-
Mfundo Zazikulu za Nyimbo ya SolomoNsanja ya Olonda—2006 | November 15
-
-
1:2, 3—N’chifukwa chiyani kukumbukira chikondi cha m’busayo kukufanana ndi vinyo ndiponso dzina lake likunga mafuta? Monga mmene vinyo amakondweretsera mtima wa munthu, ndi mmene mafuta amaziziritsira tikawadzola pa mutu, kukumbukira chikondi cha mnyamatayo ndiponso dzina lake kunalimbikitsa ndi kutonthoza namwaliyo. (Salmo 23:5; 104:15) Akhristu oona, makamaka odzozedwa, amapeza mphamvu ndiponso amalimbikitsidwa akamaganizira za chikondi chimene Yesu Khristu wawasonyeza.
-
-
Mfundo Zazikulu za Nyimbo ya SolomoNsanja ya Olonda—2006 | November 15
-
-
1:2; 2:6. Mawu ndi zochita zabwino zosonyeza chikondi zingakhale zoyenera pamene tili pachibwenzi. Komabe, mwamuna ndi mkazi ayenera kusamala kuti chimenechi chizikhala chikondi chenicheni osati chilakolako chonyansa, chimene chingawachititse chisembwere.—Agalatiya 5:19.
-