Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp21 No. 3 tsamba 6-8
  • Kodi Maphunziro Ndi Ndalama Zingatithandize Kukhala Ndi Tsogolo Labwino?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Maphunziro Ndi Ndalama Zingatithandize Kukhala Ndi Tsogolo Labwino?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE ANTHU AMBIRI AMASANKHA
  • KODI ZOTSATIRA ZAKE ZIMAKHALA ZOTANI?
  • Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani ya Maphunziro?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Makolo—kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kufunafuna Moyo Wotetezereka
    Galamukani!—1998
  • Aliyense Amafuna Kukhala Ndi Tsogolo Labwino
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
wp21 No. 3 tsamba 6-8
Atsikana awiri akuyunivesite akukalowa m’kalasi.

Kodi Maphunziro Ndi Ndalama Zingatithandize Kukhala Ndi Tsogolo Labwino?

Anthu ambiri amaganiza kuti anthu ophunzira kwambiri komanso olemera ndi amene ali ndi tsogolo labwino. Iwo amakhulupirira kuti maphunziro akuyunivesite angawathandize kukhala munthu wabwino kuntchito, m’banja, m’dera lawo komanso m’dziko lawo. Iwo amaona kuti maphunziro oterewa angathandize munthu kuti apeze ntchito yabwino yoti azilandira ndalama zambiri n’kumakhala wosangalala.

ZIMENE ANTHU AMBIRI AMASANKHA

Taganizirani zimene ananena Zhang Chen, yemwe amakhala ku China. Iye anati: “Ndinkakhulupirira kuti ndikufunikira kukhala ndi digirii kuti ndisakhale wosauka komanso kuti ndipeze ntchito yandalama zambiri zomwe zingandithandize kukhala ndi moyo wosangalala komanso wabwino kwambiri.”

Pofuna kukhala ndi tsogolo labwino, ambiri amayesetsa kupita kumayunivesite otchuka, mwinanso kumayiko ena. Anthu ambiri akhala akuchita zimenezi mpaka pamene mliri wa COVID-19 unachititsa kuti anthu asamapite kwambiri m’mayiko ena. Lipoti la mu 2012 la bungwe lina loona za chuma ndi chitukuko, linanena kuti: “52 peresenti ya ophunzira ochokera kumayiko ena inali ya anthu a ku Asia.”

Nthawi zambiri, makolo ena amalolera kudzimana zinthu zambiri n’cholinga choti atumize ana awo kumayunivesite am’mayiko ena. Qixiang, wa ku Taiwan, anati: “Ngakhale kuti makolo anga ndi osauka, anakwanitsa kutumiza ana tonse 4 ku United States kuti tikachite maphunziro akukoleji.” Kuti akwanitse kulipira maphunziro amenewa, makolo ake ankafunika kutenga ngongole ngati mmene makolo ambiri amachitira.

KODI ZOTSATIRA ZAKE ZIMAKHALA ZOTANI?

Mmodzi mwa atsikana aja ali pakompyuta usiku ndipo akuoneka wotopa komanso wokhumudwa.

Anthu ambiri omwe amafunafuna maphunziro akuyunivesite komanso chuma amakhumudwa pamapeto pake

Maphunziro amathandiza anthu m’njira zina. Koma si nthawi zonse pamene ana asukulu amapeza zomwe ankayembekezera. Mwachitsanzo, pambuyo pogwira ntchito mwakhama kwa zaka zambiri komanso kubwereka ndalama zolipirira sukulu, anthu ambiri sapeza ntchito yomwe ankafuna. Lipoti la nyuzipepala ina ya ku Singapore, lomwe analemba Rachel Mui, linati: “Zikuoneka kuti anthu ambiri amene anamaliza maphunziro akuyunivesite sakupeza ntchito.” (Business Times) Jianjie, wa ku Taiwan yemwe ndi wophunzira kwambiri, anati: “Anthu ambiri amakakamizika kugwira ntchito yosagwirizana ndi maphunziro awo.”

Anthu omwe apeza ntchito yogwirizana ndi maphunziro awo amaona kuti zomwe zikuchitika pa moyo wawo si zomwe ankayembekezera. Niran wa ku Thailand, yemwe anakachita maphunziro akuyunivesite ku United Kingdom, anapeza ntchito yogwirizana ndi maphunziro ake. Iye anati: “Digirii inandithandiza kupeza ntchito ya ndalama zambiri monga mmene ndinkayembekezera. Komabe, kuti ndizilandira ndalama zambiri ndinkafunika kugwira ntchito mwakhama kwambiri komanso kwa maola ambiri. Koma kenako kampaniyo inachotsa ntchito anthu ambiri, kuphatikizapo ineyo. Apatu ndinazindikira kuti palibe ntchito iliyonse yomwe ingathandize munthu kukhala ndi tsogolo labwino.”

Ngakhale anthu omwe ndi olemera kapena amaoneka ngati zikuwayendera, amakumana ndi mavuto am’banja, matenda komanso amangokhalira kudandaula zokhudza ndalama. Katsutoshi, wa ku Japan, anati: “Ngakhale kuti ndinali ndi ndalama zambiri, sindinkakhala mosangalala chifukwa anthu ankachita zinthu mopikisana nane, kundichitira nsanje ndi zinthu zina zoipa.” Mayi wina dzina lake Lam, yemwe amakhala ku Vietnam, anati: “Ndaonapo anthu ambiri akufunafuna ntchito yandalama zambiri n’cholinga choti akhale ndi tsogolo labwino, koma zoona zake n’zakuti sapeza zomwe amafunazo. M’malomwake amangokhalira kuda nkhawa, kudwala komanso kuvutika maganizo.”

N’CHIFUKWA CHIYANI SITIYENERA KUDALIRA MAPHUNZIRO NDI NDALAMA KUTI TIKHALE NDI TSOGOLO LABWINO?

N’zoona kuti anthu amafunika kupita kusukulu komanso kupeza ndalama kuti azipeza zinthu zofunikira pa moyo wawo komanso kuthandiza banja lawo. Ngakhale zili choncho, zinthu zimenezi si zokwanira kuti munthu akhale ndi tsogolo labwino. N’chifukwa chiyani tikutero? Tiyeni tione zimene Malemba Opatulika amanena.

KUDALIRA MAPHUNZIRO AKUYUNIVESITE SIKUNGATITHANDIZE KUKHALA NDI TSOGOLO LABWINO.

“Anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano, . . . omvetsa zinthu nawonso sapeza chuma, ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa, chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.”—MLALIKI 9:11.

Anthu omwe amaoneka kuti ndi ophunzira kwambiri, nthawi zambiri zinthu sizimawayendera bwino pa moyo wawo chifukwa amakumana ndi mavuto omwe sangathe kuwapewa. Zinthu monga kusayenda bwino kwa chuma, kupanda chilungamo komanso tsankho, zingachititse kuti anthu omwe ndi ophunzira kwambiri alephere kuchita zinthu zimene ankalakalaka.

CHUMA NDI MCHIRA WA KHOSWE.

“Usamadzitopetse ndi ntchito kuti upeze chuma. Leka kudzidalira kuti ndiwe womvetsa zinthu. Kodi maso ako amayang’anitsitsa chuma, pomwe icho sichichedwa kuchoka? Chifukwa ndithu chimadzipangira mapiko ngati a chiwombankhanga n’kuulukira kumwamba.”—MIYAMBO 23:4, 5.

Ngakhale kuti ndalama zimathandiza m’njira zambiri, zili ngati mchira wa khoswe. Zinthu zikhoza kusintha pa nkhani ya zachuma padzikoli ndipo mwadzidzidzi, ndalama zomwe munthu wakhala akusunga kwa nthawi yaitali zingakhale zopanda ntchito. Ngozi zam’chilengedwe monga zivomerezi, moto wolusa ndi mphepo zamkuntho zingachititse kuti anthu akhale opanda ndalama komanso asowe pokhala.

NTHAWI ZAMBIRI NDALAMA ZIMABWERETSA MAVUTO.

“Zambiri zimene munthu wolemera amakhala nazo zimamulepheretsa kugona.”​—MLALIKI 5:12.

Franklin, yemwe amakhala ku Hong Kong, anatsimikiza kuti mfundo yamulembali ndi yoona. Iye anapeza ntchito yandalama zambiri pambuyo pomaliza maphunziro akuyunivesite. Kenako anakwezedwa n’kukhala bwana. Iye anati: “Ndinayamba kukhala ndi nkhawa ndipo zimenezi zinakhudza thanzi langa. Ndinkangokhalira kudandaula moti ndinkasowa tulo.” Kenako pamapeto pake anangosiya ntchitoyo. Franklin ananenanso kuti: “Ndinayamba kudzifunsa kuti, N’chifukwa chiyani ndinkachita zimenezi? Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kuganizira kwambiri za cholinga cha moyo.”

“Usamadzitopetse ndi ntchito kuti upeze chuma.”​—MIYAMBO 23:4

Mofanana ndi Franklin, anthu ambiri aona kuti pali zinthu zambiri zofunika zomwe munthu angachite pa moyo kuposa maphunziro akuyunivesite kapena kufunafuna chuma. M’malo momangofunafuna chuma, anthu ena aona kuti akhoza kukhala ndi tsogolo labwino pokhala munthu wabwino komanso kuchitira ena zabwino. Koma kodi kuchita zimenezi kungathandizedi kuti munthu akhale ndi tsogolo labwino? Nkhani yotsatira iyankha funso limeneli.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena