Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 10/15 tsamba 5-7
  • Kodi Mtsogolo Mwanu Ndimolinganizidwa ndi choikidwiratu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mtsogolo Mwanu Ndimolinganizidwa ndi choikidwiratu?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zifuno za Mulungu Kaamba ka Mtsogolo
  • Kupeza Mtsogolo mwa Inumwini
  • Kusankha Moyo
  • Chilichonse Chili ndi Nthawi
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Baibulo Limaphunzitsa za Kukhulupirira Choikidwiratu?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kodi Mulungu Analemberatu Zomwe Zidzachitikire Munthu Aliyense?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi N’chikonzero cha Mulungu Kapena Zangochitika?
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 10/15 tsamba 5-7

Kodi Mtsogolo Mwanu Ndimolinganizidwa ndi choikidwiratu?

NGATI mukanapulumuka ngozi yakupha, kodi mukalingalira kuti munayanjidwa ndi choikidwiratu? Kapena kodi mmalomwake mukayamikira kuti munangokhala kumalo oyenera pa nthaŵi yoyenera?

Solomo mwamuna wanzeru anati: “Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m’liwiro, ngakhale olimba sapambana m’nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziŵitsa sawakomera mtima; [chifukwa chakuti nthaŵi ndi zobuka zamwadzidzidzi zimawafikira onse, NW]. (Mlaliki 9:11) Mmene zobuka balamanthu zimachitikira kaŵirikaŵiri! Katswiri wothamanga woyembekezeredwa kupambana avulazidwa, ndipo wosayeneretsedwa apambana. Ngozi yamwadzidzidzi imadzetsa kuwonongeka kwa ndalama pa mwini malonda wowona mtima, ikumalola wolimbana naye wosawona mtima kukhala wolemera. Koma kodi Solomo anagwirizanitsa zachilendo zosinthasintha zimenezi ndi choikidwiratu? Kutalitali. Izi ziri kokha zotulukapo za “nthaŵi ndi zobuka zamwadzidzidzi.”

Yesu Kristu ananena mofananamo. Akumaloza kuchochitika chimene mwachiwonekere chinali chodziŵika mofala pakati pa omvetsera ake, Yesu anafunsa kuti: “Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya m’Siloamu inawagwera ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala mu Yerusalemu?” (Luka 13:4) Yesu sanaike thayo langozi zakupha zimenezi pachoikidwiratu chosadziŵika kapena pachifuniro cha Mulungu, ndipo iye sanakhulupirire kuti mikholeyo inali mwinamwake yolakwa koposa ena. Ngozi yakuphayo inali kokha chitsanzo cha kugwira ntchito kwa nthaŵi ndi zobuka zamwadzidzidzi.

Palibe paliponse pamene Baibulo limachirikiza lingaliro lakuti Mulungu walinganiziratu nthaŵi yathu yakufa. Nzowona kuti Mlaliki 3:1, 2 amati: “Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake ndi chofuna chirichonse chapansi pa thambo chiri ndi mphindi yake; mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi zakudzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo.” Koma Solomo anali kungofotokoza zungulirezungulire womapitiriza wamoyo ndi imfa amene amakantha anthu opanda ungwiro. Timabadwa, ndipo pamene nthaŵi imafika, pamene utali wamoyo wachibadwa woyembekezeredwa ufikiridwa​—kaŵirikaŵiri pambuyo pa zaka 70 kapena 80 kapena chapompo​—timafa. Chikhalirechobe, mphindi yeniyeni yakufa sinalinganizidwiretu ndi Mulungu monga momwedi mphindi imene wolima munda amasankha “kubzala” kapena “kuzula zobzalazo” simalinganizidwiratu.

M’chenicheni, Solomo pambuyo pake amasonyeza kuti munthu angafe panthaŵi yamwamsanga akumati: “Usapambanitsa kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthaŵi yako isanafike?” (Mlaliki 7:17) Kodi uphungu umenewu ukapanga tanthauzo lotani ngati nthaŵi yakumwalira ya munthuyo inalinganizidwiratu mosasinthika? Chotero Baibulo limatsutsa lingaliro la choikidwiratu. Aisrayeli opatuka amene analandira chiphunzitso chachikunja chimenechi anatsutsidwa zolimba ndi Mulungu. Yesaya 65:11 amati: “Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mulungu wamwaŵi gome, ndi kudzazira mulungu [wa Choikidwiratu, NW] zikho za vinyo wosanganiza.”

Pamenepa, kuli kupusa chotani nanga, kukhulupirira kuti ngozi ndi masoka zimadzetsedwa ndi choikidwiratu kapena, zoipirapo, ndi Mulungu iye mwini! “Mulungu ndiye chikondi,” limatero Baibulo, ndipo kumzenga mlandu wakukhala magwero a nsautso za anthu kumatsutsana mwachindunji ndi chowonadi chachikulu chimenechi.​—1 Yohane 4:8.

Zifuno za Mulungu Kaamba ka Mtsogolo

Komabe, bwanji ponena za ziyembekezo zathu za chipulumutso? Kodi chenicheni chakuti palibe choikidwiratu chosapeweka chimene chimalamulira miyoyo yathu chimatanthauza kuti tiyenera kukhala ndi moyo osachita kalikonse? Kutalitali, popeza kuti Mulungu walinganiza mtsogolo mwa mtundu wonse wa anthu. Baibulo limanena za kulengedwa kwa “dziko latsopano” mmene “mukhalitsa chilungamo.”​—2 Petro 3:13.

Kuti akwaniritse zimenezi, Mulungu adzalowerera mwachindunji m’zochitika za anthu. Mosadziŵa, mungakhale munapempherera zimenezi kuchitika mwakubwereza pemphero limene limati: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Ufumu umenewu ndilo boma lenileni lokhazikitsidwa kumwamba. Mwakulipempherera kuti lidze, mukupempherera Ufumu umenewu kuti udzalande ulamuliro wadziko kuchokera ku maboma amakono.​—Danieli 2:44.

Kupeza Mtsogolo mwa Inumwini

Mmene zochitika zokondweretsa zimenezi zidzayambukirira mtsogolo mwanu kumadalira, osati pa choikidwiratu kapena ngakhale panthaŵi ndi zobuka zamwadzidzidzi, koma panjira imene musankha kuitsatira. Kumbukirani tsoka la pansanja ya Siloamu. Yesu anagwiritsira ntchito chochitika chomvetsa chisonicho kuphunzitsira phunziro lalikulu. Mikhole yakugwa kwa nsanjayo inali yosakhoza kuthaŵa zimene zinaigwera. Kumbali ina, omvetsera a Yesu angakhoze kupewa chiwonongeko chomwe chingatuluke mumkwiyo wa Mulungu. Yesu anawachenjeza kuti: “Koma ngati simutembenuka mtima, mudzawonongeka nonse chimodzimodzi.” (Luka 13:4, 5) Momvekera bwino, iwo akakhoza kusankha mtsogolo mwa iwo eni.

Mwaŵi umodzimodziwo waperekedwa kwa ife lerolino​—kugwirira ntchito chipulumutso chathu. (Afilipi 2:12) Mulungu afuna kuti “onse apulumuke, nafike pozindikira chowonadi.” (1 Timoteo 2:4) Ndipo ngakhale kuti aliyense wa ife amayambukiridwa kumlingo wakutiwakuti ndi cholowa ndi chiyambi, Mulungu watipatsa ufulu wakudzisankhira​—mphamvu yakusankha mmene tifuna kugwiritsirira ntchito moyo wathu. (Mateyu 7:13, 14) Tingachite chimene chiri cholondola kapena chimene chiri cholakwa. Tingapeze kaimidwe kabwino ndi Yehova Mulungu ndi kupeza moyo, kapena tingatsutsane naye ndi kufa.

Ambiri amasankha kukhala osadalira Mulungu. Iwo amathera miyoyo yawo akulondola zinthu zakuthupi, kusanguluka, kapena kutchuka. Koma Yesu anachenjeza kuti: “Yang’anirani, mudzisungire kupeŵa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) Pamenepa, kodi miyoyo yathu imadalira pachiyani? Pa 1 Yohane 2:15-17, Baibulo limalongosola kuti: “Musakonde dziko lapansi. . . . Chirichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe amoyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthaŵi yonse.”

Kusankha Moyo

Kodi mungakhale otsimikizira motani kuti mukuchitadi chifuniro cha Mulungu? Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe inu Mulungu wowona yekha ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Chidziŵitso cholongosoka chochokera m’Baibulo chimapereka maziko achikhulupiriro. “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndikuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.” (Ahebri 11:6) Chidziŵitso chimene mufunikira kuchipeza chirikodi. Mboni za Yehova zathandiza mamiliyoni kuchipeza kupyolera mwa phunziro lokhazikika Labaibulo.a

Kuti mukondweretse Mulungu, mudzafunikira kupanga masinthidwe. Pangakhale zizolowezi zina zoipa zimene ziyenera kulakidwa kapena ngakhale machitachita achisembwere amene ayenera kuthetsedwa. Koma musalephere, monga ngati kuti kuli kosatheka kwa inu kusintha. Lingaliro lakuti zinthu sizingasinthe nlotengedwa kuchokera ku chiphunzitso chonyenga cha choikidwiratu. Pokhala ndi chithandizo cha Yehova, kuli kotheka kwa aliyense ‘kusanduliza maganizo’ ndi kupeza ‘umunthu watsopano.’ (Aroma 12:2; Aefeso 4:22-24) Zoyesayesa zanu zakukondweretsa Mulungu sizidzakhala zosazindikiridwa. Iye ali wokonzekera kudalitsa awo amene amachita chifuniro chake.

Nzowonadi kuti, kuphunzira Baibulo sikudzathetsa mavuto anu onse. Atumiki owona a Mulungu akhoza kuyambukiridwa ndi ngozi ndi zochitika zoipa, mofanana ndi mmene ena amachitira. Komabe, Mulungu angatipatse nzeru yakuchita ndi tsoka. (Yakobo 1:5) Palinso chimwemwe chakudziŵa kuti munthuwe uli ndi unansi wabwino ndi Mulungu. “Wokhulupirira Yehova adala,” amatero Miyambo 16:20.

M’Paradaiso wobwezeretsedwanso ndi Ufumu wa Mulungu, sitidzawopsezedwanso konse ndi nthaŵi ndi zobuka zamwadzidzidzi. Ndithudi, Mulungu adzachotsa zinthu zonse zimene panthaŵi zino zimadodometsa chimwemwe cha anthu. “[Adzapukuta] misozi yonse kuichotsa pamaso [pathu]; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa,” limalonjeza motero Baibulo. (Chivumbulutso 21:4) Mikhole yangozi yosaŵerengeka idzaukitsidwa.​—Yohane 5:28, 29.

Kodi mudzakhalamo mtsogolo mowala m’menemomu? Pamene Aisrayeli anali pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawauza kuti: “Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, dalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo inu ndi mbewu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndikumamatira iye, pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka.”​—Deuteronomo 30:19, 20.

Ayi, sitiri akapolo osatetezereka m’manja mwa choikidwiratu chopanda chifundocho. Mtsogolo mwanu mwachimwemwe, ndithudi mtsogolo mwanu mosatha, muli m’manja mwanu. Tikufulumizani kusankha moyo.

[Mawu a M’munsi]

a Phunziro lotero lingalinganizidwe mwakulembera afalitsi a magazini ano.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Aisrayeli opatuka amene analandira chiphunzitso chachikunja cha choikidwiratu anatsutsidwa zolimba ndi Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena