Tili ndi Chifukwa Chofuulira ndi Chimwemwe
“Iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.”—YESAYA 35:10.
1. Kodi ndani lerolino ali ndi chifukwa chachikulu chokhalira achimwemwe?
MWINAMWAKE mwaona kuti ndi anthu oŵerengeka okha amene ali ndi chimwemwe chenicheni masiku ano. Komabe, monga Akristu oona, Mboni za Yehova zili ndi chimwemwe. Ndipo mwaŵi wa kupeza chimwemwe chimodzimodzicho ulipo kwa mamiliyoni ena amene sanabatizidwebe, achichepere ndi achikulire, amene akuyanjana ndi Mboni. Kuŵerenga kwanu mawu awa m’magazini ano kukusonyeza kuti chimwemwe chimenechi mwachipeza kale kapena kuti muli pafupi kuchipeza.
2. Kodi chimwemwe cha Mkristu chimasiyana motani ndi mkhalidwe wa anthu ambiri?
2 Anthu ochuluka amazindikira kuti moyo wawo ukusoŵa kanthu kena. Bwanji nanga za inu? Zoona, simungakhale ndi zinthu zonse zakuthupi zimene mukanagwiritsira ntchito, zinthu zimene olemera ndi amphamvu ali nazo lerolino. Ndipo mungafune kukhala ndi thanzi labwinopo kapena nyonga yowonjezereka. Komabe, tikhoza kunena motsimikiza kuti pankhani ya chimwemwe, ndinu wolemera ndi wathanzi kwambiri kuposa mabiliyoni ambiri apadziko lapansi. Motani?
3. Kodi ndi mawu ati atanthauzo omwe tiyenera kuwapenda, ndipo chifukwa ninji?
3 Kumbukirani mawu a Yesuwa: “Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chidzale.” (Yohane 15:11) “Chimwemwe chanu chidzale.” Ndi mawu abwino chotani nanga amenewo! Phunziro lozama la moyo wachikristu lidzasonyeza zifukwa zambiri zochititsa chimwemwe chathu kudzala. Koma pakali pano, taonani mawu atanthauzo pa Yesaya 35:10. Ameneŵa ali atanthauzo chifukwa chakuti akutikhudza kwambiri lerolino. Timaŵerenga kuti: “Oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yawo; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.”
4. Kodi ndi chimwemwe chotani chomwe chikutchulidwa pa Yesaya 35:10, ndipo nchifukwa ninji tiyenera kusumika maganizo pa icho?
4 Kukondwako kudzakhala kopanda mapeto, m’mikhalidwe imene idzakulola—inde, kuchirikiza—kukondwa kosatha. Kodi zimenezo sizikumveka kukhala zosangalatsa? Komabe, mwinamwake vesi limeneli likukudabwitsani monga ndemanga yonena za mkhalidwe wina wopeka, likumakuganizitsani kuti: ‘Zimenezo sizimandikhudza kwenikweni monga momwe zothetsa nzeru ndi nkhaŵa zanga zatsiku ndi tsiku zimandikhudzira.’ Koma zimaterodi. Lonjezo laulosi pa Yesaya 35:10 lili ndi tanthauzo kwa inu lerolino. Kuti tidziŵe kuti ndi motani, tiyeni tipende chaputala chabwino kwambiri chimenechi cha Yesaya 35, tikumayang’anitsitsa mbali iliyonse ya nkhaniyo. Kunena zoona, mudzakondwa nazo zimene tidzapeza.
Anthu Amene Anafunikira Kukhala Achimwemwe
5. Kodi ulosi wa Yesaya chaputala 35 ukupezeka m’chochitika chotani chaulosi?
5 Kuti zitithandize, tiyeni tione chithunzi cha nkhani yake, zochitika m’mbiri yakale, za ulosi wochititsa chidwi umenewu. Mneneri wachihebri Yesaya anaulemba pafupifupi mu 732 B.C.E. Nthaŵiyo inali kutali kwambiri ndi chiwonongeko cha Yerusalemu chochitidwa ndi Babulo. Malinga ndi zimene zasonyezedwa pa Yesaya 34:1, 2, Mulungu anali ataneneratu kuti adzabwezera chilango pa amitundu otchulidwa pa Yesaya 34:6, monga Edomu. Mwachionekere iye anagwiritsira ntchito Ababulo akale kuchita zimenezo. Momwemonso, Mulungu analola Ababulo kupasula Yuda chifukwa chakuti Ayuda anali osakhulupirika. Chotulukapo chake? Anthu a Mulungu anatengedwa ukapolo, ndipo dziko lawo linakhala lapululu kwa zaka 70.—2 Mbiri 36:15-21.
6. Kodi kusiyana kwa zimene zinalinkudza pa Aedomu ndi zimene zinalinkudza pa Ayuda nkotani?
6 Komabe, pali kusiyana kwakukulu pakati pa Aedomu ndi Ayuda. Chilango cha Mulungu pa Aedomu chinali chachikhalire; m’kupita kwa nthaŵi, iwo anazimiririka monga mtundu. Inde, mukhoza kukaona mabwinja m’dera limene Aedomu anali kukhalamo, monga mabwinja a Petra otchuka padziko lonse. Koma lerolino, kulibe mtundu kapena anthu amene angatchedwe ‘Aedomu.’ Komabe, kodi kupasula Yuda kwa Ababulo kunali kosatha, kukumasiya dzikolo lili lopanda chimwemwe ku umuyaya wonse?
7. Kodi Ayuda okhala mu ukapolo ku Babulo angakhale atalabadira motani Yesaya chaputala 35?
7 Panopa mpamene ulosi wabwino kwambiri wa Yesaya chaputala 35 uli ndi tanthauzo losangalatsa. Tingautche ulosi wa kubwezeretsa, pakuti kukwaniritsidwa kwake koyamba kunachitika pamene Ayuda anabwerera kudziko lawo mu 537 B.C.E. Aisrayeli amene anali akapolo ku Babulo anapatsidwa ufulu wa kubwerera kudziko lawo. (Ezara 1:1-11) Komabe, zimenezo zisanachitike Ayuda okhala mu ukapolo ku Babulo amene anapenda ulosi wa Mulungu umenewu angakhale atafuna kudziŵa za mikhalidwe imene anayembekezera kupeza kudziko lawo la Yuda. Kodi iwo anayembekezera kukhala mumkhalidwe wotani? Mayankho ake amakhudzadi kwambiri chifukwa chofuulira ndi chimwemwe chomwe tili nacho. Tiyeni tione.
8. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene Ayuda anayembekezera kupeza atabwerako ku Babulo? (Yerekezerani ndi Ezekieli 19:3-6; Hoseya 13:8.)
8 Ndithudi mkhalidwe sunali wabwino kwenikweni kwa Ayuda ngakhale pamene anamva kuti akanakhoza kubwerera kudziko lawo. Dziko lawo linakhala lapululu kwa zaka makumi asanu ndi aŵiri, moyo wonse wa munthu. Kodi nchiyani chimene chingakhale chitachitikira dzikolo? Minda iliyonse yolimidwa, minda ya mphesa, kapena ya zipatso, ingakhale itakhala tchire. Madimba angakhale atasanduka malo ouma kapena zipululu. (Yesaya 24:1, 4; 33:9; Ezekieli 6:14) Talingaliraninso za nyama zakutchire zimene zingakhale zitaswana kwambiri. Zimenezi zingakhale zitaphatikizapo zodya zinzake zonga mikango ndi anyalugwe. (1 Mafumu 13:24-28; 2 Mafumu 17:25, 26; Nyimbo ya Solomo 4:8) Ndipo sakananyalanyaza zimbalangondo, zimene zinali ndi mphamvu ya kukantha mwamuna, mkazi, kapena mwana. (1 Samueli 17:34-37; 2 Mafumu 2:24; Miyambo 17:12) Ndipo sitifunikira ndi kutchula za nsongo ndi njoka zina zaululu, kapena zinkhanira. (Genesis 49:17; Deuteronomo 32:33; Yobu 20:16; Salmo 58:4; 140:3; Luka 10:19) Mukanakhala ndi Ayuda obwerako ku Babulo mu 537 B.C.E., mwinamwake mukanazengereza kuyendayenda m’dera lotero. Silinali paradaiso pamene iwo anafika.
9. Kodi ndi pachifukwa chotani chimene obwererawo anakhalira ndi chiyembekezo ndi chidaliro?
9 Komabe, Yehova yekha ndiye anatsogolera olambira ake popita kwawo, ndipo ali ndi mphamvu ya kusintha mkhalidwe wapululu. Kodi simumakhulupirira zimenezo ponena za Mlengiyo? (Yobu 42:2; Yeremiya 32:17, 21, 27, 37, 41) Chotero, kodi iye anali kudzatani—kodi anatani—kwa Ayuda obwererawo ndi dziko lawo? Kodi zimenezi zimakhudza motani anthu a Mulungu masiku ano ndi mkhalidwe wanu—lero ndi mtsogolo? Choyamba tiyeni tione zimene zinachitika kalelo.
Achimwemwe Chifukwa cha Kusintha kwa Mkhalidwe
10. Kodi Yesaya 35:1, 2 analosera za kusintha kotani?
10 Kodi chinali kudzachitika nchiyani pamene Koresi analola Ayuda kubwerera kudziko lowopsalo? Ŵerengani ulosi wosangalatsawo pa Yesaya 35:1, 2: “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duŵa. Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebano, ndi ukulu wa Karimeli ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.”
11. Kodi ndi malo ati odziŵika amene Yesaya anagwiritsira ntchito monga chitsanzo?
11 M’nthaŵi za Baibulo, Lebano, Karimeli, ndi Saroni anali malo odziŵika ndi kukongola kwake kochititsa kaso. (1 Mbiri 5:16; 27:29; 2 Mbiri 26:10; Nyimbo ya Solomo 2:1; 4:15; Hoseya 14:5-7) Yesaya anagwiritsira ntchito zitsanzo zimenezo kufotokoza mmene dziko losandulikalo lidzakhalira, mwa thandizo la Mulungu. Koma kodi zimenezi zinali kungokhudza nthaka? Ndithudi ayi!
12. Kodi nchifukwa ninji tikunena kuti ulosi wa Yesaya chaputala 35 ukunena za anthu?
12 Yesaya 35:2 amalankhula za dziko kukhala ‘likusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba.’ Tikudziŵa kuti nthaka ndi zomera ‘sizinakondwe ndi kuimba’ kwenikweni. Komabe, kusintha kwake kukhala yachonde ndi yobala kunakhoza kuchititsa anthu kumva motero. (Levitiko 23:37-40; Deuteronomo 16:15; Salmo 126:5, 6; Yesaya 16:10; Yeremiya 25:30; 48:33) Kusintha kwenikweniko kwa nthaka kunaimira kusintha kwa anthu, pakuti anthuwo ndiwo nkhani yaikulu mu ulosi umenewu. Chifukwa chake, tili ndi chifukwa chomvetsera kuti mawu a Yesaya kwenikweni amanena za masinthidwe mwa Ayuda obwerera, makamaka chimwemwe chawo.
13, 14. Kodi ndi kusintha kotani kwa anthu kumene Yesaya 35:3, 4 analosera?
13 Motero, tiyeni tipende mwakuya ulosi wosangalatsa umenewu kuti tione mmene unakwaniritsidwira pambuyo pa kumasuka kwa Ayuda ku Babulo ndi kubwerera kwawo. M’vesi 3 ndi 4, Yesaya akulankhula za masinthidwe ena mwa anthu obwererawo: “Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo agwedegwede. Nenani kwa amitima yachinthenthe, Limbani, musawope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu; iye adzafika ndi kukupulumutsani.”
14 Kodi sikolimbikitsa kulingalira kuti Mulungu wathu, amene anakhoza kusintha mkhalidwe wapululu wa nthaka, amakonda kwambiri olambira ake? Sanafune Ayuda okhala mu ukapolo kumva kufooka, kulefuka, kapena kuwopa za mtsogolo. (Ahebri 12:12) Talingalirani za mkhalidwe wa akapolo achiyudawo. Kupatulapo chiyembekezo chimene anapeza m’maulosi a Mulungu onena za mtsogolo mwawo, kuyenera kuti kunali kovuta kwa iwo kuyembekezera zabwino. Kunali monga ngati anali m’ndende yapansi yamdima, osatha kuyendayenda ndi kutumikira Yehova mokangalika. Mwina kunaoneka monga ngati kunalibe zabwino zilizonse kutsogolo.—Yerekezerani ndi Deuteronomo 28:29; Yesaya 59:10.
15, 16. (a) Kodi tinganene kuti nchiyani chimene Yehova anachitira obwererawo? (b) Kodi nchifukwa ninji obwererawo sakanayembekezera machiritso ozizwitsa akuthupi, koma kodi Mulungu anachitanji mogwirizana ndi Yesaya 35:5, 6?
15 Komatu, zimenezo zinasintha chotani nanga pamene Yehova anachititsa Koresi kuwamasula kuti abwerere kwawo! Palibe umboni wa Baibulo wakuti Mulungu panthaŵiyo anatsegula mozizwitsa maso alionse akhungu a Ayuda obwerera, kutsegula makutu a agonthi, kapena kuchiritsa opunduka ziŵalo zilizonse. Koma, anachitadi kanthu kena kabwino kopambana. Anawabwezeretsa m’kuunika ndi mu ufulu wa dziko lawo lokondedwa.
16 Palibe umboni wakuti obwererawo anayembekezera Yehova kuchita machiritso ozizwitsa amenewo akuthupi. Ayenera kukhala atazindikira kuti Mulungu sanachite zimenezo kwa Isake, Samsoni, kapena Eli. (Genesis 27:1; Oweruza 16:21, 26-30; 1 Samueli 3:2-8; 4:15) Koma ngati anayembekezera Mulungu kusintha mkhalidwe wawo mophiphiritsira, sanagwiritsidwe mwala. Inde, mophiphiritsira, mavesi 5 ndi 6 anakwaniritsidwadi. Yesaya ananeneratu molondola kuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo, wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lil[i]me la wosalankhula lidzaimba.”
Kusandutsa Dzikolo Likhale Ngati Paradaiso
17. Kodi ndi masinthidwe otani akuthupi amene Yehova mwachionekere anachititsa?
17 Obwererawo ayenera kuti analidi ndi chifukwa chofuulira ndi chimwemwe pa mikhalidwe imene Yesaya anapitiriza kufotokoza kuti: “Pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se. Ndipo mchenga wong’azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m’malo a ankhandwe mmene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.” (Yesaya 35:6b, 7) Ngakhale kuti sitingaone zimenezo m’dziko lonselo lerolino, umboni umasonyeza kuti dera limene kale linali Yuda linali “paradaiso wa zifuyo.”a
18. Kodi obwerera achiyuda mwachionekere anachita motani pa madalitso a Mulungu?
18 Ponena za zochititsa chimwemwe, talingalirani mmene otsalira achiyuda angakhalire atamvera pamene anabwerera ku Dziko Lolonjezedwa! Iwo anali okhoza kusandutsa malo ouma, okhalamo ankhandwe ndi nyama zina zakutchire. Kodi simukanapeza chimwemwe pochita ntchito yobwezeretsa imeneyo, makamaka ngati mukanadziŵa kuti Mulungu anali kudalitsa zoyesayesa zanu?
19. Kuti anthu ogwidwa ukapolo ku Babulo abwerere kwawo, kodi nchiyani chimene chinafunikira kwa iwo?
19 Komabe, sikunali kwa Myuda aliyense wogwidwa ukapolo ku Babulo kusankha kubwerera ndi kukatengamo mbali m’ntchito yobwezeretsa yosangalatsayo. Mulungu ndiye amene anaika zofunika. Aliyense wodetsedwa ndi machitachita achipembedzo achikunja achibabulo analibe ufulu wa kubwerera. (Danieli 5:1, 4, 22, 23; Yesaya 52:11) Ngakhale aliyense amene mtima wake unali panjira yosayenera sakanabwerera. Anthu onse otero anali osayenera. Komabe, aja amene anakwaniritsa miyezo ya Mulungu, amene iye anaona kukhala oyera m’lingaliro lokhala ndi malire, anali okhoza kubwerera ku Yuda. Iwo anayenda monga ngati anali kuyenda pa Njira Yopatulika. Yesaya anamveketsa bwino zimenezo m’vesi 8 kuti: “Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa [N]jira [Y]opatulika; audyo sadzapita mmenemo; koma iye adzakhala nawo oyenda m’njira, ngakhale opusa, sadzasochera mmenemo.”
20. Kodi Ayuda sanafunikire kuwopa chiyani pobwerera, pakumakhala zotulukapo zotani?
20 Ayuda obwererawo sanafunikire kuwopa kuukiridwa ndi anthu onga zilombo kapena magulu a olanda. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Yehova sanalole anthu otero kuyenda pa Njira imeneyo limodzi ndi anthu ake oomboledwa. Chotero iwo anali kudzayenda ulendowo ali ndi mitima yachimwemwe, akuyembekezera zosangalatsa. Taonani mmene Yesaya anafotokozera zimenezo pomaliza ulosiwu: “Sikudzakhala mkango kumeneko, ngakhale chilombo cholusa sichidzapondapo, pena kupezedwa pamenepo; koma akuomboledwa adzayenda mmenemo; ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yawo; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.”—Yesaya 35:9, 10.
21. Kodi ife lerolino tiyenera kukuona motani kukwaniritsidwa kwa Yesaya chaputala 35 kumene kwachitika kale?
21 Ha, tili ndi chithunzi chaulosi chotani nanga panopo! Komabe, sitiyenera kuganiza kuti zimenezi zikungokhudza mbiri yakale, monga ngati zangokhala nthano yabwino yosakhudza kwenikweni mkhalidwe wathu kapena mtsogolo mwathu. Choonadi nchakuti ulosi umenewu ukukwaniritsidwa modabwitsa lerolino pakati pa anthu a Mulungu, choncho umakhudzadi aliyense wa ife. Umatipatsa chifukwa chabwino chofuulira ndi chimwemwe. Mbali zimenezi zokhudza moyo wanu tsopano ndi mtsogolo zafotokozedwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Mwa kufufuza kwake deralo, katswiri wa zaulimi Walter C. Lowdermilk (woimira Food and Agriculture Organization ya United Nations) anati: “Dzikoli kale linali paradaiso wa zifuyo.” Ndiponso ananena kuti mkhalidwe wake wakunja sunasinthe kwenikweni “chiyambire nthaŵi za Aroma,” ndipo “‘chipululu’ chimene chinakuta dziko limene linali lachonde chinakhalako chifukwa cha munthu, osati chilengedwe.”
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi liti pamene Yesaya chaputala 35 anakwaniritsidwa nthaŵi yoyamba?
◻ Kodi kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosiwo kunatulutsa chiyani?
◻ Kodi Yehova anakwaniritsa motani Yesaya 35:5, 6?
◻ Kodi ndi kusintha kotani kwa nthaka ndi mkhalidwe wawo kumene obwerera achiyuda anaona?
[Chithunzi patsamba 9]
Mabwinja a Petra, m’dera limene Aedomu anali kukhalamo
[Mawu a Chithunzi]
Garo Nalbandian
[Zithunzi patsamba 10]
Pamene Ayuda anali andende, mbali yaikulu ya Yuda inakhala ngati chipululu, yodzala zilombo zolusa zonga zimbalangondo ndi mikango
[Mawu a Chithunzi]
Garo Nalbandian
Chimbalangondo ndi mkango: Safari-Zoo ya ku Ramat-Gan, Tel Aviv