Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 11/12 tsamba 24-25
  • Kodi Kudzionetsera Kuli ndi Phindu Lililonse?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kudzionetsera Kuli ndi Phindu Lililonse?
  • Galamukani!—2012
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Munthu Wolemera Amakhala ndi Anzake Ambiri”
  • “Nzeru Zimakhala Ndi Anthu Odzichepetsa”
  • Muzikonda Anthu Chifukwa cha Makhalidwe Awo Abwino
  • Pali Anzanu Abwino ndi Anzanu Oipa
    Galamukani!—2004
  • Kupeza Anzathu Omwe Timalakalaka
    Galamukani!—2004
  • Kodi Ndingapeze Bwanji Anzanga Abwino?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Kodi Ndipeze Anzanga Ena Abwino?
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Galamukani!—2012
g 11/12 tsamba 24-25

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kudzionetsera Kuli ndi Phindu Lililonse?

“Anthu ena omwe poyamba ankadziona kuti ndi opanda pake akagula zovala zapamwamba amayamba kudziona kuti ndi apamwamba kwambiri ndipo amayesetsa kuchita zinthu zoti ena awaone.”​—Anatero dokotala wina dzina lake, Chaytor D. Mason.

ANTHU ena akakhala ndi zovala komanso zinthu zina zapamwamba, amachita zinthu modzionetsera n’cholinga choti anthu aziwatama. Nyuzipepala ina inafotokoza kuti m’dziko lina la ku Asia, “anthu amene angopeza kumene chuma chambiri amakonda kugula zinthu zodula kwambiri monga zikwama za azimayi za ku France, magalimoto apamwamba a ku Italy, ndipo amachita zinthu moonetsera [chuma chimene ali nacho].”—The Washington Post.

N’zoona kuti munthu ayenera kusangalala ndi zinthu zimene wapeza chifukwa chogwira ntchito. Ndipo Baibulo limanena kuti: “Munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Mlaliki 3:13) Koma kodi ndi bwino kuti munthu azidzionetsera kapena kunyaditsa anthu ena zimene ali nazo? Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi?

“Munthu Wolemera Amakhala ndi Anzake Ambiri”

Kodi ndi anthu otani amene amakopeka ndi munthu wamatama yemwe ndi wolemera kapena amene amadzionetsa ngati wolemera? Baibulo limatithandiza kupeza yankho la funso limeneli chifukwa limati: “Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi mnzake, koma munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri.”—Miyambo 14:20.

Lembali likutanthauza kuti anthu ambiri amafuna kucheza ndi anthu olemera chifukwa chongofuna chumacho basi. Anthu amenewa amalankhula zomutama munthu wolemerayo n’cholinga choti azingomudyera chuma chake. Baibulo limanena kuti anthu otere amalankhula zimenezi ‘mwachiphamaso chifukwa cha kusirira kwa nsanje,’ kapena dyera.—1 Atesalonika 2:5.

Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ineyo ndimafuna kuti ndizicheza ndi anthu otani? Kodi ndimafuna kuti anzanga azindikonda chifukwa cha zinthu zimene ndili nazo kapena chifukwa cha makhalidwe anga?’ Baibulo limasonyeza kuti khalidwe lathu lingachititse kuti tikhale ndi anzathu abwino kapena oipa.

“Nzeru Zimakhala Ndi Anthu Odzichepetsa”

M’Baibulo muli chitsanzo chosonyeza vuto lina lodzionetsera ndi zinthu zimene tili nazo. Limanena za Mfumu Hezekiya yemwe ankakhala ku Yerusalemu. Nthawi ina nthumwi za mfumu ya ku Babulo zinapita kukaona Hezekiya ndipo iye “anawaonetsa zonse za m’nyumba yake yosungiramo chuma.” Zikuoneka kuti alendowo anasirira chuma cha mfumu Hezekiya komanso zinawachititsa kuti ayambe kuchilakalaka. Alendowo atachoka, Yesaya, yemwe anali mneneri wa Mulungu, anauza Mfumu Hezekiya molimba mtima kuti tsiku lina chuma chake chonse ‘chidzatengedwa n’kupita ku Babulo ndipo palibe chidzatsale.’ Zimenezi zinachitikadi. Patapita nthawi, Ababulo anabwerera n’kudzatenga chuma chonse cha Hezekiya.—2 Mafumu 20:12-17; 24:12, 13.

N’chimodzimodzinso masiku ano. Anthu akhoza kuba chuma cha anthu amene amakonda kudzionetsera. Lipoti lina la ku Mexico linanena kuti: “Anthu a mumzinda wa Mexico City amene amakonda kuonetsera zimene ali nazo amaitana mbava. Mwachitsanzo, kuvala ndolo, zibangili kapena mawotchi odula kwambiri komanso kuika poyera ndalama zambiri, kumakopa chidwi cha mbava.” Choncho ndi bwino kutsatira malangizo a m’Baibulo oti ‘tisadzitamande chifukwa cha chuma’ chimene tili nacho. (Yeremiya 9:23) Komanso lemba la Miyambo 11:2 limati: “Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.”

Muzikonda Anthu Chifukwa cha Makhalidwe Awo Abwino

Munthu wodzichepetsa amaona makhalidwe abwino a anthu ena m’malo mokhala ndi mtima woti anthu azimutama. Lemba la Afilipi 2:3, limanena kuti: “Musachite chilichonse ndi mtima . . . wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.” Komanso lemba la Agalatiya 5:26 limanena kuti: “Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.”

Kodi inuyo mumafuna kuti anzanu azikukondani chifukwa cha zinthu zimene muli nazo kapena chifukwa cha makhalidwe anu?

Komanso anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo amadziwa kuti ubwenzi umakhala wolimba chifukwa chokondana kuchokera pansi pa mtima komanso chifukwa cholemekezana. Amadziwanso kuti ubwenzi woterewu sungathe ngakhale atasauka ndipo umakhala wolimba mpaka kalekale. Lemba la Miyambo 17:17 limati: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.” Komanso munthu wanzeru amachita zinthu zoti azikondweretsa Mulungu. Amadziwa kuti Mulungu sayang’ana zimene munthu ali nazo koma amayang’ana “munthu wobisika wamumtima.” (1 Petulo 3:4) Choncho amayesetsa kuti akhale ndi makhalidwe abwino amene Baibulo limanena kuti ndi “umunthu watsopano.” (Aefeso 4:24) Ena mwa makhalidwe amenewa atchulidwa pa Mika 6:8 pomwe pamati: “Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.”

Masiku ano anthu ambiri si odzichepetsa ndipo zimenezi n’zosadabwitsa kwa anthu amene amaphunzira Baibulo. Tikutero chifukwa chakuti Baibulo linaneneratu kuti ‘m’masiku otsiriza’ anthu ambiri adzakhala “odzimva, odzikweza, . . . odzitukumula ndiponso onyada.” (2 Timoteyo 3:1-5) Anthu amene amakonda kudzionetsera amasangalala, koma Mulungu amafuna kuti ‘tiziwapewa’ chifukwa tikhoza kutengera makhalidwe awo oipa.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

  • Kodi Mulungu amafuna kuti munthu akhale ndi makhalidwe ati?​—Mika 6:8.

  • Kodi tiyenera kuwaona bwanji anthu amene ali ndi makhalidwe abwino?​—Afilipi 2:3.

  • N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa kuti masiku ano anthu ambiri amakonda kuonetsera zimene ali nazo?​—2 Timoteyo 3:1-5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena