Mapindu a Kudekha
SAYANSI yamakono ya zamankhwala yadziŵa kuyambira kale kuti kupsa mtima kosalamulirika kumawononga thupi. Zaka zoposa zana limodzi zapitazo, The Journal of the American Medical Association (JAMA) inati: “Munthu atakwiya kwambiri akugwa namwalira, ndipo anthu mwinamwake akunena kuti anali ndi mtima wofooka, umene sunathe kupirira kupsinjika kwa maganizo ake. Palibe amene akulingalira kuti chimenecho chinali chimake cha nthaŵi zambirimbiri zaukali umene wachititsa kufooka kumene akunenako.”
Mawu apamwambawo si odabwitsa kwa ophunzira Mawu a Mulungu, Baibulo. Zaka ngati mazana 29 JAMA isananene za ngozi za mkwiyo, Mfumu Solomo inauziridwa kulemba kuti: “Mtima wabwino [“wodekha,” NW] ndi moyo wa thupi.” (Miyambo 14:30) Mawu amenewo akali oona lerolino.
Mwa kukhala wodekha, timapeŵa matenda ambiri amene kaŵirikaŵiri amadza ndi kupsinjika maganizo, monga BP, mutu, ndi matenda a m’chifuwa. Komabe, kuwonjezera pa kukhala ndi thanzi labwino, maunansi athu ndi ena adzakhala bwino ngati tiyesayesa ‘kuleka kupsa mtima ndi kutaya mkwiyo.’ (Salmo 37:8) Mwachibadwa anthu ankafuna kukhala ndi Yesu chifukwa cha kufatsa kwake ndi nkhaŵa yake kwa iwo yochokera mumtima. (Marko 6:31-34) Momwemonso, tidzakhala otonthoza kwa ena ngati tikhala odekha.—Mateyu 11:28-30.