Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 2/1 tsamba 32
  • ‘Kuposa Mudzi Wolimba’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Kuposa Mudzi Wolimba’
  • Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1994
w94 2/1 tsamba 32

‘Kuposa Mudzi Wolimba’

“PA MLINGO wa nthaŵi inoyo, pafupifupi 40% ya ana a ku United States adzaona kutha kwa maukwati a makolo awo asanakwanitse zaka 18.” (Science, June 7, 1991) Ha, ndi chiŵerengero chochititsa mantha chotani nanga! Kodi nchifukwa ninji zimenezi zimachitika?

Woweruza wa ku bwalo lamilandu la maunansi a m’banja ndi bwalo lamilandu lotsimikizira pangano logawa chuma chamasiye Edward M. Ginsburg, pofunsidwa ndi The Boston Globe, anapereka lingaliro lake. Iye anati: “Ndife anthu adyera. Timafuna ‘zanga.’ Timafunsa kuti, ‘Kodi nchiyani chimene chilipo cha ine tsopano lino?’ Timafuna chikhutiro chapanthaŵi yomweyo.”

Dyera lachibwana lotero limachititsa mkwiyo ndi mikangano muukwati. Woweruza Ginsburg akunena kuti pamene okwatirana potsirizira pake apita ku bwalo lamilandu lachisudzulo, mwamuna ndi mkazi amafuna chipambano. Iwo amafuna kuti wina awauze kuti iwo ngwolondola ndi kuti mnzawoyo ndiye wolakwa. Iwo amafuna kuti munthu wina anene kuti: “Wapambana nkhondoyi.”

Mawu ake amatikumbutsa mwambi wouziridwa uwu: “Mbale wochimwiridwa ali woposa mudzi wolimba.” (Miyambo 18:19, NW) Inde, pamene ndewu ibuka muukwati, magulu olimbanawo angakhale osalingalira ndi oumirira. Kaŵirikaŵiri, mwaliuma amakana kugonjera, mofanana ndi “mudzi wolimba” umene waukiridwa.

Kodi zinthu ziyenera kukhala choncho? Ayi, pali njira ina. Maukwati amakhala olimba ndi okhalitsa pamene onse aŵiri, kuyambira pachiyambi, alabadira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.” (Aefeso 4:32) Kodi nkosavuta kukulitsa mikhalidwe yoteroyo? Osati nthaŵi zonse. Koma kodi chisudzulo nchosavuta motani? Kodi mavuto a maganizo ndi a zachuma ochititsidwa ndi kusweka kwa ukwati ngwopweteka motani? Ndipo bwanji ponena za ana, amene kaŵirikaŵiri amakhala ndi zotulukapo za kusudzulana kwa makolo awo m’moyo wauchikulire?

Nkwabwino koposa kuti aŵiri onsewo agwirire ntchito pa kusunga ukwati ndipo osati kukhala osalolerana kwa wina ndi mnzake, monga “mudzi wolimba.” Uphungu wa Paulo kwa Akristu umagwira ntchito makamaka kwa okwatirana: “Khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”​—Akolose 3:14.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

The Complete Encyclopedia of Illustration/​J. G. Heck

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena