Mabuku, Mabuku, Mabuku!
“Pakuti saleka kulemba mabuku ambiri,” inalemba motero Mfumu yanzeru Solomo ya nthaŵi zakale. (Mlaliki 12:12) M’chaka cha 1995 ku Britain, pa anthu 580 alionse, pafupifupi buku limodzi latsopano linalembedwa, zikumapangitsa dziko limenelo kukhala lotsogola pa maiko onse polemba mabuku atsopano. China, dziko lomwe lili ndi anthu ochuluka koposa padziko lonse lapansi, linali lachiŵiri ndi chiŵerengero cha 92,972 cha mabuku atsopano poyerekeza ndi chiŵerengero cha Britain cha 95,015. Germany anatsatira ndi (mabuku 67,206), ndiye kenako United States (49,276), kenaka France mabuku (41,234). “Chapangitsa kuti dziko la Britain likhale patsogolo nchakuti Chingelezi ndicho chilankhulo chofala padziko lonse.” inatero nyuzipepala ya The Daily Telegraph ya ku London.
Malipoti amasonyeza kuti malonda amabuku akhala akuloŵa pansi pa zaka zingapo, ndipo tsopano ndi 80 peresenti yokha ya anthu akuluakulu m’Britain amagula buku limodzi kapena ochulukirapo pa chaka. Komabe kodi anthu amaŵerenga mabuku onse amene amagula?
Buku lina limene likufalitsidwabe ndiponso kuŵerengedwa kwambiri ndi Baibulo, lomwe tsopano limapezeka m’zilankhulo 2,120, mbali zake chabe kapenanso lathunthu. Ngati inu simunapezebe Baibulo, fikani pa ofesi ya Watch Tower Society yomwe ili pafupi ndi kwanuko kuti mukagule lanu. Ngati muli nalo kale, litengeni ndipo yang’ananimo Malemba amene alembedwa mu nkhani za m’magazini ano. Mukatero, mudzapeza chidziŵitso chopereka moyo cha m’Baibulo.