Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 January tsamba 14-15
  • February 26–March 3

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • February 26–March 3
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 January tsamba 14-15

FEBRUARY 26–MARCH 3

SALIMO 11-15

Nyimbo Na. 139 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Muziyerekezera Muli M’dziko Latsopano Lamtendere

(10 min.)

Padzikoli pakuchitika zachiwawa chifukwa choti anthu sakumvera malamulo (Sl 11:2, 3; w06 5/15 18 ¶2)

Timakhulupirira kuti Yehova athetsa zachiwawa zonse posachedwapa (Sl 11:5; wp16.4 11)

Kuganizira lonjezo la Yehova loti adzatipulumutsa, kungatithandize kuti tiziyembekezera moleza mtima dziko latsopano (Sl 13:5, 6; w17.08 7 ¶15)

Usiku mtsikana wagona mwamtendere pansi pa mtengo m’nkhalango. Kambuku wagona mumtengo.

YESANI IZI: Werengani Ezekieli 34:25, ndipo kwa kanthawi, dziyerekezereni muli m’dziko lamtendere lomwe latchulidwali.—kr 236 ¶16.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 14:1—Kodi kaganizidwe kamene kali palembali kangakhudze bwanji Akhristu? (w13 9/15 19 ¶12)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 13:1–14:7 (th phunziro 2)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Muitanireni ku Chikumbutso. (lmd phunziro 5 mfundo 3)

5. Ulendo Woyamba

(1 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Muitanireni ku Chikumbutso. (lmd phunziro 3 mfundo 4)

6. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthu wasonyeza chidwi mutamuitanira ku Chikumbutso. (lmd phunziro 7 mfundo 4)

7. Kuphunzitsa Anthu

(5 min.) lff phunziro 13 zomwe taphunzira, kubwereza komanso zolinga. Gwiritsani ntchito nkhani imene ili pa gawo lakuti “Onani Zinanso” kuti muthandize wophunzirayo kumvetsa mmene Mulungu amaonera zipembedzo zabodza. (th phunziro 12)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 8

8. “Nzeru N’zabwino Kuposa Zida Zankhondo”

(10 min.) Nkhani yokambirana

Bambo wa muvidiyo yakuti “Muzitsanzira Anthu a Chikhulupiriro, Osati Opanda Chikhulupiriro​—⁠Inoki, Osati Lameki,” akuganizira zomwe wawerenga m’Baibulo. Akuganizira Inoki atabisala kuphanga pamene anthu onyamula zida akumusakasaka.

Zachiwawa zikuchulukirachulukira padzikoli. Yehova amadziwa kuti zachiwawa zomwe zimatichitikira kapena zomwe timaona, zimatipangitsa kukhala ndi nkhawa. Amadziwanso kuti timafunikira kutetezedwa. Njira imodzi imene amagwiritsa ntchito potiteteza ndi Mawu ake Baibulo.—Sl 12:5-7.

M’Baibulo muli nzeru zimene “n’zabwino kuposa zida zankhondo.” (Mla 9:18) Ganizirani mmene mfundo za m’Baibulo zotsatirazi zingakutetezereni kuti anthu asamakuchitireni zachiwawa.

  • Mla 4:9, 10—Muzipewa kukhala nokhanokha pamalo oopsa

  • Miy 22:3—Muzikhala tcheru ndi zimene zikuchitika pamalo amene muli

  • Miy 26:17—Musamalowerere nkhani za eni

  • Miy 17:14—Muzichoka pamalo amene muli ngati pakuoneka kuti pakhoza kuyambika zachiwawa. Musamayandikire anthu amene akufuna kuchita ziwonetsero

  • Lu 12:15—Musamaike moyo wanu pachiswe pofuna kuteteza zinthu zanu

Onerani VIDIYO yakuti Muzitsanzira Anthu a Chikhulupiriro, Osati Opanda Chikhulupiriro—Inoki, Osati Lameki. Kenako funsani funso lotsatirali:

Kodi chitsanzo cha Inoki chinathandiza bwanji bamboyu kuti asankhe komanso kuchita zinthu mwanzeru pamene kunkachitika zachiwawa?—Ahe 11:5

Nthawi zina Mkhristu angaone kuti akufunika kuchita zinazake kuti adziteteze kapena ateteze zinthu zake. Ngati ndi choncho, akhoza kuchita chilichonse chomwe angathe, bola asaphe munthu n’kukhala ndi mlandu wamagazi.—Sl 51:14; onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya July 2017.

9. Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba Loweruka pa 2 March

(5 min.) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Fotokozani zimene mpingo wanu wakonza zokhudza kugwira ntchitoyi, kudzamvetsera nkhani yapadera komanso mwambo wa Chikumbutso. Kumbutsani ofalitsa kuti akhoza kuchita upainiya wothandiza wa maola 15 m’mwezi wa March ndi April.

10. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 6 ¶9-17

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 40 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena