-
Mafunso Ochokera kwa OŵerengaNsanja ya Olonda—1991 | August 1
-
-
Bukhu la Miyambo liri ndi mavesi ambiri amene amaima paokha monga ndemanga zapadera za uphungu, koma Miyambo 27:23 ndimbali ya gulu la mavesi akuti: ‘Udziwitsitse zoweta zako ziri bwanji, Samalira magulu ako. Pakuti chuma sichiri chosatha; Kodi korona alipobe mpaka mibadwo mibadwo? Amatuta maudzu, msipu uoneka, Achera masamba a kumapiri. Ana a nkhosa akuveka, Atonde aombera munda; Mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya; Ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.’—Miyambo 27:23-27.
-
-
Mafunso Ochokera kwa OŵerengaNsanja ya Olonda—1991 | August 1
-
-
‘Chuma,’ kapena katundu wopezedwa m’mabizinesi ofulumira, ndi kukhupuka kotulukapo (“korona”), zikhoza kuzimiririka mosavuta, monga momwe ambiri angachitire umboni za chimenechi. Chotero moyo wokhweka umaloŵetsamo zambiri, wonga uja wokhala ndi abusa amakedzana m’kusamalira zoweta. Njira ya moyo imeneyo sinali yokhweka m’lingaliro lakukhala wosasamala. Mbusa anafunikira kukhala watcheru ku nkhosa zake, akutsimikizira kuti nkhosazo zinali zotetezeredwa. (Salmo 23:4) Ngati, pozisamalira, anawonapo nkhosa yodwala kapena yovulala, anaidzoza mafuta otonthoza. (Salmo 23:5; Ezekieli 34:4; Zekariya 11:16) M’zochitika zambiri mbusa wakhama yemwe anaika mtima wake pa zoweta zake anaona zoyesayesa zake zikubala zipatso—kukula kwapang’onopang’ono kwa gulu lake la nkhosa.
-