Ngati Nkhunda Zoulukira Kuzikwere Zawo
NKHUNDA mwinamwake zinali pakati pa mbalame zoyambirira kufuyidwa ndi munthu. Zaka zikwi zambiri zapitazo, Aigupto—mwaluntha akumakonzekera chakudya cha chaka chonse—anamanga zikwere zankhunda pafupi ndi nyumba zawo. Nyama ya mbalamezo inayamikiridwa kwambiri, ndipo zitosi zake zinagwiritsiridwa ntchito monga ndowe. Podzafika m’Nyengo Yapakati, zikwere zankhunda zinali chuma cholakalakika kwambiri kotero kuti m’maiko ena olemera okha kapena atsogoleri achipembedzo ndiwo amene analoledwa kukhala nazo.
Ngakhale kuti nkhuku tsopano zalowa mmalo mwa nkhunda monga magwero a nyama pamagome ambiri, zikwere zina zankhunda zakalekale zingapezedwebe. Zikwere zojambulidwa panopa zikupezedwa m’Igupto.
Zikumabwerera zonse pamodzi madzulo, mtambo wakuda bii wa mbalame ukutsikira pachikwere chankhunda. Mneneri Wachihebri Yesaya anasonya kuzimenezi pamene anafunsa kuti: “Ndani awa amene auluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda ku mazenera awo?” Monga momwe matembenuzidwe ena amanenera: “Kodi ndani awa amene akuyenda ngati mitambo, amene akuuluka ngati nkhunda ku zikwere zawo?”—Yesaya 60:8; The New English Bible.
Yankho likupezedwa lerolino mwa anthu owopa Mulungu zikwi mazana ambiri amene akusonkhana muunyinji wawo kugulu la Yehova. M’Nyumba Zaufumu za Mboni za Yehova, iwo amaphunzira kuyembekezera Mulungu. (Yesaya 60:9) Pakati pa anthu a Mulungu, iwo amapeza kuti makhalidwe auzimu, chikhulupiriro chamoyo, ndi mayanjano abwino zimapereka lingaliro la mtendere ndi chisungiko zofanana ndi zija zopezedwa ndi nkhunda m’chikwere chake.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.