Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 5/1 tsamba 13-18
  • Palibe Mtendere kwa Amithenga Onyenga!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Palibe Mtendere kwa Amithenga Onyenga!
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Otchedwa Amithenga a Mtendere
  • Kodi UN Ndiyo Idzadzetsa Mtendere?
  • Zifukwa ‘Zolirira Koŵaŵa’
  • Mitundu Yogwirizana—Kodi Iri Njira Yabwinopo?
    Galamukani!—1991
  • Chinsinsi Chochititsa Mantha Chinaululika
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Ulendo wa Papa ku UN Kodi Unakwaniritsanji?
    Galamukani!—1996
  • Kutumikira Monga Amithenga a Mtendere Waumulungu
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 5/1 tsamba 13-18

Palibe Mtendere kwa Amithenga Onyenga!

“Ochita zoipa adzadulidwa . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—SALMO 37:9, 11.

1. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuyembekezera kupeza amithenga, oona ndi onyenga omwe, mu “nthaŵi ya chitsiriziro”?

AMITHENGA​—onyenga kapena oona? M’nthaŵi za Baibulo mitundu yonse iŵiri inaliko. Koma bwanji m’tsiku lathu? Pa Danieli 12:9, 10, timaŵerenga kuti mthenga wakumwamba anauza mneneri wa Mulungu kuti: “Mawuwo atsekedwa, nakhomeredwa chizindikiro mpaka nthaŵi ya chitsiriziro. Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi [“iwo amene ali ndi chidziŵitso,” NW] ndiwo adzazindikira.” Tikukhala mu “nthaŵi ya chitsiriziro” imeneyo tsopano. Kodi tikuona kusiyana kwakukulu pakati pa “oipa” ndi “iwo amene ali ndi chidziŵitso”? Ndithudi tikutero!

2. Kodi Yesaya 57:20, 21 akukwaniritsidwa motani lerolino?

2 Pa chaputala 57, mavesi 20 ndi 21, tikuŵerenga mawu a Yesaya mthenga wa Mulungu kuti: “Oipa ali ofanana ndi nyanja yoŵinduka; pakuti siingapume, ndi madzi ake autsa matope ndi ubve. Palibe mtendere, ati Mulungu wanga, kwa oipa.” Mmene mawuwa akufotokozera bwino nanga dzikoli pamene tikuyandikira zaka za zana la 21! Ndipotu ena amafunsa kuti, ‘Kodi tidzafikako nkomwe ku zaka za zana la 21 zimenezo?’ Kodi amithenga amene ali ndi chidziŵitso adzatiuzanji?

3. (a) Kodi ndi kusiyana kotani kumene kukusonyezedwa pa 1 Yohane 5:19? (b) Kodi “iwo amene ali ndi chidziŵitso” afotokozedwa motani m’Chivumbulutso chaputala 7?

3 Mtumwi Yohane anali ndi chidziŵitso chouziridwa ndi Mulungu. Pa 1 Yohane 5:19 pamati: “Tidziŵa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” Osiyana ndi dzikoli ndi Aisrayeli auzimu 144,000, otsalira amene akukalamba amene akali nafe pano. Ameneŵa lerolino agwirizana ndi “khamu lalikulu, . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe,” amene tsopano apyola pachiŵerengero cha mamiliyoni asanu, amenenso ali ndi chidziŵitso. “Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu.” Ndipo nchifukwa ninji akufupidwa? Chifukwa chakuti iwonso “anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa” mwa kusonyeza chikhulupiriro m’dipo la Yesu. Monga amithenga a kuunika, iwonso “amtumikira Iye [Mulungu] usana ndi usiku.”​—Chivumbulutso 7:4, 9, 14, 15.

Otchedwa Amithenga a Mtendere

4. (a) Kodi nchifukwa ninji otchedwa kuti amithenga a mtendere m’dziko la Satana adzalephera? (b) Kodi Aefeso 4:18, 19 akutanthauzanji lerolino?

4 Nanga bwanji ponena za otchedwa amithenga a mtendere a m’dongosolo ladziko la Satana? Pa Yesaya chaputala 33, vesi 7, timaŵerenga kuti: “Taonani, olimba mtima awo angofuula kunja, mithenga ya mtendere ilira koŵaŵa.” Umu ndi mmenedi zilili kwa aja amene akuthamangathamanga chodzandira uku ndi uko kumalikulu a dziko, poyesa kudzetsa mtendere! Nzachabe chotani nanga! Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti amayesa kuthetsa zizindikiro za mavuto a dziko m’malo moyesa kulimbana ndi zochititsa zake zenizeni. Choyamba, iwo ngakhungu ponena za kukhalako kwa Satana, amene mtumwi Paulo akuti ndiye “mulungu wa nthaŵi ino yapansi pano.” (2 Akorinto 4:4) Satana wafesa mbewu za kuipa pakati pa mtundu wa anthu, ndi chotulukapo chakuti ochuluka, kuphatikizapo olamulira ambiri, tsopano akuyenerera mafotokozedwe a pa Aefeso 4:18, 19, Chipangano Chatsopano, akuti: “Nzeru zawo zili mumdima. Chifukwa mitu yawo njouma, anakana kudziŵa Mulungu, nafulatira moyo umene Mulungu amapereka. Alibenso manyazi, ndipo anangodzipereka kuzonyansa, kuti achite zoipa zilizonse mosadziletsa.”

5. (a) Kodi nchifukwa ninji mabungwe a anthu amalephera kudzetsa mtendere? (b) Ndi uthenga wotonthoza wotani umene Salmo 37 likupereka?

5 Kulibe bungwe la anthu opanda ungwiro limene lingachotse umbombo m’mitima ya anthu, dyera, ndi udani zimene zili paliponse lerolino. Mlengi wathu yekha, Ambuye Mfumu Yehova, ndiye angachite zimenezo! Ndiponso, ndi ofatsa okha, oŵerengeka pakati pa anthu, amene ali okonzeka kugonjera chitsogozo chake. Kusiyana kwa zotulukapo za ameneŵa ndi za oipa a m’dziko kwasonyezedwa pa Salmo 37:9-11: “Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi. Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”

6, 7. Kodi ndi mbiri yotani ya zipembedzo za dziko imene ikusonyeza kuti zalephera kutumikira monga amithenga a mtendere?

6 Chotero, kodi amithenga a mtendere angapezeke pakati pa zipembedzo za dziko lodwalali? Chabwino, kodi mbiri ya chipembedzo njotani kudzafika lero? Mbiri ikusonyeza kuti chipembedzo chatengamo mbali, inde, ngakhale kusonkhezera kukhetsa mwazi kwakukulu m’zaka mazana onsewa. Mwachitsanzo, Christian Century ya mlungu wa August 30, 1995, posimba za chipwirikiti kudziko lomwe kale linali Yugoslavia, inati: “M’Bosnia wolamuliridwa ndi Serbia, ansembe amakhala m’mizera yakutsogolo m’nyumba ya malamulo yongodzikhazikitsa yokha, ndipo amakhalanso kutsogolo kwa mizera ya ankhondo, kumene magulu a asilikali ndi zida zomwe zimadalitsidwa isanayambe nkhondo.”

7 Zaka zana limodzi za ntchito yaumishonale ya Dziko Lachikristu m’Afrika sizinadzetse zotulukapo zabwino, monga zinaonekera poyera ku Rwanda, dziko lodziŵika kuti 80 peresenti ya anthu ake ndi Akatolika. The New York Times ya July 7, 1995, inasimba kuti: “Golias, magazini yaufulu ya Akatolika wamba yofalitsidwa ku Lyons [France], ikufuna kutchula maina enanso 27 a ansembe a ku Rwanda ndi avirigo anayi amene ikuti anapha kapena analimbikitsa kupha m’Rwanda chaka chatha.” African Rights, bungwe la zoyenera za munthu la ku London, linanena zotsatirazi: “Kuwonjezera pa kukhala kwawo chete, matchalitchi alinso ndi mlandu chifukwa chakuti ansembe awo, apasitala ndi avirigo anatengamo mbali m’kupululutsa anthu.” Mkhalidwewu wafanana ndi umene unali ku Israyeli pamene mthenga woona wa Yehova Yeremiya anafotokoza “manyazi” a Israyeli, pamodzi ndi olamulira ake, ansembe ake, ndi aneneri ake, nawonjezera kuti: “M’nsalu zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphaŵi osachimwa.”​—Yeremiya 2:26, 34.

8. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Yeremiya anali mthenga wa mtendere?

8 Nthaŵi zambiri Yeremiya watchedwa kuti mneneri wa chiwonongeko, koma angatchedwenso kuti mthenga wa Mulungu wa mtendere. Ananena za mtendere nthaŵi zambiri mofanana ndi Yesaya amene analiko iye asanakhaleko. Yehova anagwiritsira ntchito Yeremiya kulengeza chiweruzo pa Yerusalemu, akumati: “Mudzi uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiuchotse pamaso panga; chifukwa cha zoipa zonse za ana a Israyeli ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu awo, akulu awo, ansembe awo, aneneri awo, ndi anthu a Yuda, ndi okhala m’Yerusalemu.” (Yeremiya 32:31, 32) Zimenezi zinachitira chithunzi chiweruzo cha Yehova pa olamulira ndi atsogoleri a chipembedzo m’Dziko Lachikristu lerolino. Kuti pakhale mtendere weniweni, osonkhezera kuipa ndi chiwawa ameneŵa ayenera kuchotsedwapo! Ndithudi iwo saali amithenga a mtendere.

Kodi UN Ndiyo Idzadzetsa Mtendere?

9. Kodi UN yadzinenera motani kukhala mthenga wa mtendere?

9 Kodi United Nations singakhale mthenga woona wa mtendere? Ndipotu mawu ake oyamba a tchata chake, chimene chinaperekedwa mu June 1945, masiku 41 okha bomba la atomu lisanasakaze Hiroshima, anatchula chifuno chake: “kupulumutsa mibadwo yamtsogolo ku tsoka la nkhondo.” Maiko 50 oyembekezera kukhala mamembala a United Nations anafunikira “kugwirizanitsa nyonga [yawo] kuti asungitse mtendere ndi chisungiko padziko lapansi.” Lerolino UN ili ndi maiko 185 omwe ali mamembala ake, onse amene amati ali odzipereka pa chifuno chimodzimodzicho.

10, 11. (a) Kodi atsogoleri achipembedzo alengeza motani kuti akuchirikiza UN? (b) Kodi apapa aimira molakwika motani “Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu”?

10 Pazaka zonsezi, UN yathokozedwa kwambiri, makamaka ndi atsogoleri achipembedzo. Pa April 11, 1963, Papa John XXIII anasaina kalata yake yamutu wakuti “Pacem in Terris” (Mtendere Padziko Lapansi) mmene ananena kuti: “Chikhumbo chathu chachikulu nchakuti gulu la United Nations​—m’kakonzedwe kake ndi m’kukhoza kwake​—likhale ndi mphamvu nthaŵi zonse yakusamalira ntchito zake zazikulu ndi zofunikazo.” Kenako, m’June 1965, atsogoleri achipembedzo, amene anati akuimira theka la anthu padziko, anakondwerera tsiku lakubadwa la 20 la UN ku San Francisco. Ndiponso mu 1965, Papa Paul VI paulendo wake ku UN anaifotokoza kukhala “chiyembekezo chomalizira cha chimvano ndi mtendere.” Mu 1986, Papa John Paul II anachirikiza nawo Chaka cha Mtendere wa Dziko Lonse cha UN.

11 Nthaŵi inanso, pakucheza kwake mu October 1995, papayo analengeza kuti: “Lero tikukondwerera Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” Koma kodi iye kwenikweni alidi mthenga wa Mulungu wa uthenga wabwino wa Ufumu? Ponena za mavuto a dziko, iye anati: “Pamene tikulimbana ndi mavuto aakulu ameneŵa, kodi tingalephere bwanji kuzindikira ntchito ya Gulu la United Nations?” Papa anasankha UN, m’malo mwa Ufumu wa Mulungu.

Zifukwa ‘Zolirira Koŵaŵa’

12, 13. (a) Kodi UN yachita motani m’njira yolongosoledwa pa Yeremiya 6:14? (b) Nchifukwa ninji atsogoleri a UN akuphatikizidwa pa mafotokozedwe a pa Yesaya 33:7?

12 Kukondwerera chaka cha 50 cha UN kunalephera kusonyeza chiyembekezo chenicheni chilichonse cha “mtendere padziko lapansi.” Chifukwa china chinasonyezedwa ndi wolemba wina mu The Toronto Star ya ku Canada, amene analemba kuti: “U.N. ndi mkango wopanda mano, umene umabangula ukaona nkhanza ya anthu, koma umayembekezera mamembala ake kuupatsa mano kuti ulume.” Nthaŵi zambiri kulumako kwakhala kopanda mphamvu ndipo kochedwa kwambiri. Amithenga a mtendere m’dongosolo lilipoli la dziko, ndipo makamaka aja a m’Dziko Lachikristu, akhala akuchita monga mwa mawu a Yeremiya 6:14 akuti: “Apoletsa bala la anthu anga pang’onopang’ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.”

13 Alembi aakulu otsatizana a UN agwira ntchito molimbika, ndipotu moona mtima, kuti UN ipambane. Koma kukangana kosatha kwa mamembala ake 185 okhala ndi zolinga zosiyanasiyana ponena za njira yochepetsera nkhondo, kupanga malamulo, ndi kusamalira ndalama zapinga chiyembekezo cha chipambano. M’lipoti lake la pachaka la 1995, amene anali mlembi wake wamkulu nthaŵiyo analemba kuti kuchepa kwa “mantha a tsoka la nyukiliya” kukutsegula njira yakuti “mitundu igwirire ntchito pamodzi kulinga ku chitukuko cha chuma ndi kakhalidwe kaamba ka anthu onse.” Koma anawonjezera kuti: “Mwachisoni, mbiri ya zochitika za dziko pazaka zingapo zapitazo yawononga kwambiri ziyembekezo zabwino zimenezo.” Inde, amene akanakhala amithenga a mtendere ‘akulira koŵaŵa.’

14. (a) Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti UN ilibe ndalama ndi makhalidwe omwe? (b) Kodi Yeremiya 8:15 akukwaniritsidwa motani?

14 Mutu wina wa nkhani mu The Orange County Register ya ku California unati: “U.N. Ilibe Ndalama ndi Makhalidwe.” Nkhaniyo inafotokoza kuti pakati pa 1945 ndi 1990, panali nkhondo zoposa 80, zimene zinapha miyoyo yoposa mamiliyoni 30. Inagwira mawu wolemba wina wa Reader’s Digest ya October 1995 amene “amanena kuti mautumiki a zankhondo a U.N. amadziŵika ndi ‘akazembe osadziŵa ntchito, asilikali opulupudza, kupanga mapangano ndi oukira, kulephera kuletsa nkhanza ndipo nthaŵi zina ngakhale kuchirikiza nkhalwezo.’ Ndiponso, ‘mlingo wa kuwawanya ndalama, chinyengo, ndi nkhanza ngwaukulu kwambiri.’” Pachigawo chotchedwa kuti “U.N. Pazaka 50,” The New York Times inali ndi mutu wakuti “Uyang’aniro Woipa ndi Kuwawanya Ndalama Ziwononga Zolinga za U.N. Zabwino Koposa.” The Times ya ku London, England, inali ndi nkhani yamutu wakuti “Pokhala Yofooka Pazaka Makumi Asanu​—UN ifunikira maseŵero olimbitsa thupi kuti ipezenso nyonga.” Kwenikweni, zikufanana ndi zimene timaŵerenga pa Yeremiya chaputala 8, vesi 15 kuti: “Tinayang’anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthaŵi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!” Ndipo anthu akali ndi mantha a chipiyoyo cha nyukiliya. Ndithudi, UN sindiyo mthenga wa mtendere amene anthu akufuna.

15. Kodi ndi motani mmene Babulo wakale ndi mbadwa yake yachipembedzo akhalira ponse paŵiri owononga ndi ogodomalitsa?

15 Kodi zonsezi zidzatsogolera kuti? Mawu aulosi a Yehova ngolunjika. Choyamba, kodi nchiyani chimene chikuyembekezera zipembedzo za dzikoli zimene kaŵirikaŵiri zakhala paubwenzi wolimba ndi UN? Izo ndi mbadwa zochokera ku magwero amodzi, Babulo wakale. Moyenerera, zikufotokozedwa pa Chivumbulutso 17:5 kukhala “Babulo Waukulu, Amayi wa Achigololo ndi wa Zonyansitsa za Dziko.” Yeremiya anafotokoza chiwonongeko cha mgwirizano wachinyengo umenewu. Monga mkazi wachigololo, izo zanyenga andale a dziko, kutyasika UN ndi kukhala paunansi wosaloleka ndi maulamuliro a ndale amene ali mamembala ake. Ndizo zimene zatengamo mbali kwambiri m’nkhondo za m’mbiri. Wothirira ndemanga wina ponena za nkhondo zachipembedzo ku India anati: “Karl Marx anati chipembedzo ndi namgoneka wa anthu wamba. Koma mawuwo sangakhale olondola kwenikweni chifukwa chakuti namgoneka amaledzeretsa, amagodomalitsa anthu. M’malo mwake, chipembedzo chifanana kwambiri ndi crack cocaine. Chimatulutsa chiwawa choopsa ndipo chili ndi mphamvu yowononga kwambiri.” Wolemba ameneyo nayenso sali wolondola kwenikweni. Chipembedzo chonyenga chili ponse paŵiri chogodomalitsa ndi chowononga.

16. Kodi nchifukwa ninji anthu oona mtima tsopano ayenera kuthaŵa m’Babulo Wamkulu? (Onaninso Chivumbulutso 18:4, 5.)

16 Choncho, kodi anthu oona mtima ayenera kuchitanji? Yeremiya mthenga wa Mulungu akutipatsa yankho kuti: “Thaŵani pakati pa Babulo, yense apulumuke moyo wake . . . pakuti ndi nthaŵi ya kubwezera chilango.” Ndife okondwa kuti anthu mamiliyoni athaŵa m’mabwalo a Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Kodi ndinu mmodzi wa ameneŵa? Ndiye kuti mukumvetsa mmene Babulo Wamkulu wakhudzira mitundu ya padziko lapansi: “Amitundu amwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala.”​—Yeremiya 51:6, 7.

17. Kodi ndi chiweruzo chotani chimene chili pafupi kuperekedwa pa Babulo Wamkulu, ndipo nchiyani chidzatsatirapo?

17 Posachedwapa, Yehova adzasonkhezera mamembala ‘amisala’ a UN kutembenukira chipembedzo chonyenga, monga Chivumbulutso 17:16 chimafotokozera kuti: “Izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiŵa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsereza ndi moto.” Chimenechi chidzakhala chiyambi cha chisautso chachikulu chotchulidwa pa Mateyu 24:21 chimene chidzafika pachimake pa Armagedo, nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse. Monga Babulo wakale, Babulo Wamkulu adzalandira chiweruzo cholengezedwa pa Yeremiya 51:13, 25 kuti: “[Mkazi, NW] iwe wokhala pamadzi ambiri, wochuluka chuma, chimaliziro chako chafika, chilekezero cha kusirira kwako. Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuwononga, ati Yehova, limene liwononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa.” Mitundu yoipa, yosonkhezera nkhondo idzawonongedwa monga chipembedzo chonyenga pamene tsiku lakubwezera la Yehova lidzawagwera nawonso.

18. Kodi Yesaya 48:22 adzakwaniritsidwabe liti ndipo motani?

18 Pa 1 Atesalonika 5:3, pamati ponena za oipa: “Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zoŵaŵa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.” Awa ndiwo amene Yesaya ananena kuti: “Taonani, . . . mithenga ya mtendere ilira koŵaŵa.” (Yesaya 33:7) Ndithudi, monga timaŵerengera pa Yesaya 48:22, “kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.” Koma kodi amithenga oona a mtendere waumulungu adzakhala ndi mtsogolo motani? Nkhani yathu yotsatira idzalongosola.

Mafunso Openda

◻ Kodi aneneri a Mulungu avumbula amithenga onyenga ndi mawu amphamvu otani?

◻ Kodi nchifukwa ninji mabungwe a anthu akulephera kukhazikitsa mtendere wokhalitsa?

◻ Kodi amithenga oona a mtendere akusiyana motani ndi ochirikiza UN?

◻ Kodi ofatsa ayenera kuchitanji kuti akasangalale ndi mtendere wolonjezedwa wa Yehova?

[Zithunzi patsamba 15]

Yesaya, Yeremiya, ndi Danieli onse analosera kulephera kwa zoyesayesa wamba za anthu kuti adzetse mtendere

[Chithunzi patsamba 16]

“Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”​—Mtumwi Yohane

[Chithunzi patsamba 17]

“Nzeru zawo zili mumdima.”​—Mtumwi Paulo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena