Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mlandu wa Bwalo la Milandu la Chilengedwe Chonse Womwe Umakuyambukirani
    Nsanja ya Olonda—1988 | February 1
    • 21. Ndi mafunso otani amene akudzutsidwa ndi chitokoso cha Yehova kwa milungu ya mitundu?

      21 Chotero, monga ngati kuti akulankhula ku bwalo la milandu, Yehova akunena kuti: “Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane pamodzi. . . . Atenge mboni zawo, kuti avomerezeke [kukhala NW] olungama, pena amve, nanene ‘Nzowonadi!’” (Yesaya 43:9) Ichi ndi chitokoso chachindunji kwa milungu ya mitundu. Kodi iriyonse ya iyo inganene za zimene ziri mtsogolo? Kodi iyo inali yokhoza kunena tero m’nthaŵi zapita? Kodi iyo ingapeze wina aliyense kuchitira umboni ndi chitsimikiziro cholimba chakuti milungu yoteroyo yatsimikizira kukhala yowona, yoyenera chimvero chathu? Ndi mbiri yotani imene milungu ya mitundu, ndi atsatiri awo, yatulutsa m’nthawi yathu? Kodi yakhala yabwinopo kuposa imene milungu ya Igupto wakale, Asuri, ndi Ababulo inatulutsa? Kumbali ina, kodi awo amene achitira umboni kwa Yehova atulutsa chitsimikiziro champhamvu chakuti Yehova ali Mulungu wowona, mmodzi yekha woyenera kulambira kwathu? Nkhani yotsatira idzalongosola nkhani zimenezi.

  • Kodi Mudzakhala Mboni ya Mulungu Wowona?
    Nsanja ya Olonda—1988 | February 1
    • Chitokoso kwa Milungu Ina

      3. Ndi chitokoso chotani chimene Yehova akupereka kwa milungu ina yonse?

      3 Yehova anauzira Yesaya kulemba chitokoso ichi kwa milungu ina: “Ndani mwa iwo [milungu ya mitundu ya anthu] anganene ichi [ulosi wolongosoka]? Kapena kuwonetsa ife zinthu zakale [zomwe zidzachitika mtsogolo]? Aloleni iwo [monga milungu] atenge mboni zawo, kuti iwo [monga milungu] avomerezeke [kukhala NW] olungama, kapena aloleni iwo [anthu amitundu] amve ndi kunena, [‘Nchowonadi!’ NW]” (Yesaya 43:9) Chotero Yehova akutokosa milungu yonse imene anthu amailambira kutsimikizira kuti iyo iri milungu. Mboni zawo ziyenera kutulutsa chitsimikiziro chakuti milungu yawo iri yodalirika ndi yoyenera kulambiridwa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena