) Koma “malo” amenewa (Chigriki, toʹpos) amatanthauza mkhalidwe wadziko. Armagedo idzachitika pamene mkhalidwe wakutiwakuti uyambika umene udzayambukira Mboni za Yehova padziko lonse lapansi.
Kulemelerera kwa Mboni za Yehova kukukwiitsa Satana Mdyerekezi, amene posachedwapa adzalinganiza chiwukiro chotheratu pa Akristu owonekera kukhala osatetezeredwa amenewa. Kuwukira kwa padziko lonse kumeneku kochitidwa ndi Satana, kapena Gogi, kwafotokozedwa mu Ezekieli mutu 38 ndi 39. Mosonkhezeredwa ndi Mdyerekezi, mitundu idzaguba motsutsana ndi anthu a Yehova okonda mtendere osonkhana kuchokera m’mitundu yonse. Inde, chitsutso cha Satana chidzawonekera mwa kachitidwe ka chiunda chonse kotsutsana ndi atumiki a Yehova a padziko lapansi, oimira owoneka ndi maso ndi olengeza a Ufumu wa Mulungu.
Kaŵirikaŵiri nkhondo imadziŵidwa ndi malo amene yamenyedwerako. Motero, kutetezera mwamphamvu anthu ake kwa Mulungu kungatchedwe kumenyana, kapena nkhondo, ya Armagedo. Pamene Yehova adzatetezera atumiki ake motsutsana ndi kuwukira kwa Gogi, Armagedo idzayamba! Maboma a anthu adzagwa. Utsi wa mitambo yakuda bii, matalala akupha, makala amoto oyaka ndi sulfure, miliri yosakaza—zochitadi za Mulungu—zidzapangitsa anthu okhala kunja kwa gulu la Mboni za Yehova kuthedwa nzeru. Adani awo aumunthu adzatembenukirana ndi zida okhaokha. Ndipo opulumuka pankhondo yakudzipha imeneyi, adzaphedwa ndi Yehova.—Ezekieli 38:18-23; Danieli 2:44.
M’mantha awo, dzanja la munthu aliyense lidzatembenukira mnansi wake m’nkhondo yauchinyama koma yosaphula kanthu kaamba ka chipulumutso. (Zekariya 14:12, 13) “Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera kumalekezero ena adziko lapansi kumka kumalekezero ena adziko lapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.” (Yeremiya 25:33) Kuyesayesa kulikonse kwa kukhala wosatenga mbali m’nkhondo ya Mulungu kudzakutaikiritsani moyo wanu pa Armagedo! Ndipo monga momwe kaŵirikaŵiri kwatsimikiziridwa mwa Malemba m’maganizini ano, mbadwo wamakono uwu sudzatha Armagedo isanadze!—Mateyu 24:21, 34.
Chimene Armagedo Idzakwaniritsa
Armagedo idzachotsa chizindikiro chirichonse chotsala cha gulu lapadziko lapansi la Satana. Ndiponso, Mdyerekezi ndi ziwanda zake adzaponyedwa m’phompho. (Chivumbulutso 20:1-3) Ha ndi madalitso otani nanga amene adzayenda tawatawa kwa anthu a Yehova, opulumuka achimwemwe nkhondo yake yaikulu ya Armagedo! Iwo mosangalala adzayamba kumanganso kumene kudzasanduliza dziko lonse lapansi kukhala paradaiso, losaipitsidwa, lopanda zoŵawitsa, kulira maliro, misozi, ndi imfa. (Chivumbulutso 11:15, 18; 21:3, 4) Ndipo inu mungakhale mmenemo ngati mulabadira mawu awa a wamasalmo: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo iye adzakukweza kuti ulandire dziko; pakudulidwa oipa udzapenya.” (Salmo 37:34) Ndithudi, inu mungakhaletu ndi moyo kudzawona nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse ndi kukhala wopulumuka wachimwemwe pamene Armagedo idzakantha!
“Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Yehova.”—2 Petro 3:11, 12
[Mawu Otsindika patsamba 4]
Armagedo sindiyo nkhondo ya ndale zadziko, tsoka la kuwonongeka kwa zachuma, chipiyoyo cha nyukliya, kapena nkhondo ya anthu. Armagedo ndiyo nkhondo ya Mulungu
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Nkhondo ya Mulungu ya Armagedo idzatchinjiriza chiwonongeko cha anthu onse
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Kuyesayesa kulikonse kwa kukhala wosatenga mbali m’nkhondo ya Mulungu kudzakutaikiritsani moyo wanu pa Armagedo!