Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 10/1 tsamba 15-20
  • Chilango Chimabala Chipatso cha Mtendere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilango Chimabala Chipatso cha Mtendere
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nthyole ya Chilango
  • Magwero a Chilango
  • Kupereka ndi Kulandira Chidzudzulo
  • Pirirani Chilango ndipo Tutani Chipatso cha Mtendere
  • Kumvetsa Cholinga cha Kulanga
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kupatsidwa Chilango Kumasonyeza Kuti Yehova Amatikonda
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • ‘Nthyole ya Chilango’ Kodi Njachikale?
    Galamukani!—1992
  • Kodi Mungatani Kuti Muzilangiza Bwino Ana Anu?
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 10/1 tsamba 15-20

Chilango Chimabala Chipatso cha Mtendere

“Chilango chirichonse pakuchitika sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.”​—AHEBRI 12:11.

1. (a) Nchiyani chimene Mawu a Yehova amanena ponena za kuthekera kwa munthu kwa kutsogoza njira ya umoyo wake, koma nchiyani chimene munthu amanena? (b) Ndani amene watsimikiziridwa kukhala wowona, ndipo ndani wabodza?

MAWU A YEHOVA amanena kuti “sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Munthu amanena kuti chiri mwa iye kuchita tero, ndipo kuyambira pa kuulika kwa kuukira mu Edeni, iye wachita tero. Kuyambira pamenepo kufikira tsopano, kwa anthu ambiri chakhala monga mmene chinaliri m’masiku a Oweruza mu Israyeli: “Yense anachita chomkomera pamaso pake.” (Oweruza 21:25) Koma mawu a Yehova pa Miyambo 14:12 atsimikizira kukhala owona: “Iripo njira yowoneka kwa mwamuna ngati yowongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.” Kwa zaka 6,000, anthu atenga njira yowoneka monga yowongoka kwa iwo, ndipo kwa nthaŵi yonseyi yatsogolera ku nkhondo, njala, matenda, upandu, ndi imfa. Mbiri yakale yatsimikizira mawu a Yehova kukhala owona ndi njira za munthu kukhala za bodza.

2. Ndi kaimidwe kotani kamene akatswiri odziŵa za malingaliro a ana amatenga pa kumenya, koma ndi chipatso cha mtundu wanji chimene kulekerera kwawo kwatulutsa?

2 Anthu opanda ungwiro amafunikira chilango. Iwo amachifunikira icho kuyambira ku ubwana kupita mtsogolo. Mawu a Mulungu amanena kuti: “Wolekerera mwana wake osam’menya amuda, koma womkonda amyambize kumlanga.” (Miyambo 13:24) Akatswiri ambiri odziŵa za malingaliro a ana amatsutsa nzeru yaumulungu imeneyi. Zaka zingapo zapita mmodzi anafunsa kuti: “Kodi inu amayi mumazindikira kuti nthaŵi iriyonse pamene mumenya mwana wanu mumasonyeza kuti mukumuda mwana wanu?” Koma kulekerera kwawo kwatulutsa chigumula chaupandu wa achichepere kotero kuti woweruza m’bwalo la milandu mu Brooklyn anapanga ndemanga yamphamvu iyi: “Ndikuganiza kuti tifunikira malo osungiramo kaamba ka achichepere ena. Koma chimenecho chikulingaliridwa kukhala chamakedzana tsopano. Tsopano tikuuzidwa kuti simuyenera kumenya mwana wanu; mungakhale mukutsendereza wa nzeru zozizwitsa.” Koma kulekerera kwawo sikunatulutse mbewu za anzeru zozizwitsa​—kokha funde losaweruzika la achichepere aupandu.

3. Kuzikidwa pa ndemanga za olamulira osiyanasiyana, ndi chikhoterero chotani chimene chikukhala chowonekera?

3 Tsopano mphepo za kusintha ziri mu mpweya. Burton L. White, woyang’anira pa kukula kwa mwana, akunena kuti kusamalitsa kwanu sikudzapangitsa mwana wanu “kukukondani mocheperapo kusiyana ndi mmene akanachitira ngati munali wolekerera. . . . Ngakhale ngati mumenya iye mokhazikika, mudzapeza kuti adzapitirizabe kubwera kwa inu.” Iye akugogomezera chifuno choyambirira cha mwana kaamba ka kusefukira kwa “chikondi chosagawanika.” Dr. Joyce Brothers wasimba pa phunziro la mazana a ophunzira m’gredi lachisanu ndi lachisanu ndi chimodzi olangidwa mosamalitsa omwe anakhulupirira kuti malamulo osamalitsa “anali chisonyezero cha chikondi chaukholo.” Journal of Lifetime Living inanena kuti: “Akatswiri odziŵa za malingaliro a ana, otsutsana ponena za kudya kondandalitsidwa motsutsana ndi kolamuliridwa, kumenya motsutsana ndi kusamenya, apeza kuti palibe chirichonse cha izo chomwe chimapanga kusiyana kokha ngati mwana akukondedwa.” Ngakhale Dr. Benjamin Spock, mkonzi wa Baby and Child Care, anatenga mbali ya thayo la kusoweka kwa kusasunthika kwa makolo ndi upandu wotulukamo. Iye ananena kuti thayolo linakhala pa akatswiri, “odziŵa za kusokonezeka kwa bongo kwa ana, odziŵa za malingaliro a ana, aphunzitsi, ogwira ntchito ya mayanjano ndi madokotala a ana achichepere monga inemwini.”

Nthyole ya Chilango

4. Kodi nthyole ya chilango iri chizindikiro cha chiyani, ndipo nchiyani chimene chikusonyezedwa ndi kugwiritsiridwa ntchito kwake koyenerera motsutsana ndi kulekerera?

4 “Nthyole” monga yagwiritsiridwa ntchito pamwambapo sitanthauza kwenikweni kumenya; iyo imaimira njira ya kuwongolera, m’mtundu uliwonse umene ingakhalire. The New International Version pa versili imanena kuti: “nthyole. Mwinamwake mawu ophiphiritsira kaamba ka chilango cha mtundu uliwonse.” Nthyole iri chisonyezero cha ufumu kapena ulamuliro​—m’nkhaniyi ulamuliro wa ukholo. Kholo silimayamikiridwa kaamba ka kulekerera kwake ndi kusakaza: “Amene alekelera kapolo wake [kapena mwana] kuyambira ku ubwana wake pambuyo pake adzakhala wosayamika.” (Miyambo 29:21, NW) Kuchotsa ulamuliro wa ukholo mwa kulekerera kumabweretsa manyazi ndipo kumasonyeza osati chikondi koma kusiyana; kugwiritsira ntchito nthyole ya chilango mwa chifundo, koma mosamalitsa kumawunikira kudera nkhaŵa kwa chikondi. “Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana [Wamwamuna, NW] womlekerera achititsa amake manyazi.”​—Miyambo 29:15.

5. (a) Kodi nchiyani chimene ndemanga imodzi imanena pa Miyambo 13:​24, ndipo ndi lemba lina liti la Baibulo limene limagwirizana nalo? (b) Ndi andani amene amalangidwa ndi Yesu ndi Yehova?

5 Kulozera ku Miyambo 13:24, Keil-Delitzsch Commentary on the Old Testament ikulongosola kuti: “Tate amene mowonadi amafunira zabwino mwana wake amamuyambitsa iye mwamsanga pansi pa chilango chosamalitsa, kum’patsa iye pamene iye akali wokhoza kusonkhezeredwa ndi chitsogozo choyenera, ndi kusalola zolakwa kukhazikika mwa iye; koma iye amene ali wolekerera kulinga kwa mwana wake pamene afunikira kukhala wosamalitsa, amachita ngati kuti iye akufunitsitsadi kumusakaza iye.” Moffatt’s New Translation of the Bible pa Miyambo 19:18 imanena kuti: “Menya mwana wako, pamene padakali chiyembekezo kaamba ka iye, ndipo usamulole iye kupita ku chiwonongeko.” Chilango chokoma mtima koma chosamalitsa kuyambira ku ubwana chimawunikira chikondi chaukholo. Yesu ananena kuti: “Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga.” Ponena za Yehova, “iye amene [Yehova, NW] amkonda amlanga.”​—Chivumbulutso 3:19; Ahebri 12:6.

6. Ndi mtundu wotani umene chilango kaŵirikaŵiri chimatenga, ndipo ndi zitsanzo zotani zimene zimachirikiza yankho lanu?

6 Chilango panthaŵi zina chingaphatikizepo kumenya, koma kaŵirikaŵiri icho sichiri tero. Miyambo 8:33 siinena kuti, “kumva” chilango koma, “imvani mwambo nimukhale anzeru.” Nthaŵi zambiri chilango chimabwera mwa mtundu wa mawu, osati kumenya: “Zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.” “Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.” (Miyambo 4:13; 6:23) Pamene mtumiki wa Yehova Yobu anafunikira chilango, icho chinakwaniritsidwa ndi mawu a chidzudzulo, poyamba ndi Elihu ndipo kenaka ndi Yehova iyemwini. (Yobu, mitu 32-41) Yobu analandira chidzudzulo ndipo anati kwa Yehova: “Ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m’pfumbi ndi m’phulusa.”​—Yobu 42:6.

7. Nchiyani chimene chiri tanthauzo la liwu la Chigriki lotembenuzidwa “chilango,” ndipo ndimotani mmene icho chiyenera kuperekedwera, ndipo nchiyani chimene chimakwaniritsa?

7 Pai·deiʹa ndi liwu la Chigriki lotembenuzidwa “chilango.” M’mitundu yake yosiyanasiyana ilo limatanthauza kuwongolera, kuphunzitsa, “kulangiza mofatsa.” (2 Timoteo 2:25) Imagwirizana mokulira ndi kuwongolera mkhalidwe osati kupeza chidziŵitso. Kulanga kumeneku kuyenera kukhala “ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.” (2 Timoteo 4:2) Chachitiridwa chitsanzo bwino m’chenjezo kwa atate: “Ndipo atate inu, musamakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi m’chilangizo cha [Yehova, NW]”. (Aefeso 6:4) Mokoma mtima koma mosamalitsa, chilango chimenechi chidzalangiza wachichepere m’njira yolingalira ya Yehova.

Magwero a Chilango

8. Ndi kuchokera ku magwero ati ndipo ndi m’njira zotani mmene tingadzilangire ife eni?

8 Maprinsipulo okhudzidwa m’kupatsa chilango ana amagwiranso ntchito kwa akulu. Baibulo liri magwero a chidziŵitso chonena za chimene tingachite ndi chimene sitiyenera kuchita. Pamene tikuŵerenga ilo, tingayese kudziyesa ife eni ndi kugwiritsira ntchito kuwongolera kumene kuli kofunikira. (2 Akorinto 13:5) Pamene tisinkhasinkha pa malamulo a Yehova, malingaliro a kulakwa angabuke mwa ife, kuthandiza kuzindikiritsa masinthidwe ofunikira kwa ife. Chinatero kwa wamasalmo uyu: “Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu. [Ndithu, NW] usikunso imso zanga [“Kulingalira kwanga kozama”] zindilangiza.” (Masalmo 16:7) Tingadzilange ife eni monga mmene anachitira Paulo: “Ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotaika ndekha.”​—1 Akorinto 9:27.

9. Ndi njira zina ziti zimene ziripo kaamba ka kulanga kopindulitsa?

9 Chilango chingabwere kuchokera kwa winawake. Icho chingabwere mwakuyang’ana, kuipidwa, mawu, jesicha, chidzudzulo cha pakamwa. Yesu anapatsa Petro kayang’anidwe komwe kanamukumbutsa iye za chotulukapo cha chimo lake lalikulu, ndipo iye anatuluka ndi kulira mowaŵitsa. (Luka 22:61, 62) Nthaŵi ina chinali chidzudzulo m’mawu anayi omwe anaphwanya Petro: “Pita kumbuyo kwanga, Satana!” (Mateyu 16:23) Kuŵerenga zofalitsidwa za Watch Tower, kupezeka pa misonkhano, kulankhula ndi ena, kupirira zokumana nazo zovuta​—machitachita onse amenewa angatsegule maso athu ku madera amene tifunikira kupanga masinthidwe. Magwero ndi chitsogozo cha chilango chofunika koposa, ngakhale kuli tero, chiri Mawu a Mulungu iwo eni.​—Masalmo 119:105.

10. Kodi miyambo ya Solomo ya kulanga iri ndi phindu lanji, koma ndi njira yotani imene ena amakakamira kutsatira?

10 Miyambo ya Solomo inaperekedwa kwa anthu a misinkhu yonse, kaamba ka iwo kuti adziŵe nzeru ndi mwambo, kuzindikira mawu ozindikiritsa, kulandira mwambo wakusamalira machitidwe, chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika, kuchenjeza achibwana, kuphunzitsa mnyamata kudziŵa ndi kulingalira.” Koma mwinamwake munthu “sangalangizidwe ndi mawu, pakuti azindikira koma osavomereza.” (Miyambo 1:2-4; 29:19) Opanda chidziŵitso ena amaumilira pa kuphunzira kupyolera mu “zokumana nazo zovuta za moyo,” monga mmene anachitira mwana wolowerera “asanazindikire.”​—Luka 15:11-17.

11. (a) Ndimotani mmene mpingo wa ku Akorinto ndi Yona analangidwira? (b) Ndi zilango za mwambo zotani zimene zinaperekedwa pa Davide kaamba ka chigololo chake ndi zoyesayesa zake za kubisa chimo? (c) Ndi mawu ati a mu Masalmo 51 olembedwa ndi Davide amene amasonyeza kuzama kwa kulapa kwake?

11 Kuchitira ndemanga pa kalata imene iye analemba pasadakhale ku mpingo Wachikristu wa ku Korinto, Paulo anati: “Mwamvetsedwa chisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa chisoni chaumulungu, . . . [ndipo chinatulukapo mu] [kuwongolera cholakwa, NW]” (2 Akorinto 7:9-11) Yona analangidwa kupyolera m’mafunde a m’nyanja ndi chinsomba chachikulu. (Yona 1:2, 3, 12, 17; 2:10; 3:1-4) Chigololo cha Davide ndi zoyesayesa zake za kubisa zinabweretsa uphungu wa chilango pa iye, monga kwasonyezedwa pa 2 Samueli 12:9-14. Kulanga kwake motenthetsa maganizo kunasonyezedwa m’mawu awa kuchokera pa Masalmo 51: ‘Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa. Choipa changa chiri pamaso panga chikhalire. Mufafanize mphulupulu zanga zonse, mundilengere mtima woyera, [ikani mkati mwanga mtima watsopano, NW.] Musanditaye kundichotsa pamaso panu. Inu Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka.’​—Maversi 2, 3, 9-11, 17.

12. Ndi kachitidwe kokulira kotani kamene kafunikira kwa ena, ndipo nchiyani chimene chimakhala chotulukapo cha awo amene amakana zidzudzulo zobwerezedwa?

12 Ndi anthu ena kachitidwe kokulira kangafunikire, monga mmene Miyambo 26:3 ikusonyezera: “Chikoti chiyenera kavalo, ndi cham’kamwa chiyenera buru, ndi nthyole iyenera pamsana pa zitsiru.” Nthaŵi zina Yehova analola mtundu wake wa Israyeli kugonjetsedwa ndi mavuto omwe anadzibweretsera iwo eni: “Popeza anapikisana nawo mawu a Mulungu; napeputsa uphungu wa Wam’mwambamwamba. Kotero kuti anagonjetsa mtima wawo ndi chovuta; iwowa anakhumudwa koma panalibe mthandizi. Pamenepo anafuulira kwa Yehova mumsauko mwawo; ndipo anawapulumutsa m’kupsyinjika kwawo.” (Masalmo 107:11-13) Opusa ena, ngakhale kuli tero, amadzilimbitsa iwo eni kupyola kufikirika kwa mtundu uliwonse wa chilango chochiritsa: “Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimutsa, palibe chomchiritsa.”​—Miyambo 29:1.

Kupereka ndi Kulandira Chidzudzulo

13. Nchiyani chimene tiyenera kupewa m’kupereka chidzudzulo, ndipo ndimotani mmene icho chingaperekedwere?

13 Mosasamala kanthu za mtundu umene chilango chingatenge, sichiyenera kuperekedwa ndi mkwiyo. M’chenicheni, m’malo mwakuthandiza, “mkwiyo uputa makangano.” Tikuchenjezedwanso kuti: “Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru.” Ndiponso, “kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo, ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.” (Miyambo 29:22; 14:29; 19:11) Pamene chifunika, chilango sichiyenera kukhala chopitirira muyezo. Chiperekeni icho panthaŵi yoyenera ndi kumlingo woyenera​—osati mwamsanga kwambiri, osatinso mochedwa kwambiri, osati chochepa kwambiri, osatinso chokulira koposa.

14. Ndi zitsogozo zina zotani zimene zaperekedwa kaamba ka kupereka zidzudzulo?

14 Pano pali zitsogozo zina kaamba ka awo opereka chidzudzulo: “[Usasulize mopambanitsa mkulu, NW]. Komatu, umdandaulire ngati atate, anyamata ngati abale, akazi akulu ngati amayi, akazi ang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse.” (1 Timoteo 5:1, 2) Kodi mumadandaulira, ndipo osati kusuliza? “Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mumzimu wa chifatso, ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.” (Agalatiya 6:1) Kodi timapereka uphungu mwa chifatso, nthaŵi zonse ozindikira za zophophonya zathu za ife eni? “Nthaŵi zonse chitani ndi ena monga momwe mungafunire iwo kuchita ndi inu.” (Mateyu 7:12, The New English Bible) Kodi m’madziika inu eni m’malo mwa wina, kusonyeza kumvera chisoni?

15. Nchiyani chimene kulandira chidzudzulo kumafunikira, ndipo ndi uphungu wowonjezereka wotani umene umaperekedwa kwa awo odzudzulidwa?

15 Kulandira chidzudzulo kumafunikira kudzichepetsa. Kodi icho chimawonekera kukhala chowawa, chosayenerera, chopanda chilungamo? Musakhale ochita zinthu mwansontho. Lingalirani ponena za icho. Musakhale otsutsa. Wunikirani pa icho moyenerera. Ngati chonse sichikuwonekera chabwino, kodi mbali ya icho iri yotero? Tsegulani malingaliro anu kukhala olandira; bwererani mu icho ndi chonulirapo. Kodi mukukhala ozindikira mopambanitsa, okhumudwitsidwa mwamsanga? Chingatenge nthaŵi kuchiwona icho mukawonekedwe kabwino, pambuyo pa kutha kwa kuvulazidwa kapena kuchimwiridwa kulikonse. Chotero dikirani. Sungani lilime lanu. Moleza mtima bwererani m’chimene chinanenedwa. Kodi chiri chothekera kuti mukudzimva kukhala wapamwamba kuposa wopereka uphunguyo, ndipo munachikana icho pa maziko amenewo? Mosasamala kanthu za chimenecho, chiwoneni icho monga chochokera mu mtima ndipo chosayenera kunyalanyazidwa chabe.

16. (a) Ndi malemba ati ndi mafunso ogwirizana nawo amene ayenera kulingaliridwa pamene tikulandira uphungu? (b) Ndi malingaliro otani osonyezedwa ndi wamasalmo amene tingatsanzire?

16 Pano pali malemba ena amene amawunikira pamene mudzudzulidwa: “Wopanda chikamwakamwa apambana kudziŵa, ndipo wofatsa mtima ali wanzeru.” (Miyambo 17:27) Kodi mumamvetsera ndi kukhala bata? “Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake, koma wanzeru amamvera uphungu.” (Miyambo 12:15) Kodi inu mumalingalira mwamsanga kuti munali wolondola, kapena kodi mumamvetsera ndi kulandira? “Mukhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsya mtima.” (Yakobo 1:19) Kodi mumatsatira mawu awa pamene mukupatsidwa uphungu? “Usakangaze mumtima mwako kukwiya, pakuti mkwiyo ugona m’chifuwa cha zitsiru.” (Mlaliki 7:9) Kodi muli wokangaza kukwiya? Chingakhale chothandiza chotani nanga ngati titadzimva monga mmene anachitira wamasalmo: “Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo; akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu, mutu wanga usakane.”​—Masalmo 141:5.

Pirirani Chilango ndipo Tutani Chipatso cha Mtendere

17. Nchifukwa ninji chilango nthaŵi zonse sichiri chopepuka kuchitenga, komabe ndimotani mmene tingasungire m’maganizo Ahebri 12:​7, 11 kutithandiza ife kupirira icho?

17 Chilango sichiri chopepuka nthaŵi zonse kuchitenga. Ichi chingaphatikizemo kuchititsidwa manyazi ndipo chingabweretse ziletso zina. Chingathe ngakhale kukupangitsani chisoni. Koma pirirani zonsezo. Chidzapita; chimwemwe chimabwera pambuyo pake. Kumbukirani: “[Chiri chifukwa cha chilango kuti mupirira. Mulungu akuchita ndi inu monga ngati ana, NW.] Pakuti mwana wanji amene atate wake samlanga? Zowona, chilango chirichonse pakuchitika sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.”​—Ahebri 12:7, 11.

18, 19. Ndi malingaliro amphamvu otani amene ponse paŵiri Yeremiya ndi wamasalmo anasonyeza omwe amakhazikitsa njira yabwino kaamba ka ife pamene tikulandira chilango?

18 Chotero ngati chilango chiri chomvetsa chisoni ndi chovuta kuchipirira, dikirani kaamba ka chipatso chamtendere chomwe chimabwera pambuyo pake. Dikirani kaamba ka Yehova, monga mmene anachitira Yeremiya: “Mosalephera moyo wanu uzikumbukirabe nuwerama mwa ine. Ichi ndicho chomwe ndidzabweretsa ku mtima wanga. Chimenecho ndicho chifukwa chake ndidzasonyeza mkhalidwe wa kuyembekezera.” (Maliro 3:20, 21, NW) Kumbukirani chimene wamasalmo mu nsauko ananena kwa iyemwini: “Udziweramiranji moyo wanga iwe, ndi kuzingwa mkati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, monga chipulumutso cha nkhope yanga.”​—Masalmo 42:5, 11; 43:5.

19 Chotero pamene mulangidwa, lolani aliyense wa ife adikire Mulungu. Pambuyo pa kuphunzitsidwa ndi icho, tidzatuta zokolola za chipatso cha mtendere, chotchedwa, chilungamo.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Ndi liti limene liri phindu la kugwiritsira ntchito nthyole ya chilango?

◻ Nchiyani chimene chiri magwero enieni a chilango? Kodi ndi ati amene ali magwero ena a chilango?

◻ Kuwonjezera ku mawu a chidzudzulo, kodi ndi kachitidwe kamphamvu kotani kamene kangafunikire?

◻ Ndi ziti zomwe ziri zitsogozo zina za kuperekera chidzudzulo?

◻ Ndi uphungu wotani umene ungatithandize ife kulandira chidzudzulo?

[Chithunzi patsamba 17]

Kodi inu mwanzeru “mumamvetsera ku mwambo”?

[Chithunzi patsamba 18]

Maprinsipulo okhudzidwa m’kulanga ana amagwiranso ntchito kwa akulu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena