-
Kodi Mwakonzeka Kubatizidwa?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
5. N’zotheka kuthana ndi zinthu zimene zingakulepheretseni kubatizidwa
Aliyense amakumana ndi mavuto akasankha kudzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa. Kuti muone chitsanzo cha zimenezi, onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Kodi Narangerel anathana ndi zinthu ziti zomwe zikanamulepheretsa kutumikira Yehova?
Kodi kukonda Yehova kunamuthandiza bwanji kuti athane ndi zinthu zomwe zikanamulepheretsa kubatizidwa?
Werengani Miyambo 29:25 ndi 2 Timoteyo 1:7, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani timalimba mtima n’kuthana ndi zinthu zomwe zikanatilepheretsa kutumikira Yehova?
-
-
N’zotheka Kupirira Ena AkamakuzunzaniMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
Tiyenera kuyamba panopa kudalira kwambiri Yehova. Tsiku lililonse tizipeza nthawi yopemphera kwa iye komanso kuwerenga Mawu ake. Tiyeneranso kumachita nawo misonkhano yampingo nthawi zonse. Zinthu zimenezi zingakuthandizeni kuti musamafooke mukamakumana ndi mayesero ngakhale ochokera kwa anthu am’banja lanu. Mtumwi Paulo yemwenso nthawi zambiri ankazunzidwa analemba kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.”—Aheberi 13:6.
Tingakonzekerenso chizunzo tikamayesetsa kulalikira nthawi zonse. Kulalikira kumatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova komanso kuti tisamaope anthu. (Miyambo 29:25) Mukamalalikira molimba mtima panopa, simudzavutika kupitiriza kulalikira boma likadzaletsa ntchito yathu.—1 Atesalonika 2:2.
-