Kumamvera Yehova Pamene Mapeto Akuyandikira
“Ngwodala amene andimvera . . . pakuti wondipeza ine apeza moyo.”—MIYAMBO 8:34, 35.
1, 2. (a) Mosasamala kanthu za kusoweka kwa mtendere kuzungulira m’mbiri yonse ya munthu, kodi nchiyani chimene ena akunena tsopano? (b) Kodi nchifukwa ninji mtendere weniweni kupyolera mu zoyesayesa za munthu uli wosatheka?
MOSASAMALA KANTHU za kusoweka kwa mtendere kuzungulira m’mbiri yonse, makamaka mu zana lino la 20, ena amanena kuti mitundu ikutenga masitepi a kuthetsera mavuto awo. Iwo amaloza ku chenicheni chakuti atsogoleri a dziko amapangitsa misonkhano kulankhula ponena za mtendere ndi kusaina zigwirizano zosiyanasiyana. Nkulekeranji, popeza Mitundu Yogwirizana inalengeza chaka chatha kukhala “Chaka cha Mtendere cha Mitundu Yonse”! Chinayembekezeredwa kuti ichi chidzawona kuyambika kwa zoyesayesa zapadera za mitundu ku kupititsa patsogolo mtendere, ndi kuthekera kwa chipambano mtsogolo.
2 Komabe, m’mbiri yonse, kodi zoyesayesa zofananazo zinabweretsa mtendere wokhazikika? Ngati icho chinali chothekera ndi anthu, pakanakhala mtendere kale lomwe—kale kwambiri anthu mabiliyoni asanuwo asanagawanikane mu mitundu yoposa 160, ndi kusiyana kosawerengeka kwa ndale zadziko, chuma, ndi nthanthi za chipembedzo. Koma sipanakhalepo nkomwe mtendere; ndipo sipadzakhalanso mtendere wochokera ku zoyesayesa za atsogoleri a dziko iri. Nchifukwa ninji ayi? Chifukwa choyamba, popeza kuti mavuto a mtundu wa munthu ali ovuta kwambiri kotero kuti ali osakhoza kuthetsedwa ndi zoyesayesa za munthu zokha. Monga mmene Yeremiya 10:23 molondola amanenera: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”
Chifukwa Chimene Zoyesayesa Za Anthu Sizingapambanire
3. Kodi ndi kaamba ka chifukwa china chiti chimene anthu ndi mitundu sidzabweretsera mtendere wenieni?
3 Pali chifukwa china chimene zoyesayesa za anthu ndi mitundu sizingabweretsere mtendere weniweni. Baibulo limaloza ku icho pa 1 Yohane 5:19, likumati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” Chivumbulutso 12:9 chimasonyeza kuti “woipa” ameneyo ali “wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.” Akorinto Wachiwiri 4:4 amamutcha iye “mulungu wa dongosolo iri la zinthu.” Chotero, dongosolo lonse liripoli lakachitidwe ka zinthu landale, chuma, ndi lamulo la chipembedzo lomwe latulutsa chiwawa chambiri liri chotulukapo cha ulamuliro wa Satana, osati ulamuliro wa Mulungu. Chimenecho ndi chifukwa chake, polankhula za nzeru yochokera kwa Mulungu, 1 Akorinto 2:8 amanena kuti: “[Nzeru imeneyi NW] saidziwa m’modzi wa akulu a pansi pano.”—Luka 4:5, 6.
4. Kodi nchiyani chimene chinatulukapo pamene makolo athu oyambirira anasiya kumvera Yehova?
4 Pamene Satana anaukira Mulungu, iye anapangitsa makolo athu oyambirira kumvetsera kwa iye m’malo mwakumvetsera kwa Mulungu. Monga chotulukapo chake, iwo anapatuka kuchoka ku kumvera Mulungu ndi kubweretsa pabanja la mtundu wa anthu zaka 6, 0 za chisoni. Baibulo momvekera bwino limatiuza ife kuti, Satana anapangitsa anthu kukhulupirira kuti iwo angachite bwino popanda kumvera Mlengi wawo. (Genesis 3:1-5) Mu nzeru yake, Yehova analola dziko la mtundu wa anthu kupitiriza mu ilo lokha, popanda chitsogozo chake, kufikira kunthawi ino. Ndipo motsimikizirika, mu zaka mazana onsewa, chasonyezedwa kotheratu kuti kulamulira kwa munthu kuli kolephera.—Deutronomo 32:5; Mlaliki 8:9.
5. Ngakhale ngati mtendere ungabweretsedwe kupyolera mu zoyesayesa za anthu, kodi nchiyani chomwe chidzatsalirabe ndi ife?
5 Mkuwonjezerapo, pamene Adamu ndi Hava analeka kumvera Yehova, Magwero a moyo wangwiro, iwo anakhala opanda ungwiro ndipo kenaka anafa. Chotero, mbadwa zawo zonse zinabadwa zopanda ungwiro. Matenda, ukalamba, ndi imfa zinakhala pa mtundu wa munthu. (Aroma 5:12) Chotero, ngakhale ngati anthu akanapambana mkubweretsa mtendere, iwo sangathe kuchiritsa kupanda ungwiro kwa cholowa. Tingadwale, kukalamba, ndi kufa. Popeza Satana ali ndi thayo kaamba ka ichi, Yesu ananena za iye: “Iyeyu anali wambanda [wakupha anthu] kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’chowonadi.”(Yohane 8:44) Ndithudi, pamene muganiza ponena za mabiliyoni omwe anakhala ndi moyo ndi kufa nthawi yapitayi, chimawoneka ngati kuti Satana anapha onse a iwo.
6. Kodi ndi ndani amene ali othetsa mtendere, ndipo kodi nchiyani chomwe chidzachitika kwa iwo?
6 Satana anapangitsanso zolengedwa zina zauzimu kugwirizana naye mu kuukira, ndipo oipa onsewa anakana kumvera pamene Yehova analankhula. Chotero ali Satana, ziwanda zake, ndi anthu oukira omwe anabweretsa dziko iri ku mkhalidwe wake umene ulipowu. Onse a iwo ayenera kuchotsedwa, kumaliza chivulazo chowononga chimenechi cha zaka 6, 0 osadalira pa Mulungu. “Mulungu wa mtendere,” akutsimikizira Aroma 16:20, “adzaphwanya Satana . . . posachedwapa,” limodzi ndi ziwanda zake ndi anthu onse omwe amakana kumvetsera pamene Mulungu alikulankhula.—Mateyu 25:41.
Chifuno Chachikulu cha Kumvera Tsopano
7. Kodi ndi chifukwa ninji tiyenera kukulitsa zoyesayesa zathu za kutumikira Yehova tsopano?
7 Tsopano tiri mkati mwenimweni mwa mapeto a “masiku otsiriza” awa. (2 Timoteo 3: 1-5) Monga chotulukapo chake, pali chifuno chokulira kwambiri chakumvera zimene Yehova akunena kwa ife. Pali kufunika kofananako kwa kuwonjezera kufunitsitsa kwathu kupanga kudzipereka kumtumikira iye. Nchifukwa ninji tifunikira kukulitsa kuyesayesa kwathu? Chifukwa Satana akudziwa kuti ali kokha “ndi kanthawi komtsalira.” (Chivumbulutso 12:12) Chotero iye motsimikizirika adzakulitsa zizunzo zake za kusakaza ndi kuwononga.
8. (a) Kodi nchifukwa ninji ntchito yolalikira singaimitsidwe ndi adani ake? (b) Kodi nchiyani chimene tingachite kuti tipitirize kukhala ndi chirikizo la umulungu?
8 Satana makamaka angakonde kuletsa Mboni za Yehova kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu. Koma iye sangatero, popeza Yehova analonjeza izo: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula.” (Yesaya 54:17) Awo amene amatsutsa atumiki ake adzakhala “akupezeka otsutsana ndi Mulungu.” (Machitidwe 5:38, 39) Chotero, ndi kuchirikizidwa kwamphamvu ndi mzimu wa Yehova, Yesu Kristu, ndi unyinji wamphamvu za angelo, ntchito ya kulalikira Ufumu imakula mu mphamvu chaka chiri chonse. Kuti asunge chirikizo laumulungu limenelo, atumiki a Yehova mosamalitsa amamvera uphungu wa pa Yakobo 4:7, 8: “Potero mverani Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani. Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”
9. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kupeputsa Satana?
9 Musanyalanyaze kuthekera kwa Satana kwa kunyenga ndi kuvulaza. Mawu a Mulungu amachenjeza: “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu Mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire. Ameneyo mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro.” (1 Petro 5:8, 9) Ngati munadziwa kuti mkango wamisala unali womasuka mdera lanu, inu mungatenge chinjirizo la kutetezera inumwini ndi banja lanu. Kumene Satana akukhudzidwa, tiyenera kukhala ogalamuka kwambiri, popeza iye angachite kusakaza kosatha. Mwachisoni, anthu ambiri ali opanda chinjirizo chifukwa sadziwa nkomwe kuti Satana alipo. Nchifukwa ninji ziri tero? Chifukwa amasankha kusamvera Mawu a Yehova. Ndipo kodi nchiyani chimene chidzakhala chotulukapo cha chosankha choipa chimenecho? “Chimene munthu achifesa, chomwechonso adzachituta.”—Agalatiya 6:7.
Pamene Afuula “Mtendere ndi Chisungiko!”
10, 11. (a) Kodi chiyani chimene tiyenera kusunga m’maganizo ponena za chipambano chirichonse chimene mitundu ingakhale nacho m’kubweretsa mtendere? (b) Kodi ndi ulosi wa Baibulo uti umene umachitira umboni pa kufunafuna kaamba ka mtendere kwa mitundu mu nthawi yathu? (c) Kodi mtendere woterowo udzakhala wanthawi yaitali motani?
10 Musanyengedwe ndi chipambano chimene mitundu ingakhale itachifikira mwa kubweretsa mtendere. Nthawi zonse sungani m’maganizo kuti Yehova sakugwiritsira ntchito athenga alionse a dziko iri kulinga kumapeto amenewo. Yehova ali ndi njira yakeyake yakubweretsera mtendere weniweni, ndipo iyo iri kokha mwanjira ya Ufumu wake pansi pa Kristu. Chotero mosasamala kanthu kuti ndi chipambano chotani chimene mitundu ingakwaniritse mukukhazikitsa mtendere, udzakhala wa kanthawi ndipo kokha monga chikuto. Palibe chirichonse chimene chidzasintha kwenikweni. Upandu, chiwawa, nkhondo, njala, umphawi, kusweka kwa mabanja, khalidwe la chisembwere, matenda, imfa, ndi Satana ndi ziwanda zake adzapitirizabe kukhala ndi ife kufikira Yehova atazichotsa zonse za izo. “Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwira ntchito pachabe.”—Masalmo 127:1.
11 Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti mitundu idzapanga kuyesayesa kwamphamvu kulinga ku mtendere mu nthawi yathu. Ilo limanena: “Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la [Yehova, NW] lidzadza monga mbala usiku. Pamene angonena: ‘Mtendere ndi [chisungiko NW]!’ pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.” (1 Atesalonika 5:2, 3) Kufuula kumeneku kwa “Mtendere ndi chisungiko!”sikudzatanthauza kuti kuola kwa dziko iri kwatembenuzidwa. Timoteo Wachiwiri 3:13 amanena kuti: “Koma anthu oipa ndi onyenga adzaipa chiipire.” Zenizeni zidzakhalabe monga momwe mtsogoleri wa gulu la mikhalidwe yotizinga ananenera: “Vuto lenileni lomwe likuyang’anizana ndi mtundu wa anthu liri lakuti iwo wakhala wosalamulirika.”
12. Kodi nchiyani chimene atumiki a Yehova amadziwa ponena za kufunika kwenikweni kwa kubwera kwa mfuu ya ‘mtendere ndi chisungiko’?
12 Ambiri mu dziko adzanyengedwa ndi ziyembekezo zopanda pake mkati mwa kubwera kwa mfuu ya “Mtendere ndi chisungiko!”Koma atumiki a Yehova sadzatero, popeza iwo amamvera pamene Mulungu akulankhula. Chotero iwo amadziwa kuchokera ku mawu ake kuti chilengezo choterocho sichidzabweretsa mtendere weniweni ndi chisungiko. M’malo mwake, icho mchenicheni chidzakhala chizindikiro chomalizira chakuti “chiwonongeko chobukapo chidzawagwera.” Icho chidzabukitsa kuyambika kotsimikizirika kwa “chisautso chachikulu” chimene Yesu ananeneratu kaamba ka nthawi yathu. Iye anati: “Pakuti pomwepo padzakhala masauko akulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi chadziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.”—Mateyu 24:21.
13. Kodi ndimotani mmene Baibulo limalongosolera kutha kwa ulamuliro wa munthu?
13 Mkati mwa “chisautso chachikulu, 0 ulamuliro wa munthu udzabweretsedwa kumapeto. Masalmo 2:2-6 amanena kuti: “Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, kutsutsana naye Yehova, ndi wodzozedwa wake, ndi kuti, tidule zomangira zawo, titaye nsinga zawo. Wokhala m’mwambayo adzawaseka; [Yehova, NW] adzawanyoza. Pomwepo adzalankhula nawo mu mkwiyo wake, nadzawaopsya m’ukali wake; koma ine ndadzoza mfumu yanga pa Ziyoni [wakumwamba], phiri langa loyera.” Masalmo 110:5, 6 akuwonjezera: “Yehova iye mwini . . . adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake. Adzaweruza mwa amitundu.” Upo wonse wa ndale zadziko udzatha, popeza Yesaya 8:9, 10 akunena: “Kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka; kwindani nokha koma mudzathyokathyoka. Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mawu, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife!”
Otsimikizira za Kupulumuka
14. Kodi nchifukwa ninji tiri otsimikizira kutipadzakhala opulumuka a mapeto a dziko iri?
14 Tiri otsimikizira kuti Yehova adzasunga anthu ake odziŵitsidwa bwino kotero kuti angatenge masitepi oyenerera kaamba ka kupulumuka “chisautso chachikulu” chikudzacho. Kodi ndimotani mmene tingakhalire otsimikizira motero? Chifukwa ulosi wa pa Chivumbulutso 7:9, 14 umasonyeza kuti “khamu lalikulu” limapulumukadi. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakumvetsera pamene Yehova akulankhula kukhala ndi olangizidwa moyenerera. Mu njira imeneyi awo a “khamu lalikulu” ali okhoza kuchita zimene Chivumbulutso 7:15 chimanena: “Amtumikira iye usana ndi usiku.” Chotero iwo amachita chifuno cha Mulungu, kufikira chivomerezo chake, ndipo ali ochinjirizidwa kupulumuka mapeto adziko iri. —1 Yohane 2:15-17.
15. Kodi ndimotani mmene Yoweli akulongosolera kupondedwa kwa dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu, ndipo nchiyani chimene chidzakhala chotulukapo kaamba ka atumiki a Mulungu?
15 Yoweli 3:13-16 amalozanso kukupulumuka kwa atumiki a Mulungu pamene dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu lipondedwa monga mphesa mu choponderamo. Iro limati: “Longani zenga, pakuti dzinthu dzacha; . . . choponderamo mphesa, zosungiramo zisefukira; pakuti zoipa zawo nzazikulu. Aunyinji aunyinji m’chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m’chigwa chotsirizira mlandu. Dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwawo. Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, [wakumwamba] . . . ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu ake.”
16. Kodi ndi maulosi ena ati amene amasonyeza kuti Yehova adzasunga anthu ake kupyolera mu chiwonongeko chadziko?
16 Mofananamo, pa Yesaya 26:20, 21 ponena za nthawi ikudzayo Yehova akuti: “Idzani, anthu anga, lowani m’zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita. Pakuti tawonani, Yehova adza kuchokera ku malo ake kudzazonda okhala pa dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwawo.” Chotero, Zefaniya 2:2, 3 akufulumiza: “Lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova. Funani Yehova, ofatsa inu nonsea m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”
‘Kuthamangira’ kwa Yehova
17. (a) Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa kuti tipeze chinjirizo la Yehova? (b) Kodi ndi cholakwa chiti chimene anthu a m’ntnawi ya Chigumula chisanafike anachita?
17 Miyambo 18:10 imanena kuti: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” Kodi inu ‘mukuthamangira’ kwa Yehova? Kumbukirani chimene Yesu ananena ponena za anthu m’tsiku la Nowa. Iwo anali “kudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa; ndipo iwo sanadziwa kanthu koma kufikira kumene chigumula chinadza, nichipululutsa iwo onse.” (Mateyu 24:38, 39) Chimene chinali cholakwa chinali kukhala otanganidwa ndi chiri chonse kuchotsapo kumvera Yehova pamene iye analankhula kupyolera mwa mtumiki wake Nowa, “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petro 2:5) Chifukwa chakuti iwo sanamvere, pamene chigumula chinadza “chinapululutsa iwo onse” ku chiwonongeko.
18. Kodi nchifukwa ninji kungokhala kwawo kokha anthu “abwino” sikunapulumutse awo amene anawonongedwa mu Chigumula?
18 Ambiri a iwo amene anafa pa Chigumula mosakaikira anadzilingalira iwo eni kukhala anthu” abwino, osalowetsedwa mu chiwawa chomwe chinadzaza mtundu wa anthu m’masiku amenewo. Koma kungokhala chabe “abwino” sikunapulumutse iwo. Mwakupanda kwawo chikondwerero anakhululukira zolakwa za mu tsiku lawo. Chinthu chofunika kwambiri chinali chakuti iwo ‘sanathamangire kwa Yehova; iwo sanamvere pamene atumiki a Mulungu analankhula. Chotero iwo sanatenge njira zoyenerera kaamba ka chipulumuko. Kumbali ina, awo amene anamvera anapulumuka.
19. Kodi ndi phindu lozizwitsa lotani limene atumiki a Yehova amatuta ngakhale tsopano, ndipo nchifukwa ninji?
19 Lerolino Mulungu’ akulankhula mtendere kwa awo amene akumvera iye. Ndi chotulukapo chotani kwa iwo? Yesaya 54:13 amanena kuti: “Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” Inde, “Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.” (Masalmo 29:11) Chotero, mkati mwa dziko iri la chiwawa, Mboni za Yehova ziri ndi mtendere wowona, mtendere wosasweka pakati pawo. Iwo ali ndi ubale wa dziko lonse wa chikondi umene atsogoleri adziko, mitundu yawo, ndi zipembedzo zawo sizingathe kuutsanzira. Nchifukwa ninji iwo sangathe kutero? Chifukwa iwo samvera kwenikweni pamene Mulungu akulankhula. Chotero iwo sagwirira ntchito pa zimene iye amanena. Koma Mboni za Yehova zimamvera Mulungu. Izo zimatenga mosamalitsa mawu a pa Mlaliki 12:13: “Opa Mulungu, nusunge malamulo ake; pa kuti choyenera anthu onse ndi ichi.”
20. Kodi nchiyani chimene munthu aliyense ayenera kuchita kuti apulumuke kulowa mu dziko latsopano la Mulungu?
20 Chimenechi ndi chimene munthu aliyense—inde, onse amene akufuna kudzakhala mu dziko latsopano la Mulungu—ayenera kuchita. Iwo ayenera ‘kuthamangira’ kwa Yehova mosachedwa. Indedi, iwo ayenera kutsogozedwa ndi nzeru yopatsidwa ndi Mulungu yomwe ikuimiridwa mwa kunena kuti: “Mundimvere ine, ngwodala akusunga njira zanga. Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana. Ngwodala amene andimvera ine . . . Pakuti wondipeza ine apeza moyo.”—Miyambo 8:32-35.
Kodi Mukanayankha Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji zoyesayesa za anthu sizidzapambana m’kubweretsa mtendere?
◻ Kodi nchifukwa ninji pali kufunika kokulira tsopano kwa kumvera Yehova?
◻ Kodi nchiyani chimene kufuula kwa “Mtendere ndi chisungiko!’ kudzatanthauza kwenikweni?
◻ Kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita ngati tikufuna kupulumuka kulowa mu dongosolo la kachitidwe ka zinthu katsopano la Mulungu?
[Chithunzi patsamba 17]
Monga mkango wobuma, Satana akukulitsa zoyesayesa zake za kuwononga ndi kusakaza
[Chithunzi patsamba 18]
Pamene dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu lipondedwa monga mphesa mu choponderamo, “Yehova adzakhala linga kwa anthu ake”