Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingatani Kuti Aleke Kundiimba Mlandu Nthaŵi Zonse?
“Amakonda kundiimba mlandu pa chilichonse. Ngati m’nyumba munali mosakhoma kapena chitofu chinasiyidwa chosazima kapena chinachake sichinaikidwe pa malo ake kapena sichinapangidwe, amangoti wachita zimenezi si winanso ayi koma Ramon!”—Ramon.
PAMENE mukali wachinyamata, nthaŵi zina zingaoneke kuti amangokuimbani mlandu pa chilichonse chimene chalakwika. M’nkhani yakumbuyoku, tinavomereza kuti nthaŵi zinadi makolo amafulumira kuimba mlandu ana awo.a Izi zimachitika chifukwa cha nkhaŵa za makolowo komanso mwina chifukwa cha kupsa mtima. Mosasamala kanthu kuti zachitika chifukwa cha chiyani, kudzudzulidwa pa chinthu chimene sunachite kungakhale kopweteka m’maganizo komanso kochititsa manyazi.
Ndithudi, monga munthu wopanda ungwiro, mudzaphophonyabe nthaŵi ndi nthaŵi. (Aroma 3:23) Komanso popeza kuti mudakali wochepa msinkhu, mwachionekere musanazindikire zinthu zambiri. (Miyambo 1:4) Ndipo nthaŵi zina mungathe kuweruza molakwa. Choncho, pamene mwalakwa, ndi bwino kuti muyankhe mlandu wake.—Mlaliki 11:9.
Kodi mungatani pamene akuimbani mlandu pa zinthu zimene mwachitadi? Achinyamata ena amaona ngati kuti akuwachitira nkhanza. Iwo amadandaula mwaukali kuti makolo awo amangowaimba mlandu pa chilichonse. Chotulukapo chake? Makolo okwiyawo amaumitsa zinthu pofuna kuti ana amve. Baibulo limapereka malangizo aŵa: “Opusa anyoza nzeru ndi mwambo. Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amako.” (Miyambo 1:7, 8) Ngati muvomereza zolakwa zanu ndi kupanga masinthidwe oyenerera, mungathe kuphunzirapo kanthu pa zolakwa zanu.—Ahebri 12:11.
Kuchita “Upo” ndi Makolo
Komabe, kuimbidwa mlandu pa zinthu zimene simunachite kapena kuimbidwa mlandu kosaleka, ndi nkhani inanso. Nzachidziŵikire kuti mungakwiye. Mwinanso mungafune kupulupudza polingalira kuti mulimonse mmene zidzakhalira, adzakuimbani mlandu. (Mlaliki 7:7) Komabe, aliyense amanyansidwa ndi mnyozo. (Yerekezerani ndi Yobu 36:18.) Miyambo 15:22 imasonyeza mmene tingachitire zinthu molongosoka, iyo imati: “Zolingalira zizimidwa popanda upo.” Zoonadi, makolo anu angasinthe njira imene amachitira ndi inu ngati muwafotokozera mmene imakukhudzirani.
Choyamba, pezani chimene Baibulo limatcha “nthaŵi yake.” (Miyambo 15:23) Wolemba Clayton Barbeau akulingalira motere: “Pezani nthaŵi ndi malo pamene mitima yanu yakhazikika ndipo mukulingalira bwino.” Ndiponso, Baibulo limachenjeza kuti: “Mawu oŵaŵitsa aputa msunamo.” (Miyambo 15:1) Choncho, yesetsani kukhala wokoma mtima ndi waulemu m’mayankhidwe anu, osakhala achiwawa. Pewani mkwiyo. (Miyambo 29:11) M’malo mokangana ndi makolo anu (‘Mumakonda kundiimba mlandu pa chilichonse!’), tayesani kuwafotokozera mmene kukuimbani mlandu kwawo kobwerezabwerezako kumakukhudzirani. (‘Ndimakwiya mukamandiimba mlandu pa zinthu zimene sindinachite.’)—Yerekezerani ndi Genesis 30:1, 2.
Malingaliro ofananawo angagwire ntchito ngati makolo anu akwiya chifukwa chakuti mwasemphana maganizo. Pamene Yesu anali wamng’ono, makolo ake anakwiya pamene iye anasoŵa. Koma Yesu sanakalipe kapena kudandaula. Iye anafotokoza zimene zinachitika mwachifatse. (Luka 2:49) Bwanji osayesa kukambitsirana ndi makolo anu mwauchikulire pamene zinthu zalakwika? Zindikirani kuti iwo amakwiya chifukwa chakuti amadera nkhaŵa kaamba ka ubwino wanu! Mvetserani mwaulemu. (Miyambo 4:1) Yembekezani kuti mitima yawo ikhale pansi musanayambe kupereka maganizo anu.
‘Kuonetsa Ntchito Zanu’
Nchifukwa chiyani nanga makolo ena ali ndi khalidwe longoyamba kuweruza ana awo asanamvetsetse zimene zachitika? Kunena zoona, nthaŵi zina zochita za ana zimapangitsa kuti makolo awo aziwakayikira. Miyambo 20:11 imati: “Ngakhale mwana adziŵika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.” Kodi mumapereka chitsanzo chotani kwa makolo anu? Kodi “ntchito” zanu zimaonetsa kuti ndinu ‘wolungama’ ndi wosamala zinthu kapena ndinu wosasamala ndi wosadalirika? Ngati ndinu wosasamala ndi wosadalirika, nzosadabwitsa kuona makolo anu akukuweruzani molakwa. “Sindikanakana zimenezo pakuti zinali zoona,” anavomereza motero Ramon, mnyamata amene watchulidwa poyambirira paja, ponena za kuimbidwa mlandu ndi makolo ake. “Nthaŵi zina zimene iwo amaganiza nzoona.”
Ngati zili choncho kwa inuyo, palibe chimene mungachite koposa kungowongolera zakale. Ngati mukulitsa khalidwe la kudalirika ndi kusamala zinthu, m’kupita kwa nthaŵi makolo anu angaone kuti mwasinthadi ndipo angayambe kukukhulupirirani.
Chokumana nacho cha Ramon chikusonyeza zimenezi. Mogwirizana ndi khalidwe lake, mabwenzi ndi makolo ake amamunena kuti ndi profesa wongokhala maganizo ali kwina chifukwa chakuti ankakonda kuiŵala zinthu. Kodi makolo anu akupatsani dzina losasangalatsa monga “wachibwana” kapena “wosasamala”? Monga momwe akulongosolera wolemba Kathleen McCoy, makolo angalingalire kuti maina otero adzathandiza “kumveketsa chimene chili cholakwika kwa wachinyamatayo kotero kuti iye asinthe.” Koma kunena zoona, maina otero nthaŵi zambiri amabweretsa mkwiyo waukulu. Ngakhale zili choncho, Ramon anazindikira kuti dzina lomunenalo linali ndi mfundo yofunika. “Nthaŵi zonse ndinali kusumika maganizo anga pa chinthu chimodzi, choncho ndinkatha kutaya makiyi kapena homuweki yanga ndipo ndinkaiŵalanso kugwira ntchito zapanyumba,” iye akuvomereza motero.
Choncho, Ramon anayamba kusintha. “Ndinaphunzira kusamala ntchito ndi kuika zinthu zofunika m’malo mwake,” iye akukumbukira motero. “Ndinakonza ndandanda ndipo ndinayamba kuchita phunziro la Baibulo laumwini mosamalitsa. Ndinaphunzira kuti Yehova amasamalira zinthu zazing’ono ndi zazikulu zomwe.” (Luka 16:10) Mwa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo, Ramon potsirizira pake anagonjetsa chizoloŵezi chake choiŵala zinthu. Bwanji osayesa kuchita zofananazo? Ndipo ngati dzina lokunenanilo limakunyansani, mungafotokoze zimenezo kwa makolo anu. Mwinamwake iwo adzaona nkhaniyo mmene mukuionera.
Pamene Kuoneka Ngati Kukondera
Nthaŵi zina zimakhala ngati kuti akuimba mlandu mokondera. Ramon akukumbukira kuti: “Abale ndi alongo anga aakulu atabwera mochedwa panyumba, sanali kuwalanga nkomwe. Koma nditakhala ineyo ndinali kuvutika.” Mwamuna wina wachigayana wotchedwa Albert akukumbukira kuti anali ndi zokumana nazo zofananazo pamene anali wamng’ono. Nthaŵi zonse amayi ake anali kumdzudzula mwaukali kuposa mmene amachitira kwa mbale wake.
Komabe, nthaŵi zina tingayerekezere zinthu molakwa. Nthaŵi zambiri makolo amapereka ufulu wokulirapo kwa ana aakulu, osati chifukwa cha kukondera, koma chifukwa chakuti iwo amaganiza kuti ana otere angachite zinthu mosamala. Komanso mwina pangakhale zifukwa zina zoloŵetsedwamo. Albert akuvomereza kuti mbale wakeyo sanali kumenyedwa chifukwa chakuti anali “wamng’ono ndiponso wodwaladwala.” Kodi nkukondera pamene makolo azindikira kuti mwana wina amafunikira chisamaliro chapadera?
Inde, nthaŵi zina makolo amakhala ndi ana omwe amakonda kwambiri. (Yerekezerani ndi Genesis 37:3.) Ponena za mbale wake wodwaladwalayo, Albert akuti: “Amayi anali kumkonda kwambiri.” Chosangalatsa nchakuti chikondi chachikristu sichisankha. (2 Akorinto 6:11-13) Choncho, pamene makolo “akonda kwambiri” mmodzi wa abale anu, sizitanthauza kuti chikondi chawo kwa inuyo chatha ayi. Funso lingakhale lakuti, Kodi iwo amakudzudzulani mwaukali chifukwa chokondera, akumaikira kumbuyo mbale wanu? Ngati zili choncho, muyenera kuwafotokozera malingaliro anu. Fotokozani mwachifatse komanso mwaulemu, zitsanzo zodziŵika bwino za zimene zikukupangitsani kulingalira kuti iwo akuchita zinthu mokondera. Mwinamwake adzamvetsetsa.
Mabanja Okhala m’Mavuto
Zoonadi, nthaŵi zina kumakhala kovuta kusintha. Kwa makolo ena kunyoza ndi kudzudzula ndilo khalidwe lawo. Izi makamaka zingakhale choncho kwa makolo opsinjika maganizo kapena omwe ali ndi vuto la kumwerekera. Mu mkhalidwe umenewu, kukambitsirana sikungathandize konse. Ngati zili choncho kwa inuyo, zindikirani kuti vuto la makolo anu simungalithetse, pafunikira chithandizo cha ena. Chimene mungachite ndicho kuwachitira ulemu ndi kuyesetsa kupewa mkangano. (Aefeso 6:1, 2) Miyambo 22:3 imati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.”b
Panthaŵi imodzimodziyo, pemphani ena osakhala a m’banja lanu kuti akuthandizeni. Longosolani nkhaniyi kwa munthu wachikulire, mwinamwake mkulu wachikristu. Kumvetsera kwake kwa chikondi kungathandize kuthetsa malingaliro akuti ndinu wolakwa nthaŵi zonse. Panthaŵi imodzimodziyo, “yandikirani kwa Mulungu.” (Yakobo 4:8) Pamene kuli kwakuti ena angamakuimbeni mlandu mosayenera, ‘(Mulungu) sadzatsutsana nafe nthaŵi zonse; ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha. . . . Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.’ (Salmo 103:9, 14) Kuzindikira kuti ndinu wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu kungakuthandizeni kupirira ngati amakuimbani mlandu pa zinthu zimene simunachite.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Bwanji Amaimba Ine Mlandu Nthaŵi Zonse?” m’kope lathu la August 8, 1997.
b Onani nkhani yakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Ndingawapirire Motani Mawu Onyoza?” m’kope lathu lachingelezi la June 8, 1989. Onaninso nkhani zakuti “Kuleka Mawu Opweteka ndi Kunena Mawu Omangirira” mu Galamukani! ya November 8, 1996.
[Chithunzi patsamba 22]
Kuvomereza zolakwa zathu kumatithandiza kuphunzirapo kanthu pa zolakwazo