Yehova—Mphamvu Yathu
“Ya, Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyonga yanga.”—YESAYA 12:2, NW.
1. (a) Nchifukwa ninji Mboni za Yehova ziri zosiyana motero? (b) Ndimotani mmene Yesaya 12:2 akulongosolera chimene Yehova wachita kwa anthu ake?
KODI mumapezekapo pa misonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova? Kumeneko mumapeza anthu osiyana ndi ena alionse! Kodi anthu amenewa ndani, ndipo nchifukwa ninji iwo ali osiyana? Ndife anthu ake a Mulungu, ndipo tiri osiyana chifukwa timanyamula dzina lapamwamba pa ena onse—lija la Mlengi wa ulemerero wa zozizwitsa zonse za chilengedwe chotizungulira. Dzina lake liri pa ife. Muli m’dzina lake mmene mwachimwemwe timakumana kutengako mbali m’chakudya chosankhika chauzimu chimene iye amapereka “panthaŵi yoyenera” kupyolera mwa gulu lake. (Luka 12:42) Monga Mboni za Yehova, moyamikira timalemekeza dzina lake losayerekezeka m’mawu a Yesaya mutu 12, versi 2, NW, omwe amaŵerengedwa kuti: “Tawonani! Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzawopa; pakuti Ya Yehova, ndiye mphamvu yanga ndi nyonga yanga, iye ndiye chipulumutso changa.” Mulungu wathu watibweretsa ife kupyola ziyeso zambiri! Tsopano chipulumutso chathu chomalizira chikuyandikira—nachonso pa dzanja la Ya Yehova!
2. (a) Ndi mobwerezabwereza chotani mmene kalongosoledwe kakuti “Ya Yehova” kamawoneka m’Baibulo, ndipo pati? (b) Ndi kaŵerengedwe kosiyana kotani ka “nyonga” pa Yesaya 12:2, NW ndipo nchifukwa ninji iko kalinso koyenera?
2 Kalongosoledwe kameneka kakuti “Ya Yehova,” kuwirikiza kaŵiri kwa dzina laumulungu, kamapezeka kokha kaŵiri m’Baibulo, pano ndi pa Yesaya 26:4. Ngakhale atembenuzi a King James Version anachiwona icho kukhala choyenera kulemba ilo monga “AMBUYE YEHOVA.” Mogwirizana ndi mawu a m’munsi a mu New World Translation Reference Bible, kuŵerenga kosiyana kaamba ka “nyonga” pa Yesaya 12:2, NW kuli “nyimbo” ndi “chitamando.” Ndi chowona chotani nanga kuti Ya Yehova wamphamvuyonse, amene amapereka kwa alambiri ake mphamvu yaikulu, ali woyenera nyimbo zathu za chitamando!—Yesaya 40:28-31.
3. (a) Kodi Ya Yehova watsegula njira kaamba ka chiyani, ndipo pa maziko a chiyani? (b) Nchiyani chimene chiri chiyambukiro cha mawu a Paulo pa Aroma 11:33-36 pa Mboni za Yehova?
3 Mphamvu ya Yehova iri yolinganizidwa ndi nzeru yake, chilungamo, ndi chikondi. M’kusonyeza mikhalidwe ya umulungu imeneyo, Ya Yehova watsegula njira kaamba ka chipulumutso kwa mtundu wokhulupirira wa anthu pa maziko a nsembe ya dipo ya Yesu. M’chigwirizano ndi ichi, mtumwi Paulo anafuula kuti: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka! Pakuti ‘anadziŵitsa ndani mtima wake wa [Yehova, NW], kapena anakhala m’phungu wake ndani?’ Ndipo, ‘Anayamba ndani kumpatsa iye, ndipo adzambwezeranso?’ Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa iye, zichitika mwa iye, ndi kufikira kwa iye. Kwa iyeyo ukhale ulemerero ku nthaŵi zonse. Amen.” (Aroma 11:33-36) Chotero, chiri choyenerera chotani nanga kuti tigwiririre kwa Ya Yehova ndi kulengeza chidaliro chathu chotheratu ndi kukhulupirira iye monga Mulungu wathu wamphamvuyonse ndi Mbuye wathu Wolamulira!—Yerekezani ndi Ahebri 3:14.
4. (a) Nchifukwa ninji mneneri Yesaya anali ndi chifukwa chabwino cha kulengezera, ‘Ndidzakhulupirira ndipo sindidzawopa’? (b) Nchifukwa ninji anthu a Yehova ali ndi chifukwa chabwino cha kukhulupirira mwa Ya Yehova m’zana lino la 20?
4 Yesaya anali ndi chifukwa chabwino cha kulengezera kuti, ‘Ndidzakhulupirira ndipo sindidzawopa.’ Mneneriyo pambuyo pake anakhala wozolowerana kwambiri ndi machitachita opulumutsa a Mulungu. Iye anali mboni yowona ndi maso pamene Yehova anakwaniritsa mawu Ake mwakuchepetsa Asuri ndi mfumu yake yodzitukumula, Sanakeribu. Mu usiku umodzi, ankhondo a Asuri 185,000 anaphedwa kokha ndi mngelo mmodzi wotumizidwa ndi Mulungu wathu wamphamvuyonse, Yehova! Chipulumutso chachikulu chimenecho chinatulukapo chifukwa chakuti Mfumu Hezekiya ndi Yuda yense anakhulupirira kotheratu mwa Ya Yehova. (Yesaya 37:6, 7, 21, 36-38) M’zana lino la 20, Yehova wapulumutsanso anthu ake kuchokera ku chitsenderezo, kuletsedwa, zizunzo, ndi ndende za chibalo. Mofanana ndi Asuri odzitukumula amenewo a m’nthaŵi ya Yesaya, wolamulira wa chiNazi Adolf Hitler anatsekereza motsutsana ndi Mboni za Yehova, pa chochitika chimodzi akumafuula kuti, “Mbadwo uwu udzachotsedweratu mu Germany!” Koma anali Hitler ndi chiNazi chake amene anachotsedwa. Ndipo tsopano gulu lochepa la Mboni za chiGerman zomwe zinakhulupirira mwa Yehova zakula kufika ku chiŵerengero choposa 121,200!—Masalmo 27:1, 2; Aroma 8:31, 37.
5. Ndimotani mmene mawu a pa Yesaya 12:3-5 amagwirira ntchito kwa anthu okhulupirira mwa Mulungu lerolino?
5 Kulikonse kumene chizunzo chimabuka, anthu okhulupirira a Yehova amatsitsimulidwa ndi kulimbikitsidwa mwakumwa madzi opatsa moyo a chowonadi. Chiri monga mmene mneneri wa Mulungu ananenera pa Yesaya 12:3-5: “Chifukwa chake mudzakondwera pakutunga madzi m’zitsime za chipulumutso. Tsiku lomwelo mudzati, ‘Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa. Muimbire Yehova, pakuti wachita zaulemerero. Chidziŵike ichi m’dziko lonse.’” Lolani kuti tipitirize kumwa mozama chowonadi cha Ufumu ndipo moyamikira kukwezeka dzina la Ambuye wathu Wolamulira, Yehova. Ndi chidaliro chotheratu mwa Yehova, tiyeni ife “tilalike mawu, kuchita nawo panthaŵi yake, popanda nthaŵi yake.” (2 Timoteo 4:2) Chirichonse chimene otsutsa angachite, Ya Yehova mwachikondi adzatitsogoza ife m’njira ya chipulumutso!
‘Mudzi wa Mitundu Yakuwopsya’
6, 7. (a) M’chigwirizano ndi Yesaya 25:1, kodi alambiri a Yehova ayenera kumulemekeza kaamba ka chifukwa chiti? (b) Ndimotani mmene Yesaya 25:2, 3 amalongosolera mzinda winawake? (c) Ndi ku mzinda uti kumene mneneriyo mwachiwonekere akulozerako, ndipo nchifukwa ninji?
6 Tiyeni tsopano titembenukire ku Yesaya mutu 25. Mu versi 1 timaŵerenga kuti: “Yehova, inu ndinu Mulungu wanga. Ndidzakukuzani inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m’zowonadi.” Alambiri okhulupirira a Yehova amalemekeza iye kaamba ka ntchito zodabwitsa zimene iye wachita pakati pawo. Koma Yesaya kenaka akusonyeza kusiyana kwakukulu, akumanena kwa Yehova kuti: “Chifukwa inu mwasandutsa mudzi muunda, mudzi walinga bwinja, nyumba ya alendo kuti isakhale mudzi, sudzamangidwa konse. . . . Mudzi wa mitundu yakuwopsya udzakuwopani [Yehova].”—Yesaya 25:2, 3.
7 Kodi ndi uti umene uli mzinda wosatchulidwa dzina wakuwopsya umenewo? Yesaya angakhale anali kulozera ku Ar, likulu la Moabu, lomwe nthaŵi zonse linali mdani wa anthu a Mulungu. Koma mawu anzake a lembali pano akuwoneka kukhala oyenerana bwino ndi nthambi ina ya gulu la Satana—mdani wamkulu, Babulo. M’kupita kwa nthaŵi, Babulo akasakaza Yuda ndi Yerusalemu, kuwononga nyumba yolambirira ya Yehova, ndi kutenga anthu opulumuka kupita mu ukapolo. Yesaya akugwira mawu mfumu ya Babulo kukhala ikudzitukumula kuti: “Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu . . . ndidzafanana ndi Wam’mwambamwamba.” Koma Yehova akaukitsa Koresi wa ku Perisiya kugwetsa Babulo ndi kubwezeretsa anthu a Mulungu ku dziko lawo. Monga mmene kunaloseredwera, malo a Babulo wakale sanatsale chirichonse choposa “muulu wa miyala” ndi “bwinja lopasuka.”—Yesaya 14:12-14; 13:17-22.
8, 9. (a) Ndi Babulo wina uti amene alambiri a Yehova ayenera kulimbana naye, ndipo iye anakhalako motani? (b) Ndimotani mmene Yesaya akumlongosolera iye, ndipo nchifukwa ninji katchulidweko kali koyenera?
8 Komabe, zaka zoposa 2,500 pambuyo pa kugwetsedwa kwa Babulo, alambiri a Yehova adakali kupikisana ndi Babulo wina—“Babulo Wamkulu, amayi wa achigololo ndi wa zonyansitsa za dziko.” (Chivumbulutso 17:5) Iye ali ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Iye anabadwa mwamsanga pambuyo pa Chigumula cha tsiku la Nowa, pamene Nimrode anamanga Babulo woyambirira, yemwe anakhala chikuta cha chipembedzo chonyenga, champatuko. Pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa Chikristu ndi Yesu ndi atumwi ake, ampatuko anaipsya chowonadi cha Baibulo mwakubweretsamo “ziphunzitso za uchiwanda,” zachikunja za Chibabulo, ndipo dongosolo la chipembedzo la Chikristu cha Dziko linayambika. (1 Timoteo 4:1) Chikristu chotsanzira chimenechi chakhala mbali yaikulu ya “Babulo Wamkulu,” chomwe chimafutukulika kuzungulira dziko lonse lapansi m’mitundu yonse ya anthu. Yesaya akumulongosola iye monga ‘mudzi wa mitundu yakuwopsya.’
9 Kwa zaka zoposa zikwi zinayi, kuyambira pa kukhazikitsidwa kwa Babulo woyambirira kufikira tsopano, olamulira ankhalwe agwiritsira ntchito atsogoleri a chipembedzo odidikiza monga akalambula bwalo m’kutsendereza ndi kulamulira anthu wamba. Chotero, “munthu alamulira munthu ku chivulazo chake.” (Mlaliki 8:9, NW) Yesu anamverera chifundo anthu “chifukwa anali okambululudwa ndi omwazikana” ndi abusa a zipembedzo zonyenga oterowo. Lerolino, gulu losuliza koposa likuzindikiritsidwa monga “munthu wosayeruzika,” lopangidwa ndi atsogoleri a chipembedzo odzikweza a Chikristu cha Dziko, omwe atenga chitsogozo m’kutsutsa ndi kuzunza Mboni za Yehova.—Mateyu 9:36; 2 Atesalonika 2:3, 4.
10. (a) M’chigwirizano ndi Yesaya 25:3, ndimotani mmene ‘mudzi wa mitundu ya akuwopsya’ unakakamizidwira kulemekeza Yehova, limodzinso ndi kumuwopa iye? (b) Pa Yesaya 25:4, 5, ndimotani mmene Yesaya akulankhulira za Yehova, ponse paŵiri m’chigwirizano ndi “odzichepetsa” ndi “akuwopsya”?
10 M’chaka cha 1919 Yehova anamasula anthu ake owona kuchokera ku ulamuliro wa “Babulo Wamkulu.” ‘Mudzi wa mitundu ya kuwopsya’ umenewo unakakamizidwa kulemekeza Yehova m’chakuti iye anafunikira kuwona ndi kuwaŵidwa mtima “zinthu zodabwitsa” zimene iye anakwaniritsa mwakubwezeretsanso alambiri ake ku ntchito yamphamvu. Anthu a chipembedzo chonyenga akukakamizidwa kuwopa Yehova, kachiŵirinso, m’kuyembekezera zimene ziri kutsogolo kaamba ka iwo. Kwa zaka mazana, atsogoleri a chipembedzo odidikiza adzikweza iwo eni pamwamba pa anthu a chikhulupiriro cha chipembedzo. Koma tsopano Yesaya akulankhula za Yehova, akumanena kuti: “Inu mwakhala linga la aumphaŵi, linga la osowa m’kuvutidwa kwake, pobisalira chimphepo, mthunzi wa pa dzuŵa, pamene kuwomba kwa akuwopsya kufanana ndi chimphepo chakuwomba chemba. Monga kutentha m’malo ouma, inu mudzaletsa phokoso la alendo, nyimbo ya akuwopsya idzaletseka, monga mthunzi uletsa dzuŵa.”—Yesaya 25:4, 5.
Mulibe Nyimbo ya Chimwemwe mu “Babulo”!
11. Nchifukwa ninji palibe nyimbo ya chimwemwe m’mabwalo onse a “Babulo Wamkulu,” ndipo ndimotani mmene ichi chinachitidwira chitsanzo pa kusonkhana kwa kusakaniza zipembedzo pa Assisi, Italy?
11 Umenewo, ndithudi, uli mkhalidwe lerolino kuzungulira mabwalo a “Babulo Wamkulu.” Palibe nyimbo ya chimwemwe imene ikupezedwa kumeneko. Atsogoleri ake a chipembedzo asokonezedwa ponena za milungu imene iwo ayenera kulambira. Ichi chinasonyezedwa mowonekera bwino pa kusonkhana kwa zipembedzo zosakanizana pa Assisi, Italy, pa October 27, 1986. Kumeneko, m’chigwirizano ndi Chaka cha Mtendere wa Mitundu Yonse cha Mitundu Yogwirizana, Papa, John Paul II anasonkhanitsa atsogoleri a zipembedzo zazikulu za “Babulo Wamkulu.” Iwo onse anapemphera kaamba ka mtendere, anthu a chipembedzo ena a chiBuddha kwa utali wa maora 12 tsiku limodzi. Koma ndi kwa ndani kumene iwo anapemphera? Kodi kunali kwa Mariya? Kapena kwa Utatu woyera wa Chikristu cha Dziko? Kapena kwa utatu wa chiHindu? Kapena kwa zikwi za milungu ya chiBuddha? Kapena kwa Allah? Kapena kwa nyama yotsika ija, nkhandwe, imene a Shinto amalambira? Kapena kodi mapemphero olandiridwa koposa anali aja a m’Mwenye wa ku America wa fuko la Crow? Iye anasimbidwa kukhala ‘waulemerero mu nduwira ya ufumu,’ pamene iye anayatsa kaliwo wa mtendere ndi kunena pemphero lake “mu utsi pamene unakwera ngati chofukiza m’mpweya wozizira.”
12. Ndi ku mawu ati a Mika ndi Yesaya amene a zipembedzo amenewo samagwirizana nawo?
12 Chinthu chimodzi chiri chotsimikizirika: Palibe ndi mmodzi yense wa anthu a chipembedzo amenewo, kuchokera ku chiBuddha cha Dalai Lama kufikira ku “Wolemekezeka wake” Methodius wa Tchalitchi cha Greek Orthodox, amagwirizana ndi mawu a Baibulo pa Mika 4:5: “Ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yomka muyaya.” Iwo sagwirizana ndi chowonadi cha mawu ouziridwa a Yesaya pa mutu 42, mu maversi 5 ndi 8: “Atero Mulungu Yehova, iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka mmenemo, iye amene amapatsa anthu a mmenemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda mmenemo: ‘Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.’”
13. Nchiyani kwenikweni chimene chinachitika pa Assisi, ndipo kodi ichi chinatsutsidwa motani ndi Yesu pamene anali padziko lapansi?
13 Pa Assisi, phwando la chiwonetsero, zovala zosiyanasiyana, ndi mapemphero obwerezabwereza anali mtundu wa kupangira chiwonetsero chapoyera chachikulu. Ichi ndi chimene Mwana wa Yehova Yesu anatsutsa pamene iye anali pano padziko lapansi. Iye ananena za atsogoleri a chipembedzo a m’tsiku lake kuti: “Koma amachita ntchito zawo zonse kuti awonekere kwa anthu,” ndipo iye analankhula nawo mwachindunji akumanena kuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! chifukwa mutsekera anthu ufumu wa kumwamba pamaso pawo, pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.” (Mateyu 23:5, 13; onaninso Mateyu 6:1-8.) Sikali kawonekedwe ka kunja kapena malo olambirira amene amaŵerengera kwa Mulungu. Monga mmene Yesu ananenera kuti: “Mulungu ndiye Mzimu, ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mu mzimu ndi m’chowonadi.”—Yohane 4:21, 24.
Magwero Owona a Mtendere
14. (a) Nchifukwa ninji mapemphero a zipembedzo za dziko kaamba ka mtendere ali onyenga? (b) Nchiyani chimene chiri chiweruzo chaumulungu pa chipembedzo cha Chikristu cha Dziko?
14 Tikumawona kusokonezeka m’zipembedzo za dziko, kodi wina aliyense angakhale wopusa kulingalira kuti mapemphero a atsogoleri a zipembedzo angabweretse mtendere wa dziko lonse? Iwo akhala akupemphera monyenga kwa zaka mazana angapo, pamene pa nthaŵi imodzimodziyo akugawanamo kotheratu m’nkhondo za amitundu, za Chipembedzo, ndi chizunzo chankhanza. Mneneri wa Yehova anafunsa kuti: “Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake? kapena nyalungwe maanga ake? Pamenepo mungathe inunso kuchita zabwino, inu amene muzolowera kuchita zoipa.” (Yeremiya 13:23) Monga mbali yowonekera ya “Babulo Wamkulu”—ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga—chipembedzo cha Chikristu cha Dziko mwapadera chayesedwa ndi zoyesera za umulungu ndipo chapezedwa chosowa kanthu momvetsa chisoni. Icho chaweruzidwa!—Yeremiya 2:34, 35, 37; 5:29-31; Danieli 5:27.
15. Ndimotani mmene Yehova adzabweretsera mtendere wosatha, ndipo ndimotani mmene awo amene amakhulupirira iye amatumikira magwero a mtendere?
15 Yehova, “Mulungu wa mtendere,” adzabweretsa mtendere wosatha mwakuwononga onse okhala ndi liwongo la mwazi ndi kudzadza dziko lapansi ndi anthu amene mowonadi amakonda chowonadi ndi chilungamo. (Afilipi 4:9) Mogwirizana ndi Mfumu Davide, ali ofatsa amene “amakhulupirira Yehova ndi kuchita chokoma” amene “adzalandira dziko lapansi” ndipo “nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Masalmo 37:3, 11) Awo amene ‘nthaŵi zonse amakhulupirira Yehova ndi kuchita chokoma’ amatumikira magwero a mtendere m’njira imene awo amene amapereka mapemphero osakanizika kwa milungu yotsutsana, zosema, ndi mafano sangachite.—Masalmo 115:2-8; Yesaya 44:14-20.
16. Ndi phwando lotani limene Yehova akupereka kaamba ka ofatsa amene akusonkhanitsidwa kutuluka “m’mudzi wa mitundu ya akuwopsya”?
16 Ndi kusiyana kotani nanga kumene kulipo pakati pa mapemphero ndi ziyembekezo za anthu ake a Mulungu ndi awo a achirikizi a “Babulo Wamkulu”! Timayamikira bwino chotani nanga kuti “nyimbo ya akuwopsya idzaletseka”! (Yesaya 25:5) Koma ponena za ofatsa omwe akusonkhanitsidwa kuchokera “m’mudzi wa mitundu ya akuwopsya,” Yesaya akupitiriza kunena kuti: “Ndipo m’phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okha okha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.” (Yesaya 25:6) Phwando lauzimu logawanamo lerolino ndi awo amene amabwera kudzalambira Yehova liri lokwaniritsa mosangalatsa, liri phwando ndithudi! Mitima yathu imalimbikitsidwa kupirira ndipo chimwemwe chathu chimasefukira pamene timatumikira Yehova mwachangu m’chiyembekezo cha kubadwanso ndi phwando la zinthu zonona zimene Yehova walonjeza kaamba ka dziko lapansi latsopano.—Masalmo 104:1, 14, 15; Mateyu 19:28, KJ.
17. Ndi “zinthu zodabwitsa” zotani zimene Yehova adzakwaniritsa, kubweretsa chimwemwe chotani?
17 Posachedwapa, Ya Yehova adzachita “zinthu zodabwitsa” m’kuchotsa osati kokha “Babulo Wamkulu” komanso “nsalu yokuta” ya chitsutso yomwe imaphimba mtundu wa anthu chifukwa cha chimo la Adamu. (Yesaya 25:7) Inde, pa maziko a nsembe ya Yesu, Mulungu wathu adzakwaniritsa ulosi wa Yesaya 25:8: “Iye wameza imfa ku nthaŵi yonse, ndipo [Mfumu Ambuye Yehova, NW] adzapukuta misozi pa nkhope zonse, ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa pa dziko lonse lapansi, chifukwa Yehova wanena.” Chidzakhala chosangalatsa chotani nanga kuwona chimo la Adamu ndi imfa zikuchotsedwa ndi kulandira okondedwa pamene adzabwera kuchokera ku zogwirira za imfa! Chiri chosangalatsa chotani nanga kudziŵa kuti mboni zokhulupirika za Yehova zapereka yankho lokwanira kwa Wotonza wamkulu, Satana Mdyerekezi! (Miyambo 27:11) Palibe wina aliyense amene adzapereka chitonzo pa iwo, popeza iwo adzakhala atapambana m’chigwirizano ndi umphumphu wawo. “Mokhulupirika, ndi m’zowonadi,” Yehova iyemwini adzakhala atakwaniritsa zinthu zoloseredwa—“zauphungu zake zakale.” Dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso wolungama, wodzazidwa ndi anthu olungama. Chiyembekezo chachikuludi!
18. Mosasamala kanthu za zitsenderezo, nchiyani chimene tagamulapo kuchita, m’chigwirizano ndi Yesaya 25:9?
18 Kukhulupirira kwathu Yehova nthaŵi zonse kupyola m’masiku a mdima awa kudzakhala ndi mphoto yake yotsimikizirika. Mosasamala kanthu kuti ndi zitsenderezo zotani zimene tiyenera kulimbana nazo m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku—kaya m’kupereka kaamba ka mabanja athu, m’kusungilira ku maprinsipulo a Baibulo pa sukulu, kapena m’kupereka umboni m’magawo ovuta—lolani kuti tikhulupirire Yehova nthaŵi zonse. Kusunga kwathu unansi wathithithi ndi Yehova monga “wakumva pemphero” kudzatitsimikizira ife za chipulumutso. (Masalmo 65:2) Chotero, tiyeni tigamulepo kukhaladi pakati pa awo amene amanena m’mawu a Yesaya 25:9 kuti: “Tawonani! Uyu ndiye Mulungu wathu. Tamlindirira iye, adzatipulumutsa. Uyu ndiye Yehova. Tamlindirira iye, tidzakondwa ndi kusekerera m’chipulumutso chake.”
Mafunso Akubwereramo
◻ Ndimotani mmene Ya Yehova aliri mphamvu yathu ndi nyonga yathu?
◻ Nchiyani chimene chiri “mudzi wa mitundu ya akuwopsya”?
◻ Ndimotani mmene ‘mudzi wa mitundu ya akuwopsya’ unakakamizidwira kulemekeza Yehova, limodzi ndi kumuwopa iye?
◻ Nchiyani chimene chikusonyeza kuti mulibe nyimbo ya chimwemwe mu “Babulo Wamkulu”?
◻ Ndi “zinthu zodabwitsa” zotani zimene Yehova adzachitanso kwa anthu ake?