Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Nchifukwa Ninji Tiyenera Kuwopa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1989 | January 1
    • Ngati ndi tero, lingalirani chomwe chimatanthauza kukhala Mkristu. Mogwirizana ndi Baibulo, kukhala Mkristu kumaphatikizapo kutsatira mosamalitsa m’mapazi a Yesu Kristu. (1 Petro 2:21) Tsopano, pamene kuli kwakuti palibe kukaikira kuti Yesu anakonda Mulungu, Baibulo limachipangitsa icho kukhala chomvekera kuti iye anamuwopanso iye. Yesaya, akumalankhula mwaulosi ponena za Yesu, ananena kuti adzakhala ndi “mzimu wa kudziŵa ndi kuwopa Yehova.” (Yesaya 11:2) Mosangalatsa, ngakhale ndi tero, kuwopa kumeneku sikunali katundu wolemetsa pa Yesu. Sitiyenera kulingalira za uko kukhala njira mu imene mwana amawopera tate wa nkhalwe kapena unyinji wa anthu osautsidwa ndi wolamulira wotsendereza. M’chenicheni, Yesaya analoseranso ponena za Yesu: “Ndipo adzakondwera nako kumuwopa Yehova.” (Yesaya 11:3) Ndimotani mmene mungasangalalire ndi kuwopa winawake?

      Chenicheni chiri chakuti, m’Baibulo liwu lakuti “kuwopa” liri ndi unyinji wa matanthauzo. Pali kuwopa kwa kuthupi kapena mantha omwe timamva pamene winawake afuna kutivulaza ife. Chotero, magulu ankhondo a Chiisrayeli “anamuwopa kwambiri” Goliati. (1 Samueli 17:23, 24) Kenaka pali kuwopa kwa kudzidzimutsa kosayembekezereka kapena kosadziŵika, monga ngati mmene Zekariya anamverera pamene mwadzidzidzi anakumanizana ndi mngelo wa Yehova m’kachisi. (Luka 1:11, 12) Ngakhale kuli tero, kuwopa kumene Yesu anakumva kaamba ka Atate wake sikunali kofanana ndi kulikonse kwa uku.

      M’malomwake, mawu oyambirira a Chihebri ndi Chigriki ogwiritsidwa ntchito m’Baibulo kaamba ka “kuwopa” kaŵirikaŵiri amalozera ku ulemu wakuya ndi mantha a Mulungu. Kumeneko kunali kuwopa kwaumulungu kumene Yesu anali nako ndi kumene mngelo anali kulimbikitsa aliyense kukulitsa lerolino. Mantha a ulemu amenewa, kapena kuwopa, kumayambika m’mitima mwathu pamene tisinkhasinkha pa nyonga ndi mphamvu ya Yehova ndi kulinganiza iyo ndi kuchepera kwathu kotheratu. Kumakula pamene tilingalira ntchito zake zamphamvu, ndipo kumakulitsidwanso mwakukumbukira mwa pemphero chenicheni chakuti ali Woŵeruza Wamkulu, wokhala ndi mphamvu ya kupatsa moyo limodzinso ndi kulanga ndi imfa yosatha.

  • Nchifukwa Ninji Tiyenera Kuwopa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1989 | January 1
    • Pa Salmo 19:9 tikuphunzitsidwa kuti: “Kuwopa Yehova kuli mbe, kwakukhalabe nthaŵi zonse. Maŵeruzo a Yehova ali owona; alungama konsekonse.” Chotero palibe china chirichonse choipa ponena za kuwopa Mulungu. Kuli koyera ndi kochinjiriza ndipo kumapangitsa mtumiki wa Mulungu kukhala wamphamvu kuposa adani ake. Mofanana ndi Yesu, Mkristu amapeza chikhutiritso m’kuwopa kumeneku m’njira imodzimodzi ndi imene iye amasangalalira ndi madalitso ena onse ochokera kwa Yehova.​—Yesaya 11:3.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena