Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 195
  • Kodi “Kukonda Adani Anu” Kumatanthauza Chiyani”?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi “Kukonda Adani Anu” Kumatanthauza Chiyani”?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda adani athu?
  • Mungasonyeze m’njira ziti kuti mumakonda adani anu?
  • Kodi muyenera kupita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu?
  • Maganizo olakwika pankhani yokonda adani athu
  • Pitirizani Kuchita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi N’zotheka Kukonda Adani Athu?
    Galamukani!—2009
  • Chikondi (Agape)—Zimene Sichili ndi ZImene Chili
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Chikondi Chimatithandiza Kupirira Ena Akamadana Nafe
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 195
Azimayi awiri aimirira, pakati pawo pali chiphedi. Amene ali kumanzere akupepesa mnzake amene ali kumanja koma mnzakeyo akumuyang’ana mokwiya.

Kodi Yesu Ankatanthauza Chiyani Pomwe Ananena Kuti ‘Kondani Adani Anu’?

Yankho la m’Baibulo

Pa ulaliki wake wotchuka wapaphiri, Yesu anati: ‘Kondani adani anu.’ (Mateyu 5:44; Luka 6:27, 35) Mawu a Yesu amenewa amatanthauza kuti tiyenera kuchitira zabwino anthu amene amatida kapenanso kutichitira zinthu zopanda chilungamo.

Yesu anasonyeza kuti ankakonda adani ake pomwe anawakhululukira ngakhale kuti anamuchitira zankhanza. (Luka 23:33, 34) Zimene anaphunzitsa pankhani yokhudza kukonda adani athu, zimagwirizana ndi zimene zili m’Malemba a Chiheberi, amene amadziwikanso kuti Chipangano Chakale.—Ekisodo 23:4, 5; Miyambo 24:17; 25:21.

“Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.”—Mateyu 5:43, 44.

Zimene zili munkhaniyi

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda adani athu?

  • Mungasonyeze m’njira ziti kuti mumakonda adani anu?

  • Kodi muyenera kupita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu?

  • Maganizo olakwika pankhani yokonda adani athu

  • Mavesi a Baibulo omwe amatilimbikitsa kukonda adani athu

N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda adani athu?

  • Mulungu amatipatsa chitsanzo pankhaniyi. Mulungu “ndi wachifundo kwa osayamika ndi kwa oipa.” (Luka 6:35) Iye “amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa.”—Mateyu 5:45.

  • Chikondi chingapangitse mdani wathu kuti asinthe. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizikomera mtima mdani wathu chifukwa tikatero timakhala ngati ‘tikumuunjikira makala amoto pamutu pake.’ (Miy. 25:22) Fanizo limeneli limanena zomwe zimachitika posungunula mwala womwe umakhala ndi zitsulo zamtengo wapatali mkati mwake. Choncho tikamakomera mtima anthu amene amatida, tikhoza kusungunula mkwiyo wawo ndi kuwathandiza kukhala ndi makhalidwe abwino.

Mungasonyeze m’njira ziti kuti mumakonda adani anu?

  • ‘Muzichitira zabwino amene amadana nanu.’ (Luka 6:27) Baibulo limati: “Ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse chakumwa.” (Aroma 12:20) Mungapeze njira zina zosonyezera kukonda mdani wanu potsatira mawu a Yesu odziwika kwambiri akuti: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.”—Luka 6:31.

  • ‘Muzidalitsa omwe amakutembererani.’ (Luka 6:28) Timadalitsa adani athu polankhula nawo mokoma mtima ndiponso mowaganizira, ngakhale pomwe iwowo akutilankhula mwachipongwe. Baibulo limati: “Osabwezera . . . chipongwe pa chipongwe, koma m’malomwake muzidalitsa.” (1 Petulo 3:9) Malangizo amenewa angatithandize kuthetsa chidani.

  • ‘Muzipempherera amene amakunyozani.’ (Luka 6:28) Ngati munthu akukunyozani, musabwezere “choipa pa choipa.” (Aroma 12:17) Koma m’malomwake, muzipempha Mulungu kuti amukhululukire. (Luka 23:34; Machitidwe 7:59, 60) Komanso m’malo mobwezera, muzisiya zonse m’manja mwa Mulungu kuti iye aweruze munthuyo mogwirizana ndi mfundo zake zolungama.—Levitiko 19:18; Aroma 12:19.

Zithunzi: 1. Mzimayi wangoima n’kumamvetsera pomwe mnzake wogwira naye ntchito akumulalatira. 2. Pambuyo pake, mzimayi uja wakhala patebulo ndipo akupemphera.

“Pitirizani kukonda adani anu ndi kuchita zabwino kwa amene akudana nanu. Pitirizani kudalitsa okutembererani ndi kupempherera amene akukunyozani.”—Luka 6:27, 28.

  • Muzikhala ‘oleza mtima ndiponso okoma mtima.’ (1 Akorinto 13:4) M’mawu ake odziwika bwino ofotokozera tanthauzo la mawu akuti chikondi, Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito mawu ena ochokera ku mawu a Chigiriki akuti a·gaʹpe omwe amapezeka pa Mateyu 5:44 ndi Luka 6:27, 35. Timasonyeza chikondi chachikhristu chimenechi ngakhale kwa adani athu pokhala oleza mtima komanso okoma mtima. Tingachitenso zimenezi tikamapewa mtima wansanje, wodzitukumula komanso tikamapewa kukhala amwano.

Mzimayi akupatsa wantchito mnzake uja kapu ya tiyi ndipo mnzake wolalata uja akudabwa.

“Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.” Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama, koma chimakondwera ndi choonadi. Chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha.”—1 Akorinto 13:4-8.

Kodi muyenera kupita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu?

Ayi, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti sayenera kumenyana ndi adani awo. Mwachitsanzo, atawachenjeza za kuukiridwa kwa Yerusalemu, sanawauze kuti akhalebe mumzindawo ndi kumenya nkhondo, koma anawauza kuti athawe. (Luka 21:20, 21) Yesu anauzanso mtumwi Petulo kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Baibulo komanso mabuku ofotokoza mbiri, amasonyeza kuti otsatira a Yesu oyambirira sankamenya nkhondo yolimbana ndi adani awo.a—2 Timoteyo 2:24.

Maganizo olakwika pankhani yokonda adani athu

Maganizo olakwika: Chilamulo cha Mulungu chinkalola Aisiraeli kuti azidana ndi adani awo.

Zoona zake: M’chilamulo munalibe lamulo limeneli. Koma chinkalimbikitsa Aisiraeli kuti azikonda anzawo. (Levitiko 19:18) Ngakhale kuti mawu akuti “mnzako” anganene za munthu wina aliyense, Ayuda ena ankaona kuti mawuwa ankanena za Ayuda anzawo basi, ndipo ankakhulupirira kuti anthu amene sanali Ayuda anali adani awo ndipo ankayenera kudana nawo. (Mateyu 5:43, 44) Yesu anawongolera maganizo olakwikawo powauza fanizo la Msamariya wachifundo.—Luka 10:29-37.

Maganizo olakwika: Ukamakonda mdani wako umasonyeza kuti ukugwirizana ndi khalidwe lake loipa.

Zoona zake: Baibulo limasonyeza kuti ndi zotheka kukonda munthu popanda kusekerera khalidwe lake loipa. Mwachitsanzo, Yesu ankadana ndi zachiwawa komabe anapempherera anthu amene anamupha. (Luka 23:34) Yesu ankadananso ndi kusamvera malamulo kapena kuti kuchita machimo. Komabe ngakhale zinali choncho, iye anapereka moyo wake chifukwa cha anthu ochimwa.—Yohane 3:16; Aroma 6:23.

a Buku lina lomwe analemba E. W. Barnes limati: “Tikaona bwinobwino maumboni amene alipo, amasonyeza kuti pofika m’nthawi ya Marcus Aurelius [yemwe anali Mfumu yachiroma kuyambira mu 161 kudzafika mu 180 C.E.] palibe Mkhristu amene analowa usilikali; komanso palibe amene anapitiriza kugwira ntchito yausilikali atakhala Mkhristu.”—The Rise of Christianity.

Mavesi a Baibulo omwe amatilimbikitsa kukonda adani athu

Ekisodo 23:5: “Ukaona bulu wa munthu wodana nawe atagona pansi polemedwa ndi katundu, pamenepo usam’siye yekha munthu wodana naweyo. Uthandizane naye kumasula katunduyo.”

Tanthauzo lake: Timasonyeza kuti timakonda mdani wathu pomuthandiza.

Miyambo 24:17, 18: “Mdani wako akagwa usamasangalale ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere, kuti Yehovab angaone ndipo zingamuipire.”

Tanthauzo lake: Mulungu safuna kuti tizisangalala adani athu akakumana ndi mavuto, ngakhale titachita zimenezi mosaonetsera.

Luka 6:28: ‘Dalitsani okutembererani ndi kupempherera amene akukunyozani.’

Tanthauzo lake: Muzilankhula mokoma mtima komanso mwaulemu ndi anthu amene amadana nanu kapena kukuchitirani zinthu zosakhala bwino, ndipo muzipempha Mulungu kuti awakhululukire.

1 Petulo 2:23: “Pamene [Yesu] anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.”

Tanthauzo lake: Yesu anasiya zonse m’manja mwa Mulungu kuti athane ndi zinthu zonse zopanda chilungamo.

1 Petulo 3:9: “Osabwezera choipa pa choipa kapena chipongwe pa chipongwe.”

Tanthauzo lake: M’malo mobwezera, muziyesetsa kuthetsa mikangano mwamtendere.

b Yehova ndi dzina lake lenileni la Mulungu. (Salmo 83:18) Werengani nkhani yakuti “Kodi Yehova ndi ndani?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena