Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwaŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati mwatero, mudzasangalala kukumbukira zotsatirazi:
◻ Kodi nchifukwa chiyani tiyenera kudalira anthu amene Yehova amasankha kuti atsogoze anthu ake?
Yehova amasankha anthu kuti akhale ndi maudindo ena ngati iwo ali ndi mikhalidwe yoyenerera yowatheketsa kutsogolera anthu ake m’njira imene iye akufuna kuti ayendemo panthaŵiyo.—8/15, tsamba 14.
◻ Kodi tingaphunzirenji pankhani ya Yona?
Yona sanali kukonda ena monga momwe anali kudzikondera. Pazimene zinachitikira Yona tingaphunzire kudera nkhaŵa ena osati kudzidera nkhaŵa tokha.—8/15 tsamba 19.
◻ Kodi tinganene bwanji kuti “dzina la Yehova ndilo linga lolimba”? (Miyambo 18:10)
Kuthaŵira m’dzina la Yehova kumatanthauza kumkhulupirira Yehova mwiniyo. (Salmo 20:1; 122:4) Zimatanthauza kuchirikiza uchifumu wake, kumvera malamulo ndi mapulinsipulo ake, kukhulupirira malonjezo ake, ndi kudzipereka kwa iye ndi mtima wonse. (Yesaya 50:10; Ahebri 11:6)—9/1, tsamba 10.
◻ Kodi njira ya Paulo yochitira umboni kwa akuluakulu a boma imatipatsa chitsanzo chotani?
Polankhula ndi Mfumu Agripa, Paulo anali kulankhula mwanzeru, nagogomezera nkhani zimene iyeyo ndi Agripa anali kuzidziŵa. Ifenso tiyenera kugogomezera mbali zolimbikitsa za uthenga wabwino, kutchula makamaka ziyembekezo zimene ifeyo ndi iwowo timazidziŵa. (1 Akorinto 9:22)—9/1 tsamba 31.
◻ Kodi ndani amene akupindula ndi kuleza mtima kwa Yehova?
Chifukwa cha kuleza mtima kwa Yehova, lero anthu ambirimbiri akupatsidwa mwayi wakupulumuka “tsiku la Ambuye” likudzalo. (2 Petro 3:9-15) Kuleza mtima kwake kwatipatsanso mpata ‘wakugwira ntchito ya chipulumutso chathu ndi mantha ndi kunthunthumira.’ (Afilipi 2:12)—9/15, tsamba 20.
◻ Kodi Baibulo la Septuagint linali laphindu motani?
Baibulo limeneli linathandiza kwambiri pofalitsa chidziŵitso chonena za Yehova Mulungu ndi Ufumu wake, wokhala ndi Yesu Kristu monga Mfumu. Mwa kugwiritsa ntchito Baibulo la Septuagint, maziko ofunika kwambiri anayalidwa kuthandiza. Ayuda olankhula Chigiriki limodzi ndi Akunja a m’zaka za zana loyamba kulandira uthenga wabwino wa Ufumu.—9/15, tsamba 30.
◻ Kodi fanizo la mwana woloŵerera limatiphunzitsanji za Mulungu?
Choyamba, kuti Yehova ali “wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” (Eksodo 34:6) Chachiŵiri, kuti ali “wokhululukira” pamene mtima wolapa upereka maziko osonyezera chifundo. (Salmo 86:5)—10/1, tsamba 12, 13.
◻ Kodi mtendere womwe walonjezedwa pa Yesaya 65:21-25 udzakhalako liti?
Pokhala olambira Yehova ogwirizana m’paradaiso wauzimu lerolino, odzozedwa limodzi ndi a “nkhosa zina” tsopanolino akukondwera nawo mtendere umene Mulugu wawapatsa. (Yohane 10:16) Ndipo mtendere umenewu udzafika mpaka m’Paradaiso weniweni, pamene ‘kufuna kwa Mulungu kudzachitika padziko lapansi, monga kumwamba.’ Panthaŵi imeneyo, mawu a mneneri Yesaya adzakhala atakwanira ndendende. (Mateyu 6:10)—10/15, tsamba 24.
◻ Kodi nchifukwa chiyani Akristu amakumbukira masiku a ukwati koma osati masiku a kubadwa?
Baibulo silinena kuti ukwati ngwoipa. Yangokhala nkhani yofuna mwini ngati Akristu akufuna kusunga tsiku la ukwati, namakumbukira mmene anasangalalira pa chochitikacho ndi mmenenso anatsimikizirana kuti adzachita zotheka kuti banja lawolo likhale bwino. Komabe, mapwando a tsiku lakubadwa amene Baibulo limatchula ndi okhawo a anthu akunja, ndipo pamapwandopo panachitika nkhanza.—10/15, masamba 30-31.
◻ M’fanizo la Paulo lolembedwa pa 1 Akorinto 3:12, 13, kodi “moto” ukuimira chiyani, ndipo Akristu ayenera kusamala za chiyani?
Pali moto umene tonsefe timakumana nawo m’moyo—ziyeso za chikhulupiriro chathu. (Yohane 15:20; Yakobo 1:2, 3) Aliyense amene tikuphunzitsa choonadi adzayesedwa. Tikapanda kumphunzitsa bwino, zotsatira zake zingakhale zachisoni, monga momwe Paulo anachenjezera. (1 Akorinto 3:15)—11/1, tsamba 11.
◻ Kodi Nowa ‘anayenda ndi Mulungu’ motani? (Genesis 6:9)
Nowa anayenda ndi Mulungu mwa njira yakuti anachita zonse zimene Mulungu anamuuza. Chifukwa chakuti Nowa anapereka moyo wake pakuchita chifuniro cha Mulungu, anali ndi unansi wabwino ndiponso wolimba ndi Mulungu.—11/15, tsamba 10.
◻ Kodi kusadziŵa kwathu nthaŵi yeniyeni imene Mulungu adzaweruza oipa kumatipatsa mpata wotani?
Kumatipatsa mpata wosonyeza kuti timakondadi Yehova ndipo tikufuna kuyenda m’njira zake kwamuyaya. Kumasonyezanso kuti tili okhulupirika kwa Mulungu ndipo timakhulupirira njira imene iye amachitira zinthu. Ndiponso, kumatithandiza kukhala atcheru ndi ogalamuka mwauzimu. (Mateyu 24:42-44)—11/15, tsamba 18.
◻ Kodi kukhulupirira “dzina la Mwana wa Mulungu” kumatanthauzanji? (1 Yohane 5:13)
Kumatanthauza kumvera malamulo onse a Kristu, kuphatikizapo lamulo lake la ‘kukondana wina ndi mnzake.’ (Yohane 15:14, 17) Chikondi chimafuna kuchitira ena zabwino. Chimaletsa tsankho losankhana mitundu, zipembedzo, ndi zachikhalidwe.—12/1, tsamba 7.
◻ Kodi nchifukwa chiyani Mboni za Yehova ‘zimadedwa’? (Mateyu 10:22)
Mboni za Yehova zimadedwa pazifukwa zofanana ndi zimene Akristu oyambirira ankazunzidwira. Choyamba, Mboni za Yehova zimasonyeza zikhulupiriro zawo zachipembedzo m’njira imene ena amanyansidwa nayo. Chachiŵiri, zakhala zikunenezedwa mabodza—mabodza a mkunkhuniza ndiponso ena amapotoza zikhulupiriro zawo.—12/1, tsamba 14.