Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 3/15 tsamba 24-25
  • Anazindikira Chikhumbo cha Mtima Wake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anazindikira Chikhumbo cha Mtima Wake
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maulosi Aumesiya Apereka Chiyembekezo
  • Kulibeko Mesiya!
  • Munthu Wopemphera
  • Mawu Aulosi a Simeoni
  • Mawu a Simeoni kwa Mariya
  • Simeoni Atanthauzira Maulosi Aumesiya
  • Mwana wa Lonjezo
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Mwana Amene Mulungu Analonjeza
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Mmene Mungayandikirire kwa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • ‘Analingalira Mawuwo Mumtima Mwake’
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 3/15 tsamba 24-25

Anazindikira Chikhumbo cha Mtima Wake

KODI ndi chikhumbo cha mtima wanu kuona Ufumu Waumesiya ukulamulira padziko lonse lapansi? Ngati ndichoncho, mumalakalaka ndi kupempherera madalitso apadziko lapansi olonjezedwa pansi pa Ufumu wakumwamba umenewo. Pamenepo, sonyezani kuleza mtima pakuti “pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.”​—Miyambo 13:12; Yakobo 5:7, 8.

Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, ku Yerusalemu kunali Simeoni munthu “wolungama mtima ndi wopemphera.” Iye anakhulupirira maulosi a Umesiya ndipo moleza mtima “analikulindirira matonthozedwe a Israyeli.”​—Luka 2:25.

Maulosi Aumesiya Apereka Chiyembekezo

Yehova ndiye anachititsa ulosi woyamba wa Umesiya​—umene unapereka chiyembekezo kwa anthu ochimwa omafa. Mulungu ananeneratu za kudza kwa Mbewu ya “mkazi” wake, kapena gulu la chilengedwe chonse.​—Genesis 3:15.

Ameneyo anazindikiridwa kukhala mbewu ya Abrahamu, ndipo Yakobo ananeneratu za kudza kwake. (Genesis 22:17, 18; 49:10) Maulemerero a Ufumu wa Mesiya anatamandidwa m’masalmo. (Salmo 72:1-20) Yesaya ananeneratu kuti Mbewuyo ikabadwa kwa namwali, ndipo Mika analosera kuti kubadwako kukachitikira ku Betelehemu. (Yesaya 7:14; Mika 5:2) Amenewa ndi oŵerengeka okha a maulosi ambiri Aumesiya.

Kulibeko Mesiya!

Talingalirani zakale, ndipo tayerekezerani kuti zaka za zana loyamba C. E. zikuyandikira. Ulosi woyambirira wa Mulungu wonena za Mesiya tsopano uli ndi zaka 4,000. Ayuda anakumana kale ndi chiwonongeko cha kachisi wa Yehova, chipasuko cha dziko lawo, kumangidwa ukapolo ku Babulo kwa zaka 70, ndi zaka zina zoposa 500 pansi pa olamulira Achikunja. Kulibeko Mesiya!

Ayuda owopa Mulungu analakalaka chotani nanga kudza kwa Mesiya! Madalitso akachokera kwa iye akumayenda monga madzi kumka kwa iwo ndi mitundu yonse.

Munthu Wopemphera

Pakati pa Ayuda opemphera olakalaka ndi opempherera kudza kwa Mesiya pali Simeoni, mtumiki wokhulupirika wokalamba wa Yehova wokhala mu mzinda waukulu wa Yudeya. Chinthu chapadera chachitika kwa Simeoni.

Mulungu waika mzimu wake woyera pa Simeoni ndipo wamfupa ndi vumbulutso. Simeoni sadzafa kufikira ataona Amene adzakhala Mesiya. Koma pakupita masiku ndi miyezi. Simeoni akukalamba ndipo sangayembekezere konse kukhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali. Kodi lonjezo la Mulungu kwa iye lidzakwaniritsidwa?

Tsiku lina (mu 2 B.C.E.), okwatirana achichepere okhala ndi khanda akufika ku kachisi kuchokera ku Betelehemu. Mzimu woyera ukuvumbula kwa Simeoni kuti ili nditsiku lija loyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali. Iye akupita ku kachisi, kumene adzaona Amene aneneri analemba za iye. Akumayenda mofulumira kwambiri malinga ndi ukalamba wake, iye akuona Yosefe, Mariya, ndi mwanayo.

Simeoni ali ndi chikondwerero chotani nanga pamene akutenga mwanayo Yesu m’manja mwake! Ameneyu adzakhala Mesiya wolonjezedwayo​—“Kristu wa Yehova.” (NW) Pausinkhu waukalamba umenewo, Simeoni sangayembekezere kuona Yesu akukwaniritsa ntchito Yake yapadziko lapansi. Komabe, nkokondweretsa kumuona monga khanda. Maulosi Aumesiya akuyamba kukwaniritsidwa. Simeoni ngwachimwemwe chotani nanga! Adzakhala wokhutira tsopano kugona tulo ta imfa kufikira chiukiriro.​—Luka 2:25-28.

Mawu Aulosi a Simeoni

Pamene Simeoni akukweza mawu ake m’chitamando kwa Yehova, tikumumva akunena kuti: “Tsopano, Ambuye, monga mwa mawu anu aja, lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere; chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu, chimene munakonza pamaso pa anthu onse, kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israyeli.” Yosefe, atate olera a Yesu, ndi amayi Ake, Mariya, akupitiriza kudabwa ndi mawuwa.​—Luka 2:29-33.

Nkhope ya Simeoni njosangalala pamene akudalitsa Yosefe ndi Mariya, mwachionekere kuwafunira madalitso a Yehova pokwaniritsa mathayo awo kulinga kwa mwanayo. Ndiyeno nkhope ya nkhalambayo ikusonyeza chisoni. Akumalunjikitsa mawu ake kwa Mariya yekha, akuwonjezera kuti: “Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israyeli; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho; eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m’mitima yambiri akaululidwe.”​—Luka 2:34, 35.

Mawu a Simeoni kwa Mariya

Tangoyerekezerani mmene Mariya anamvera. Kodi Simeoni anatanthauzanji? Ena akalandira Kristu ndi kunyamulidwa m’mkhalidwe wawo wakugwa. Komabe, ena akamukana, kukhumudwa pa iye, ndi kugwa. Monga kunanenedweratu, Yesu anatsimikizira kukhala mwala wokhumudwitsa kwa Ayuda ambiri. (Yesaya 8:14; 28:16) Mawu a Simeoni samatanthauza kuti Mwiisrayeli aliyense payekha akayamba wagwera m’kusakhulupirira ndiyeno kuuka ndi kukhulupirira mwa kulandira Yesu. Mmalomwake, anthu akuchita mosiyanasiyana kwa iye, kuvumbula zolingalira za mitima yambiri ndi kutsogolera ku chiweruzo cha Mulungu kwa iwo kaya chabwino kapena choipa. Kwa osakhulupirira, iye akakhala ngati chizindikiro, kapena munthu wonyozeka. Mwakusonyeza chikhulupiriro mwa iye, ena akadzutsidwa mumkhalidwe wakufa m’zolakwa ndi machimo, ndipo adzasangalala ndi kaimidwe kolungama ndi Mulungu. Zochita za anthu kulinga kwa Mesiya zikasonyeza zimene zili m’mitima mwawo.

Bwanji ponena za mawu a Simeoni akuti: “Lupanga lidzakupyoza iwe m’moyo mwako”? Palibe chisonyezero cha Malemba chakuti Mariya anapyozedwa ndi lupanga lenileni. Komabe, kukanidwa kwa Yesu ndi anthu ambiri kukamsautsa. Ndipo kunali kopweteka chotani nanga kwa Mariya kuona Yesu akukhomeredwa pamtengo! Kumeneku kunali ngati kupyozedwa ndi lupanga.

Simeoni Atanthauzira Maulosi Aumesiya

Mzimu wa Mulungu unasonkhezera Simeoni kugwiritsira ntchito maulosi Aumesiya kwa Yesu. Simeoni akanatha kufa mumtendere, kapena bata, ‘chifukwa maso ake adaona chipulumutso cha Mulungu, chimene Anakonza pamaso pa anthu onse, kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu Ake Israyeli.’ (Luka 2:30-32) Ha, mawu ameneŵa amagwirizana bwino motani nanga ndi mawu aulosi a Yesaya!

Mneneri ameneyo ananeneratu kuti: “Ulemerero wa Yehova udzavumbulutsidwa, ndipo anthu onse adzauona pamodzi.” ‘[Yehova] adzakupatsanso [Mesiya] akhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.’ (Yesaya 40:5; 42:6; 49:6; 52:10) Malemba Achigiriki Achikristu ndi maumboni oonekera atsimikizira kuti Mesiyayo, Yesu Kristu, ali kuunika kowona kwa mitundu, Amene adzachotsa chophimba cha mdima wauzimu ndi kubweretsa chipulumutso kwa anthu.

Mawu a Mulungu samanena zowonjezereka ponena za Simeoni wokalambayo. Mwachionekere iye anamwalira Kristu asanatsegule njira ya ku moyo wakumwamba. Pamenepo, posachedwapa, Simeoni adzaukitsidwa ku moyo padziko lapansi. Ndichimwemwe chotani nanga chimene iye​—ndi inu​—mungakhale nacho m’dziko latsopano pansi pa Ufumu Waumesiya wa Mulungu!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena