Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 5/15 tsamba 30
  • Peŵani Mzimu Wodzikweza!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Peŵani Mzimu Wodzikweza!
  • Nsanja ya Olonda—1993
Nsanja ya Olonda—1993
w93 5/15 tsamba 30

Peŵani Mzimu Wodzikweza!

Mwambi wina wanzeru m’Baibulo umati: “Wotalikitsa khomo lake afunafuna kuwonongeka.” (Miyambo 17:19) Kodi cholakwika nchiyani ndi khomo lotalikitsidwa? Ndipo kodi mfundo yaikulu ya mwambiwu njotani?

M’NTHAŴI zakale mbala ndi magulu a achifwamba oyenda pa akavalo anali ofala. Nyumba zosatetezeredwa zomangidwa pazokha zinali paupandu wothyoledwa ndi mbala. Kuti atetezere chuma chawo, eninyumba ena ankamanga linga lokhala ndi chipata cha mpangidwe wapadera. Lingalo linali lalitali, koma khomo lachipata chake linali lalifupi. Kwenikweni, zipata zina zinali zosaposa msinkhu wa mitala imodzi​—zotsika kwambiri koti kavalo ndi womkwera wake sakanatha kuloŵa. Awo amene sanafupikitse chipata choloŵera m’bwalo la nyumba yawo anadziika patsoka la kutheketsa okwera pa akavalo kuloŵa ndi kufunkha katundu wawo.

Makomo oloŵera m’bwalo la nyumba za m’mizinda kaŵirikaŵiri anali aafupi ndi osakopa anthu, osapereka chithunzi chakuti mkati mwa lingalo mungakhale muli chuma. Komabe, ku Perisiya chipata chotalikitsidwa chinali chimodzi cha zizindikiro za uchifumu, chimene nzika zina zinayesa kutsanzira koma zikudziitanira tsoka lalikulu. Aliyense amene anamanga chipata chachitali cha nyumba yake anali kuitana mbala chifukwa cha kuwonetsera ulemerero wake.

Motero Miyambo 17:19 imasonyeza kuti awo amene anatalikitsa zipata zawo anadziitanira tsoka mwakudzikweza kuposa pamalo awo enieni. Mwambi umenewu ungatanthauzenso pakamwa monga ngati khomo lotalikitsidwa mwa mawu odzikweza ndi onyada. Mawu otero amasonkhezera chidani ndipo potsirizira pake angadzetse tsoka kwa munthu wonyadayo. Motero, nkwanzeru chotani nanga, kupeŵa mzimu wodzikweza!

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

Picturesque Palestine, Sinai and Egypt, Volyumu 1, ya Colonel Wilson (1881)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena