-
Pangani Ubwenzi Wathithithi ndi YehovaNsanja ya Olonda—2000 | January 15
-
-
Mfumu yanzeru ikupitiriza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze [“um’zindikire,” NW] m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.”—Miyambo 3:5, 6.
-
-
Pangani Ubwenzi Wathithithi ndi YehovaNsanja ya Olonda—2000 | January 15
-
-
Kodi ‘tingam’zindikire Yehova m’njira zathu zonse’ motani? Wamasalmo wouziridwayo akuti: “Ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.” (Salmo 77:12) Popeza Mulungu saoneka, kuti tipange unansi wathithithi ndi iye, n’kofunika kusinkhasinkha pa zochita zake zazikulu ndi mmene amachitira ndi anthu ake.
Pemphero ndi njiranso yofunika pakuzindikira Yehova. Mfumu Davide anaitanira pa Yehova “tsiku lonse.” (Salmo 86:3) Nthaŵi zambiri Davide anali kupemphera usiku wonse, monga pamene anathaŵira m’chipululu. (Salmo 63:6, 7) “Mupemphere nthaŵi yonse mwa Mzimu,” analangiza motero mtumwi Paulo. (Aefeso 6:18) Kodi timapemphera kangati? Kodi timasangalala kulankhulana moona mtima ndi Mulungu? Pamene tili m’mikhalidwe yovuta, kodi timapemphera kuti atithandize? Kodi mwapemphero timafuna chitsogozo chake tisanasankhe zofunika? Mapemphero athu a mtima wonse kwa Yehova adzapangitsa iye kutikonda. Ndipo tili ndi chidaliro kuti adzamva mapemphero athu ndipo ‘adzaongola mayendedwe athu.’
-