“Chuma ndi Lilime Lonama . . . Nkhungu”
MASIKU ANO Kunama ndi kunyenga kawirikawiri zimawonedwa monga zoyenerera—ndipo njira yapamwamba ya chipambano—ya bizinesi. Ichi chinali chowona mnthawi za Baibulo. Wamasalmo Asafu analemba ponena za awo omwe “anawonjezerapo pa chuma chawo,“ mwachiwonekere ndi machitidwe onyenga. Oterowo anawonekera kukhala ali “pokhazikika chikhazikikire“ chifukwa cha chuma chimene kunyenga kwawo kunawabweretsera iwo.—Masalmo 73:8, 12.
Akristu lerolino, ngakhale kuli tero, ayenera kupewa ‘kukonda phindu lonyansa’ ndi kutembenukira kukusawona mtima kapena kachitidwe ka zinthu ka bizinesi kosawona mtima. (1 Petro 5:2) Akuchenjeza Miyambo 21:6: “Kupata chuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.” Inde, “chuma” chirichonse chopezedwa mwakunama ndi kunyenga chiri chotsimikizirika kukhala cha kanthawi monga “nkhungu,“ chosakhalitsa monga mthunzi. “Chuma cha uchimo sichithangata“ mkupita kwanthawi. (Miyambo 10:2) Ndithudi, wonama “akufuna imfa“ mwakulondola njira yopatsa imfa. Moyo wake ungafupikitsidwe pamene njira zake zonama zilephera. (Yerekezani ndi Estere 7:10) Kapena mkupita kwa nthawi kwenikweni, moyo wake udzathedwa pa tsiku la chiweruzo la Mulungu.