Moyo Pambuyo pa Imfa—Motani, Kuti, Liti?
MLENGI wa munthu ndi Mpatsi wa Moyo amapereka chitsimikizo chake chakuti imfa ya munthu simathetsa kwenikweni moyo kosatha. Ndiponso, Mulungu amatitsimikizira kuti nkotheka kukhalanso ndi moyo osati chabe kwa nyengo yaifupi koma kukhala ndi moyo ndi chiyembekezo cha kusadzafanso! Mtumwi Paulo ananena mosavuta, komanso mwachidaliro kuti: ‘[Mulungu a]napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa iye [Kristu Yesu] kwa akufa.’—Machitidwe 17:31.
Zoonadi, zimenezi zimasiyabe mafunso atatu aakulu ali osayankhidwa: Kodi munthu wakufa angakhalenso wamoyo motani? Kodi zimenezi zidzachitika liti? Kodi nkuti kumene kudzakhala moyo watsopano umenewo? Kuzungulira dziko lonse, anthu apereka mayankho osiyanasiyana pa mafunso ameneŵa, komano mfungulo yofunika pa kudziŵa choonadi cha nkhaniyi ndiyo kumvetsetsa zimene zimachitika kwa anthu pa nthaŵi ya imfa yawo.
Kodi Kusafa Ndiko Yankho?
Chikhulupiriro cha ambiri nchakuti mbali ina ya munthu aliyense siimafa ndi kuti thupi lake lokha ndilo limafa. Inu ndithudi mwamva mawu amenewo. Mbali imeneyi imene imanenedwa kuti njosafa imatchedwa mosiyanasiyana kukhala “sou” kapena “mzimu.” Amati imasiyana ndi thupi pa imfa yake ndi kupitiriza kukhala ndi moyo kumalo ena. Kunena mosabisa mawu, chikhulupiriro chimenecho sichili cha m’Baibulo. Zoonadi, anthu akale achihebri a m’Baibulo anayembekezera moyo wa pambuyo pa imfa, komano osati mwa kupulumuka kwa mbali yawo ina yosafa. Iwo mwachidaliro anayembekezera kukhalanso ndi moyo mtsogolo padziko lapansi kupyolera mwa chozizwitsa cha chiukiriro.
Khololo Abrahamu ndilo chitsanzo chapadera cha munthu amene anali ndi chikhulupiriro chakuti kudzakhala chiukiriro cha akufa mtsogolo. Polongosola za kufunitsitsa kwa Abrahamu kupereka nsembe mwana wake Isake, Ahebri 11:17-19 amatiuza kuti: “Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake, . . . poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anamlandiranso,” popeza kuti Mulungu sanafune kuti Isake aperekedwe nsembe. Poperekanso umboni wina wa chikhulupiriro choyambirira cha Aisrayeli chakuti adzakhalanso ndi moyo mtsogolo (mosiyana ndi moyo womapitiriza kukhalako m’malo a mizimu), mneneri Hoseya analemba kuti: “Ndidzawaombola ku mphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa.”—Hoseya 13:14.
Chotero kodi ndi liti pamene lingaliro lakuti munthu mwachibadwa samafa linaloŵa m’maganizo ndi m’chikhulupiriro chachiyuda? Encyclopaedia Judaica ikuvomereza kuti “mwinamwake chiphunzitso cha kusafa kwa sou chinaloŵa m’Chiyuda chifukwa cha chisonkhezero cha Agiriki.” Chikhalirechobe, Ayuda odzipereka kufikira pa nthaŵi ya Kristu anakhulupirirabe ndi kuyembekezera chiukiriro chamtsogolo. Tingathe kuona zimenezi bwino lomwe m’makambitsirano a Yesu ndi Marita pa imfa ya mlongo wake Lazaro: “Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa. . . . Yesu ananena naye, Mlongo wako adzauka. Marita ananena ndi iye, Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.”—Yohane 11:21-24.
Mkhalidwe wa Akufa
Panonso, sitifunikira kungolotera za nkhaniyo. Choonadi chosavuta cha Baibulo nchakuti akufa “ali m’tulo,” osadziŵa kanthu, osakhoza konse kumva kanthu kapena kulingalira. Choonadi chimenecho sichinafotokozedwe mocholoŵana, ndi movuta kuchimvetsa m’Baibulo. Lingalirani malemba awa osavuta kumvetsa: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi . . . Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” (Mlaliki 9:5, 10) “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”—Salmo 146:3, 4.
Pamenepa, nkomveka kuti Yesu Kristu anatcha imfa kukhala tulo. Mtumwi Yohane analemba makambitsirano ochitika pakati pa Yesu ndi ophunzira ake kuti: “Ananena nawo, Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take. Chifukwa chake akuphunzira ake anati kwa iye, Ambuye, ngati ali m’tulo adzachira. Koma Yesu adanena za imfa yake; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo. Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira.”—Yohane 11:11-14.
Munthu Yense Amafa
Kuchitika kwa imfa ya munthu kumaloŵetsamo munthu yense, osati imfa ya thupi lokha. Malinga ndi mawu achimvekere a Baibulo, tiyenera kunena kuti munthu alibe sou yosafa imene imapulumuka imfa ya thupi. Malemba amasonyeza mwachionekere kuti sou ingathe kufa. “Taonani! Sou zonse—nzanga. Monga sou ya atate momwemonso sou ya mwana—ndi zanga. Sou imene ichimwa—imeneyo ndiyo idzafa.” (Ezekieli 18:4, NW) Palibe paliponse pamene mawu akuti “chosafa” kapena “kusafa” amanenedwa kukhala chibadwa cha anthu.
New Catholic Encyclopedia ikupereka umboni uwu wa mawu achihebri ndi achigiriki otembenuzidwa kuti “sou” m’Baibulo: “Sou mu OT [Chipangano Chakale] ndiyo nepeš, mu NT [Chipangano Chatsopano] [psy·kheʹ]. . . . Nepeš yachokera pa phata la mawuwo mwinamwake otanthauza kupuma, ndipo chotero . . . popeza kuti mpweya umasiyanitsa amoyo ndi akufa, nepeš inadzatanthauza moyo kapena mwini kapena moyo pawokha. . . . Palibe dichotomy [kugaŵa kukhala mbali ziŵiri] ya thupi ndi sou mu OT. Mwisrayeli anaona zinthu monga momwe zinalili, mu umphumphu wake, ndipo chotero anaona anthu monga momwe alili ndipo osati opangidwa ndi mbali ziŵiri. Liwu lakuti nepeš, ngakhale kuti limatembenuzidwa m’mawu athu akuti sou, silimatanthauza konse kuti sou njosiyana ndi thupi kapena ndi munthu mwini. . . . Liwulo [psy·kheʹ] ndilo liwu la mu NT lolingana ndi nepeš. Lingatanthauze magwero a moyo, moyo weniweniwo, kapena munthu wamoyo.”
Chotero mungathe kuona kuti pa nthaŵi ya imfa, munthu amene anali wamoyo, kapena sou yamoyo, amaleka kukhalako. Thupi limabwerera ku “fumbi” kapena ku zinthu za m’nthaka mwa kuliika m’manda ndiyeno likumaola pang’onopang’ono kapena kufulumiza zimenezo mwa kutentha mtembo. Yehova anauza Adamu kuti: “Chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Nangano, kodi moyo wa pambuyo pa imfa ngwotheka motani? Chili chifukwa chakuti Mulungu amakumbukira munthu amene anafa. Yehova ali ndi mphamvu zozizwitsa ndi luso la kulenga anthu, chotero siziyenera kutidabwitsa kuti iyeyo m’maganizo mwake angathe kusunga mbiri ya moyo wa munthu. Inde, ziyembekezo zonse za munthuyo za kukhala wamoyo kachiŵirinso zimakhala kwa Mulungu.
Limeneli ndilo tanthauzo la liwulo “mzimu,” umene umanenedwa kukhala ukubwerera kwa Mulungu woona amene anaupereka. Pofotokoza chochitika chimenechi, mlembi wouziridwa wa buku la Mlaliki akulongosola kuti: “Fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.”—Mlaliki 12:7.
Mulungu yekha ndiye amene angapangitse munthu wina kukhala ndi moyo. Pamene Mulungu analenga munthu mu Edene nauzira “mpweya wa moyo” m’mphuno mwake, kuwonjezera pa kudzaza mpweya m’mapapu mwa Adamu, Yehova anachititsa mphamvu ya moyo kupereka nyonga ku maselo onse m’thupi lake. (Genesis 2:7) Chifukwa chakuti mphamvu ya moyo imeneyi ingaperekedwe ndi makolo kwa ana kupyolera mwa kukhala ndi pakati ndi kubala, moyo wa munthu unganenedwe moyenera kuti ngwochokera kwa Mulungu, ngakhaledi kuti umalandiridwa kudzera mwa makolo.
Chiukiriro—Nthaŵi Yachimwemwe
Chiukiriro sichiyenera kusokonezedwa ndi kubadwanso kwa sou, kumene sikumachirikizidwa ndi Malemba Opatulika. Kubadwanso kwa sou ndiko chikhulupiriro chakuti munthu atafa, amabadwanso kachiŵiri kapena kambirimbiri. Amanena kuti kumeneko kumakhala kwa moyo wapamwamba kapena wotsika poyerekezera ndi moyo wapapitapo wa munthuyo, zikumadalira pa mbiri imene anali kupanga m’moyo wake wapapitawo. Malinga ndi chikhulupirirochi, munthu ‘angabadwenso’ monga munthu kapena monga nyama. Zimenezo nzowombana kwambiri ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.
Liwulo “chiukiriro” latembenuzidwa kuchokera ku liwu lachigiriki a·naʹsta·sis, limene kwenikweni limatanthauza “kuimirira kachiŵiri.” (Otembenuza Chigiriki m’Chihebri atembenuza liwulo a·naʹsta·sis ndi mawu achihebri akuti techi·yathʹ ham·me·thimʹ, kutanthauza “kutsitsimuka kwa akufa.”) Chiukiriro chimaloŵetsamo kuyambitsanso moyo wa munthu wina, moyo umene Mulungu wausunga m’maganizo mwake. Malinga ndi chifuniro cha Mulungu kwa munthuyo, iyeyo amabwezeretsedwa m’thupi laumunthu kapena m’thupi lauzimu; komabe amakhala wozindikirika, akumakhala ndi umunthu umodzimodziwo ndi maganizo amene anali nawo pakufa.
Inde, Baibulo limalankhula za mitundu iŵiri ya chiukiriro. Umodzi ndiwo chiukiriro cha kumwamba m’thupi lauzimu; chimenechi ndi cha oŵerengeka. Yesu Kristu analandira chiukiriro chimenecho. (1 Petro 3:18) Ndipo anasonyeza kuti chimenecho chidzachitika kwa osankhidwa pakati pa otsatira mapazi ake, kuyambira pa atumwi okhulupirika, amene anawalonjeza kuti: “Ndipita kukukonzerani inu malo. . . . Ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa ine ndekha; kuti kumene kuli ineko, mukakhale inunso.” (Yohane 14:2, 3) Baibulo limatchula zimenezi kukhala “kuuka koyamba,” koyamba malinga ndi nthaŵi ndi malo. Malemba amafotokoza awo oukitsidwira motero kumoyo wakumwamba kukhala ansembe a Mulungu ndi olamulira monga mafumu ndi Kristu Yesu. (Chivumbulutso 20:6) “Kuuka koyamba” kumeneku nkwachiŵerengero chaching’ono, ndipo Malemba enieniwo amavumbula kuti anthu 144,000 okha ndiwo adzatengedwa pakati pa amuna ndi akazi okhulupirika. Adzakhala atasonyeza umphumphu wawo kwa Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu kufikira pa imfa yawo, pokhala anali okangalika pa kuchitira umboni kwa ena za chikhulupiriro chawo.—Chivumbulutso 14:1, 3, 4.
Mosakayikira, chiukiriro cha akufa chili nthaŵi ya chimwemwe chosaneneka kwa aja oukitsidwira kumoyo wakumwamba. Koma chimwemwecho sichimangothera pamenepo, pakuti pali lonjezo linanso la chiukiriro cha kumoyo pompano padziko lapansi. Oukitsidwawo adzagwirizana ndi chiŵerengero chopanda malire cha opulumuka mapeto a dongosolo loipa la zinthu. Ataona chiŵerengero chaching’ono cha amene ali oyenerera chiukiriro chakumwamba, mtumwi Yohane anasonyezedwa masomphenya a “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” Ha, imeneyo idzakhala nthaŵi yachimwemwe chachikulu chotani nanga pamene mamiliyoni, mwinamwake mabiliyoni, adzakhalanso ndi moyo padziko lapansi pompano!—Chivumbulutso 7:9, 16, 17.
Kodi Zimenezi Zidzachitika Liti?
Chisangalalo ndi chimwemwe chilichonse chingakhale chakanthaŵi ngati akufawo abwerera ku dziko lapansi lodzala ndi nkhondo, kukhetsa mwazi, kuipitsa, ndi chiwawa—monga momwe ulili mkhalidwe lerolino. Aha, chiukiriro chidzayembekezera kuti “dziko latsopano” likhazikitsidwe. Tangoganizani, pulaneti lopanda anthu ndi magulu amene kufikira pano akuumirira kuwononga dziko lapansi ndi kuipitsa kukongola kwake, kuwonjezera pa mavuto osaneneka amene awabweretsa pa nzika zake.—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 11:18.
Mwachionekere, nthaŵi ya kuuka kwa anthu onse ikali mtsogolo. Komabe uthenga wabwino ngwakuti sikuli kutali kwambiri. Zoonadi, kuyenera kuyembekezera mapeto a dongosolo la zinthu loipa limene lilipoli. Komabe, umboni wochuluka ukusonyeza kuti nthaŵi ya “masauko aakulu” [“chisautso chachikulu,” NW] ili pafupi, ikumathera mu “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse”—yodziŵika ndi ambiri kukhala Armagedo. (Mateyu 24:3-14, 21; Chivumbulutso 16:14, 16) Zimenezi zidzachititsa kuti kuipa konse kuchotsedwe pa pulaneti lino losangalatsa, Dziko Lapansi. Pambuyo pa zimenezo padzadza Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu Yesu, pamene dziko lapansi lidzasandulizidwa pang’ono ndi pang’ono kukhala paradaiso.
Baibulo limasonyeza kuti mu ulamuliro wa Zaka Chikwi umenewu, kuuka kwa anthu akufa kudzachitika. Pa nthaŵiyo lonjezo la Yesu limene ananena padziko lapansi lidzakwaniritsidwa: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, . . . kukuuka.”—Yohane 5:28, 29.
Chiyambukiro cha Chiyembekezo cha Chiukiriro
Ha, chimenechi ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chotani nanga chamtsogolo cha chiukiriro—nthaŵi pamene akufa adzakhalanso ndi moyo! Mmene chimatilimbikitsira nanga pamene tiyang’anizana ndi mavuto a ukalamba, matenda, masoka osayembekezereka ndi chisoni, ndi zitsenderezo zatsiku lililonse ndi mavuto a moyo! Chimachotsa mbola ya imfa—komabe osati kuchotsa chisoni chonse koma chimatilekanitsa ndi aja amene alibe chiyembekezo chamtsogolo. Mtumwi Paulo anavomereza za chiyambukiro chimenechi chotonthoza cha chiyembekezo cha chiukiriro ndi mawu awa: “Sitifuna, abale, kuti mukhale osadziŵa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo. Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi iye iwo akugona mwa Yesu.”—1 Atesalonika 4:13, 14.
Tingakhale titaona kale choonadi cha mawu ena onenedwa ndi mwamuna Wakummaŵa Yobu akuti: “Munthu akutha ngati chinthu chowola, ngati chovala chodyedwa ndi numbi. Munthu wobadwa ndi mkazi ngwamasiku oŵerengeka, nakhuta mavuto. Atuluka ngati duŵa, nafota; athaŵa ngati mthunzi, osakhalitsa.” (Yobu 13:28–14:2) Timadziŵanso za kusatsimikizirika kwa moyo ndi choonadi chosakondweretsa chakuti “nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika” zingagwere aliyense wa ife. (Mlaliki 9:11, NW) Kunenadi zoona, palibe aliyense wa ife amene amasangalala ndi lingaliro la kufa. Chikhalirechobe, chiyembekezo chotsimikizirika cha chiukiriro chimathandiza kuchotsa mantha aakulu a imfa.
Chotero, limbani mtima! Musayembekezere kugona mu imfa chabe kumene kungachitike, koma kukhalanso ndi moyo mwa chozizwitsa cha chiukiriro. Yembekezerani ndi chidaliro moyo wamtsogolo wopanda mapeto, ndipo pa zimenezi wonjezeranipo chimwemwe cha kudziŵa kuti nthaŵi yodalitsidwa imeneyi ili pafupi patsogolopa.