CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 38-42
Yehova Amapereka Mphamvu kwa Munthu Wotopa
Chiwombankhanga chikhoza kuuluka nthawi yaitali pogwiritsa ntchito mpweya wotentha. Chikafika pamene pakuwomba mpweyawu chimauluka mozungulira pamwamba pa mpweyawo ndipo chimakankhidwa mpaka kupita m’mwamba. Chikafika m’mwambamo, chimafufuza pomwe pali mpweya wina wotentha womwe umachikankhanso mpaka m’mwamba kwambiri
Zimene zimachitika kuti chiwombankhanga chizitha kuuluka kwa nthawi yaitali zikufanana ndi mmene Yehova amatipatsira mphamvu kuti tisatope pomutumikira