Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ‘Wodala Munthu Wopeza Nzeru’
    Nsanja ya Olonda—2001 | March 15
    • “Ifuula”

      Chaputala 8 cha Miyambo chikuyamba ndi funso losafuna yankho: “Kodi nzeru siitana, luntha ndi kukweza mawu ake?”a Inde, nzeru ndi luntha zimafuula, koma mosiyana ndi mkazi wachiwerewere yemwe amabisala m’malo a mdima kumanong’ona mawu okopa kwa mnyamata wachibwana wokhala yekhayekha. (Miyambo 7:12) “Liima pamwamba pamtunda, pamphambano za makwalala; pambali pa chipata poloŵera m’mudzi, poloŵa anthu pamakomo ifuula.” (Miyambo 8:1-3) Mawu amphamvu ndi okuwa a nzeru akumvekera bwino m’malo onse onga pazipata, m’makwalala ndi poloŵera mu mzinda. Anthu akumva mawuwo mosavuta ndipo akulabadira.

      Ndani angatsutse mfundo yakuti pafupifupi aliyense padziko lapansi wofuna nzeru ya Mulungu yolembedwa m’Mawu ake ouziridwa, m’Baibulo, akhoza kuipeza? Buku lakuti The World Book Encyclopedia limati: “Baibulo ndi buku lomwe laŵerengedwa ndi anthu ambiri ndiponso lafalitsidwa kwambiri kuposa lililonse. Baibulo lamasuliridwa m’zilankhulo zambiri kuposa buku lina lililonse.” Baibulo lonse kapena mbali yake likupezeka m’zilankhulo zazikulu ndi zazing’ono zoposa 2,100. Anthu oposa 90 peresenti padziko lonse angapeze mbali ya Mawu a Mulungu m’chilankhulo chawo.

      Mboni za Yehova zimalengeza uthenga wa m’Baibulo paliponse. M’mayiko 235, izo zikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa anthu choonadi cha m’Mawu a Mulungu. Magazini awo ozikidwa pa Baibulo a Nsanja ya Olonda akufalitsidwa m’zinenero 140, ndipo Galamukani!, m’zinenero 83. Magazini a mtundu umodzi oposa 20 miliyoni amafalitsidwa nthaŵi zonse. Ndithudi, nzeru ikufuula ponseponse!

  • ‘Wodala Munthu Wopeza Nzeru’
    Nsanja ya Olonda—2001 | March 15
    • a Liwu lachihebri lakuti “nzeru,” lili m’gulu la mawu osonyeza chinthu chachikazi. N’chifukwa chake otembenuza ena amagwiritsa ntchito mawu osonyeza mkazi potchula nzeru.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena