Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 4/1 tsamba 28-31
  • Khalani Achimwemwe ndi Adongosolo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Achimwemwe ndi Adongosolo
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Adongosolo ndi Achimwemwe
  • Musadzichitire Nkhanza
  • Galu Wamoyo Kapena Mkango Wakufa?
  • Chitirani Moyo Wanu Zokoma
  • Chitirani Ena Zokoma
  • Kusamalira Munthu Aliyense Payekha
  • Khalani Pafupi ndi Gulu Lankhosa
  • Atumiki a Mulungu—Anthu Olinganizidwa ndi Achimwemwe
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Anthu Amene Amatumikira “Mulungu Wachimwemwe” Amakhala Osangalala
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Kuŵeta Gulu la Mulungu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Zimene Tingachite Kuti Tikhale Osangalala
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 4/1 tsamba 28-31

Khalani Achimwemwe ndi Adongosolo

KUKHALA wadongosolo kumatipangitsa kuchita zinthu bwino. Kuyendetsa zinthu bwino kumatithandiza kugwiritsira ntchito bwino lomwe nthaŵi ndi chuma. (Agalatiya 6:16; Afilipi 3:16; 1 Timoteo 3:2) Koma pali zambiri kumoyo kuposa kungokhala chabe wadongosolo ndi woyendetsa zinthu bwino. Wamasalmo wouziridwa analemba kuti: “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Salmo 144:15) Vuto lili pakukhala wachimwemwe ndi wadongosolo m’zonse zimene tichita.

Adongosolo ndi Achimwemwe

Yehova Mulungu ali chitsanzo chabwino koposa cha dongosolo labwino. Zolengedwa zake zonse, kuyambira pa selo limodzi kufikira ku zolengedwa zamoyo zocholoŵanacholoŵana, kuyambira pa maatomu aang’onong’ono kufikira ku makamu anyenyezi zazikulu, zimasonyeza dongosolo ndi kulinganiza kwabwino. Malamulo ake achilengedwe amatichititsa kulinganiza miyoyo yathu mwa chidaliro. Timadziŵa kuti dzuŵa limatuluka m’maŵa uliwonse ndi kuti chilimwe chimatsatira chisanu.​—Genesis 8:22; Yesaya 40:26.

Koma Yehova sali chabe Mulungu wadongosolo. Iye alinso “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW; 1 Akorinto 14:33) Chimwemwe chake chimawonekera m’zimene iye analenga. Ana a mphaka okonda kuseŵera, kuloŵa kwa dzuŵa kokongola, chakudya chokoma, nyimbo zogwira mtima, ntchito yotsitsimula, ndi zinthu zina zambirimbiri zimasonyeza kuti iye anafuna kuti tisangalale ndi moyo. Malamulo ake saali ziletso zolimba koma amatetezera chimwemwe chathu.

Yesu Kristu mwiniyo amatsanzira chitsanzo cha Atate wake. Iye ali “Mwinimphamvu wodala ndi wayekha” ndipo amachita mofanana ndi mmene Atate wake amachitira. (1 Timoteo 6:15; Yohane 5:19) Pamene anagwira ntchito zolimba limodzi ndi Atate wake m’ntchito yakulenga, iye anali woposa “mmisiri” waluso. Iye anakondwera ndi zimene anachita. Iye anali “kukondwera pamaso [pa Yehova] nthaŵi zonse; ndi kukondwera ndi dziko lake lokhalamo anthu, ndi kusekerera ndi ana a anthu.”​—Miyambo 8:30, 31.

Tifuna kusonyeza chifundo, chikondwerero, ndi chikondi chofananacho pa anthu m’zonse zimene tichita. Komabe, nthaŵi zina, poyesayesa kuchita mwaluso, tingaiŵale kuti “kuyenda mwadongosolo . . . mwa mzimu [wa Mulungu]” kumaphatikizapo kubala zipatso za mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22-25, NW) Chotero timachita bwino kufunsa kuti, Kodi ndimotani mmene tingakhalire adongosolo ndi achimwemwe ponse paŵiri m’ntchito yathu ndi potsogoza ntchito ya ena?

Musadzichitire Nkhanza

Talingalirani uphungu wabwino wolembedwa pa Miyambo 11:17. Choyamba wolemba wouziridwayo akutiuza kuti “wachifundo achitira moyo wake zokoma.” Ndiyeno mosiyana iye akuti: “Koma wankhanza avuta nyama yake.” New International Version imati: “Munthu wachifundo amadzipindulitsa, koma munthu wankhanza amadzivulaza.”

Kodi ndimotani mmene tingadzichitire nkhanza ife eni mosadziŵa? Njira imodzi ndiyo mwa kukhala ndi chifuno chabwino koma wopanda dongosolo konse. Kodi nchiyani chimatsatirapo? Katswiri wina akuti: “Kuiŵala, chikalata chosalembedwa bwino, malangizo osamvedwa bwino lomwe, mawu a patelefoni olembedwa mosalondola​—zimenezi ndizophophonya zazing’ono, zimene zimadodometsa kuyendetsedwa bwino kwa zinthu ndi kuwononga zolinga zabwino.”​—Teach Yourself Personal Efficiency.

Zimenezi zimagwirizana ndi zonena za wolemba wouziridwa amene anati: “Wogwira ntchito mwaulesi ndiye mbale wake wa wosakaza.” (Miyambo 18:9) Inde, anthu opanda dongosolo, osayendetsa zinthu bwino angadzetse tsoka ndi chiwonongeko pa iwo eni ndi ena. Chifukwa chake, ena kaŵirikaŵiri amawanyanyala. Chifukwa cha ulesi wawo, amadzichititsa kukhala onyalanyazidwa.

Galu Wamoyo Kapena Mkango Wakufa?

Koma tingadzichitirenso nkhanza mwa kudziikira miyezo yapamwamba koposa. Tingathe kukhala ndi chonulirapo, akutero wolemba za kuyendetsa zinthu bwino wotchulidwa pamwambapa, cha kufikira “njira yapamwamba koposa yochitira zinthu bwino kopambana yosafikirika.” Iye akuti chimene chimatsatira ndicho “kudziloŵetsa tokha mumkhalidwe wachisoni ndi kugwiritsidwa mwala.” Wofuna kuchita zinthu mosalakwitsa angakhale wadongosolo ndi woyendetsa zinthu bwino, koma iye sadzakhala wachimwemwe konse. Panthaŵi ina iye adzangokhala wachisoni basi.

Ngati tiumirira pakufuna kuchita zinthu bwino kopambana, tingachite bwino kukumbukira kuti, “galu wamoyo aposa mkango wakufa.” (Mlaliki 9:4) Ife kwenikweni sitingadziphe mwa kuyesayesa mosayenera kuchita zinthu bwino kopambana, koma tingadzivulaze kwambiri mwa kudzitopetsa. Zimenezi, akutero katswiri wina, zimaloŵetsamo “kutopa kwakuthupi, kwamaganizo, kwauzimu, kwaluntha, ndi kuwonongeka kwa maunansi.” (Job Stress and Burnout) Kudzitopetsa mwa kuyesayesa kufikira zonulirapo zosatheka kulidi kudzichitira nkhanza ife eni ndipo kumatilandadi chimwemwe.

Chitirani Moyo Wanu Zokoma

Kumbukirani kuti: “Wachifundo achitira moyo wake zokoma.” (Miyambo 11:17) Timadzichitira zokoma pamene tiika zonulirapo zabwino ndi zoyenera, tikumakumbukira kuti Yehova, Mulungu wachimwemwe, amadziŵa kupereŵera kwathu. (Salmo 103:8-14) Tingakhale achimwemwe ngati nafenso tizindikira kupereŵera kumeneko ndiyeno ‘kuchita changu,’ mogwirizana ndi mphamvu zathu, kuti tikwaniritse mathayo athu.​—Ahebri 4:11; 2 Timoteo 2:15; 2 Petro 1:10.

Ndithudi, nthaŵi zonse pamakhala ngozi yakuchita mopambanitsa​—kudzimvera chisoni mopambanitsa. Musaiŵale yankho la Yesu pa lingaliro la mtumwi Petro lakuti, “Dzichitireni chifundo, Ambuye,” pamene, kunena zowona, panafunikira kulimba mtima. Maganizo a Petro anali aupandu kwambiri kotero kuti Yesu anati: “Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.” (Mateyu 16:22, 23) Kuchitira moyo wathu zokoma sikumalola kuti tikhale ndi mkhalidwe wamaganizo wakusasamala, wakudzikondweretsa. Nawonso ungatiwonongere chimwemwe chathu chonse. Chimene timafunikira ndicho kukhala wachikatikati, osati wonkitsa.​—Afilipi 4:5.

Chitirani Ena Zokoma

Mwachiwonekere alembi ndi Afarisi m’tsiku la Yesu anaganiza kuti anali kuyendetsa zinthu bwino ndi kuti anali adongosolo kwambiri. Ponena za njira yawo yakulambira, A Dictionary of the Bible imati: “Lamulo la Baibulo limodzi ndi limodzi linazingidwa ndi timalamulo tating’ono tambirimbiri. Panalibe mpata wololera mikhalidwe yomasinthasintha; kumvera kotheratu Lamulo m’mbali zake zonse kunali kofunika zivute zitani kwa Myuda aliyense . . . Tsatanetsatane wa malamulo anachuluka kwambiri kotero kuti chipembedzo chinakhala mwambo, ndipo moyo unakhala mtolo wosapiririka. Anthu anakhala ngati makina ongouzidwa chochita ponena za chikhalidwe chabwino. Chikumbumtima chinasiya kuwalamulira; mphamvu yogwira ntchito ya mawu a Mulungu inatsukuluzidwa ndi kuphimbidwa ndi malamulo ambirimbiri.”

Nkosadabwitsa kuti Yesu Kristu anawatsutsira zimenezi. “Amanga akatundu olemera,” iye anatero, “ndi osautsa ponyamula, nawasenza pamapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo.” (Mateyu 23:4) Akulu achikondi amapeŵa kuika katundu wolemera pa gulu lankhosa ndi kuchulukitsa timalamulo ndi timalangizo. Iwo amachitira zokoma gulu la Mulungu mwa kutsatira chitsanzo chakukoma mtima, chotsitsimula cha Kristu Yesu.​—Mateyu 11:28-30; Afilipi 2:1-5.

Ngakhale pamene mathayo a kuyang’anira gulu awonjezereka, akulu amene amasamala sadzaiŵala mfundo yakuti iwo akuchita ndi anthu​—anthu amene Mulungu akonda. (1 Petro 5:2, 3, 7; 1 Yohane 4:8-10) Iwo sadzakhala konse otanganitsidwa kwambiri ndi nkhani za gulu kapena njira zochitira zinthu kotero kuti nkuiŵala ntchito yawo yaikulu monga abusa, oyang’anira, ndi otetezera gulu lankhosa.​—Miyambo 3:3; 19:22; 21:21; Yesaya 32:1, 2; Yeremiya 23:3, 4.

Mwachitsanzo, kusamala mopambanitsa za programu ndi ziŵerengero kungaphimbe chisamaliro chake kwa anthu. Talingalirani woyendetsa basi amene amaganiza kuti ntchito yake yaikulu ndiyo kumamatira mosamalitsa ku programu yake zivute zitani. Iye amatengeka maganizo ndi chikhumbo cha kutha mtunda wonse wa ulendo wake panthaŵi yeniyeni yoperekedwa. Mwachisoni, malinga ndi kuganiza kwake, apaulendo amamdodometsa. Iwo amachedwa, alibe dongosolo, ndipo nthaŵi zonse amafika pa sitesheni ya basi pamene iye akuchoka. Mmalo mwa kukumbukira kuti cholinga chenicheni cha ntchito yake ndicho kutumikira zosoŵa za apaulendo ake, iye amawawona monga chopinga cha kuyendetsa zinthu bwino ndipo amawapeŵa.

Kusamalira Munthu Aliyense Payekha

Kaŵirikaŵiri kuyendetsa galimoto kosalingalira ena chifukwa chofuna kuchita zinthu bwino kumanyalanyaza zosoŵa za munthu aliyense payekha. Anthu ofookerapo, osachita zinthu bwino angawonedwe kukhala olepheretsa zinthu. Zimenezi zitachitika, pamakhala zotsatirapo zowopsa. Mwachitsanzo, mu likulu la Girisi wakale la Sparta, ana ofooka ndi odwala anali kusiidwa kuti afe. Iwo sakanakhala asirikali amphamvu, okhoza kutetezera boma loyendetsa zinthu bwino ndi lamphamvu limenelo. “Pamene mwana anabadwa,” akutero katswiri wa nthanthi Bertrand Russell, “atate anampereka kwa akulu a banja lake kuti apendedwe: ngati mwanayo anali wathanzi labwino, anali kubwezeredwa kwa atate wake kuti akamlele; ngati sanali wotero, anali kuponyedwa m’dzenje lakuya lamadzi.”​—History of Western Philosophy.

Liuma ndi malamulo olimba, osati chimwemwe, ndizo zinali m’boma lankhalwe limenelo. (Yerekezerani ndi Mlaliki 8:9.) Mosakaikira akuluakulu a Sparta analingalira kuti anali kuchita bwino pa maziko akufuna kuyendetsa zinthu bwino, koma khalidwe lawo silinali lokoma mtima konse kapena lachifundo. Njira yawo siinali njira ya Mulungu. (Salmo 41:1; Miyambo 14:21) Mosiyana, oyang’anira mpingo Wachikristu amakumbukira kuti nkhosa zonse za Mulungu nza mtengo wapatali m’maso mwake, ndipo amachitira zokoma imodzi ndi imodzi ya izo. Iwo samangosamalira chabe 99 zimene ziri zathanzi labwino komanso imodzi yofooka kapena yopsinjika mtima.​—Mateyu 18:12-14; Machitidwe 20:28; 1 Atesalonika 5:14, 15; 1 Petro 5:7.

Khalani Pafupi ndi Gulu Lankhosa

Akulu amakhala pafupi ndi gulu lankhosa limene akulisamalira. Komabe, kufufuza kwamakono njira zogwirira ntchito, kungapereke lingaliro lakuti manijala kapena woyang’anira ayenera kukhala patali ndi awo amene akuwayang’anira kuti zinthu ziyende mwataŵataŵa. Wofufuza wina akulongosola zotsatirapo zosiyana zimene zinachitikira mkulu wa ankhondo ya m’mlengalenga pamene iye anali pafupi kapena patali ndi antchito ake: “Pamene anayanjana mwathithithi ndi asirikali [ake], iwo anawoneka kukhala otetezereka ndipo sanadere nkhaŵa kwambiri za kugwira bwino ntchito kwa timagulu tawo. Atangosiya kulankhula nawo kaŵirikaŵiri ndi kumamatira ku ntchito, akazembe ogwira ntchito pansi pake anayamba kudera nkhaŵa kuti kanthu kena kanalakwika . . . ndipo nkhaŵa zawo zinawachititsa kusumika maganizo awo pa ntchito yawo. Chotero, panakhala kupita patsogolo kowonekeratu m’kayendetsedwe ka zinthu pa msasawo.”​—Understanding Organizations.

Komabe, mpingo Wachikristu suli gulu lankhondo. Akulu Achikristu amene amayang’anira ntchito ya ena amatsatira chitsanzo cha Yesu Kristu. Iye nthaŵi zonse anali pafupi ndi ophunzira ake. (Mateyu 12:49, 50, Yohane 13:34, 35) Iye sanagwiritsirepo ntchito nkhaŵa zawo kuti achititse zinthu kuyenda bwino. Iye anamanga unansi wolimba wakudalirana ndi kukhulupirirana pakati pa iyemwini ndi otsatira ake. Unansi wolimba wokoma mtima unasonyezedwa ndi ophunzira ake. (1 Atesalonika 2:7, 8) Pamene pali mgwirizano wotero, gulu lankhosa lachimwemwe, losonkhezeredwa kwambiri ndi chikondi pa Mulungu, lidzalabadira malangizo mosakakamizika ndipo lidzachita changu muutumiki wake mofunitsitsa.​—Yerekezerani ndi Eksodo 35:21.

Malemba ambiri amagogomezera mikhalidwe Yachikristu yonga chimwemwe ndi chikondi yofunika pa ubale. (Mateyu 5:3-12; 1 Akorinto 13:1-13) Ngoŵerengeka chabe amene amagogomezera kufunika kwa kuchita zinthu mwataŵataŵa. Kunena zowona, dongosolo labwino nlofunika. Anthu a Mulungu nthaŵi zonse akhala adongosolo. Mwachitsanzo, talingalirani kuchuluka kwa nthaŵi imene olemba masalmo amafotokozera atumiki a Mulungu kukhala odala. Salmo 119, limene limanena zambiri ponena za malamulo a Yehova, zikumbutso, ndi maŵeruzo, limayamba mwakumati: “Odala angwiro m’mayendedwe awo, akuyenda m’chilamulo cha Yehova. Odala iwo akusunga mboni zake, akumfuna ndi mtima wonse.” (Salmo 119:1, 2) Kodi mungathe kukwaniritsa ziŵiri zonsezo kukhala wadongosolo ndi wachimwemwe?

[Chithunzi patsamba 28]

“Armillary sphere”​—chipangizo choyambirira chosonyeza mikombero yaikulu ya kumwamba

[Chithunzi patsamba 31]

Yehova, monga Mbusa wachikondi, ali Mulungu osati wadongosolo chabe komanso wachimwemwe

[Mawu a Chithunzi]

Garo Nalbandian

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena