Kodi Ndani Adzathetsa Chiwawa?
MU September 1999, Mlembi Wamkulu wa United Nations, Kofi Annan, analandira nthumwi za msonkhano wa nambala 54 wapachaka wa General Assembly. Malinga ndi lipoti la mu The Toronto Star, anadzutsa nkhani yothetsa nzeru kwa olamulira a dziko akumati: “Pali anthu ambiri amene akufunikira zambiri osati chabe mawu otonthoza kuchokera ku mayiko onse. Akufunikira pangano lotsimikizika ndi lopitirira lowathandiza kuthetsa chiwawa chopitiriza ndi kuwaika panjira yabwino yopezera chitukuko.”
Kodi United Nations ndi mayiko amene ali mamembala ake angapereke “pangano lotsimikizika ndi lokhazikika,” lofunika pothetsa chiwawa? Pogwidwa mawu m’lipoti lomwelo la nyuzipepala ya Star, Pulezidenti wa dziko la United States Bill Clinton anati: “Tikaona magazi onse amene akhetsedwa m’zaka zana linoli, tikudziŵa kuti n’kosavuta kunena kuti ‘zisadzachitikenso,’ koma n’kovuta kwambiri kutsata zomwezo.” Anawonjezanso kuti: “Kulonjeza kopitirira muyeso ndi nkhanza yofanana ndi kusasamala n’komwe.”
Zaka zoposa 2,500 zapitazo, mneneri Yeremiya anatchulapo za zoyesayesa za anthu: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Nanga pali chiyembekezo chotani chothetsera chiwawa?
Pamene tiŵerenga pa Yesaya 60:18, Mulungu anapereka chitsimikizo chakuti: “Chiwawa sichidzamvekanso m’dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m’malire ako.” Ulosi umenewo unakwaniritsidwa nthaŵi yoyamba pamene Mulungu anabwezeretsa anthu ake otengedwa ukapolowo kudziko lakwawo. Komanso uli ndi kukwaniritsidwa kwakukulu kumene tingasangalale nako. Yehova Mulungu ‘sakulonjeza mopitirira muyeso.’ Pokhala Wam’mwambamwamba ndi Mlengi wa mtundu wa anthu, ali woyenera kuthetsa “chiwawa chonse.” Mu Ufumu wa Mulungu, mudzakhala mtendere wokhawokha. Chiwawa chidzakhala chitachotsedwa kosatha!—Danieli 2:44.