Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 7/15 tsamba 9-14
  • Musaleme Pakuchita Zabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musaleme Pakuchita Zabwino
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Munda Ndiwo Dziko Lapansi”
  • Mmene Mungachitire Ntchitoyo
  • Mkhalidwe Lerolino
  • Kusungirira Mkhalidwe Wabwino
  • Chifukwa Chimene Tifunikira “Kupitiriza Kulankhula”
  • “Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzira Anga”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
  • “Tafola Gawo Lathu Kambirimbiri!”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • “Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Perekani Chisamaliro Chokhazikika ku Chiphunzitso Chanu
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 7/15 tsamba 9-14

Musaleme Pakuchita Zabwino

“Koma tisaleme pakuchita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.”​—AGALATIYA 6:9.

1. Ndi ntchito yotani imene Yesu anapereka kwa otsatira ake?

NDI ntchito yabwino chotani nanga imene Akristu amaichita monga mbali ya kulambira kwawo! Iyo yaphatikizidwa mu lamulo lomvekera: “Chifukwa chake mukani ndi kupanga ophunzira a anthu a mitundu yonse, kuwabatiza iwo . . . , kuwaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu. Ndipo, tawonani! Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse kufikira chimaliziro cha pansi pano.” (Mateyu 28:19, 20) Anali Yesu Kristu iyemwini yemwe anapatsa ophunzira ake ntchito ya kuchita ntchito yophunzitsa ya dziko lonse.

2. (a) Nchifukwa ninji tinganene kuti kupanga ophunzira kunali ntchito yofunika koposa ndipo yabwino? (b) Ndi zifuno zotani zimene ntchito yopanga ophunzira imatumikira?

2 Popeza ntchito yopanga ophunzirayo inali imodzi ya ndemanga zomalizira zimene Yesu anapanga kwa ophunzira ake oyambirira asanakwere kupita kumwamba, kodi iyo sinali ntchito yofunika koposa? Inde, chifukwa kukwaniritsa iyo kukapulumutsa miyoyo. (1 Timoteo 4:16) Chimenecho chimaipangitsa iyo kukhala ntchito yabwino. Imapereka maphunziro abwino a Baibulo kwa awo olabadira uthenga wa Ufumu, ndipo ntchito yolalikira imaika chizindikiro pa osavomereza aliwonse. (Luka 10:10, 11) Chotero, kuchita kwawo ntchito imeneyi kumazindikiritsa Akristu owona mongadi mmene kumachitira kugwirizana kwawo ndi ziphunzitso zina zonse za Yesu.​—Yohane 8:31.

3. (a) Ndimotani mmene ophunzira a Yesu anavomerezera ku chitsanzo chake chaumwini ndi lamulo? (b) Ndi mkhalidwe wotani umene Yesu anamangirira mwa ophunzira ake?

3 Monga Mphunzitsi Wamkulu, Yesu anakhazikitsa chitsanzo chabwino koposa kaamba ka atsatiri ake. Iye anaphunzitsa mwapoyera ndi kupanga ophunzira mwa “kulalikira mbiri yabwino ya ufumu.” (Mateyu 9:35) M’kutsanzira iye, otsatira atsopanowo iwo eni anakhala opanga ophunzira, popeza wophunzira wowona ali “iye wolandira ndi kuthandiza m’kubukitsa ziphunzitso za wina.” Poyambirira, ntchito yawo yopanga ophunzira inalekezera kwa Ayuda ndi otembenuzidwira ku chiyuda. Mosasamala kanthu za chivomerezo choipa m’munda umenewo, ngakhale kuli tero, kodi otsatira a Yesu anachita lamulo lake la “kupitirizabe” “osalema”? Nkulekelanji, inde, iwo anapita “ku nkhosa zosokera za banja la Israyeli” kufikira Akunja oyamba anakhala akhulupiriri mu 36 C.E. (Mateyu 10:5, 6; Machitidwe 5:42) Chinanenedwa kuti ophunzirawo “anadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso [chawo].” (Machitidwe 5:28) Iwo sanaleke ntchito yawo yabwino. M’malomwake, iwo mokhulupirika anaiwona kufikira kumapeto.

“Munda Ndiwo Dziko Lapansi”

4. Kodi unali ndi mkhalidwe wotani umene atsatiri a Yesu analondolera gawo lawo lofutukulidwa?

4 Yesu anasonyeza kuti munda ukaphatikizapo “anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 28:19) M’fanizo lonena za kufesa mbewu ya Ufumu, iye ananena kuti: “Munda ndiwo dziko lapansi.” (Mateyu 13:38) Chotero, Akristu akakhala “mboni” za Ufumu za iye kulikonse. Iwo kachiŵirinso “akapita mopitiriza,” pa nthaŵi ino “kumalekezero ake a dziko lapansi.” (Machitidwe 1:8) Mtumwi Paulo anali “wotanganitsidwa kotheratu ndi mawu,” ndipo tingakhale otsimikizira kuti Akristu ena anateronso.​—Machitidwe 18:5, NW.

5. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuti iye anayembekezera ophunzira ake kukhala otanganitsidwa kotheratu ndi ntchito yochitira umboni kufikira mapeto a dongosolo lino?

5 Yesu anayembekezera ntchito yochitira umboni kutanganitsa Akristu kotheratu kufikira mapeto a dongosolo lino a kachitidwe ka zinthu. Ichi chikusonyezedwa ndi chimene iye ananeneratu ponena za utumiki wa Chikristu ndi gawo limene ukakwaniritsa. Yesu ananena kuti: “Mbiri imeneyi yabwino ya ufumu idzalalikidwa pa dziko lonse lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”​—Mateyu 24:14.

6. Ndi kwa utali wotani umene ntchito yolalikira Ufumu ikachitidwa, ndipo ndimotani mmene chimenechi chiyenera kuyambukirira mkhalidwe wathu kulinga ku iyo?

6 Pamene Yesu anapereka lamulo lakudziloŵetsa mu ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira pa dziko lonse lapansi, iye anadziŵa kuti ntchito yabwino imeneyo tsiku lina ikafika pachimake, monga mmene inachitira m’munda wa Chiyuda. Koma ikakwaniritsa chifuno chake. “Ndipo pomwepo,” monga mmene iye ananenera, “chidzafika chimaliziro.” Chotero, kufikira chimaliziro, Mboni za Yehova mwachidaliro ndipo mwachimwemwe zikupitiriza mu ntchito yogawiridwayo. Icho chimawathandiza iwo kupitiriza mu ntchitoyo m’tsiku lathu kufikira itamalizidwa.

Mmene Mungachitire Ntchitoyo

7. Ndi mutu wotani umene unazindikiritsa utumiki wa Yesu ndi uja wa ophunzira ake?

7 Yesu anaphunzitsa ophunzira ake oyamba mmene akachitira utumiki wawo wapoyera. Iwo mwachangu anavomereza ku lamulo lake lakuti “mukani.” Pamene anali kuwaphunzitsa iwo kaamba ka ntchito yawo yochitira umboni, Yesu ananena kuti: “Ndipo pamene muli kupita, lalikirani kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’” (Mateyu 10:7) Chimenecho chinapatsa uthenga wawo mutu wa Ufumu umodzimodziwo womwe unazindikiritsa utumiki wake. Ikakhala mbiri yabwino kwa anthu owona mtima. Pamene otsatira a Yesu anayamba ntchito yawo, kodi iye anaisiya? Ayi, ndithudi, popeza “pamene Yesu anatha kuwafotokozera ophunzira ake khumi ndi aŵiri, iye anachokera kumeneko kukaphunzitsa ndi kukalalikira m’midzi mwawo.”​—Mateyu 11:1.

8. (a) Ndi kuti ndipo ndimotani mmene olalikira Ufumu amayenera kupangira kafikiridwe kawo? (b) Nchifukwa ninji chiri choyenerera kutenga mbiri yabwino ku nyumba za anthu? (c) Ndi mwaŵi wotani umene ulipo m’kupatsa moni mwininyumba moyenerera?

8 Ndi kuti ndipo ndimotani mmene olengeza Ufumu amenewa akanapanga kafikiridwe kawo? Yesu anawauza iwo: “Polowa m’nyumba, muwalankhule.” (Mateyu 10:12) Kupita ku nyumba ya munthu ndi mbiri yabwino kumalemekeza mwininyumbayo, kumpatsa iye mwaŵi wa kuchita ndi uthenga wa Ufumu pa mabwalo a nyumba yake. Siziri kokha mitundu yamwambo ndi njira zolandiridwa zopatsira moni zaulemu ndi zosonyeza kulingalira za kuyambira kukambitsirana koma palinso mwaŵi wofunika kupezedwa kuchokera ku kukhala waubwenzi ndi kupatsa moni kwachimwemwe kutembenuza kuitanira kosaitanidwa kukhala kolandiridwa. (Yerekezani ndi Mateyu 28:9; Luka 1:28.) Kamvekedwe ka liwu ndi kayankhidwe ka munthu pa khomo kamakuuzani inu zambiri ponena za mkhalidwe wake wamwamuna kapena wamkazi. Mufunikira kudziŵa chimenecho musanapitirize chifukwa chidziŵitso choterocho chimachipangitsa icho kukhala chopepuka kusinthira ndemanga yanu ku zosowa za mwininyumbayo.​—Yerekezani ndi Machitidwe 22:1, 2; 23:6.

9. Nchiyani chimene chimasonyeza kuti si onse amene adzamvetsera ku uthenga wa Ufumu ndi chiyamikiro, ndipo nchiyani chimene chinayenera kukhala chivomerezo kwa awo amene sakasonyeza chikondwerero mu iwo?

9 Yesu analola ophunzira ake kudziŵa kuti si anthu onse m’gawo amene akavomereza mwachiyanjo. Iye ananena kuti: “Ndipo m’mzinda uliwonse kapena m’mudzi mukalowamo, mufunitse amene ali woyenera.” Ngati onse anayenera kulandira uthenga wa Ufumu, sipakanakhala chifukwa cha kugwiritsira ntchito mawu akuti “mufunitse.” Nchiyani chimene chikakhala chivomerezo cha awo amene sanasonyeze chikondwerero mu uthengawo? “Ndipo yemwe sadzakulandirani inu kapena kusamva mawu anu, pamene muli kutuluka m’nyumbayo kapena m’mudzimo, sansani fumbi m’mapazi anu,” kuchoka mu mtendere ndi kusiya zotulukapo zake ku chiŵeruzo cha Yehova.​—Mateyu 10:11, 14.

Mkhalidwe Lerolino

10. Nchiyani chimene chakhala chikunenedwa ponena za ntchito yolalikira Ufumu ya Mboni za Yehova?

10 M’kugwirizana mokhulupirika ndi ntchito ya Chikristu, Mboni za Yehova zikukuta dziko lapansi ndi uthenga wa Ufumu. Chotero, A. P. Wisse, wolemba nkhani m’nyuzipepala mu Netherlands, anachitira ndemanga kuti: “Iwo ali osiyana ndi anthu ena. Mbali ya kusiyana kumeneku iri chotulukapo cha kulengeza kwawo kokangalika. Iwo amawona Chikristu chowona osati monga chipembedzo chokhala ndi ma cathedral, ndi ophunzira maphunziro a chipembedzo omwe aliyense ali ndi malo ake otsimikizirika ndiponso amene chipembedzo chake sichimafunsa zambiri kuchokera kwa iye koposa kumvetsera. Iwo amalankhula ndi kumasuka kwa Paulo kwa aliyense amene angamvetsere.” Changu choterocho kaamba ka utumiki ndithudi chadalitsidwa ndi Yehova Mulungu.

11, 12. (a) Ndi zotulukapo zotani zimene zatulutsidwa mu utumiki m’zaka za posachedwapa? (b) Pamene tikukula m’ziŵerengero, nchiyani chimene chikuchitika ku gawo lomwe liripo limene timalalikira? (c) Ndi mafunso otani amene amadzutsidwa?

11 Olengeza Ufumu oposa 3,000,000 tsopano akugwira ntchito mwachangu m’maiko 210. Tikuwona kuwonjezereka kwabwino mwa ophunzira atsopano​—1,246,204 akumabatizidwa mkati mwa zaka zisanu ndi ziŵiri zapita. Dalitso la Yehova pa kuyesayesa kwakhama liri lowonekeratu. (Yesaya 60:8-10, 22) Nkulekelanji, popeza m’chifupifupi maiko 40 ndi zisumbu, pali Mboni imodzi kwa nzika 300 zirizonse kapena ocheperapo, kapena mmodzi ku chifupifupi mabanja 100! M’kuwonjezerapo, m’malo ena a maiko onga ngati Canada ndi Guadeloupe, chiŵerengerocho chiri Mboni imodzi ku anthu 45 kapena 50 m’gawo la mpingo​—kokha chifupifupi nyumba 15 kapena zocheperapo kaamba ka wofalitsa aliyense kuitanirapo! Ambiri a magawo amenewa amakwaniritsidwa mwezi uliwonse. Ngakhale m’maiko mmene muli ziŵerengero zokulirapo, madera ena a m’tauni akupeza kukwaniritsidwa kobwerezabwereza m’ntchito yathu yochitira umboni. Mu Seoul, Republic la Korea, magawo ena mu mzinda amagwira ntchito masiku asanu aliwonse! Pamene tikukula m’chiŵerengero, ndipo pamene Mboni zowonjezerekawonjezereka zitenga ntchito ya upainiya ndi upainiya wothandizira, tidzakhala tikuitanira pamakomo a anansi athu ndi kubwerezabwereza kowonjezereka. Kodi chimenecho chimabweretsa vuto?

12 Chiyenera kuvomerezedwa kuti pali mavuto m’madera ena, ponse paŵiri kwa Mboni za Yehova ndi kwa awo pa amene timaitanirapo. Kuwonjezera ku mavutowo kuli kukula kwa kusakondweretsedwa pakati pa anthu m’maiko ambiri. Chabwino, pamene tikuwonjezereka m’chiŵerengero, kodi mwapang’onopang’ono timaleka kuchita ntchito yabwino? Kodi timamaliza kuti ntchito yathu iri pafupi kutha ndipo kuti ‘tafunitsitsa’ kale onse omwe akavomereza ndi kukhala ophunzira? Kodi inu mwaumwini mukutopa ndipo mwinamwake kukwiyitsidwa pa kuitanira kwa anthu osavomereza amodzimodziwo? Nchiyani chimene chingachitidwe kuti tisungirire mlingo wapamwamba koposa wa ntchito yathu?

Kusungirira Mkhalidwe Wabwino

13, 14. (a) Ndimotani mmene tiyenera kuwonera mikhalidwe yomakula ya kugwira ntchito m’gawo mobwerezabwereza? (b) Nchifukwa ninji sitiletsedwa ndi awo amene amakhala “osavomereza”? (c) Ndimotani mmene tingatsatirire chitsanzo cha atumwi m’kuyang’anizana ndi awo amene amakana kuitanira kwathu?

13 Yankho kwakukulukulu limakhudza mkhalidwe wathu monga mboni za Yehova. Kaamba ka chinthu chimodzi, lolani kuti ife nthaŵi zonse tiyang’ane ku mbali yowala. Kukwaniritsa gawo kobwerezabwereza chifukwa cha kukula kwa mlingo wa ofalitsa ku chiŵerengero cha anthu kunali kotsimikizirika kukula m’malo ambiri pamene ntchito yathu ikufika pachimake. Koma kodi ife sitinapempherere ponena za ichi? (2 Atesalonika 3:1) Chimene tikuwona tsopano chiyenera kutipangitsa ife kusangalala ndipo chiyenera kutitsimikizira ife kuti tiri m’mbali zomalizira za ntchito yopanga ophunzira! Ufumu ulidi kulalikidwa, monga mmene Yesu ananeneratu. Ndipo ngakhale m’malo mmene anthu ‘sadzamvetsera ku mawu athu,’ iwo akudziŵitsidwa kupyolera mwa ntchito yathu yolalikira Ufumu. Kumbukirani, pambali pa kupanga ophunzira, tikulengeza mbiri yabwino “kaamba ka umboni.”​—Mateyu 10:14; 24:14.

14 M’kuwonjezerapo, chiyenera kuyembekezeredwa kuti chiŵerengero chomakula chidzakana uthenga wa Ufumu pamene mapeto akuyandikira. Zoneneratu ziri zachiwonekere, ndipo zokumana nazo za ponse paŵiri Yesu ndi Paulo zimatitsimikizira ife kuti pakakhala awo amene akakhala “osavomereza” ndi amene mitima yawo ikakhala “yosalandira.” Chotero, pa nthaŵi ino tiyenera kukhala osamalitsa kuti ife sitiri osavomereza ku ntchito yathu. Ngakhale kwa awo amene ali osavomereza, tiyenera kupita “mobwerezabwereza.” (Yesaya 6:9-11; Mateyu 13:14, 15; Miyambo 10:21) Zowona, chimatenga kulimba mtima kupita kaŵirikaŵiri kwa anthu omwe amakana kuitanira kwathu. Ngakhale kuli tero, palibe mkhalidwe wa gawo kulikonse umene uyenera kunena kwa ife, ‘Lekani kulankhula.’ M’malomwake, mofanana ndi atumwi, tiyenera kupemphera kaamba ka kulimba mtima kuti “tipitirize kulankhula”​—mosasamala kanthu za chitsutso kapena nkhalwe​—kufikira ntchitoyo itachitidwa.​—Machitidwe 4:18-20, 24-31.

15. Ndi chilimbikitso chotani chimene chaperekedwa pa Agalatiya 6:9, ndipo ndimotani mmene chiyenera kuyambukirira kawonedwe kathu ka kuchezera anansi athu ndi mbiri yabwino?

15 Kwakukulukulu, pali kokha mitundu iŵiri ya anthu m’magawo athu onse​—awo amene pa nthaŵi ino ali okondweretsedwa ndi awo amene sali. Chotero, tifunikira kupitiriza ntchito yathu ya ‘kufunitsitsa oyenera.’ Kuchita ichi kuli pakati pa ntchito zambiri zabwino koposa zimene tiyenera kutulutsa monga Akristu kusonyeza chikondi chathu kaamba ka Yehova ndi kukhulupirika kwathu kwa iye. Chotero, “tisaleme pa kuchita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.” (Agalatiya 6:9) Popeza tsopano tiri pafupi kwenikweni ndi mapeto a dongosolo iri, iyo si nthaŵi ya kuleka kapena kulema ndi kuchezera anansi athu ndi mbiri yabwino ya Ufumu. Yehova sananene kuti ntchito yatsirizidwa.

Chifukwa Chimene Tifunikira “Kupitiriza Kulankhula”

16. (a) Ndi iti imene iri ina ya mikhalidwe imene ingasinthe chivomerezo cha anthu m’gawo? (b) Ndi zitsanzo zotani za kumaloko za kasinthidwe m’kuyankha zimene mungapereke?

16 Tidzathandizidwanso kusungirira mkhalidwe wabwino ngati tikumbukira kuti kukhulupirika kwa Yehova kumasonyezedwa ndi machitachita a kulalikira Ufumu achangu. M’kuwonjezerapo, magawo amapitirizabe kusintha m’njira zosiyanasiyana. Anthu amasamuka, kapena mikhalidwe yawo ingasinthe. Iwo angakhale anali osakondweretsedwa pa nthaŵi yomalizira imene tinaitanira, koma kutaya kwa ntchito, imfa ya wokondedwa, kusintha kokulira m’kulimbana pakati pa mphamvu zazikulu, matenda akulu​—masinthidwe awa ndi ena angatanthauze kuti iwo adzakhala ovomereza nthaŵi yotsatira imene tidzaitanira. Ena, pokhala ataphunzira kuti bwenzi kapena wokondedwa wakhala mmodzi wa Mboni za Yehova, angafune tsopano kulankhula ndi ife kuphunzira zimene timakhulupirira kuti zinatulutsa kusintha kumeneku.

17. Ndimotani mmene ena tsopano akuvomerezera ku uthenga wa Ufumu? Perekani zitsanzo zirizonse za kumaloko.

17 Kumbukirani, kachiŵirinso, kuti awo amene akula m’zaka za posachedwapa tsopano ali ndi mabanja, akutenga moyo mosamalitsa, ndipo akufunsa mafunso amene Mawu a Mulungu okha angayankhe. Mwachitsanzo, mayi wachichepere anaitana Mboni ziŵiri m’nyumba yake ndi kunena kuti: ‘Monga mtsikana wachichepere, sindinamvetsetse chifukwa chimene mayi anga anathamangitsira Mboni ndi kuziwuza izo kuti sanali okondweretsedwa, pamene zonse zimene munafuna kuchita zinali kulankhula ponena za Baibulo. Ndinachipanga m’malingaliro anga pa nthaŵiyo kuti pamene ndikula, kukwatiwa, ndi kukhala ndi nyumba yanga, ndidzafunsa Mboni za Yehova kubwera ndi kulongosola Baibulo kwa ine.’

18. Ndimotani mmene kusintha kwa kawonekedwe ka chipembedzo kukuyambukirira gawo mu limene timalalikira ndi kuphunzitsa?

18 Kodi mwazindikira kuti anthu ena omwe sanalankhule kwa ife kwa zaka ndi kulingalira kuti anali “opulumutsidwa” tsopano akutifunsa ife mafunso mowona mtima? Nchifukwa ninji? Kusintha kwachitika m’kulingalira kwawo kwa chipembedzo. Iwo akunena kuti akhala okhumudwitsidwa ndi oipidwa ndi kuvumbulutsidwa kwa mkhalidwe woipa wa chisembwere, machitachita a ndale zadziko, ndi kuwononga ndalama za matchalitchi kwa ena a alengezi otchuka a pa wailesi ya kanema amene iwo poyambapo anawakhulupirira. Mwachidziŵikire, padzakhala zambiri za ichi pamene mikhalidwe mkati mwa Babulo Wamkulu ikupitirizabe kunyonyotsoka kufikira ku nthaŵi ya chiwonongeko chake.​—Chivumbulutso 18:1-8.

19, 20. Nchiyani chimene chikusonyeza chifukwa chimene sitifunikira kukhumudwitsidwa ponena za kupita mobwerezabwereza kwa anthu omwe amakana uthengawo?

19 Mwa njira iriyonse, sitiyenera kukhala okhumudwitsidwa pamene anthu ambiri ali osavomereza. Pambuyo pa kuwasiya iwo, mwinamwake tidakali m’malingaliro awo. Mu Canada mwininyumba mmodzi amene anachezeredwa ndi Mboni ziŵiri anachipanga icho kukhala chomvekera kuti sanali wokondweretsedwa. Pambuyo pake, iye anayamba kulingalira ponena za zimene ananena ndipo anafuna kuwapeza iwo kotero kuti ayankhe mafunso amene anadzutsidwa m’malingaliro ake. Iye analowa m’galimoto yake ndi kuyamba kufunafuna kaamba ka iwo kukwera ndi kutsika m’makwalala a m’mudzi wake koma osakhoza kuwapeza iwo. Kodi iye analeka? Ayi, anaima pa nyumba ya mnzake ndi kufunsa ngati anafikako kumeneko. Iwo sanafike, koma bwenzilo linanena kuti kunali Mboni pa malo ake a ntchito ndipo adzagwirizanitsa mkazi wokondwererayo ndi Mboniyo. Chotulukapo chake chinali mipambo ya maulendo pa nyumba ya munthu wokondwererayo, kumene anaitanira mabwenzi, anansi, achibale, ndi ogwira nawo ntchito. Anthu ambiri kufika ku 15 anapezekapo pa nthaŵi zina, ndipo mabukhu 430 ndi maBaibulo limodzinso ndi magazini 2,015 anagawiridwa.

20 Ambiri amayamikira kuitanira kwathu. M’kalata ku ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society, mkazi wina ananena kuti: “Ndikuyamikani kaamba ka kuika kudzipereka kokulira m’mitima ya awo a chikhulupiriro chanu. Ndikuyamikani kaamba ka kufika kuno . . . ndi kugawana chikondi cha Ambuye ndi ena. Kachitidwe kopepuka kameneko kamachita zambiri koposa kwa ena. . . . Ngakhale kuti ena amakhala ankhalwe, ena osiyanako, ndipo ena ovomereza, . . . icho ndithudi chimapanga dziko labwino kukhala ndi wina akumabwera kukukumbutsa zinthu zauzimu. Ndimachipeza chinthuchi kukhala chabwino, kulankhula za Ambuye wina ndi mnzake.” M’kalata ina, mwininyumba anatifunsa ife ‘kusalema ndi anthu,’ mosasamala kanthu ndi mmene adzachitira nafe. “Koma tisaleme pakuchita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.” (Agalatiya 6:9) Ntchito iyi iri ndi chivomerezo ndi dalitso la Yehova, ndipo kutengamo mbali kwathu kumatsimikizira chikondi chathu kaamba ka iye ndi mnansi wathu. (Mateyu 22:37-39) Chotero lolani kuti ife tichite ntchitoyo kufikira mapeto.​—Yerekezani ndi Afilipi 1:6.

21. (a) Ndi kuti, moyenerera, kumene kuli mbali ya chitokoso m’kupita mobwerezabwereza ku magawo ogwiridwa ntchito kaŵirikaŵiri? (b) Nchiyani chimene tidzakambitsirana m’nkhani yotsatira?

21 Tiyenera kuyang’anizana ndi chenicheni chakuti nthaŵi zonse sangakhale anthu amene amachipangitsa icho kuwoneka chovuta kugwira ntchito m’gawo mobwerezabwereza. Nthaŵi zina timakhala ife enife. Kodi timayamba ndi malingaliro oipa, kudzimva kuti tikudziŵa anthu onse ndipo zimene kayankhidwe kawo kadzakhala? Chimenecho chingayambukire mkhalidwe wathu ndipo mwachidziŵikire kamvekedwe kathu ka liwu ndi kalongosoledwe ka pamaso. Kodi tidakagwiritsira ntchito njira zimodzimodzizo ndi mawu amene takhala tikugwiritsira ntchito kwa zaka zambiri? Tsopano popeza gawo likusintha, chimene poyambapo chinali ndi chipambano tsopano sichingakhale chofikira ‘oyenerera.’ Mwinamwake tifunikira kafikiridwe katsopano ndi kayang’anidwe katsopano ka ntchito yathu. Potsatira, tiyeni tiwone zimene tingachite kotero kuti ‘tisaleme koma kuti titute m’nyengo yake.’

Kodi Mungalongosole?

◻ Nchifukwa ninji sitiyenera “kulema” m’kupita kwa anansi athu ndi mbiri yabwino?

◻ Ndani amene anatiwuza ife kupanga ophunzira njira imene timachitira, ndipo nziti zomwe ziri mbali zenizeni za njira imeneyo?

◻ Ndi mkhalidwe wotani umene wakula m’magawo ambiri, ndipo nchiyani chimene chidzatithandiza ife kusungirira mkhalidwe wabwino ponena za mkhalidwe umenewo?

◻ Nchifukwa ninji tiyenera “kupitiriza kulankhula” mbiri yabwino “popanda kuleka”?

[Bokosi patsamba 14]

IFE “SITIDZALEMA” M’KULALIKIRA UFUMU NGATI TIKUMBUKIRA:

◻ Amene anatipatsa ife ntchito ndi malangizo a mmene tingachitire ntchitoyo

◻ Kuti dalitso la Yehova liri pa zimene zachitidwa kale pa dziko lonse

◻ Kusunga mkhalidwe woyenera mosasamala kanthu za “osavomereza” aliwonse

◻ Kupemphera kuti “tipitirize kulankhula” monga mmene anachitira atumwi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena