Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ws mutu 21 tsamba 170-179
  • Kubwezeretsedwa kwa Munda wa Edene—Padziko Lonse Lapansi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwezeretsedwa kwa Munda wa Edene—Padziko Lonse Lapansi
  • Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko m’Paradaiso Wobwezeretsedwa
  • Masinthidwe m’Chinenero ndi m’Nyengo
  • Malo Okongola m’Chilengedwe Chonse Chopanda Malire
  • “Iwe Udzakhala ndi Ine m’Paradaiso”
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Kodi Paradaiso Amene Baibulo Limatchula ali Kuti?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • “Tidzaonana M’Paradaiso”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Kodi Dzikoli Lidzakhaladi Paradaiso Kapena ndi Maloto Chabe?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
Onani Zambiri
Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
ws mutu 21 tsamba 170-179

Chaputala 21

Kubwezeretsedwa kwa Munda wa Edene—Padziko Lonse Lapansi

1. (a) Kodi ndim’lingaliro lotani m’limene munda wa Edene udzabwezeretsedwa, ndipo chifukwa ninji sudzakhala kokha m’chigawo chochepa cha dziko lapansi? (b) Kodi mawu a Yesu kwa wochita zoipa amasonyeza chiyani?

MUNDA wa Edene unali “paradaiso wachisangalalo,” ndipo udzabwezeretsedwa m’lingaliro limenelo. (Genesis 2:8, Douay Version) Paradaiso woyambirira anali pambali yochepa ya dziko lapansi. Koma Yehova adalinganiza kuti banja laumunthu lomakulakula lifutukulire malire ake, kumalo onse, kufikira pamene Paradaiso akakuta dziko lonse lapansi ndi kulikongoletsa ndi ubwino wokwanira wa chilengedwe. (Genesis 1:26-28; 2:8, 9, 15) Mawu a Yesu kwa wochita zoipa womvera chifundo amene anafera pambali pake pa Golgota anatsimikizira mwamunayo kuti akaukitsidwa pamene kubwezeretsedwa kwa Paradaiso kukapita patsogolo kwambiri, pamenepo iye akazindikira masinthidwe okondweretsa padziko lapansi. (Luka 23:43) Kodi Paradaiso wa mbulumbwa yonse wobwezeretsedwa akakhala wotani? Kodi akakhala wosiyana motani ndi munda woyambirira wa Edene?

2. (a) Kodi nchiyani chimene chinali m’munda wa Edene woyambirira chimene sichidzakhala m’Paradaiso wa dziko lonse lapansi? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kuti Mulungu sadzayesa kumvera kwa anthu mwa mtengo umodzi?

2 M’maulosi ochititsa chidwi a zinthu zothutsa mtima zimene ziri patsogolopa, tikuwona kanthu kena kamene m’Paradaiso wa padziko lonse lapansi wobwezeretsedwa mulibe. Kodi ndiko chiyani? Ndiwo “mtengo wa kudziŵa zabwino ndi zoipa” umene unali “pakati pa munda.” (Genesis 2:17; 3:3) Mwachiwonekere umenewo unali mtengo umodzi. Kodi kukakhala kwanzeru kulingalira kuti pakati pa munda wa Edene wobwezeretsedwa, padziko lonse lapansi payenera kukhala mtengo umodzi wotero pamene lamulo la Mulungu loletsa lingaikidwepo? Ayi. Pangafunikire kuti anthu ayende ulendo wautali m’ngondya zakutali za dziko lapansi kupita kumalo okhala mtengo wotero ku Middle East kuti kukhale kotheka kwa iwo kuti mwinamwake adye zipatso zake mosamvera Mulungu Wam’mwambamwamba.

3. Kodi nchiyaninso chimene sichidzakhala m’Paradaiso wobwezeretsedwanso?

3 Ndiponso, kumalowo sikungakhale “njoka yolankhula” yoitana awo oyandikira mtengowo kuti adye zipatso zake zokoma m’masozo monyozera kotheratu malamulo a Mulungu. Ndipo sikudzakhala mzimu woipa wosawoneka uliwonse wogwiritsira ntchito njoka mwa machenjera ndi kuipangitsa kuwonekera kukhala ikulankhula kukopa wopenyerera kupandukira Mulungu mwa kutenga njira yosamvera Mlengi, ndizotulukapo zakupha.

4. Kodi nchifukwa ninji Satana Mdyerekezi sadzakhalapo mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa “Kalonga wa Mtendere”?

4 Ayi, cholengedwa chamzimu chosawoneka chimene chinasonkhezera njoka “kulankhula” kalero m’munda wa Edene sichidzakhalako mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa “Kalonga wa Mtendere,” Kristu Yesu. Woipa ameneyo, Satana Mdyerekezi, adzakhala wobindikiritsidwa kotheratu pambuyo pa Armagedo. Chivumbulutso 20:2, 3 chimatiuza kuti “Kalonga wa Mtendere” adzagwira “njoka yakaleyo, [ndiye] Mdyerekezi ndi Satana,” kummanga ndi kumponya kuphompho kwa zaka chikwi.

Mtendere Weniweni ndi Chisungiko m’Paradaiso Wobwezeretsedwa

5. M’Paradaiso wobwezeretsedwanso, kodi nchifukwa ninji mtendere wowona ndi chisungiko zidzafunga padziko lonse lapansi?

5 Ha ndimtendere ndi chisungiko zotani nanga zimene zidzatsatira! Sikudzakhala chisonkhezero cha Satana ndi ulamuliro wake pa anthu monga “wolamulira wadziko”! (Yohane 14:30) Popeza kuli kwakuti nawonso magulu a ziŵanda a Satana adzakhala ataikidwa m’phompho, potsirizira pake dziko lapansi lidzamasuka kumitundu iriyonse ya kulankhula ndi mizimu, ufiti, ndi matsenga—inde, mpangidwe uliwonse wauchiŵanda umene uli wonyansa kwa Yehova.—Deuteronomo 18:10-12.

6, 7. (a) Kodi nchifukwa ninji zinyama sizidzakhala chiwopsezo chirichonse kwa anthu? (b) Kodi ndiulosi wotani pa mfundoyi umene udzakwaniritsidwa kwenikweni?

6 Zolengedwa zanyama sizidzavulaza kapena kuwopseza nzika za Paradaiso wobwezeretsedwanso. Mulungu adzabwezeretsa mlingo uliwonse wotayika wa kuwopa anthu. Motero tingayembekezere kuti malongosoledwe okondweretsa onena za nyama operekedwa pa Yesaya 11:6-9 akakhala ndi kukwaniritsidwa kwenikweni mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa “Kalonga wa Mtendere” kuti:

7 “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wang’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. Ndipo ng’ombe yaikazi ndi chirombo zidzadya pamodzi; ndipo ana awo aang’ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzaseŵera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’funkha la mphiri. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”

8. Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa mwa mawu olosera akutiwo fumbi lidzakhala ‘chakudya cha njoka’?

8 Kukakhala kusanena chimodzi kuti Mulungu auzire ulosi wotere kukhala ndi tanthauzo lauzimu lokha ndipo osati kusonyeza zinthu zotere m’moyo weniweni wa padziko lapansi. Mofananamo, Yesaya 65:25 amatiuza kuti: “Mmbulu ndi mwana wa nkhosa zidzadya pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng’ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka.” Kodi zimenezi zikusonyeza kusolotsedwa kwa njoka pambulumbwa yonse munda wa Edene? Ayi, mawu aulosi akuti “fumbi lidzakhala chakudya cha njoka amatathauza kuti zirombo zokwaŵa sizidzakhalanso chiwopsezo kumoyo ndi kuthanzi labwino la zolengedwa zaumunthu. Zidzafunikira kuvomereza kuti anthu ali mbuye wawo amene ali ndi ulamuliro pa chirichonse chamoyo padziko lapansi, monga momwedi zinaliri ndi Adamu m’munda wa Edene pamene anatcha nyama zonse maina popanda kuchita mantha.—Genesis 2:19, 20; Hoseya 2:18.

9, 10. Kodi nchiyani chimene Salmo 65 ndi Yesaya 25:6 amaneneratu ponena za kulamulira kwa dziko lonse lapansi kwa “Kalongo wa Mtendere”?

9 Kukongola ndi kuchuluka kwa zinthu za munda umenewo wa Edene wa padziko lonse lapansi kuli kosayerekezeka ndi ife. Koma Baibulo limatipatsa malongosoledwe ake olosera m’salmo 65, lolunjikitsidwa kwa Mulungu. Mwapang’ono, salmo limeneli limati: “Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira, mulilemeza kwambiri; mtsinje wa Mulungu udzala nawo madzi: muwameretsera tirigu mmene munakonzera nthaka.” Sipadzakhala chilala panthaŵiyo, mmalo mwake, padzakhala “mvumbi”! (Salmo 65:1, 9-13) Padzakhala chakudya cha mwana alirenji kaamba ka nzika zonse za padziko lapansi.

10 Kuchuluka kwa zakudya kumeneku kwanenedweratunso pa Yesaya 25:6: “M’phiri limeneli Yehova wamakamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe.” Nzika za Paradaiso wobwezeretsedwa zidzadya zakudya zonona zimene zimachirikiza mtima ndi kuŵalitsa nkhope. Adzamwa vinyo, wokunthidwa bwino pamitsokwe ndi wosuzidwa bwino, wokondweretsa mitima yawo. (Salmo 104:14, 15) Sikudzakhala kupereŵera kwa chakudya m’Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa “Kalonga wa Mtendere”! Mmalo mwake, mudzakhala “dzinthu zochuluka.”—Salmo 72:16.

Masinthidwe m’Chinenero ndi m’Nyengo

11. Kodi ndimasinthidwe otani achinenero amene adzachitika, ndipo kodi zimenezi zidzayambukira anthu motani?

11 Kodi Paradaiso wa padziko lonse lapansi adzakanthidwa ndi chisokonezo cha kukhala ndi zinenero zambiri? Ayi, chifukwa chakuti “Kalonga wa Mtendere” akunenedwanso kukhala “Mulungu Wamphamvu.” (Yesaya 9:6) Motero iye ali wokhoza kuthetsa chisokonezo cha chinenero chimene chinayambira pa Nsanja ya Babele. (Genesis 11:6-9) Kodi nchiti chimene chidzakhala chinenero cha ana onse a padziko lapansi a “Atate Wosatha”? Kodi chidzakhala chinenero choyambirira cha Adamu woyamba, chimene Yehova anampatsa? Mwinamwake. Mulimonse mmene ziti zidzakhalire, zopinga zonse za chinenero zidzathetsedwa. Mudzakhoza kudzayenda ulendo kulikonse ndi kulankhula ndi anthu. Mudzakhoza kuwamva, ndipo iwo adzakhoza kukumvani. Padzakhala chinenero chimodzi kaamba ka anthu onse, ndipo kudzakhala koyenerera kuti Baibulo lathunthu lipezeke m’chinenero chimenecho. (Yerekezerani ndi Zefaniya 3:9.) M’chinenero chimenecho dziko lonse lapansi lidzadzazidwa ndi kudziŵa Yehova “monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.

12. Kodi ndimotani mmene Zekariya 14:9 adzakwaniritsidwira?

12 Pamenepo okwaniritsidwa adzakhala mawu a Zekariya 14:9: “Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala iye yekha ndi dzina lake iro lokha.” Yehova yekha adzalambiridwa monga Mulungu wowona yekha. ‘M’tsiku limenelo’ la Ufumu wa Yehova mwa “Kalonga wa Mtendere,” Mulungu adzavumbula matchulidwe enieni a dzina lake. Pamenepo padzakhala matchulidwe amodzi okha a dzina lopatulika limenelo ochitidwa ndi aliyense padziko lapansi. Dzina lake lidzakhala limodzi.

13. Kodi nchifukwa ninji nyengo, mphepo, ndi mafunde sizidzakhala chiwopsezo kwa nzika za dziko lapansi?

13 Kuti ndinyengo ndi masinthidwe a malo zotani zimene zidzakhalako ndizo nkhani yokondweretsa kwa awo oyembekezera Paradaiso wa dziko lonse wa “Kalonga wa Mtendere.” Chinthu chimodzi chidzatsimikizirika: Dziko lonse lapansi lidzakhala malo okondweretsa akukhalamo. Paradaiso ameneyo sadzadodometsedwa ndi mikuntho yowononga, mabingu, mafunde, maliyambwe, kapena anamondwe. Zimphepo, mafunde, ndi nyengo zonsezo zidzamvera “Kalonga wa Mtendere.” (Marko 4:37-41) Munda wa Edene wa padziko lonse udzakhala ndi kulamulirika kotheratu kwa nyengo. Dziko lonse lapansi lidzakongoletsedwa kukhala paradaiso wachisangalalo, umene udzakhala mwaŵi wachimwemwe kwa anthu onse kukhalamo motetezereka ku umuyaya wonse.

14, 15. (a) Kodi ndilonjezo lotani lolembedwa pa Chivumbulutso 21:3, 4 limene lidzakwaniritsidwa? (b) Kodi ndimotani mmene Mulungu adzakhalira pakati pa anthu? (c) Kodi ndimisozi ya mtundu wanji imene idzapukutidwa kosatha?

14 Pamenepo sipadzakhala konse chifukwa cha kukhalira ndi misozi yachisoni! Mawu olosera a Yehova akutitsimikizira kuti: “Chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

15 Miyamba ndiyo mpando wachifumu wa Mulungu, ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi ake. (Yesaya 66:1) Motero Mulungu sangakhale padziko lapansi mwa lingaliro lenileni. Koma adzakhala ndi anthu. Mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi, Yehova adzakhala pakati pa anthu moimiridwa ndi Mwana wake wolemekezedwayo, Yesu Kristu. Ha nkoyenerera chotani nanga kuti kukhalapo kwa Yehova kudzaimiridwa ndi ‘Kalonga wake wa Mtendere’! Zimenezi zikutikumbutsa mawu a Yesaya 7:14 onena za dzina logwiritsiridwa ntchito kwa Mesiya—Emanueli. Dzina limenelo limatanthauza ‘Mulungu Ali Nafe.’ (Mateyu 1:23) Ha nkokondweretsa chotani nanga, kuti kudzera mwa Mwana wake wokondedwa, Mulungu “adzakhala” ndi anthu! Pamenepo mwachiwonekere maso athu adzatulutsa misozi yachisangalalo pamene tiwona zozizwitsa zikuchitidwa ndi “Mulungu Wamphamvu” ameneyu, makamaka pamene akufa okondedwa akubwezeretsedwa kumoyo m’chiukiriro kuloŵa m’mikhalidwe ya Paradaiso. (Machitidwe 24:15) Zozizwitsa zotero zidzakhala umboni wothutsa mtima wakuti Mulungu ali ndi anthu ndi kuti iye akupukuta misozi yonse yachisoni m’maso mwathu kosatha.

Malo Okongola m’Chilengedwe Chonse Chopanda Malire

16. Kodi chiukiriro cha akufa chidzafunikira kuyembekezera kufikira Paradaiso atafutukulidwira padziko lonse lapansi? Longosolani.

16 Adamu woyamba anauzidwa mmene akayambira ntchito ya kuwonjezera Paradaiso kuyambira m’munda wa Edene mwenimwenimo. Kukwaniritsidwa kwa chifuno choyambirira chimenecho cha kuufutukulira padziko lonse lapansi kudzakwaniritsidwa. Koma kodi kuukitsidwa kwa akufa kudzafunikira kuyembekezera kufikira Paradaiso afutukulidwira padziko lonse lapansi? Ayi. Mwachitsanzo awo amene auka choyamba adzaukira kuzigawo za dziko lapansi zimene zidzakhala ndi opulumuka Armagedo ndipo amene adzakhala atasanduliza zigawo zimenezo kukhala paradaiso. Pamene chiukiriro cha anthu onse chikuchitika, zigawo za Paradaiso zimenezi zidzafutukuka kufikira zigwirizana kupanga Paradaiso wa dziko lonse lapansi.

17. Kodi ndimalongosoledwe otani amene aperekedwa ponena za Paradaiso wa padziko lonse?

17 Paradaiso alinkudza adzaposa mapaki onse kapena minda yokongola lerolino. Mong’animira, dziko lonse lapansi lidzaphukira kukhala paradaiso wamtendere, wokondweretsa osati kokha maso a anthu komanso ngakhale maso a Mlengi. Udzakhala munda wa Edene wa padziko lonse wokometseredwa ndi zomera ndi mitengo—wokoma m’maso ndi wotulutsa chakudya chochirikizira moyo wa zolengedwa muungwiro. Dziko lapansi lidzakhala malo okongola kosatha m’chilengedwe chonse chopanda malire cha Yehova. Ndipo anthu onse ogwirizanitsidwa adzakhala ndi thayo ndi mwaŵi wosatha wa kupanga dziko lapansi kukhala malo okongola.

18. Kodi tidziŵa bwanji kuti, amuna ndi akazi omwe, adzakhalira pamodzi mu mtendere monga abale ndi alongo?

18 Mamembala onse a banja laumunthu lopembedza limeneli adzakhalira pamodzi mu mtendere monga abale ndi alongo m’chiyero chonse, chifukwa chakuti kwenikweni iwo adzakhala ana a “Atate Wosatha,” “Kalonga wa Mtendere.” Motero sipadzakhala kulamulira kwankhalwe kochitidwa ndi amuna pa akazi, alongo awo. Koma Yehova Mulungu amalinganiza kukhala ndi akazi angwiro, monga momwedi analinganizira Hava kukhala ‘wothandiza’ kwa mwamuna wake wangwiro, Adamu.—Genesis 2:18; wonaninso 1 Petro 3:7.

19. Kodi dziko lapansi Laparadaiso lidzapereka mawonekedwe otani kwa okhala m’miyamba yosawoneka?

19 Mkhalidwe umene panthaŵiyo dziko lapansi la paradaiso lodzazidwa ndi amuna ndi akazi angwiro lidzapereka kwa okhala m’miyamba yosawoneka udzakhala waulemerero kwambiri ndi wokongola kwambiri kuposa mawonekedwe a dziko lapansi pamene linalengedwa poyamba, panthaŵi imene “nyenyezi zammaŵa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe.” (Yobu 38:7) Pamenepo Mulungu Wam’mwambamwamba, Yehova, adzakhala atalemekezedwa mokwanira kukhala Uyo amene chifuno chake chaulemerero sichingagonjetsedwe konse. Ulemerero wonse upite kwa iye!

[Chithunzi pamasamba 172, 173]

Paradaiso weniweni adzapangitsa “chopondapo mapazi” chonse cha Mulungu dziko lapansi, kukhala lokongola

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena