Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 6/15 tsamba 18-23
  • “Utumiki Wopatulika ndi Mphamvu Yanu ya Kulingalira”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Utumiki Wopatulika ndi Mphamvu Yanu ya Kulingalira”
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukulitsa Mphamvu Yanu ya Kulingalira
  • Akapolo a Mulungu ndi Kristu, Osati a Anthu
  • Kukulitsa “Maganizo a Kristu”
  • Kutsatira Chilamulo cha Kristu
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kodi Tingasankhe Bwanji Zosangalatsa?
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Kodi Mungasankhe Bwanji Zosangalatsa Zabwino?
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kodi Chikumbumtima Chanu Mungachikhulupirire?
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 6/15 tsamba 18-23

“Utumiki Wopatulika ndi Mphamvu Yanu ya Kulingalira”

“Perekani matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yolandirika kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika ndi mphamvu yanu ya kulingalira.” ​—AROMA 12:1, NW.

1, 2. Kodi ndimotani mmene kuphunzira kugwiritsira ntchito zitsogozo za Baibulo kulili kofanana ndi kuphunzira chinenero chatsopano?

KODI munayesapo kuphunzira chinenero chatsopano? Ngati munatero, mosakayikira mukuvomereza kuti ndi ntchito yovuta. Ndithudi, pali zambiri zoloŵetsedwamo kuposa kuphunzira mawu atsopano chabe. Kudziŵa bwino kulankhula chinenero kumafunanso kudziŵa malamulo a chinenerocho. Muyenera kudziŵa mmene mawu amaimira moyenerana ndi mmene amagwirizanira kupanga ziganizo zokwanira.

2 Ndi mmenenso zakhalira ndi kupeza chidziŵitso cha Mawu a Mulungu. Zambiri zikuloŵetsedwamo kuposa kuphunzira chabe Malemba otengedwa apa ndi apo. Tiyeneranso kuphunzira malamulo a chinenero cha Baibulo, titero kunena kwake. Tiyenera kuzindikira mmene malemba amagwirizanirana ndi mmene amakhalira zitsogozo zimene tingagwiritsire ntchito m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Mwa kutero tingakhale ‘oyenera okonzeka kuchita nchito iliyonse yabwino.’​—2 Timoteo 3:17.

3. Ponena za utumiki kwa Mulungu, kodi ndi kusintha kotani kumene kunachitika mu 33 C.E.?

3 Pamene kakonzedwe ka Chilamulo cha Mose kanali kugwira ntchito, kukhulupirika kunasonyezedwa makamaka mwa kusunga malamulo olongosoledwa bwino. Komabe, mu 33 C.E., Yehova anafafaniza Chilamulocho, “nachikhomera pamtengo wozunzirapo” pamene Mwana wake anafera. (Akolose 2:13, 14, NW) Pambuyo pake, anthu a Mulungu sanapatsidwe mndandanda wautali wa nsembe zomazipereka ndi malamulo owatsatira. M’malo mwake, anauzidwa kuti: “Perekani matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yolandirika kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika ndi mphamvu yanu ya kulingalira.” (Aroma 12:1) Inde, Akristu anayenera kudzipereka iwo eni, ndi mtima wawo wonse, moyo, maganizo, ndi mphamvu mu utumiki wa Mulungu. (Marko 12:30; yerekezerani ndi Salmo 110:3) Koma kodi kumatanthauzanji kupereka “utumiki wopatulika ndi mphamvu yanu ya kulingalira”?

4, 5. Kodi nchiyani chimene chikuloŵetsedwa m’kutumikira Yehova ndi mphamvu yathu ya kulingalira?

4 Mawu akuti “mphamvu ya kulingalira” atembenuzidwa ku liwu Lachigiriki lakuti lo·gi·kosʹ, limene limatanthauza “wanzeru” kapena “waluntha.” Atumiki a Mulungu akulimbikitsidwa kugwiritsira ntchito chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo. M’malo mwa kuzika zosankha zawo pa malamulo oikidwiratu, Akristu ayenera kupenda zitsogozo za Baibulo mosamala. Afunikira kudziŵa bwino “malamulo a chinenero” cha Baibulo, kapena mmene zitsogozo zake zosiyanasiyana zimagwirizanira. Mwa kutero, angapange zosankha zoyenera mwa kugwiritsira ntchito mphamvu yawo ya kulingalira.

5 Kodi zimenezi zimatanthauza kuti Akristu alibe malamulo? Iyayi. Malemba Achigiriki Achikristu momvekera bwino amaletsa kulambira mafano, chisembwere, mbanda, kunama, kukhulupirira mizimu, kugwiritsira ntchito mwazi, ndi machimo ena ambiri. (Machitidwe 15:28, 29; 1 Akorinto 6:9, 10; Chivumbulutso 21:8) Komabe, kuposa mmene zinaliri kwa Aisrayeli, ife tifunikira kugwiritsira ntchito kwambiri mphamvu yathu ya kulingalira kuti tiphunzire ndi kutsatira zitsogozo za Baibulo. Mofanana ndi kuphunzira chinenero chatsopano, zimenezi zimafuna nthaŵi ndi kuyesayesa. Kodi ndimotani mmene tingakulitsire mphamvu yathu ya kulingalira?

Kukulitsa Mphamvu Yanu ya Kulingalira

6. Kodi kuphunzira Baibulo kumaloŵetsamo chiyani?

6 Choyamba, tiyenera kukhala ophunzira Baibulo akhama. Mawu ouziridwa a Mulungu ‘amapindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.’ (2 Timoteo 3:16) Sitiyenera nthaŵi zonse kuyembekezera kupeza yankho la vuto pa vesi limodzi lokha la m’Baibulo. M’malo mwake, tingafunikire kulingalira pa malemba angapo amene amapatsa chidziŵitso pamkhalidwe kapena vuto lakutilakuti. Tifunikira kufufuza mwakhama kuti tipeze lingaliro la Mulungu pa nkhaniyo. (Miyambo 2:3-5) Tiyeneranso kuzindikira, pakuti ‘wozindikira afikira uphungu.’ (Miyambo 1:5) Munthu wozindikira angasiyanitse mbali zosiyanasiyana za nkhani ndiyeno kuona mmene zimakhudzirana. Mofanana ndi seŵero lotchedwa jigsaw puzzle, iye amalumikiza zidutswazo kuti akhoze kuona chithunzi chonse.

7. Kodi ndimotani mmene makolo angalingalirire pa zitsogozo za Baibulo ponena za chilango?

7 Mwachitsanzo, titenge nkhani ya ukholo. Miyambo 13:24 imanena kuti tate amene akonda mwana wake “amyambize kumlanga.” Kulitenga palokha, lembali lingamvedwe molakwa kuti limavomereza chilango chankhanza, chosalolera. Komabe, Akolose 3:21 amapereka uphungu wolinganiza bwino: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.” Makolo amene agwiritsira ntchito mphamvu yawo ya kulingalira ndi kugwirizanitsa malamulo ameneŵa sadzatembenukira pa kulanga kumene kungatchedwe “nkhanza.” Iwo adzachita ndi ana awo mwachikondi, kumvetsetsa, ndi ulemu. (Aefeso 6:4) Chifukwa chake, pochita ukholo kapena m’nkhani ina iliyonse yoloŵetsamo zitsogozo za Baibulo, tingakulitse mphamvu yathu ya kulingalira mwa kupenda mbali zonse. Mwa njira imeneyi, tingadziŵe “malamulo a chinenero” a zitsogozo za Baibulo, chimene chinali cholinga cha Mulungu ndi mmene tingachikwaniritsire.

8. Kodi tingapeŵe motani kutengera malingaliro osasintha ndi oumirira pankhani ya zosangulutsa?

8 Njira yachiŵiri imene tingakulitsire mphamvu yathu ya kulingalira ndiyo kupeŵa kutengera malingaliro osasinthika, oumirira. Kaonedwe ka zinthu kosasinthika kamaletsa kukula kwa mphamvu yathu ya kulingalira. Talingalirani nkhani ya zosangulutsa. Baibulo limati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Kodi zimenezi zimatanthauza kuti buku lililonse, kanema, kapena programu ya pawailesi yakanema yopangidwa ndi dziko, ili yoluluza ndi yausatana? Kaonedwe koteroko sikali kulingalira kwabwino. Inde, ena angasankhe kusaonerera wailesi yakanema, mafilimu, kapena kuŵerenga mabuku adziko. Chimenecho chili chosankha chawo, ndipo sayenera kusulizidwa chifukwa cha zimenezo. Komanso iwo sayeneranso kusonkhezera ena kutsatira njira yodziletsa imeneyo. Sosaite yafalitsa nkhani zopereka zitsogozo za Baibulo zimene ziyenera kutikhozetsa kusankha mwanzeru zosangulutsa zathu. Kupitirira pa zitsogozo zimenezi ndi kudzipereka ku kalingaliridwe ka zachisembwere, chiwawa choipitsitsa, kapena kukhulupirira mizimu zimene zimapezeka m’zosangulutsa zochuluka za dzikoli kuli kopanda nzeru kwambiri. Ndithudi, kusankha mwanzeru zosangulutsa kumafuna kuti tigwiritsire ntchito mphamvu yathu ya kulingalira kuti titsatire zitsogozo za Baibulo ndi kukhala ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu ndi anthu.​—1 Akorinto 10:31-33.

9. Kodi “kuzindikira kokwanira” kumatanthauzanji?

9 Zosangulutsa zambiri za lerolino nzoonekeratu kukhala zosayenera Akristu.a Chifukwa chake, tiyenera kuphunzitsa mitima yathu ‘kudana nacho choipa’ kotero kuti tisafanane ndi ena a m’zaka za zana loyamba amene “analibenso chikumbumtima cha makhalidwe.” (Salmo 97:10; Aefeso 4:17-19, NW) Kuti tilingalire bwino pa nkhani zoterozo, tifunikira “chidziŵitso cholongosoka ndi kuzindikira kokwanira.” (Afilipi 1:9, NW) Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kuti “kuzindikira” limatanthauza “kuganizira makhalidwe kosamala.” Liwulo limanena za kuzindikira kwa thupi la munthu, monga kwa kuona. Ponena za zosangulutsa kapena nkhani ina iliyonse yofuna chosankha chaumwini, kuzindikira kwathu makhalidwe kuyenera kukhala kogalamuka kotero kuti tikhale okhoza kuona osati chabe nkhani zoonekeratu kukhala zabwino ndi zoipa, komanso zija zosazindikirika bwino. Panthaŵi imodzimodzi, tiyenera kupeŵa kugwiritsira ntchito zitsogozo za Baibulo mopambanitsa ndi kuumirira kuti abale ena onse achite chimodzimodzi.​—Afilipi 4:5.

10. Kodi ndimotani mmene tingadziŵire bwino umunthu wa Yehova malinga ndi Salmo 15?

10 Njira yachitatu yokulitsira mphamvu yathu ya kulingalira ndiyo kudziŵa kalingaliridwe ka Yehova ndi kukazika mozama m’mitima mwathu. M’Mawu ake, Yehova wavumbula umunthu wake ndi miyezo yake. Mwachitsanzo, m’Salmo 15, timaŵerenga za mtundu wa munthu amene Yehova amaitana kukhala mlendo m’chihema chake. Munthu wotero amachita chilungamo, amalankhula choonadi mumtima mwake, ali wokhulupirika pa malonjezo ake, ndipo samadyera anzake masuku pamutu. Poŵerenga salmo limeneli, dzifunseni kuti, ‘Kodi mikhalidwe imeneyi imasonyeza umunthu wanga? Kodi Yehova akundiitana kukhala mlendo m’chihema chake?’ Mphamvu zathu za kulingalira zimakhwima pamene titsatira njira za Yehova ndi kalingaliridwe kake.​—Miyambo 3:5, 6; Ahebri 5:14.

11. Kodi ndimotani mmene Afarisi ‘analekera chiweruziro ndi chikondi cha Mulungu’?

11 Makamaka pambali imeneyi ndi pamene Afarisi analephereratu. Afarisiwo anadziŵa kagwiridwe ka ntchito ka Chilamulo koma sanazindikire “malamulo a chinenero” chake. Anakhoza kutchula mbali zochuluka za Chilamulo, koma analephera kudziŵa bwino Mwiniwake wa chilamulocho. Yesu anawauza kuti: “Mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruziro ndi chikondi cha Mulungu.” (Luka 11:42) Ndi kuuma kwawo mutu ndi mitima, Afarisiwo analephera kugwiritsira ntchito mphamvu yawo ya kulingalira. Kalingaliridwe kawo kosokonezeka kanaonekera pamene anaimba mlandu ophunzira a Yesu kaamba ka kubudula mbewu ndi kudya ngala zake pa Sabata; komabe, pambuyo pake tsiku lomwelo, sanamve ngakhale kugunda kwa chikumbumtima chawo pamene anapanga chiwembu cha kupha Yesu!​—Mateyu 12:1, 2, 14.

12. Kodi ndimotani mmene tingafananire kwambiri ndi Umunthu wa Yehova?

12 Tikufuna kukhala osiyana ndi Afarisiwo. Chidziŵitso chathu cha Mawu a Mulungu chiyenera kutithandiza kukhala ofanana kwambiri ndi Umunthu wa Yehova. Kodi tingachite motani zimenezo? Ataŵerenga chigawo cha Baibulo kapena mabuku ozikidwa pa Baibulo, ena athandizidwa mwa kusinkhasinkha pa mafunso onga aŵa, ‘Kodi mawuŵa akundiphunzitsanji ponena za Yehova ndi mikhalidwe yake? Kodi ndingasonyeze motani mikhalidwe ya Yehova m’zochita zanga ndi ena?’ Kusinkhasinkha pa mafunso otere kumakulitsa mphamvu yathu ya kulingalira ndi kutikhozetsa kukhala “akutsanza a Mulungu.”​—Aefeso 5:1.

Akapolo a Mulungu ndi Kristu, Osati a Anthu

13. Kodi ndimotani mmene Afarisi anachitira monga olamulira oumiriza makhalidwe?

13 Akulu ayenera kulola aja okhala m’chisamaliro chawo kugwiritsira ntchito mphamvu yawo ya kulingalira. Ziŵalo za mpingo sizili akapolo a anthu. “Ndikadakhala wokondweretsabe anthu,” analemba motero Paulo, “sindikadakhala kapolo wa Kristu.” (Agalatiya 1:10; Akolose 3:23, 24) Mosiyana ndi zimenezo, Afarisi anafuna kuti anthu akhulupirire kuti kunali kofunika kwambiri kupeza chiyanjo cha anthu kuposa cha Mulungu. (Mateyu 23:2-7; Yohane 12:42, 43) Afarisiwo anadziika okha kukhala olamulira oumiriza makhalidwe ndipo anapanga malamulo awoawo ndi kumaweruza ena malinga ndi mmene anakhozera kuwatsatira. Aja amene anatsatira Afarisi anafooketsedwa pa kugwiritsira ntchito chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo, akumakhala akapolo a anthu.

14, 15. (a) Kodi akulu angasonyeze motani kuti ali antchito anzawo a nkhosa? (b) Kodi ndimotani mmene akulu ayenera kusamalirira nkhani za chikumbumtima?

14 Akulu Achikristu lerolino amadziŵa kuti gulu la nkhosa silili kwenikweni loŵengeredwa kwa iwo. Mkristu aliyense ayenera kusenza katundu wake. (Aroma 14:4; 2 Akorinto 1:24; Agalatiya 6:5) Umu ndi mmene ziyenera kukhalira. Ndithudi, ngati ziŵalo za gulu la nkhosa zikanakhala akapolo a anthu, kumangomvera chifukwa chakuti ena akuwayang’anira, kodi zingakhale motani ngati amunawo achokapo? Paulo anali ndi chifukwa chokhalira wokondwera kaamba ka Afilipi: “Monga momwe mumvera nthaŵi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira.” Iwo analidi akapolo a Kristu, osati a Paulo.​—Afilipi 2:12.

15 Chifukwa chake, m’nkhani za chikumbumtima, akulu samapangira zosankha aja okhala m’chisamaliro chawo. Amalongosola zitsogozo za Baibulo zogwira ntchito m’nkhaniyo ndiyeno kulola anthuwo kugwiritsira ntchito mphamvu zawo za kulingalira kuti apange chosankha. Limeneli ndi thayo lalikulu kwambiri, komabe limakhala la munthuyo kulisenza.

16. Kodi ndi njira yotani imene inali mu Israyeli yosamalirira mavuto?

16 Talingalirani za nthaŵi pamene Yehova anagwiritsira ntchito oweruza kutsogolera Israyeli. Baibulo limatiuza kuti: “Panalibe mfumu m’Israyeli masiku aja; yense anachita chomkomera pamaso pake.” (Oweruza 21:25) Komabe Yehova anapereka njira yakuti anthu ake apeze chitsogozo. Mzinda uliwonse unali ndi amuna aakulu amene anapereka chithandizo cholamitsa pamafunso ndi mavuto. Ndiponso, ansembe Achilevi anachititsa kukhalapo kwa khalidwe labwino mwa kuphunzitsa anthu malamulo a Mulungu. Makamaka pamene panabuka nkhani zovuta, mkulu wansembe anafunsira kwa Mulungu mwa Urimu ndi Tumimu. Insight on the Scriptures imanena kuti: “Munthu amene anagwiritsira ntchito makonzedwe ameneŵa, amene anapeza chidziŵitso cha lamulo la Mulungu ndi kuchitsatira, anali ndi chitsogozo chabwino cha chikumbumtima chake. Kuchita kwake ‘chomkomera pamaso pake’ m’nkhani yotero sikunatulukepo choipa. Yehova analola anthu kusonyeza maganizo ndi kachitidwe kofuna kapena kosafuna.”​—Voliyumu 2, masamba 162-3.b

17. Kodi ndimotani mmene akulu angasonyezere kuti amapereka uphungu mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu m’malo mwa yawoyawo?

17 Mofanana ndi oweruza ndi ansembe Achiisrayeli, akulu ampingo amapereka chithandizo cholamitsa pa mavuto ndipo amapereka uphungu wothandiza. Nthaŵi zina, angafunikire ngakhale ‘kutsutsa, kudzudzula, kuchenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.’ (2 Timoteo 4:2) Amachita motsatira miyezo ya Mulungu, osati yawoyawo. Kumakhala kothandiza chotani nanga pamene akulu apereka chitsanzo ndi kuyesayesa kufikira mitima!

18. Kodi nchifukwa ninji kuli kothandiza makamaka kuti akulu afikire mitima?

18 Mtima ndiwo “injini” ya zochita zathu Zachikristu. Chifukwa chake Baibulo limati: “Magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Akulu amene amasonkhezera mitima adzapeza kuti aja amene ali mumpingo akusonkhezeredwa kuchita zonse zimene angathe mu utumiki wa Mulungu. Adzakhala oyamba okha, osati ofuna kukankhidwa ndi ena nthaŵi zonse. Yehova samafuna kumvera kokakamiza. Amafuna kumvera kochokera mumtima wodzala ndi chikondi. Akulu angalimbikitse utumiki wotero wochitidwa ndi mtima wofunitsitsa mwa kuthandiza a m’gulu la nkhosa kukulitsa mphamvu ya kulingalira.

Kukulitsa “Maganizo a Kristu”

19, 20. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa ife kukulitsa maganizo a Kristu?

19 Monga momwe taonera, sikokwanira kungodziŵa malamulo a Mulungu. “Mundizindikiritse,” anapempha motero wamasalmo, “ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.” (Salmo 119:34) Yehova wavumbula m’Mawu ake “maganizo a Kristu.” (1 Akorinto 2:16, NW) Pokhala munthu amene anatumikira Yehova ndi mphamvu ya kulingalira, Yesu anatisiyira chitsanzo changwiro. Iye anadziŵa bwino lomwe malamulo a Mulungu ndi zitsogozo zake, ndipo anazigwiritsira ntchito mosalakwa. Mwa kupenda chitsanzo chake, ‘tidzakhoza kuzindikira . . . kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Kristu, chakuposa mazindikiridwe.’ (Aefeso 3:17-19) Inde, zimene timaphunzira m’Baibulo ponena za Yesu zimaposa kwambiri chidziŵitso cha m’mutu; zimatipatsa chithunzi chabwino cha mmene Yehova alili.​—Yohane 14:9, 10.

20 Motero, pamene tiphunzira Mawu a Mulungu, tingazindikire kalingaliridwe ka Yehova pankhani ndi kupanga zosankha zoyenera. Zimenezi zimafuna kuyesayesa. Tiyenera kukhala ophunzira Mawu a Mulungu akhama, tikumazindikira umunthu wa Yehova ndi miyezo yake. Tikuphunzira malamulo achinenero atsopano, titero kunena kwake. Komabe, aja amene akutero adzakhala akutsatira uphungu wa Paulo wa “kupereka matupi [awo] nsembe yamoyo, yoyera, yolandirika kwa Mulungu, ndiwo utumiki wopatulika ndi mphamvu [yawo] ya kulingalira.”​—Aroma 12:1.

[Mawu a M’munsi]

a Zosangulutsa zonenedwa pano sizikuphatikizapo zija zimene zili ndi mbali zaziŵanda, zamaliseche, kapena zausatana, limodzinso ndi zotchedwa zosangulutsa za banja zimene zimachirikiza uchiŵereŵere kapena malingaliro olekerera osayenera Akristu.

b Yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mwaphunziranji?

◻ Kodi ndi kusintha kotani kwa utumiki wa kwa Mulungu kumene kunachitika mu 33 C.E.?

◻ Kodi tingakulitse motani mphamvu yathu ya kulingalira?

◻ Kodi akulu angathandize motani aja amene ali m’gulu la nkhosa kukhala akapolo a Mulungu ndi Kristu?

◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukulitsa “maganizo a Kristu”?

[Chithunzi patsamba 23]

Akulu amathandiza ena kugwiritsira ntchito mphamvu yawo ya kulingalira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena