“Mphindi ya Mtendere” Ili Pafupi!
“Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake; . . . mphindi ya nkhondo ndi mphindi ya mtendere.”—MLALIKI 3:1, 8.
1. Kodi chodabwitsa n’chiyani ponena za nkhondo ndi mtendere m’zaka za zana la 20?
ANTHU ochuluka amafuna atakhala pamtendere, ndipo m’pomveka. Palibe zaka zana zinanso m’mbiri yonse zimene zasoŵa mtendere monga zaka za zana la 20. Koma zimenezi n’zodabwitsa chifukwa chakuti anthu sanayesetsepo kudzetsa mtendere monga momwe achitira m’zaka za zana lino. Mu 1920 bungwe la League of Nations linapangidwa. Mu 1928 pangano lotchedwa Kellogg-Briand Pact, limene buku lina limati ndilo linali “loyerekedwa koposa pa zoyesayesa zonse zofuna kudzetsa mtendere pambuyo pa nkhondo yoyamba yapadziko lonse,” linavomerezedwa “pafupifupi ndi mayiko onse a padziko lapansi . . . kuvomerezana kuti nkhondo isakhalenso njira yothetsera mikangano pakati pa mayiko.” Kenako, mu 1945 bungwe la United Nations linakhazikitsidwa kuti liloŵe m’malo bungwe la League of Nations lomwe linali litatha.
2. Kodi cholinga cha bungwe la United Nations n’chiyani, ndipo kodi lachita zambiri motani?
2 Mofanana ndi bungwe la League of Nations, cholinga cha bungwe la United Nations ndicho kudzetsa mtendere padziko lonse. Koma silinathe kuchita zambiri. Zoona, kulibe kulikonse padziko lapansi kumene kukuchitika nkhondo yaikulu yofanana ndi nkhondo ziŵirizo zapadziko lonse. Komabe, nkhondo zing’onozing’ono zambirimbiri zikusoŵetsa anthu zikwi mazana ambiri mtendere wa maganizo, kuwawonongera katundu, ndiponso nthaŵi zambiri kuwapha. Kodi tingayesere n’komwe kuyembekeza kuti bungwe la United Nations lingadzasinthe zaka za zana la 21 kukhala “mphindi ya mtendere”?
Maziko a Mtendere Weniweni
3. N’chifukwa chiyani mtendere weniweni sungakhalepo ngati palinso udani?
3 Mtendere pakati pa anthu ndi mayiko sumangofuna kulolerana kokha. Kodi munthu angakhaledi mwamtendere ndi munthu amene amadana naye? N’zosatheka malinga ndi 1 Yohane 3:15: “Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu.” Monga momwe zochitika m’mbiri yaposachedwapa zasonyezera, udani waukulu umapangitsa anthu odanawo kuchitana chiwawa mosavuta.
4. Kodi ndani okha amene angakhale ndi mtendere, ndipo chifukwa chiyani?
4 Popeza kuti Yehova ndi “Mulungu wa mtendere,” anthu amene amakonda Mulungu ndipo amalemekezadi mapulinsipulo ake olungama ndi okhawo amene amakhala ndi mtendere. Inde, Yehova sapereka mtendere kwa wina aliyense. “Palibe mtendere, ati Mulungu wanga, kwa oipa.” Zili choncho chifukwa chakuti anthu oipa amakana kutsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, umene chipatso chake ndicho mtendere.—Aroma 15:33; Yesaya 57:21; Agalatiya 5:22.
5. Kodi n’chiyani chosatheka kwa Akristu enieni ngakhale kuchiganizira?
5 Kuthira nkhondo anthu anzawo—monga momwe achitira nthaŵi zambiri enawo amene amati ndi Akristu, makamaka m’zaka za zana la 20, ndi chinthu chosatheka kwa Akristu enieni ngakhale kuchiganizira. (Yakobo 4:1-4) Inde, iwo akuthira nkhondo ziphunzitso zosokoneza anthu ponena za Mulungu, koma nkhondo imeneyi ikumenyedwa kuti ithandize anthu, osati kuwavulaza. Kuzunza ena chifukwa cha nkhani zachipembedzo kapena chifukwa cha zifukwa zautundu n’kosemphana kotheratu ndi Chikristu chenicheni. “Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza,” anatero Paulo polangiza Akristu a ku Roma, “khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”—Aroma 12:17-19; 2 Timoteo 2:24, 25.
6. Kodi n’kuti kokha kumene kungapezeke mtendere weniweni lerolino?
6 Lerolino, mtendere wochokera kwa Mulungu umangopezeka pakati pa olambira oona a Yehova Mulungu. (Salmo 119:165; Yesaya 48:18) Palibe nkhani zandale zimene zimasokoneza umodzi wawo, popeza kuti kulikonse saloŵa m’ndale. (Yohane 15:19; 17:14) Chifukwa chakuti ali ‘omangika mumtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho,’ palibe kusiyana malingaliro pankhani zachipembedzo kumene kumasokoneza mtendere wawo. (1 Akorinto 1:10) Mtendere umene Mboni za Yehova zili nawo ndi chozizwitsa chamakono, woperekedwa ndi Mulungu monga mwa lonjezo lake lakuti: “Ndidzakuikira akapitawo amtendere, ndi oyang’anira ntchito achilungamo.”—Yesaya 60:17; Ahebri 8:10.
“Mphindi ya Nkhondo”—Chifukwa Chiyani?
7, 8. (a) Ngakhale kuti Mboni za Yehova zili pamtendere, kodi nthaŵi ino zimaiona motani? (b) Kodi chida chachikulu cha nkhondo ya Mkristu n’chiyani?
7 Ngakhale kuti Mboni za Yehova zili pamtendere, zimaonabe nthaŵi ino kukhala makamaka “mphindi ya nkhondo.” Si nkhondo yeniyeni iyayi, popeza kuti kukakamiza ena kuti alandire uthenga wa m’Baibulo pogwiritsa ntchito zida zenizeni kungakhale kosemphana ndi chiitano cha Mulungu chakuti ‘iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.’ (Chivumbulutso 22:17) Sitikakamiza anthu kutembenuka! Nkhondo imene Mboni za Yehova zikumenya ndi yauzimu basi. Paulo analemba kuti: “Zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga.”—2 Akorinto 10:4; 1 Timoteo 1:18.
8 Chida chachikulu mwa “zida za nkhondo yathu” ndi “lupanga la Mzimu, ndilo Mawu a Mulungu.” (Aefeso 6:17) Lupanga limeneli ndi lamphamvu. “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugaŵira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:12) Mwa kugwiritsa ntchito lupanga limeneli, Akristu amatha kugwetsa “matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziŵitso cha Mulungu.” (2 Akorinto 10:5) Limawatheketsa kuvumbula ziphunzitso zonama, machitidwe ovulaza, malingaliro osonyeza nzeru zaumunthu m’malo mwa nzeru zaumulungu.—1 Akorinto 2:6-8; Aefeso 6:11-13.
9. N’chifukwa chiyani sitingasiye kulimbana ndi thupi lauchimo?
9 Mtundu winanso wa nkhondo yauzimu ndiyo nkhondo yolimbana ndi thupi lauchimo. Akristu amatsatira chitsanzo cha Paulo, amene anavomereza kuti: “Ndipumphuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.” (1 Akorinto 9:27) Akristu a ku Kolose analangizidwa kuti afetse “ziŵalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano.” (Akolose 3:5) Ndipo wolemba Baibulo Yuda analimbikitsa Akristu kuti ‘alimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.’ (Yuda 3) N’chifukwa chiyani tiyenera kutero? Paulo anayankha kuti: “Ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo.” (Aroma 8:13) Chifukwa cha mawu ameneŵa osapita m’mbali, sitingasiye kumenyana nkhondo ndi zizoloŵezi zoipa.
10. N’chiyani chinachitika mu 1914, chimene chidzachititsa chiyani posachedwapa?
10 Koma chifukwa chinanso chimene tingaonere nthaŵi ino kukhala nthaŵi yankhondo n’chakuti “tsiku lakubwezera la Mulungu wathu” lili pafupi. (Yesaya 61:1, 2) Mu 1914, nthaŵi yoikidwiratu ya Yehova inafika yoti akhazikitse Ufumu Waumesiya ndi kuupatsa mphamvu yoti uthire nkhondo yamphamvu pa dongosolo la Satana. Nthaŵi yoyesa ulamuliro wa anthu popanda chitsogozo cha Mulungu inatha panthaŵiyo. M’malo molandira Wolamulira Waumesiya wa Mulungu, anthu ochuluka akum’kanabe, monga momwe ochuluka anachitira m’zaka za zana loyamba. (Machitidwe 28:27) Ndiyeno, chifukwa cha otsutsa Ufumu ameneŵa, Kristu sangachitire mwina koma ‘kuchita ufumu [“kugonjetsa,” NW] pakati pa adani [ake].’ (Salmo 110:2) Ndipo Chivumbulutso 6:2 chimalonjeza kuti iye ‘adzalakika.’ Adzachita zimenezi mkati mwa “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse . . . , [y]otchedwa m’Chihebri Harmagedo.”—Chivumbulutso 16:14, 16.
Inoyi Ndi “Mphindi Yakulankhula”
11. N’chifukwa chiyani Yehova waleza mtima chotere, koma padzakhalabe chiyani?
11 Kuyambira pamene zochitika za anthu zinatembenuka mu 1914, papita zaka 85. Yehova waleza mtima kwambiri ndi anthu. Mboni zake anazisonyeza bwino lomwe za kufunika kwa kuchita machaŵi. Miyoyo ya anthu miyandamiyanda ili pangozi. Makamu ameneŵa ayenera kuchenjezedwa chifukwa “Ambuye . . . safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Ngakhale zili choncho, posachedwapa padzakhala “vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake.” Kenako, onse amene akana dala uthenga wa Ufumu wa Mulungu ‘adzawabwezera chilango’ chimene Yesu adzadzetsa “kwa iwo osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu.”—2 Atesalonika 1:6-9.
12. (a) N’chifukwa chiyani kuyesa kudziŵa pamene chisautso chachikulu chidzayamba kuli kutaya nthaŵi? (b) Kodi Yesu anachenjeza za ngozi yotani pankhani imeneyi?
12 Kodi kuleza mtima kwa Yehovaku kudzatha liti? N’kutaya nthaŵi kuyesa kudziŵa pamene “chisautso chachikulu” chidzayamba. Yesu anafotokoza mosapita mbali kuti: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense.” Komanso analangiza kuti: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu. . . . Khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.” (Mateyu 24:21, 36, 42, 44) Kulongosola bwino mawuŵa, zimenezi zikutanthauza kuti tsiku lililonse tiyenera kumayang’anira zochitika za m’dziko ndi kumasinkhasinkha za kuyambika kwa chisautso chachikulu. (1 Atesalonika 5:1-5) N’zoopsatu kwambiri kumaganiza kuti tingachepetseko changu chathu, kumakhala umene amati moyo wabwino, n’kukhala phee kuti tione mmene zinthu zidzachitikira! Yesu anati: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha.” (Luka 21:34) Tikhale otsimikiza kuti: “Mphepo zinayi” zachiwonongeko zimene panopo zagwiridwa ndi “angelo anayi” a Yehova sizidzagwiridwabe choncho kosatha.—Chivumbulutso 7:1-3.
13. Kodi n’chiyani chimene anthu pafupifupi mamiliyoni asanu ndi imodzi azindikira?
13 Chifukwa cha tsiku lachiweruzo limene likuyandikira mofulumirali, mawu a Solomo onena zoti pali “mphindi yakulankhula” akukhala ndi tanthauzo lapadera. (Mlaliki 3:7) Pozindikira kuti inoyo ndi nthaŵidi yolankhula, Mboni za Yehova pafupifupi mamiliyoni asanu ndi imodzi zikulankhula mwachangu za ulemerero wa uchifumu wa Mulungu ndi kuchenjeza za tsiku lake lodzabwezera chilango. Iwo akudzipereka okha m’tsikuli la chamuna cha Kristu.—Salmo 110:3; 145:10-12.
Awo Amene Amanena za “Mtendere, Pamene Palibe Mtendere”
14. Ndi aneneri onyenga otani amene analiko m’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E.?
14 M’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E., aneneri a Mulunguwo Yeremiya ndi Ezekieli anapereka mauthenga ochokera kwa Mulungu achiweruzo pa Yerusalemu chifukwa cha kupanduka mwa kusamvera Mulungu. Chiwonongeko chimene analoseracho chinachitika mu 607 B.C.E., ngakhale kuti aneneri a Mulunguwo anatsutsidwa ndi atsogoleri achipembedzo otchuka ndi amphamvu. Atsogoleriŵa anapezeka kukhala ‘aneneri opusa [amene] . . . anasokeretsa anthu [a Mulungu], ndi kuti, Mtendere, pokhala palibe mtendere.’—Ezekieli 13:1-16; Yeremiya 6:14, 15; 8:8-12.
15. Kodi aneneri onyenga ofanana alipo lerolino? Fotokozani.
15 Mofanana ndi “aneneri opusawo” a panthaŵiyo, atsogoleri achipembedzo ochulukanso lerolino sakuchenjeza anthu zatsiku la Mulungu lachiweruzo likudzalo. M’malo mwake, akupereka chiyembekezo chakuti pomalizira pake magulu andale adzakhazikitsa mtendere ndi chisungiko. Pofunitsitsa kukondweretsa anthu osati kukondweretsa Mulungu, amauza anthu awo zimene anthuwo amayembekeza kumva m’malo mofotokoza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa ndi kuti Mfumu Yaumesiya posachedwapa idzamalizitsa chilakiko chake. (Danieli 2:44; 2 Timoteo 4:3, 4; Chivumbulutso 6:2) Pokhala aneneri onyenga, iwonso amalankhula za “mtendere, pamene palibe mtendere.” Koma mwadzidzidzi chikhulupiriro chawocho chidzasanduka mantha pamene adzakumana ndi mkwiyo wa Uyo amene am’fotokoza molakwika ndiponso amene dzina lake alidzetsera chitonzo chosaneneka. Atsogoleri a ufumu wapadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, wofotokozedwa m’Baibulo monga mkazi wachigololo, adzakanthidwa pofuula mawu awo osocheza onena za mtendere.—Chivumbulutso 18:7, 8.
16. (a) Kodi Mboni za Yehova zadzidziŵikitsa kukhala anthu otani? (b) Kodi Mboni zimasiyana motani ndi awo amene amafuula kuti “mtendere, pamene palibe mtendere”?
16 Kulimbikira kwa atsogoleri otchuka ndi amphamvu pa lonjezo lawo lachinyengo la mtendere sikumafoola chidaliro cha okhulupirira lonjezo la Mulungu la mtendere weniweni. Kwa zaka zoposa zana limodzi, Mboni za Yehova zadzidziŵikitsa kukhala ochirikiza okhulupirika a Mawu a Mulungu, otsutsa chipembedzo chonyenga olimba mtima, ndi ochirikiza Ufumu wa Mulungu motsimikiza mtima. Popanda kupangitsa anthu kuodzera ndi mawu obwerezabwereza omveka ngati okoma onena za mtendere, iwo amayesetsa mwakhama kuwagalamutsa kuti aone kuti lero ndi nthaŵi ya nkhondo.—Yesaya 56:10-12; Aroma 13:11, 12; 1 Atesalonika 5:6.
Yehova Alankhula
17. Kodi zikutanthauzanji kunena kuti posachedwapa Yehova adzalankhula?
17 Solomo anatinso: “Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse.” (Mlaliki 3:17) Inde, Yehova ali ndi nthaŵi yake pamene adzaweruza chipembedzo chonyenga ndi “mafumu a dziko lapansi . . . [o]tsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake.” (Salmo 2:1-6; Chivumbulutso 16:13-16) Nthaŵi imeneyo ikadzafika, masiku a Yehova okhala “chete” adzakhala atatha. (Salmo 83:1; Yesaya 62:1; Yeremiya 47:6, 7) Kudzera mwa Mfumu yake Yaumesiya, Yesu Kristu, iye ‘adzalankhula’ m’chinenero chokhacho chimene otsutsa ake akuoneka kuti amamva: ‘Yehova adzatuluka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wankhondo; iye adzafuula, inde adzakuwa zolimba; adzachita zamphamvu pa adani ake. Ndakhala nthaŵi yambiri wosalankhula; ndakhala chete ndi kudzithungata ndekha; tsopano ndidzafuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi ŵefuŵefu pamodzi. Ndidzapasula mapiri ndi zitunda, ndi kuumitsa zitsamba zawo zonse; ndi kusandutsa nyanja zisumbu, ndi kuumitsa matamanda. Ndipo ndidzayendetsa akhungu m’khwalala, limene iwo salidziŵa; m’njira zimene iwo sazidziŵa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m’tsogolo mwawo, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzaŵasiya.’—Yesaya 42:13-16.
18. Kodi anthu a Mulungu posachedwapa ‘adzatonthola’ m’lingaliro lotani?
18 Pamene Yehova ‘adzalankhula’ kuchirikiza Umulungu wake, anthu ake sadzafunikiranso kudzilankhulira okha. Idzakhala nthaŵi yawo “yakutonthola.” Mawuŵa adzagwiranso ntchito monga momwe anachitira kwa atumiki a Mulungu m’nthaŵi zakale kuti: “Si kwanu kuchita nkhondo kuno ayi; chirimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu.”—2 Mbiri 20:17.
19. Kodi ndi mwayi wotani umene abale auzimu a Kristu adzakhala nawo posachedwapa?
19 Kudzakhalatu kugonja kochititsa manyazi kwa Satana ndi gulu lake! Abale a Kristu amene alandira ulemererowo adzatengamo mbali m’nkhondo yachilakiko cha chilungamo, mongadi mwa lonjezo lakuti: “Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino.” (Aroma 16:20) Pomalizira pake, nthaŵi ya mtendere yoyembekezedwa kwanthaŵi yaitaliyo idzakhala ili pafupi kwenikweni.
20. Kodi posachedwapa idzakhala mphindi ya chiyani?
20 Onse amene adzapulumuka chisonyezero chachikulu chimenechi cha mphamvu ya Yehova padziko lapansi adzakhalatu ndi moyo wodalitsidwa kwambiri! Pakadzangopita nthaŵi yochepa iwo adzagwirizana ndi amuna ndi akazi okhulupirika akale amene nthaŵi yawo yoikidwiratu youkitsidwa idzakhala itafika. Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi udzakhaladi “mphindi yakubzala . . . , mphindi yakuchiza . . . , mphindi yakumanga . . . , mphindi yakuseka . . . , mphindi yakuvina . . . , mphindi yakufungatirana ndi . . . mphindi yakukonda.” Inde, imeneyo idzakhalanso “mphindi ya mtendere” kosatha!—Mlaliki 3:1-8; Salmo 29:11; 37:11; 72:7.
Kodi Mungayankhe Kuti Bwanji?
◻ Kodi maziko a mtendere wosatha ndi chiyani?
◻ N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimaona nthaŵi ino kukhala “mphindi ya nkhondo”?
◻ Kodi ndi liti pamene anthu a Mulungu ayenera ‘kulankhula,’ ndipo ndi liti pamene ‘adzatonthola’?
◻ Kodi ndi liti pamene Yehova adzalankhula ndiponso adzalankhula motani?
[Bokosi/Zithunzi patsamba 13]
Yehova Ali ndi Nthaŵi Yoikidwiratu
◻ yokopa Gogi kuti afune kuukira anthu a Mulungu.— Ezekieli 38:3, 4, 10-12
◻ yosonkhezera mitima ya olamulira kuti awononge Babulo Wamkulu.—Chivumbulutso 17:15-17; 19:2
◻ yochititsa ukwati wa Mwanawankhosa.—Chivumbulutso 19:6, 7
◻ yoyamba nkhondo ya Harmagedo.—Chivumbulutso 19:11-16, 19-21
◻ yomanga Satana kuti Yesu ayambe Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi.—Chivumbulutso 20:1-3
Zochitika zimenezi zangondandalitsidwa malinga ndi ndondomeko imene Malemba amasonyeza. Ndife otsimikiza kuti zochitika zonse zisanu zidzachitika motsatira mpambo umene Yehova adzausankha komanso panthaŵi yeniyeniyo imene wasankha.
[Zithunzi patsamba 15]
Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi udzakhaladi mphindi . . .
yakuseka . . .
yakufungatirana . . .
yakukonda . . .
yakubzala . . .
yakuvina . . .
yakumanga . . .