Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 136-tsamba 139
  • Filosofi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Filosofi
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Akugwiritsira Ntchito “Chopusa” Kupulumutsa Okhulupirirawo
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Nzeru Yeniyeni Ikufuula
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • ‘Nzeru za Mulungu N’zozama’
    Yandikirani Yehova
  • ‘Wodala Munthu Wopeza Nzeru’
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 136-tsamba 139

Filosofi

Tanthauzo: Liwu lakuti filosofi latengedwa kuchokera ku magwero Achigiriki amene amatanthauza “kukonda nzeru.” Monga momwe lagwiritsidwira ntchito panopa, filosofi siiri yozikidwa pakuvomereza kukhulupirira Mulungu, koma imayesa kupatsa anthu lingaliro logwirizanitsidwa ndi chilengedwe chonse ndi kuyesayesa kuŵapangitsa kukhala olingalira osuliza. Kwakukulukulu imagwiritsira ntchito njira zoyerekezera mmalo mwakutsimikizira pofunafuna chowonadi.

Kodi ndimotani mmene aliyense wa ife angapezere chidziŵitso chowona ndi nzeru?

Miy. 1:7; Sal. 111:10: “Kuwopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziŵa . . . [ndi] cha nzeru.” (Ngati chilengedwe chonse sichinali chopangidwa ndi Mlengi waluntha, koma chopangidwa ndi mphamvu yopanda luntha ndi yaumbuli, pamenepo sipakanakhala lingaliro logwirizana la chilengedwe, kodi sichoncho? Palibe chimene chikanayeneretsedwa kutchedwa nzeru m’chimene chingachokere m’kupenda chinthu chimene mwa icho chokha chinali chopusa, kodi sichoncho? Awo amene amayesayesa kumvetsetsa chilengedwe chonse kapena moyo weniweniwo, pamene akuyesayesa kusiya Mulungu ndi chifuno chake m’nkhaniyo, amagwiritsidwa mwala mosalekeza. Iwo amamasulira molakwa zimene amaphunzira nagwiritsira ntchito molakwa maumboni amene amatulukira. Kusiya kukhulupirira Mulungu kumawononga mfungulo yopezera chidziŵitso cholongosoka ndipo kumakupangitsa kukhala kosatheka ndi kosagwirizanadi ndi malingaliro onse.)

Miy. 2:4-7: “Ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuwopa Yehova ndi kumdziŵadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake; iye asungira owongoka mtima nzeru yeniyeni.” (Yehova amapereka chithandizo chofunika kupyolera mwa Mawu ake olembedwa ndi gulu lake lowoneka. Chikhumbo chowona mtima ndi kuyesayesa kwaumwini kuphatikizapo kugwiritsidwa ntchito kwa luntha lamunthuyo mwanjira yolimbikitsa, zirinso zofunika.)

Kodi kuli kwanzeru kuyembekezera kupeza chowonadi chotheratu kuchokera ku Magwero amenewa?

2 Tim. 3:16; Yoh. 17:17: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu.” “[Yesu anati kwa Atate wake wakumwamba:] Mawu anu ndichowonadi.” (Kodi sikuli kwanzeru kuti Mlengi wachilengedwe chonse akazindikira mokwanira? Iye sanatiuze kanthu kalikonse ponena za chilengedwe chonse m’Baibulo, koma zimene anachititsa kuti zilembedwe m’menemo sindizo zoyerekezera; nchowonadi. Iye walongosolanso m’Baibulo chimene chiri chifuno chake kaamba ka dziko lapansi ndi kaamba ka anthu ndi mmene adzachikwaniritsira. Mphamvu yake yonse, nzeru zake zapamwamba, chilungamo chake changwiro, ndi chikondi chake chachikulu zimatsimikizira kuti chifuno chimenechi chidzakwaniritsidwa mokwanira, ndipo mu mpangidwe wothekera wabwino koposa. Motero mikhalidwe yake imatitsimikizira kuti mawu ake achifuno ngodalirika kotheratu; ndiwo chowonadi.)

Kodi mafilosofi a anthu amachokera kuti?

Amachokera kwa anthu okhala ndi zopereŵera: Baibulo limatiuza kuti: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yer. 10:23) Mbiri imachitira umboni kuti kuyesayesa kunyalanyaza kupelewera kumeneko sikunatulutse zotulukapo zabwino. Panthaŵi ina, “Yehova anayankha Yobu m’kamvumvulu, nati, Ndani uyu adetsa uphungu, ndi mawu opanda nzeru? Udzimangire m’chuuno tsono; ngati mwamuna; ndikufunsa, undidziŵitse. Unali kuti munja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziŵa kuzindikira.” (Yobu 38:1-4) (Anthu mwachibadwa ali ndi zopereŵera. Kuwonjezera, chidziŵitso chawo m’moyo chiri chachifupi kwambiri ndipo kaŵirikaŵiri chiri cholekezera kumtundu umodzi kapena malo amodzi. Motero chidziŵitso chimene ali nacho chiri ndi polekezera, ndipo chirichonse chiri cholukanalukana kumlingo wakuti nthaŵi zonse amapeza mbali zimene sanazilingalire mokwanira. Filosofi iriyonse imene amayambitsa idzasonyeza zopereŵera zimenezi.)

Amayambidwa ndi anthu opanda ungwiro: “Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) “Iripo njira yowoneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.” (Miy. 14:12) (Chifukwa cha kupanda ungwiro kotero, kaŵirikaŵiri mafilosofi a anthu amasonyeza dyera lalikulu limene mwinamwake limatsogolera ku chikondwerero cha kanthaŵi komanso ku kugwiritsidwa mwala ndi chisoni chachikulu.)

Amasonkhezeredwa ndi mizimu ya ziŵanda: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) “Iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana . . . akusocheza dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.” (Chiv. 12:9, NW) “Zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” (Aef. 2:2) (Mafilosofi amene amalimbikitsa anthu kusamvera malamulo abwino ndi olungama a Mulungu ali ndi chisonkhezero chotero. Nkosadabwitsa kuti, monga momwe mbiri ikutsimikizirira, kaŵirikaŵiri mafilosofi ndi zolinganiza za anthu zimadzetsa chisoni ku zigawo zazikulu za anthu ambiri.)

Kodi nchifukwa ninji uli umboni wa kulingalira kwabwino kuphuzira ziphunzitso za Yesu Kristu mmalo mwa filosofi ya anthu?

Akol. 1:15-17: “Amene [Yesu Kristu] ali fanizo la Mulungu wosawonekayo, wobadwa woyamba wachilengedwe chonse; pakuti mwa iye zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi zapadziko . . . zinthu zonse zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye. Ndipo iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa iye.” (Unansi wake wapafupi ndi Mulungu umamkhozetsa kutithandiza kuphunzira chowonadi chonena za Mulungu. Ndiponso, monga munthu mwa amene zinthu zina zonse zinalengedwa, Yesu ali ndi chidziŵitso chokwanira cha chilengedwe chathunthu. Palibe wa filosofi yaumunthu amene angalonjeze zirizonse za zimenezi.)

Akol. 1:19, 20: “Kunamkomera Atate [Mulungu] kuti mwa iye [Yesu Kristu] chidzalo chonse chikhalire, mwa iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa iyemwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake.” (Motero Yesu Kristu ndiye uyo amene Mulungu walinganiza kubwezeretseranso chilengedwe chonse m’chigwirizano ndi iyemwini. Kwa Yesu, Mulungu waikiziranso ulamuliro padziko lonse lapansi, monga momwe kwasonyezedwera pa Danieli 7:13, 14. Chotero ziyembekezo zathu za moyo wamtsogolo zimadalira pakumdziŵa ndi kulabadira malangizo ake.)

Akol. 2:8: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.” (Ncholakwa chomvetsa chisoni chotani nanga mmene chingakhalire kusankha filosofi yonyenga ya anthu mmalo mwa kufunafuna nzeru yowona monga wophunzira wa Yesu Kristu, munthu wachiŵiri paukulu kuposa onse m’chilengedwe chonse, woposedwa ndi Mulungu yekha!)

Kodi Mulungu amaiwona motani “nzeru” yoperekedwa ndi nthanthi za anthu?

1 Akor. 1:19-25: “Kulembedwa, Ndidzawononga nzeru za anzeru, ndi kuchenjera kwa ochenjera ndidzakutha. Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthaŵi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitsa nzeru ya dziko lapansi? Pakuti popeza m’nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziŵe Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirirawo mwa chopusa [monga momwe chimawonekerera kudziko] cha kulalikira . . . Chifukwa kuti chopusa [monga momwe dziko limachiwonera] cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zawo; ndipo chofooka [monga momwe dziko limachiwonera] cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yawo.” (Ndithudi lingaliro lotero la Mulungu siliri lachabechabe kapena lopambanitsa. M’Baibulo, bukhu lofalitsidwa koposa onse m’dziko, wanenamo mawu omvekera bwino a chifuno chake. Iye watuma mboni zake kukalikambitsirana ndi onse amene adzamvetsera. Ha nkupusa kotani nanga kwa cholengedwa chirichonse kulingalira kuti chiri ndi nzeru zazikulu kuposa za Mulungu!)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena