Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 9/8 tsamba 22-24
  • Nchifukwa Ninji Ndimapsya Mtima?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nchifukwa Ninji Ndimapsya Mtima?
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chimene Timakwiyira
  • Kulekelera Mkwiyo
  • Kodi Ndingalamulire Motani Kupsya Mtima Kwanga?
    Galamukani!—1987
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kukwiya?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Nthaŵi Zonse Kumakhala Kulakwa Kukwiya?
    Galamukani!—1994
  • Nkulamuliriranji Mkwiyo Wanu?
    Galamukani!—1997
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 9/8 tsamba 22-24

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Nchifukwa Ninji Ndimapsya Mtima?

“Pamene ndiri wokalipa, ndimakhala wokwiyitsidwa, ndipo simungafune kusendera pafupi ndi ine. . . . Ndimawoneka wokwiya pamaso . . . Nthaŵi zina ndimangofuula.”—Evan wa zaka zakubadwa 11.

MLONGO wanu wawononga chovala chanu chapamtima. Mphunzitsi wanu sanawonetse chilungamo mu kuchonga mayeso anu. Pamene mukuchifunitsitsa, choumitsa tsitsi lanu chaleka kugwira ntchito. Kwa achichepere ambiri, chirichonse cha zolowereramo zoterezi, chisalungamo, ndi zokhumudwitsa zingabweretse kudzimva kwakukulu kwa mkwiyo.

Nkhani ina mu magazini ya Health yolembedwa ndi Dr. Georgia Witkin-Lanoil inalongosola kuti: “Pamene bongo liyankha ku chochititsa mkwiyo, dongosolo la m’mitsempha ya uthenga yogwira ntchito payokha imadzutsidwa. Zodzutsa ziwalo zathupi, zomwe zimatulutsidwa kuchokera ku ziwalo zathupi zosunga zodzutsazo, zimayamba kuthira m’mitsempha ya mwazi, kuwonjezera liwiro la mtima, ndi kupuma, ndi kuchititsa kutulutsidwa kwa shuga yosungidwa kaamba ka mphamvu.”

Ndi zotulukapo zotani? “Zochita zomwe timatenga pansi pa chisonkhezero ndi zodzutsa ziwalo zathupi lathu,” akupitiriza Dr. Witkin-Lanoil, “zimakhala kaŵirikaŵiri kuyankha kopambanitsa. Timafuula, kukankhira pambali chowonadi chosatsimikizirika, kutidzimula, kuvulaza, kuwononga kapena kusiya mkhalidwe m’mkangano.” Nkhani ina mu magazini ya ’Teen inawona mofananamo kuti mkwiyo “ungakuchititseni inu kukamba zinthu zomwe simunatanthauze, kutaya mabwenzi anu—ndipo ngakhale kumvera kuwawa cha mkatikati.”

Kodi munapsyapo mtima ndi kalelonse? Ngati ndi tero, simuli nokha. Monga ambiri a ife, inu mosakaikira munadzimva wopusa pambuyo pake ndipo munadabwitsidwa, ‘nchifukwa ninji ndinachita chotero?’ Inde, nchifukwa ninji chiri chovuta chotero kwa ena kulamulira mkwiyo wawo? Kodi chiri chophulapo kanthu kuyesa kuchita tero?

Chifukwa Chimene Timakwiyira

Mbali ya chifukwa chimene ife tiri okhoza kumvera mkwiyo kuchokera ku nthaŵi ndi nthaŵi chiri chakuti tinapangidwa “m’chifaniziro cha Mulungu.” (Genesis 1:27) Mulungu iye mwiniyo angakwiye! Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ananena kuti: “Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera kumwamba, uwonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungamo cha anthu, amene akanikiza pansi chowonadi m’chosalungama chawo.”—Aroma 1:18.

Tadziwani, ngakhale kuli tero, kuti mkwiyo wa Yehova Mulungu umatuluka kuchokera mu chikondi cha chilungamo ndi chiweruzo. Mkwiyo wa Mulungu suli kokha kaamba ka ‘kungolekerera mkwiyo.’ Iye amalamulira mkwiyo wake ndipo amaulongosola iwo mu njira ya chilungamo. Chotero, pamene anabweretsa chiwonongeko pa dziko loipa ndi chigumula chadziko lonse, iye sanalephere kulamulira mkhalidwewo. M’malo mwake, iye anasunga “Nowa ndi anzake asanu ndi aŵiri.” (2 Petro 2:5) Yehova motero angalongosoledwe kukhala monga “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekerera, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi.”—Eksodo 34:6.

Chifukwa chakuti Mulungu analenga anthu mu chifaniziro chake, tiri ndi nzeru ya mkatikati ya chilungamo. Chotero titakumana ndi kuchitiridwa kosalingaliridwa kapena chisalungamo, ife mwachibadwa tingangomva ukali ukuima mkati mwathu. Ichi chinachitika kwa oŵerengeka a anthu a Mulungu mu nthaŵi za Baibulo.

Mwachitsanzo, Mose, mtsogoleri wa mtundu wa Aisrayeli, anakalipa pamene amuna osiyanasiyana anatsogolera kukutsutsana naye. (Numeri 16:1, 15) Ndipo ngakhale Yesu Kristu anakwiyapo! Pamene anawona kuti anthu anali kuchita za malonda m’kachisi wa Mulungu wa kulambiriramo, iye anawalamulira mwaukali: “Chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.” (Yohane 2:13-16) Kukwiya kwa chilungamo kuli motero koyenerera kaamba ka Akristu.

Mwatsoka, kukwiya kwathu kwambiri sikuli kochititsidwa ndi chilungamo. Ichi chiri chifukwa chakuti, monga mmene Baibulo limanenera, ife “tonsefe tiri ogwidwa ndi uchimo.” Motero limapitiriza kuti: “Palibe m’modzi wolungama, inde, palibe m’modzi.” (Aroma 3:9, 10) Chotero, ndiko kuti, uchimo wathu weniweniwo—ndi zolephera za ena—ziri magwero ochititsa a ziyambukirozo. “Nthaŵi zina anthu amangokuputani kwambiri,” watero Stephanie wachichepere.

Koma kaŵirikaŵiri timakwiyitsidwa popanda chochititsa chenicheni! Mosiyana ndi Yehova yemwe amawona chirichonse, tiri ndi kawonedwe kokhala ndi polekezera ka chifukwa chirichonse. (Ahebri 4:12, 13) Mwachitsanzo, munthu wanzeru Solomo anawona kuti “mawu owawitsa aputa msunamo.” (Miyambo 15:1) Nthaŵi zina, ngakhale kuli tero, “mawu” amakambidwa ndi chilungamo, kapena angangokhala kuseka kopusa kopangidwa mwadala kapena kuseka chiphwete chochepa cha kungofuna kusewera. Popanda kuzindikira izi, timavutitsidwa.

Potsirizira pake, pali nsonga yakuti kukwiyitsidwa kumasiyanasiyana, ndipo ena a ife timawonekera kukhala ovutitsidwa kwenikweni ndi mkwiyo kuposa ena. Ndipo monga wachichepere, inu mwangoyamba kumene kuphunzira mmene mungalamulire zifuno zonse zatsopano ndi zisonkhezero zimene zimabweretsedwa ndi unamwali. Inu mungadzimve kukhala osadzitsimikizira inumwini, wozindikira kwenikweni ku kusulizidwa. Kufikira mutapeza kulamulira kwa malingaliro anu, inu muli wosalimba ku kukwiyitsidwa—makamaka kuchokera mkatikati mwa banja. “Ndimapsya mtima ndi mlongo wanga,” anaulula tero Lorie wa zaka zakubadwa 15. “Iye amadziŵa kundiputa mwakunena chinthu chinachake chopusa kapena mwakungolungamitsa chirichonse chimene ndimanena.” Kusamvana kungabuke mofananamo pakati pa inu ndi makolo anu.

Ndithudi, ngakhale ndi tero, kokha chirichonse chingakupangitseni inu kukhala wokwiya ngati mwachilekerera. Funso ndi lakuti, Kodi mumachita bwanji ndi malingaliro oterowo a mkwiyo?

Kulekelera Mkwiyo

Bukhu lakuti Reaching Your Teenager linawona kuti “anthu ambiri sadziŵa mmene angawonetsere mkwiyo mwanzeru.” Ena amangochita kukalipa kwaubwana. Ena amakhala achiwawa, mwinamwake mwa pakamwa kapena mwa kuthupi. Ena amawoneka odekha kunja koma mkati ali okwiyitsidwa. Monga mmene mkazi wina wachichepere ananenera kuti: “Ndikakwiya sindifuula, ndimangokhala chete ndipo osalankhulalankhula,” ndipo enanso amangolowa mu galimoto lawo ndi kuchotsapo mkwiyo wawo mu njira imene akuyendetsera.

Mkwiyo wolekereredwa, ngakhale kuli tero, sumakhala womangirira nthaŵi zambiri. Profesa Gary Schwartz wa Yuniversite ya Yale anadzimva kuti ukali ‘umatulutsa ziyambukiro zowawa kwambiri pa mtima ndi zokhalitsa kuposa kudzimva kwina kuli konse, ngakhale mantha.’ Dr. Redford B. Williams, Jr., wa Yuniversite ya ku Duke ananena kuti: “Maphunziro ambiri tsopano amalingalira kuti kuchuluka kowopsya kwa imfa za ana osakwana masiku kungakhale kogwirizana ndi ukali.” Ndithudi sichingakhale chaumoyo kukhazikitsa mkhalidwe wa ‘kutulutsa mawu olongolola’ pa kukwiyitsidwa kulikonse. “Mtima wabwino ndi moyo wathupi,” unatero mwambo wakale.—Miyambo 14:30.

Kuwonjezerapo, kukwiya kosadziletsa nthaŵi zambiri kumapangitsa mkhalidwe woipa kuipirako. Kumbukirani cholemba cha Baibulo cha abale aŵiri otchedwa Simeoni ndi Levi amene mlongo wawo anaipsyidwa mwa kugonana. Mwachimvekere, iwo analidi okwiyitsidwa pamene anamva ponena za icho! Koma ndimotani mmene anawonetsera mkwiyo wawo? Baibulo limati kuti iwo anayendetsa zochitikazo kotero kuti akhale okhoza kupha mopanda chifundo mnyamata wachichepere yemwe anali ndi thayo la kuchita chigololo chogwirira—kuphatikizapo ndi amuna a m’banja lake ndi amuna a mu mzinda wake!—Genesis, mutu 34.

Zaka zingapo pambuyo pake pakama wake wa imfa, atate wawo Yakobo anakhala wokhoza kukumbukira chochitika chachiwawacho. Kodi iye anawayamikira kaamba ka kubwezera kwaukaliku? Mosiyanako, iye anatemberera mkwiyo wawo chifukwa chakuti “kunali kowopsya; ndi kupsya mtima kwawo, chifukwa kunali kwankhalwe.” (Genesis 49:7) Inde, chimene iwo anachita mkupsya mtima chinali choipitsitsa kuposa kukwiyitsidwa kumene kunawaputa iwo poyambapo! Palibe chomangirira chimene iwo anafikiritsa ndipo anawononga dzina lawo.

Nchosadabwitsa, mwakutero, kuti miyambo imati: “Wokangaza kukwiya adzachita utsiru.” (Miyambo 14:17) Sinthaŵi zonse pamene wina m’mkhalidwe wa kukwiyitsidwa angaganize ndi kuchita mokomera mbali imodzi. Sinthaŵi zonse pamene wokwiyitsidwa angafunefune njira Yachikristu yothetseramo choipa. Mawu a wolemba wa Baibulo Yakobo mwakutero amakhala owona: “Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.” (Yakobo 1:20) Mkwiyo wa kukalipa, kutukwana kowirikiza, ndi kukwiyitsidwa kwa mkatikati ziri zosamangirira.

Ndithudi, kulekerera unyinji wa mawu achipongwe pa wina wake yemwe wakulakwirani kungawonekere kukhala kwabwino panthaŵiyo. Koma inu nthaŵi zambiri mumadzakhala wachisoni kaamba ka kubwetukako—makamaka pamene wina ameneyo ali wokulembani ntchito, mphunzitsi, kapena kholo! (Yerekezani Mlaliki 10:4.) Miyambo 29:11 mwakutero imati: “Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse [mwakupsya mtima]; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.”

Koma kodi ndimotani mmene mungachitire ichi? Nkhani yotsatira idzalongosola ichi.

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Kusalungama kwathu—ndi kulephera kwa ena—kuli magwero ochititsa kuphophonya

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi chiri chophulapo kanthu kulekerera mkwiyo wanu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena