Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 5/15 tsamba 24-27
  • Mungapite Patsogolo Mwauzimu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mungapite Patsogolo Mwauzimu
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amalimbitsa Atumiki Ake
  • ‘Vulani Munthu Wakale’
  • Ngati “Moto” m’Kati Mwathu
  • Monga Ngati Kunoledwa ndi Chitsulo
  • Zifukwa Zabwino Zopitira Patsogolo Mwauzimu
  • Kodi Mumayamikira Gulu Lapadziko Lapansi la Yehova?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Ndinapeza Chinthu Chamtengo Wapatali Kuposa Dayamondi
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2014
  • Kodi Tingatani Kuti Tizichita Zambiri M’gulu la Yehova?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Achinyamata, Pitirizani Kupita Patsogolo Mwauzimu Pambuyo Pobatizidwa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 5/15 tsamba 24-27

Mungapite Patsogolo Mwauzimu

CHUMA chenicheni chingavute kuchizindikira. Nzoteronso ndi madiamondi. Ngakhale kuti diamondi wopukutidwa amanyezimira kwambiri, diamondi wosapukuta sanyezimira kwenikweni. Komabe, diamondi wosapukutidwa angakhale mwala wokongola.

Akristu amafanana ndi madiamondi osapukutidwa m’njira zambiri. Ngakhale kuti sitinakhalebe angwiro, tili ndi chuma chimene Yehova amasangalala nacho. Monga madiamondi, tonsefe tili ndi mikhalidwe yathu yosiyanasiyana. Ndipo aliyense wa ife angapitebe patsogolo mwauzimu ngati ndicho chikhumbo chathu chochokera pansi pamtima. Umunthu wathu ukhoza kupukutidwa, kotero kuti unganyezimire kwambiri molemekeza Yehova.​—1 Akorinto 10:31.

Atadulidwa ndi kupukutidwa, diamondi amaikidwa m’malo amene amawonjezera kunyezimira kwakeko. Mofananamo, Yehova angatigwiritsire ntchito m’malo, kapena maudindo, osiyanasiyana ngati ‘tivala munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.’​—Aefeso 4:20-24.

Kupita patsogolo mwauzimu kumeneku sikungangochitika, monganso mmene diamondi wokumbidwa kumene saoneka ngati mwala wokongola. Tingafunikire kuthetsa chofooka china chomwe chimatibwezera m’mbuyo, kusintha kaonedwe kanthu ka udindo, kapena ngakhale kuyesa kusintha zizoloŵezi zina zauzimu. Koma tingathe kupita patsogolo ngati tikufunadi kutero, popeza kuti Yehova Mulungu amatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.”​—2 Akorinto 4:7, NW; Afilipi 4:13.

Yehova Amalimbitsa Atumiki Ake

Kudula madiamondi kumadalira pa kudziŵa kadulidwe kake kenikeni, popeza kuti mutangobenthula diamondi wosapukutidwayo, kachidutswako kaŵirikaŵiri kamakhala kopanda ntchito. Zinthu zamtengo wapatali​—nthaŵi zina kukwana 50 peresenti ya mwala wosadulidwawo​—zimafunika kuchotsedwa kuti mupange maonekedwe omwe mukufuna. Ifenso timafunikira chidaliro chodza ndi chidziŵitso cholongosoka kuti tithe kukonza umunthu wathu ndi kupita patsogolo mwauzimu. Makamaka tikhale ndi chidaliro chakuti Yehova adzatipatsa mphamvu.

Komabe, tingadzimve kukhala wosakwanira, kapena tingaganize kuti sitingachite zambiri. M’mbuyomu, atumiki enanso okhulupirika a Mulungu nthaŵi zina ankamva motero. (Eksodo 3:11, 12; 1 Mafumu 19:1-4) Mulungu atamsankha kuti akhale “mneneri wa mitundu ya anthu,” Yeremiya anati: “Taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana.” (Yeremiya 1:5, 6) Komabe mosasamala kanthu za kunyinyirika kwake, Yeremiya anadzakhala mneneri wolimba mtima amene anapereka mauthenga achindunji kwa anthu ovuta. Kodi zinatheka bwanji? Anaphunzira kudalira Yehova. Kenako Yeremiya anadzalemba kuti: “Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova.”​—Yeremiya 17:7; 20:11.

Lerolino, Yehova amalimbikitsanso amene amamkhulupirira. Edward,a tate wa ana anayi amene ankapita patsogolo pang’onopang’ono, anaona kuti izi nzoona. Iye anasimba kuti: “Ndinali mmodzi wa Mboni za Yehova kwa zaka zisanu ndi zinayi, koma ndinkaoneka kuti ndinaima pamodzimodzi mwauzimu. Vuto linali lakuti sindinali kusonkhezeredwa kwenikweni ndipo ndinali wosatsimikizira. Nditasamukira ku Spain, ndinafikira pampingo waung’ono umene unali ndi mkulu mmodzi ndi mtumiki wotumikira mmodzinso. Chifukwa cha kusoŵako, mkuluyo anandipempha kuchita ntchito zochuluka. Poyambirira ndinkanjenjemera pamene ndinali kukamba nkhani ndiponso mbali zina za misonkhano. Komatu, ndinaphunzira kudalira Yehova. Nthaŵi zonse mkuluyo anali kundiyamikira ndipo ankandipatsa malingaliro aluso ondithandiza kuwongolera.

“Panthaŵi yomweyonso, ndinawonjezera utumiki wanga wa m’munda ndiponso ndinayamba kutsogolera bwino banja langa mwauzimu. Monga chotsatirapo, choonadi chinali ndi tanthauzo lalikulu kwa onse m’banjamo, ndipo ndinali wokhutira kwambiri. Tsopano ndine mtumiki wotumikira, ndipo ndikuyesetsa kuti ndikulitse mikhalidwe yofunikira woyang’anira wachikristu.”

‘Vulani Munthu Wakale’

Monga mmene Edward anazindikirira, kupita patsogolo mwauzimu kumafuna kukhulupirira Yehova. Kukulitsanso ‘umunthu watsopano’ wonga wa Kristu kulinso kofunika. Kodi izi zingachitidwe motani? Sitepe loyamba ndilo ‘kuvula’ mikhalidwe ija yomwe ndi yamunthu wakale. (Akolose 3:9, 10) Monga mmene zinthu zosafunikira, monga ngati miyala ina, zimafunikira kuchotsedwa mu diamondi wosapukutidwa kuti akhale mwala wonyezimira, chomwechonso kaganizidwe ka “dziko lapansi” kamafunika kuchotsedwa kuti umunthu wathu watsopano ukhoze kuŵala.​—Agalatiya 4:3.

Malingaliro ena oterowo ndi kusafuna kulandira udindo poopa kuti zambiri zidzafunidwa kwa ife. Zoonadi, udindo ndi ntchito, koma ndi ntchito yokhutiritsa. (Yerekezerani ndi Machitidwe 20:35.) Paulo anavomereza kuti kudzipereka kwaumulungu kumafuna kuti ‘tigwiritse ntchito ndi kuyesetsa.’ Iye anati, timatero mwachimwemwe, “chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo,” iye amene saiŵala ntchito imene timachita m’malo mwa Akristu anzathu ndi anthu ena.​—1 Timoteo 4:9, 10; Ahebri 6:10.

Madiamondi ena amakhala ndi “timing’alu” tomwe timang’ambika pamene anali kupangika ndipo amafunika kusamala nawo. Komabe, ndi chida chofufuzira chotchedwa polariscope, wopukuta angaone pamene pali mng’alu ndipo angapukute mwalawo bwinobwino. Mwina tili ndi vuto la mng’alu mumtima, kapena tili ndi vuto ndi umunthu wathu, chifukwa cha mmene tinakulira kapenanso zosautsa zimene takumana nazo. Kodi tingatani? Choyamba, tiyenera kuvomereza mwa ife tokha kuti tili ndi vuto, ndiyeno nkutsimikizira kulithetsa kumlingo umene tingathe. Tiyeneradi kutula zolemetsa zilizonse pamaso pa Yehova m’pemphero, mwinanso tikumafuna chithandizo chauzimu kwa mkulu wachikristu.​—Salmo 55:22; Yakobo 5:14, 15.

Nicholas anavutikapo ndi mng’alu wa mumtima woterewo. Anasimba kuti: “Atate anga anali chidakwa, ndipo anali kutivutitsa kwambiri ine ndi mlongo wanga. Nditasiya sukulu ndinaloŵa usilikali, koma chizoloŵezi changa choukira chinandiika m’mavuto mwamsanga. Akuluakulu a asilikali anandiika m’ndende chifukwa chogulitsa mankhwala osokoneza bongo, nthaŵi inanso ndinathaŵa. Kenako ndinasiya usilikaliwo, koma mavuto ndinali nawobe. Ngakhale kuti moyo wanga unali wosokonezeka chifukwa cha mankhwala osokoneza bongo ndi uchidakwa, ndinkakonda Baibulo ndipo ndinali kufuna nditapeza chifuno cha moyo. Kenaka ndinakumana ndi Mboni za Yehova, ndinasintha moyo wanga, ndipo ndinalandira choonadi.

“Komabe, zinanditengera zaka kuti ndivomereze ndi kuthetsa vuto lomwe ndinali nalo. Ndinkadana ndi kundilamulira ndipo ndinkakula mtima pamene ndinkapatsidwa uphungu. Ngakhale kuti ndinali kufuna kuti Yehova andigwiritsire ntchito mmene angafunire, chofooka chimenechi chinali kundilepheretsa. Kenaka, ndi chithandizo cha akulu aŵiri omvetsetsa, ndinavomereza vuto langa ndipo ndinayamba kugwiritsira ntchito uphungu wawo wachikondi wa m’Malemba. Ngakhale kuti nthaŵi zina ndimakhala ndi mkwiyo, tsopano ndimatha kulamulira mzimu wanga wopanduka. Ndikuthokoza kuti Yehova analeza nane mtima ndiponso kuti akulu anandithandiza. Chifukwa cha kupita kwanga patsogolo mwauzimu, posachedwapa ndaikidwa kukhala mtumiki wotumikira.”

Monga mmene Nicholas anaonera, kusintha mikhalidwe yozoloŵereka kwambiri si kwapafupi. Tingakhale ndi vuto lofananalo. Mwinamwake timakhudzidwa ndi zilizonse. Tingakhale tili ndi dandaulo, kapena tingamafune kukhala aufulu mopambanitsa. Choncho, kupita kwathu patsogolo kwachikristu kungadodometsedwe. Opukuta diamondi amakumananso nzofananazo ndi miyala yomwe amaitcha kuti naats. Kwenikweni imeneyi ndi miyala iŵiri imene inaphatikana pamene diamondi anali kupangika. Kaamba ka chimenecho, ma naats amakhala ndi mapangidwe aŵiri osiyana amene amasautsa podula molondolera mizere ya mwalawo. Ifeyo, timapeza kuti mzimu wathu wofunitsitsa ukulimbana ndi thupi lathu lopanda ungwiro. (Mateyu 26:41; Agalatiya 5:17) Nthaŵi zina, tingafune kungosiya osalimbana nazonso, tikumati zolakwika zaumunthu wathu zilibe kanthu. Tingaganize kuti, ‘palibe vuto, poti makolo anga ndi anzanga amandikondabe.’

Komabe, ngati titi titumikire abale athu ndi kulemekeza Atate wathu wakumwamba, tifunikira ‘kukonzedwa atsopano mu mzimu wa mtima wathu,’ mwa kuvala munthu watsopano. Kuyesayesa nkopindulitsadi, monga mmene Nicholas ndi enanso ambiri angachitire umboni. Wopukuta diamondi amadziŵa kuti kulakwitsa pamodzi kukhoza kuwononga diamondi yense. Mofananamo, kulekerera mbali yofooka ya umunthu wathu kungawononge kaonekedwe kathu kauzimu. Choipa zedi nchakuti chofooka chachikulu chingatigwetse mwauzimu.​—Miyambo 8:33.

Ngati “Moto” m’Kati Mwathu

Wopukuta diamondi amafuna atatulutsa kuwala komwe kuli m’diamondi. Izi zimachitika mwa kukonza mbali ndi mbali za diamondiyo kuti zipange chomwe amatcha kuti utawaleza. M’diamondimo, kuwala kwa mitundumitundu kumang’anipira, ndi kutulutsa kuwala kumene kumapangitsa madiamondi kunyezimira. Mofananamo, mzimu wa Mulungu ungakhale ngati “moto” m’kati mwathu.​—1 Atesalonika 5:19, NW; Machitidwe 18:25; Aroma 12:11.

Koma bwanji ngati tiona kuti tikufunikira kusonkhezeredwa mwauzimu? Kodi zingachitike motani? Tifunikira ‘kuganizira njira zathu.’ (Salmo 119:59, 60) Zimenezi zingaphatikizepo kudziŵa zinthu zimene zimatibwezera m’mbuyo mwauzimu ndipo kenaka kuona zochita za teokratiki zimene tifunikira kuzilondola mwamphamphu. Tingakulitse kuyamikira zinthu zauzimu mwa phunziro laumwini la nthaŵi zonse ndi kupemphera mofunitsitsa. (Salmo 119:18, 32; 143:1, 5, 8, 10) Ndiponso, mwa kugwirizana ndi amene ali olimba m’chikhulupiriro, tidzapangitsa chosankha chathu cha kutumikira Yehova mwachangu kukhala cholimba.​—Tito 2:14.

Louise, mtsikana wachikristu, anavomereza kuti: “Ndinalingalira za kuchita upainiya wokhazikika kwa zaka ziŵiri ndisanalembetse kuti ndikhale mpainiya, kapena wolengeza Ufumu wa nthaŵi zonse. Palibe chomwe chinali kundiletsa, koma kuti ndinali ndi moyo wofewa, ndipo sindinkayesera kuusiya. Kenaka atate anamwalira mwadzidzidzi. Ndinazindikira kuti moyo ndi wosakhala kutha ndi kuti ine ndinali kuseŵera nawo. Motero ndinasintha kaonekedwe kanga kauzimu, ndinawonjezera utumiki wanga, ndipo ndinakhala mpainiya wokhazikika. Amene anandithandiza kwenikweni pankhaniyi anali abale ndi alongo anga auzimu amene nthaŵi zonse anali kuchirikiza makonzedwe autumiki wakumunda ndi amene anali kutsagana nane mu utumiki. Ndaphunzira kuti kaya pazabwino kapena pazoipa, timagaŵana mapindu ndi zolinga za anzathu.”

Monga Ngati Kunoledwa ndi Chitsulo

Madiamondi ndi miyala yolimba kwambiri padziko lapansi. Choncho, diamondi amadulidwa ndi mwalanso wa diamondi. Izi zingakumbutse ophunzira Baibulo za mwambi umene umati: “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.” (Miyambo 27:17) Kodi nkhope ya munthu ‘imanoledwa’ bwanji? Munthu wina anganole kaganizidwe ndi mkhalidwe wauzimu wa munthu winanso, monga mmene chitsulo chingagwiritsiridwe ntchito kunola mpeni wopangidwa ndi chitsulo chomwecho. Mwachitsanzo, ngati titachita tondovi chifukwa cha kukhumudwa ndi zinazake, tingapeze bwino pamene munthu wina atilimbikitsa. Motero nkhope yathu yachisoni ingaoneke yosangalala, ndipo tingakhalenso ndi mphamvu zochitira utumiki ndi changu china. (Miyambo 13:12) Akulu a mpingo makamaka ndiwo angathandize kutinola mwa kupereka chilimbikitso ndi uphungu wam’malemba kuti tiwongolere. Amatsatira pulinsipulo lomwe Solomo analemba kuti: “Ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake; ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira.”​—Miyambo 9:9.

Zoonadi, maphunziro auzimu amatenga nthaŵi. Kwazaka zoposa khumi, mtumwi Paulo anali kugaŵana ndi Timoteo zimene iye anali kudziŵa ndiponso njira zake zophunzitsira. (1 Akorinto 4:17; 1 Timoteo 4:6, 16) Maphunziro anthaŵi yaitali amene Mose anapatsa Yoswa kwa zaka zoposa 40 anapindulitsa mtundu wa Israyeli kwanthaŵi yaitali. (Yoswa 1:1, 2; 24:29, 31) Elisa anayenda ndi mneneri Eliya mwinamwake kwa zaka 6, akumalandira maziko abwino a utumiki wake umene unali kudzatenga pafupifupi zaka 60. (1 Mafumu 19:21; 2 Mafumu 3:11) Mwakupereka maphunziro anthaŵi zonse moleza mtima, akulu amatsatira chitsanzo cha Paulo, Mose, ndi Eliya.

Kumyamikira munthu ndi mbali yofunika yakuphunzitsa. Kuyamikira munthu moona mtima chifukwa chokamba nkhani bwino kapena zochita zina zimene ziyenera kutamandidwa kungachititse ena kufuna kutumikira Mulungu mokulirapo. Chiyamikiro chimabweretsa chidaliro chimene chimasonkhezera kuwongolera zofooka. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 11:2.) Kukhala otanganitsidwa ndi ntchito yolalikira Ufumu ndi zochita zina zampingo kumaperekanso chilimbikitso kuti munthu apite patsogolo m’choonadi. (Machitidwe 18:5) Pamene akulu akupatsa abale ntchito mogwirizana ndi kupita kwawo patsogolo mwauzimu, zimapatsa amuna amenewa chidziŵitso chamtengo wapatali ndipo zingalimbikitsedi chikhumbo chawo cha kupitabe patsogolo mwauzimu.​—Afilipi 1:8, 9.

Zifukwa Zabwino Zopitira Patsogolo Mwauzimu

Madiamondi amaonedwa kukhala amtengo wapatali. Ndi zoteronso ndi awo amene tsopano akugwirizana ndi banja lapadziko lonse la olambira Yehova. Ndipotu, Yehova mwiniyo amawatcha kuti zinthu “zofunika,” kapena “zamtengo wapatali,” za amitundu onse. (Hagai 2:7, NW, mawu amtsinde) Chaka chatha, anthu 375,923 anakhala Mboni za Yehova zobatizidwa. Kuti onsewa asamaliridwe, pali kufunika ‘kukuza malo a hema.’ Mwakupita patsogolo mwauzimu​—ndi mwakukalimira maudindo autumiki achikristu​—nkotheka kusamalira nawo anthu omawonjezerekawa.​—Yesaya 54:2; 60:22.

Mosiyana ndi madiamondi amene amawasungira m’nyumba ndipo saonekaoneka, chuma chathu chauzimu chingawale kwambiri. Ndipo pamene nthaŵi ndi nthaŵi tipukuta ndi kusonyeza mikhalidwe yathu yachikristu, timalemekeza Yehova Mulungu. Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti: “Muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:16) Ndithudi, zimenezi zimatipatsa chifukwa chokwanira chopitira patsogolo mwauzimu.

[Mawu a M’munsi]

a Tabwerekera maina m’nkhaniyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena