MUTU 2
Kuzindikira Udindo Umene Khristu Anapatsidwa Ndi Mulungu
“PA CHIYAMBI, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Ndipo zonse zimene analenga zinali “zabwino kwambiri.” (Gen. 1:1, 31) Yehova analenga anthu kuti akhale ndi tsogolo labwino. Koma Adamu ndi Hava atasankha kusamvera Mulungu m’munda wa Edeni, zinapangitsa kuti anthu asakhalenso ndi moyo wosangalala. Koma cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi komanso anthu sichinasinthe. Pa nthawi imene ankaweruza Adamu ndi Hava, Mulungu analonjeza kuti ana omvera a Adamu adzapulumutsidwa. Anasonyezanso kuti adzabwezeretsa kulambira koona ndipo adzawononga Satana ndi ntchito zake zoipa. (Gen. 3:15) Zimenezi zikadzachitika zinthu zidzakhalanso “zabwino kwambiri” ngati mmene zinalili poyamba. Yehova adzagwiritsa ntchito Mwana wake Yesu Khristu kuti akwaniritse lonjezo lakeli. (1 Yoh. 3:8) Choncho m’pofunika kuzindikira udindo umene Khristu anapatsidwa ndi Mulungu.—Mac. 4:12; Afil. 2: 9, 11.
UDINDO UMENE KHRISTU ALI NAWO
2 Tikamaganizira za udindo umene Khristu ali nawo, timaona kuti udindo wakewu uli ndi mbali zambiri. Yesu ndi Mpulumutsi, Mkulu wa Ansembe, Mutu wa mpingo wachikhristu komanso panopa ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Kuganizira mozama za maudindo amenewa, kungatithandize kuti tiziyamikira kwambiri zimene Mulungu anachita komanso kuti tizikonda kwambiri Khristu Yesu. Baibulo limafotokoza bwino maudindo ake osiyanasiyana amenewa.
Yesu ali ndi udindo waukulu pokwaniritsa cholinga cha Yehova pa anthu
3 Pamene Khristu anali padziko lapansi, zinadziwika bwino kuti anthu omvera angathe kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu kudzera mwa Yesu. (Yoh. 14:6) Pokhala Mpulumutsi, Yesu anapereka moyo wake monga dipo kuti apulumutse anthu ambiri. (Mat. 20:28) Choncho, sikuti Yesu wangokhala chitsanzo pa nkhani ya makhalidwe abwino amene tingatengere, koma iye ndi wofunika kwambiri kuti cholinga chimene Mulungu anali nacho pa anthu chikwaniritsidwe. Ndi iye yekha amene angatithandize kuti tikhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Mac. 5:31; 2 Akor. 5:18, 19) Chifukwa choti Yesu anatifera ndipo anaukitsidwa, n’zotheka kuti anthu omvera adzapeze madalitso osatha mu Ufumu wa Mulungu.
4 Monga Mkulu wa Ansembe, Yesu ‘amatimvera chisoni pa zofooka zathu’ ndipo anapereka nsembe yophimba machimo a otsatira ake odzipereka a pa dziko lapansi. Mtumwi Paulo anati: “Pakuti mkulu wa ansembe amene tili naye si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni pa zofooka zathu. Koma tili ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.” Kenako Paulo analimbikitsa anthu okhulupirira Yesu Khristu kuti azigwiritsa ntchito mwayi womwe ali nawo woti agwirizanenso ndi Mulungu. Iye anati: “Choncho, tiyeni tiyandikire mpando wachifumu wa kukoma mtima kwakukulu ndipo tipemphere kwa Mulungu ndi ufulu wa kulankhula, kuti atichitire chifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.”—Aheb. 4:14-16; 1 Yoh. 2:2.
5 Komanso Yesu ndi Mutu wa mpingo wachikhristu. Monga mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, ifenso masiku ano sitimafunikira munthu winawake kukhala mtsogoleri wathu. Yesu amatsogolera nkhosa zake pogwiritsa ntchito mzimu woyera ndiponso abusa aang’ono oyenerera. Abusawa amadziwa kuti adzayankha mlandu kwa Yesuyo ndi Atate ake akumwamba wokhudza mmene akuchitira ndi nkhosazo. (Aheb. 13:17; 1 Pet. 5:2, 3) Yehova anafotokoza za Yesu mwaulosi kuti: “Taonani! Ine ndamupereka iye monga mboni kwa mitundu ya anthu, ndiponso monga mtsogoleri ndi wolamulira wa mitundu ya anthu.” (Yes. 55:4) Yesu anasonyeza kuti ulosiwu unakwaniritsidwa pamene anauza ophunzira ake kuti: “Musamatchedwe ‘atsogoleri,’ pakuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.”—Mat. 23:10.
6 Posonyeza kuti ali ndi mtima wabwino ndipo ndi wofunitsitsa kutithandiza, Yesu anati: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Yesu Khristu amatsogolera mpingo wachikhristu mokoma mtima komanso m’njira yotsitsimula. Pochita zimenezi amasonyeza kuti ndi “m’busa wabwino” ngati mmene Atate wake Yehova Mulungu alili.—Yoh. 10:11; Yes. 40:11.
7 M’kalata yake yoyamba yopita kwa Akhristu a ku Korinto, Paulo anafotokoza za udindo wina wa Yesu Khristu pamene ananena kuti: “Pakuti ayenera kulamulira monga mfumu kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Koma zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwanayonso adzadziika pansi pa amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.” (1 Akor. 15:25, 28) Popeza Yesu anali woyambirira kulengedwa, asanabwere padziko lapansi ankagwira ntchito ndi Mulungu ngati “mmisiri waluso.” (Miy. 8:22-31) Yesu atatumizidwa padziko lapansi, ankachita chifuniro cha Mulungu nthawi zonse. Anapirira mayesero aakulu ndipo anafa ali wokhulupirika kwa Atate wake. (Yoh. 4:34; 15:10) Chifukwa choti Yesu anali wokhulupirika mpaka imfa yake, Mulungu anamuukitsa n’kupita kumwamba ndipo anamupatsa udindo wokhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba. (Mac. 2:32-36) Choncho Yesu Khristu ali ndi ntchito yaikulu imene Mulungu wam’patsa yotsogolera angelo amphamvu mamiliyoni ambiri pochotsa ulamuliro wa anthu komanso pochotsa zinthu zoipa padziko lapansi. (Miy. 2:21, 22; 2 Ates. 1:6-9; Chiv. 19:11-21; 20:1-3) Kenako, Ufumu wakumwamba ndi umene uzidzalamulira dziko lonse lapansi.—Chiv. 11:15.
KODI KUZINDIKIRA UDINDO WAKE KUMATANTHAUZA CHIYANI?
8 Yesu Khristu, yemwe ndi chitsanzo chathu, ndi wangwiro ndipo wapatsidwa udindo woti azitisamalira. Kuti tipitirize kusamaliridwa mwachikondi tiyenera kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ndiponso tiyenera kuyendabe ndi gulu lake limene likupita patsogolo.
9 Otsatira a Yesu a m’nthawi ya atumwi ankazindikira udindo umene Khristu anapatsidwa ndi Mulungu. Anasonyeza zimenezi pogwira ntchito mogwirizana ndipo ankatsatira malangizo amene Khristu ankawapatsa kudzera mwa mzimu woyera. (Mac. 15:12-21) Pofotokoza za mgwirizano womwe unalipo mu mpingo wa Akhristu odzozedwa, mtumwi Paulo analemba kuti: “Polankhula zoona, tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzera m’chikondi, pansi pa iye amene ndi mutu, Khristu. Kuchokera kwa iye, thupi lonselo limakula podzimanga lokha mwachikondi, pokhala lolumikizika bwino ndi logwirizana mwa mfundo iliyonse yogwira ntchito yake yofunikira, malinga ndi ntchito yoyenerera ya chiwalo chilichonse.”—Aef. 4:15, 16.
10 Aliyense mu mpingo akamagwirizana ndi ena komanso akamatsatira malamulo a Khristu monga Mutu, mpingo umakula ndiponso anthu ake amakhala achikondi chomwe “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”—Yoh. 10:16; Akol. 3:14; 1 Akor. 12:14-26.
11 Zinthu zimene zikuchitika padzikoli zomwe zikukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo, zikusonyezeratu kuti kuyambira mu 1914, Yesu Khristu anapatsidwa Ufumu. Panopa akulamulira pakati pa adani ake. (Sal. 2:1-12; 110:1, 2) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani kwa anthu amene akukhala padzikoli? Zikusonyeza kuti posachedwapa Yesu adzasonyeza mphamvu zake monga Mfumu ya mafumu komanso Mbuye wa ambuye popereka chiweruzo cha Mulungu kwa adani ake. (Chiv. 11:15; 12:10; 19:16) Zimenezi zikadzachitika, Yehova adzakhala kuti wakwaniritsa lonjezo limene anapereka anthu oyambirira atachimwa, loti adzapulumutsa anthu amene amamumvera. (Mat. 25:34) Tikusangalala kwambiri chifukwa choti tazindikira udindo umene Khristu anapatsidwa ndi Mulungu. Choncho, tiyeni tipitirize kukhala ogwirizana pogwira ntchito yolalikira padziko lonse imene ikutsogoleredwa ndi Khristu m’masiku otsiriza ano.