Chidziŵitso pa Nyuzi
Chizindikiro Cholakwa
“Kodi chizindikiro chanu nchiyani?” Kwa anthu mamiliyoni angapo omwe amafunsira ndandanda ya “chizindikiro cha nyenyezi” chokonzekeretsedwa ndi openda nyenyezi, funso limenelo liri lofunika koposa. Iwo amakhulupirira kuti mkhalidwe wa nyenyezi, mapulaneti, dzuŵa, ndi mwezi m’chigwirizano ndi magulu a zakuthambo pa nthaŵi ya kubadwa zimayambukira mwachindunji moyo wa munthu. Komabe, mogwirizana ndi nyuzipepala ya tsiku ndi tsiku ya ku London Independent, openda nyenyezi akupatsa anthu chizindikiro cholakwika. Machati a “Chizindikiro cha nyenyezi” ogwiritsiridwa ntchito kaamba ka zisonyezero zothandizira kulongosola makhalidwe a nyenyezi ali ozikidwa pa “malamulo” a kupenda nyenyezi okonzekeretsedwa zaka 2,000 zapitazo.
Yatero Independent kuti: Wopenda nyenyezi adzauza makolo a khanda lobadwa lero kuti iye ali wa nyenyezi ya Cancer.” Komabe, ripotilo likudziŵitsa kuti: “Ngati iwo m’malo mwake ayang’ana pa mkhalidwe wa dzuŵa m’thambo, iwo angakhoze kupeza kuti dzuŵa liri m’chenicheni m’nyenyezi ya Gemini.” Kodi nchiyani chimene chimapangitsa chimenechi? Akatswiri a sayansi ya nyenyezi amachitcha icho “nthaŵi ya nyengo pamene dzuŵa litafika pamutu limayenda pang’onopang’ono,” mkhalidwe mu umene pomwe pamazungulira dziko lapansi, m’chenicheni, pagwedezeka kwambiri monga mmene pamachitira pamwamba pake pamene likuyenda pang’onopang’ono. Kayendedweka, kapena “kugwedezeka,” kumatsiriza ukulu wa kuzungulira 360 zaka 25,800 zirizonse, chimene chimatanthauza kuti kusiyana kwa nyengo kumasendera patsogolo timphindi 50 m’dongosolo chaka chirichonse, kapena ukulu umodzi m’zaka 72. Chotero, m’zaka 2,000 zapitazo, khalidwe lowonekera la dzuŵa m’thambo labwerera m’mbuyo ndi chizindikiro chimodzi chathunthu cha zakuthambo. Monga chotulukapo, “chisonyezero chothandiza kulongosola zizindikiro za pa kubadwa sichiri chithunzi chenicheni cha m’mwamba pa nthaŵi ya kubadwa kwa wina,” walongosola tero Richard F. Smith m’bukhu lake Prelude to Science. “Ambiri a nyenyezi ya Scorpio a dziko lino,” iye akulongosola tero, “anabadwa kwenikweni pamene dzuŵa linali m’nyenyezi ya Libra, ambiri a nyenyezi ya Leo ali kwenikweni a nyenyezi ya Cancer, a nyenyezi ya Cancer alinso a nyenyezi ya Gemini, ndi kupitirizabe.”
Kusadalirika kwa ndandanda ya nyenyezi ndi zisonyezero zothandiza kulongosola zizindikiro zimangogogomezera nzeru ya kuyang’ana kwa Mlengi kaamba ka chitsogozo ndipo osati ku zinthu zomwe iye analenga. (Aroma 1:24, 25) Komabe, chifukwa chachikulube cha kupewera kugwiritsira ntchito zisonyezero zothandiza kulongosola zizindikiro chiri chakuti ichi chingatsogolere ku kupereka kulambira kwathu ku “dzuŵa kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, chinthu chimene [Mulungu] sanalamulire.”—Deuteronomo 17:2-5.
Popanda Madzi—Palibe Moyo
Awa ndi mapeto amene anafikiridwa ndi Profesa Norman H. Horowitz, wa sayansi wozolowerana ndi maulendo a Mariner ndi Viking a mu 1965-76 a kupita ku pulaneti ya Mars.
Mu bukhu lake To Utopia and Back: The Search for Life in the Solar System, Profesa Horowitz anadziŵitsa kuti zopeza m’maulendo amenewa mwachiwonekere zinathetsa funso lakuti kaya pali zamoyo pa pulaneti ya Mars kapena pa pulaneti ina iriyonse m’dongosolo lathu la miyamba. Pulaneti ya “Mars,” iye watero, “Imasowa mbali yapadera ija imene imalamulira mkhalidwe wa pulaneti yathu, nyanja za madzi m’kawonedwe kotheratu ka dzuŵa.” Kufufuza kwatsimikizira kuti pulanetilo liribe madzi.
Pambuyo pakuti kufufuza kosamalitsa kunathetsa kuthekera kulikonse kwa zofunika zamoyo pa pulaneti ya Mars, Horowitz anavomereza kuti: “Kulephera kwa kupeza zamoyo pa pulaneti ya Mars kunali kogwiritsa mwala, koma kunalinso vumbulutso. Popeza kuti pulaneti ya Mars inapereka lonjezo lokulira la malo okhalako kaamba ka moyo wosakhala padziko lapansi m’dongosolo lathu la miyamba, icho tsopano chiri mwachiwonekere chotsimikizirika kuti dziko lapansi liri pulaneti lokha lomwe liri ndi zamoyo m’mbali yathu ya mlalang’amba.”
Chiri chogwirizana chotani nanga kuti, polemba za dziko lapansi, mneneri wakaleyo Yesaya ananena kuti Mpangi wake “analiumba kuti akhalemo anthu.”! (Yesaya 45:18) Madzi akutchulidwa koyambirira mu zolembedwa za chilengedwe za Baibulo. Mwachiwonekere, kupereka madzi chilengedwe cha padziko lapansi cha zamoyo zonse chisanakhale chinali chinthu chofunika. Monga mmene maulendo onka ku pulaneti ya Mars achitira umboni kuti: Kunja kwa dziko la mizimu, kumene kulibe madzi, sikungakhale moyo.—Genesis 1:1-10.
[Chithunzi patsamba 7]
Mbali yopanda zamoyo ya pulaneti ya Mars, ikuwonedwa kuchokera m’ndege ya “Viking II”
[Mawu a Chithunzi]
NASA photo