Kodi Mukudya Pagome Liti?
“Simungathe kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziŵanda.”—1 AKORINTO 10:21.
1. Kodi ndi magome otani amene ali pamaso pathu, ndipo kodi ndi chenjezo lotani limene mtumwi Paulo akupereka ponena za iwo?
MAWU ouziridwa ameneŵa a mtumwi Paulo amasonyeza kuti pamaso pa mtundu wa anthu paikidwa magome aŵiri ophiphiritsira. Gome lililonse limadziŵika ndi mtundu wa chakudya chophiphiritsira chimene chilipo, ndipo tonsefe tikudya pa limodzilo kapena pa linalo. Komabe, ngati tifuna kukondweretsa Mulungu, sitingadzidya pagome lake ndipo panthaŵi imodzimodziyo nkumachecheta pagome la ziŵanda. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziŵanda, [ndipo osati kwa Mulungu, NW]; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziŵanda. Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziŵanda; simungathe kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziŵanda.”—1 Akorinto 10:20, 21.
2. (a) Kodi ndi gome liti la Yehova limene linaliko m’masiku a Israyeli wakale, ndipo kodi ndani anagaŵanamo m’nsembe zoyamika? (b) Kodi kulandirako ku gome la Yehova lerolino kumatanthauzanji?
2 Mawu a Paulo amatikumbutsa za nsembe zoyamika zimene Aisrayeli akale anapereka pansi pa Chilamulo cha Yehova. Guwa la nsembe la Mulungu linkatchedwa gome, ndipo wobweretsa nyama yoyenera kuperekedwa nsembe ananenedwa kukhala akuyanjana ndi Yehova ndi ansembe. Motani? Choyamba, Yehova anagaŵanamo m’nsembeyo chifukwa chakuti mwazi unawazidwa pa guwa lake la nsembe ndipo mafuta anatenthedwa ndi malaŵi apansi pake. Chachiŵiri, wansembe anagaŵanako m’lingaliro lakuti iye (ndi banja lake) anadya nganga yowotcha ndi mwendo wakulamanja wa nyama yoperekedwa nsembeyo. Ndipo chachitatu, woperekayo anagaŵanako mwa kudya yonse yotsala. (Levitiko 7:11-36) Lerolino, kulandirako ku gome la Yehova kumatanthauza kuti tikumpatsa mtundu wa kulambira umene iye amafuna, monga momwe Yesu ndi atumwi ake anaperekera chitsanzo. Kuti tichite zimenezi, tifunikira kudya mwauzimu zimene Yehova akugaŵira kupyolera mwa Mawu ndi gulu lake. Aisrayeli, amene anakhala ndi chiyanjano chapadera ndi Yehova pagome lake, analetsedwa kupereka nsembe kwa ziŵanda pagome lawo. Aisrayeli auzimu ndi atsamwali awo a “nkhosa zina” ali pansi pa chiletso chaumulungu chofananacho.—Yohane 10:16.
3. Kodi wina akhoza kukhala motani ndi liwongo la kulandirako ku gome la ziŵanda m’tsiku lathu?
3 Kodi wina akhoza kukhala motani ndi liwongo la kulandirako ku gome la ziŵanda m’tsiku lathu? Mwa kutumikira zofuna za chilichonse chimene Yehova amatsutsa. Gome la ziŵanda limaphatikizapo manenanena auchiŵanda onse, amene amalinganizidwira kutisocheretsa ndi kutichotsa kwa Yehova. Kodi ndani amene angafune kudyetsa mtima ndi maganizo ake ululu wotero? Akristu oona amakana kugaŵanamo m’nsembe zimene anthu ochuluka lerolino amapereka kwa milungu ya nkhondo ndi chuma.—Mateyu 6:24.
Kupeŵa “Gome la Ziŵanda”
4. Kodi ndi funso lotani limene tonsefe tikuyang’anizana nalo, ndipo kodi nchifukwa ninji sitingafune mwadala kulandirako ku gome la ziŵanda?
4 Funso limene tonsefe tikuyang’anizana nalo nlakuti, Kodi ndikudya pagome liti? Sitingapeŵe choonadi chakuti tiyenera kudya pagome limodzilo kapena linalo. (Yerekezerani ndi Mateyu 12:30.) Sitingafune kumalandirako mwadala ku gome la ziŵanda. Kuchita motero kungatitayitse chiyanjo cha Mulungu woona yekha ndi wamoyo, Yehova. Kumbali ina, kulandirako chakudya ku gome la Yehova lokha kumatsogolera ku moyo wathu wosatha m’chimwemwe! (Yohane 17:3) Pali mwambi wakuti munthu ali chimene iye amadya. Chotero, aliyense amene afuna kukhala ndi thanzi labwino lakuthupi ndi lamaganizo ayenera kusamala ndi zakudya zake. Monga momwedi zakudya zamafuta ochuluka zosagwira thupi sizimachirikizira thanzi lathu lakuthupi, ngakhale kuti zimakonzedwa bwino ndi zokoleretsa, nawonso manenanena a dziko limeneli okometseredwa ndi malingaliro auchiŵanda ali zakudya zoipa zophiphiritsira zosagwira thupi zimene zidzaipitsa maganizo athu.
5. Kodi tingapeŵe motani kuloŵetsa m’maganizo ziphunzitso za ziŵanda lerolino?
5 Mtumwi Paulo analosera kuti m’masiku otsiriza, anthu akasocheretsedwa ndi “maphunziro a ziŵanda.” (1 Timoteo 4:1) Maphunziro auchiŵanda otero samangopezeka m’zikhulupiriro zonyenga zachipembedzo komanso amafalitsidwa mwanjira zina. Mwachitsanzo, tifunikira kupenda ndi kuyesa mabuku ndi magazini amene ife ndi ana athu timaŵerenga, maprogramu apawailesi yakanema amene timapenyerera, ndi maseŵero ndi mafilimu amene timaonerera. (Miyambo 14:15) Ngati pofuna kusanguluka tiŵerenga zopeka, kodi zimasimba chiwawa chopanda pake, kugonana kosaloledwa, kapena machitachita amatsenga? Ngati tikuŵerenga zosapeka kuti tiphunzire, kodi zimafotokoza nthanthi kapena njira ya moyo “osati potsata Kristu”? (Akolose 2:8) Kodi zongoyerekezera zopanda pake nzimene zikuperekedwa, kapena kodi kulowerera m’magulu adziko a m’chitaganya nkumene kukuchirikizidwa? Kodi zimasonkhezera chifuno cha kukhala wachuma kwambiri? (1 Timoteo 6:9) Kodi ndi chofalitsa chimene mwamachenjera chimapereka ziphunzitso zogaŵanitsa zimene zili zosemphana ndi Kristu? Ngati yankho nlakuti inde ndipo tipitirizabe kuŵerenga kapena kuonerera zinthu zotero, tikudziika pangozi ya kudya pagome la ziŵanda. Lerolino, pali zikwi mazanamazana za zofalitsidwa zimene zimachirikiza nthanthi zadziko zimene zimaoneka kukhala zopita patsogolo ndi zofala. (Mlaliki 12:12) Koma palibe alionse a manenanena ameneŵa amene alidi atsopano; ndipo samatumikira phindu kapena ubwino wa munthu, monga momwe zimene Satana ananena mwamachenjera kwa Hava sizinatumikire ubwino wake.—2 Akorinto 11:3.
6. Pamene Satana atipempha kulaŵa zakudya zake zosagwira thupi zauchiŵanda, kodi ife, kwenikweni, tiyenera kuchita motani?
6 Chotero, pamene Satana atipempha kulaŵa zakudya zake zosagwira thupi zauchiŵanda, kodi tiyenera kuchita motani? Monga momwe Yesu anachitira pamene anayesedwa ndi Satana kusanduliza miyala kukhala mkate. Yesu anayankha kuti: “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.” Ndiyeno pamene Mdyerekezi anati akapatsa Yesu “maiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo” ngati akagwa pansi ndi kugwadira Satana, Yesu anayankha kuti: “Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.”—Mateyu 4:3, 4, 8-10.
7. Kodi nchifukwa ninji tikudzinyenga ife eni ngati tiganiza kuti tingadye popanda vuto pagome la Yehova ndi pagome la ziŵanda lomwe?
7 Gome la Yehova silingayanjanitsidwe konse ndi gome loyalidwa ndi adani ake auchiŵanda! O, inde, zimenezo zinayesedwapo. Kumbukirani Aisrayeli akale m’masiku a mneneri Eliya. Anthuwo ananena kuti analambira Yehova, koma anakhulupirira kuti milungu ina, yonga ngati Baala, ikadzetsa kukhupuka. Eliya anayandikira kwa anthuwo nati: “Mukayikakayika kufikira liti? ngati Yehova ndiye Mulungu [woona, NW], mtsateni iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo.” Mosakayikira, Aisrayeli anali kutsimphina “choyamba pa mwendo umodzi ndiyeno pa winawo.” (1 Mafumu 18:21; The Jerusalem Bible) Eliya anatokosa ansembe a Baala kuti atsimikizire umulungu wa mulungu wawo. Mulungu amene akakhoza kubweretsa moto pa nsembeyo kuchokera kumwamba akatsimikizira kukhala Mulungu woona. Mosasamala kanthu za kuyesayesa kochuluka, ansembe a Baala analephera. Ndiyeno Eliya anangopemphera kuti: “Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu aŵa adziŵe kuti inu Yehova ndinu Mulungu [woona, NW].” Pomwepo moto wochokera kwa Yehova unatsika kumwamba ndi kutentha nsembe yanyama yokhathamira ndi madzi. Posonkhezeredwa ndi chionetsero chokhutiritsa cha umulungu wa Yehova, anthuwo anamvera Eliya napha aneneri onse a Baala 450. (1 Mafumu 18:24-40) Chotero lerolino, tiyenera kuzindikira Yehova monga Mulungu woona ndipo motsimikiza kuyamba kudya pagome lake lokha ngati sitinaterobe.
“Kapolo Wokhulupirika” Amayala Gome la Yehova
8. Kodi ndi kapolo wotani amene Yesu analosera kuti akamgwiritsira ntchito kudyetsa ophunzira ake mwauzimu mkati mwa kukhalapo kwake, ndipo kodi kapolo ameneyu ndani?
8 Ambuye Yesu Kristu analosera kuti mkati mwa kukhalapo kwawo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akagaŵira chakudya chauzimu kwa atumwi ake: “Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero. Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.” (Mateyu 24:45-47) Kapolo ameneyu watsimikizira kukhala, osati munthu mmodzi yekha, koma kagulu ka Akristu odzozedwa ndi odzipatulira. Kagulu kameneka kaika pa gome la Yehova chakudya chauzimu chabwino koposa kaamba ka otsalira odzozedwa ndi “khamu lalikulu” lomwe. Tsopano loposa mamiliyoni anayi, khamu lalikulu laima kumbali ya otsalira odzozedwa kuchirikiza uchifumu wa chilengedwe chonse wa Yehova Mulungu ndi Ufumu wake umene adzayeretsa nawo dzina lake loyera.—Chivumbulutso 7:9-17.
9. Kodi ndi chiŵiya chiti chimene kagulu ka kapolo kakhala kakugwiritsira ntchito kugaŵira chakudya chauzimu kwa Mboni za Yehova, ndipo kodi phwando lawo lauzimu limafotokozedwa motani mu ulosi?
9 Kagulu ka kapolo wokhulupirika kameneka kakhala kakugwiritsira ntchito Watch Tower Bible and Tract Society kugaŵira chakudya chauzimu kwa Mboni za Yehova zonse. Pamene Dziko Lachikristu ndi mbali yotsala ya dongosolo ili la zinthu lili ndi njala chifukwa cha kusoŵa chakudya chauzimu chopatsa moyo, anthu a Yehova akuchita phwando. (Amosi 8:11) Zimenezi zikukwaniritsa ulosi wa pa Yesaya 25:6: “Ndipo m’phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.” Monga momwe mavesi 7 ndi 8 asonyezera, phwando limeneli lidzapitirizabe kosatha. Ha, ndi dalitso chotani nanga limeneli kwa onse amene ali m’gulu looneka la Yehova tsopano lino, ndipo lidzapitirizabe kukhala dalitso chotani nanga mtsogolo!
Chenjerani ndi Chakudya Chaululu Chimene Chili pa Gome la Ziŵanda
10. (a) Kodi ndi chakudya chamtundu wotani chimene chikugaŵiridwa ndi kagulu ka kapolo woipa, ndipo kodi cholinga chawo nchiyani? (b) Kodi kagulu ka kapolo woipa kamachitira motani awo amene kale anali akapolo anzawo?
10 Chakudya chimene chili pa gome la ziŵanda nchaululu. Mwachitsanzo, talingalirani chakudya choperekedwa ndi kagulu ka kapolo woipa ndi ampatuko. Sichimapatsa zofunikira kapena kumangirira; nchosayenera. Sichingatero, pakuti ampatuko aleka kudya pagome la Yehova. Chotero, umunthu watsopano uliwonse umene anali atakulitsa alibenso. Chimene chimawasonkhezera, si mzimu woyera, koma kuipidwa kwanjiru. Iwo ali otengeka maganizo ndi chinthu chimodzi chokha—kupanda amene kale anali akapolo anzawo, monga momwe Yesu analoserera.—Mateyu 24:48, 49.
11. Kodi nchiyani chimene C. T. Russell analemba ponena za chosankha cha wina cha chakudya chauzimu, ndipo ndimotani mmene anafotokozera awo amene amasiya gome la Yehova?
11 Mwachitsanzo, kalelo mu 1909, amene anali prezidenti wa Watch Tower Society panthaŵiyo, C. T. Russell, analemba za awo amene anachoka ku gome la Yehova ndiyeno nkuyamba kuvutitsa amene kale anali akapolo anzawo. The Watch Tower ya October 1, 1909, inati: “Onse amene amadzipatula ku Sosaite ndi ntchito yake, mmalo mwa kupita patsogolo iwo eniwo kapena kumangirira ena m’chikhulupiriro ndi m’zisomo za mzimu, mwachionekere amachita zosiyana—amayesa kulepheretsa Chifuno chimene ankatumikira, ndipo, ndi phokoso laling’ono kapena lalikulu, amazimiririka pang’onopang’ono, akumadzivulaza iwo okha ndi ena okhala ndi mzimu wandewu wofananawo. . . . Ngati ena aganiza kuti angaike phoso labwino kapena labwinopo lofananalo pa magome ena, kapena kuti akhoza kutulutsa labwino kapena labwinopo iwo eni—alekeni atenge njira yawo. . . . Koma pamene tilola ena kupita kulikonse ndi ponseponse kukapeza chakudya ndi kuunika zimene zingawakhutiritse, modabwitsa, awo amene amakhala adani athu amatenga njira yosiyana kwambiri. Mmalo mwa kunena mwanjira yachimuna ya dziko kuti, ‘Ndapeza kanthu kamene ndimafuna; tsalani bwino!’ ameneŵa amasonyeza mkwiyo, dumbo, chidani, nkhwidzi, ‘ntchito za thupi ndi za mdyerekezi’ zimene sitinawaonepo anthu adziko akuzisonyeza. Amaoneka kukhala odzala ndi misala, hydrophobia [chiwewe] Zausatana. Ena a iwo amatimenya ndiyeno nkunena kuti tinawamenya. Iwo ali okonzeka kunena ndi kulemba mabodza onyoza ndi kugwera mumkhalidwe wakuchita njiru.”
12. (a) Kodi ampatuko amapanda motani akapolo anzawo? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kowopsa kudya zolemba za ampatuko chifukwa cha chidwi?
12 Inde, ampatuko amafalitsa mabuku amene amagwiritsira ntchito mawu opotoza zinthu, mawu odyolera, ndi bodza lamkunkhuniza. Ndipo amakwaŵira mtseri pamisonkhano ya Mboni, akumayesa kukola opusa. Nchifukwa chake, kungakhale kowopsa kulola chidwi chathu kutisonkhezera kudya zolemba zotero kapena kumvetsera nkhani zawo zoipa! Pamene kuli kwakuti sitingazione kukhala zangozi kwa ife enife, kuwopsa kulipobe. Chifukwa ninji? Chimodzi cha zifukwa nchakuti, mabuku ena a ampatuko amafotokoza mabodza mwa “mawu osalaza” ndi “mawu onyenga.” (Aroma 16:17, 18; 2 Petro 2:3) Kodi nchiyani chimene mungayembekezere ku gome la ziŵanda? Ndipo pamene kuli kwakuti ampatuko angafotokozenso zoona zakutizakuti, zimenezi kaŵirikaŵiri zimapotozedwa ndi cholinga cha kuchotsa ena ku gome la Yehova. Zolemba zawo zonse zimangosuliza ndi kunyoza! Palibe zimene zili zomangirira.
13, 14. Kodi nziti zimene zili zipatso za ampatuko ndi manenanena awo?
13 Yesu anati: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.” (Mateyu 7:16) Tsopano, kodi nziti zimene zili zipatso za ampatuko ndi zofalitsa zawo? Zinthu zinayi zimapezeka m’manenanena awo. (1) Machenjera. Pa Aefeso 4:14 pamafotokoza kuti ali ndi “kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa.” (2) Nzeru yonyada. (3) Kusoŵa chikondi. (4) Kusaona mtima kwa mitundu yosiyanasiyana. Zimenezi ndizo misanganizo ya chakudya chimene chili pa gome la ziŵanda, zonsezo nzolinganizidwira kukhwetemula chikhulupiriro cha anthu a Yehova.
14 Ndipo pali mbali ina. Kodi nkuti kumene ampatuko abwerera? M’zochitika zambiri, aloŵanso mumdima wa Dziko Lachikristu ndi ziphunzitso zake, zonga ngati chikhulupiriro chakuti Akristu onse amapita kumwamba. Ndiponso, ochuluka samatenga kaimidwe kolimba ka Malemba ponena za mwazi, uchete, ndi kufunika kwa kuchitira umboni za Ufumu wa Mulungu. Komabe, ifeyo tapulumuka mdima wa Babulo Wamkulu, ndipo sitifuna kubwereramo ayi. (Chivumbulutso 18:2, 4) Monga atumiki okhulupirika a Yehova, kodi tingafunirenji kuyang’ana ngakhale mobera pa manenanena operekedwa ndi okana gome la Yehova ameneŵa amene tsopano mwamawu amapanda awo amene akutithandiza kuloŵetsa “mawu a moyo”?—2 Timoteo 1:13.
15. Kodi ndi lamulo la mkhalidwe la Baibulo lotani limene limatithandiza kutenga njira yanzeru pamene timva za zinenezo zimene ampatuko amapanga?
15 Ena angakhale ofunsafunsa ponena za zinenezo zimene ampatuko amapanga. Koma tiyenera kulabadira lamulo la mkhalidwe la pa Deuteronomo 12:30, 31. Panopo Yehova kupyolera mwa Mose anachenjeza Aisrayeli ponena za zofunikira kupeŵedwa atangolanda malo anthu akunja okhala m’Dziko Lolonjezedwa. “Dzichenjerani nokha mungakodwe ndi kuwatsata, atawonongeka pamaso panu; ndi kuti mungafunsire milungu yawo, ndi kuti, Amitundu awa atumikira milungu yawo bwanji? ndichite momwemo inenso. Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu.” Inde, Yehova Mulungu adziŵa mmene chidwi chaumunthu chimagwirira ntchito. Kumbukirani Hava, limodzinso ndi mkazi wa Loti! (Luka 17:32; 1 Timoteo 2:14) Tisatchere khutu konse ku zimene ampatuko akunena kapena kuchita. Mmalomwake, tiyeni tikhale otanganitsidwa kumangirira anthu ndi kudya mokhulupirika pagome la Yehova!
Gome la Yehova Lokha Ndilo Lidzatsala
16. (a) Kodi posachedwapa nchiyani chimene chidzachitikira Satana, ziŵanda zake, ndi gome lophiphiritsira limene mitundu ya dzikoli yakhala ikudyapo? (b) Kodi nchiyani chimene chidzachitikira anthu onse amene apitirizabe kudya pagome la ziŵanda?
16 Posachedwapa, chisautso chachikulu chidzaulika mwadzidzidzi, chikumapita mofulumira ku mapeto ake mu “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Chidzafika pachimake pamene Yehova awononga dongosolo ili la zinthu ndi gome lophiphiritsira limene mitundu ya dzikoli yakhala ikudyapo. Yehova adzagonjetsanso gulu lonse losaoneka la Satana Mdyerekezi ndi makamu ake a ziŵanda. Awo amene apitirizabe kudya pagome lauzimu la Satana, gome la ziŵanda, adzakakamizidwa kupezeka pa phwando lenileni, ayi, osati monga odyako, koma monga mbali yaikulu ya chakudyacho—kufikira chiwonongeko chawo!—Onani Ezekieli 39:4; Chivumbulutso 19:17, 18.
17. Kodi ndi madalitso otani amene amadza kwa awo amene amadya pagome la Yehova pokha?
17 Gome la Yehova lokha ndilo lidzatsala. Awo amene moyamikira akudya pa ilo adzasungidwa ndipo adzakhala ndi mwaŵi wa kudya pamenepo ku nthaŵi zonse. Kupereŵera kwa chakudya kwa mtundu uliwonse sikudzawawopsezanso. (Salmo 67:6; 72:16) Ndi thanzi langwiro adzatumikira Yehova Mulungu m’Paradaiso! Pomalizira pake, mawu osonkhezera a Chivumbulutso 21:4 adzakwaniritsidwa bwino kwambiri: “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” Chitsutso pokhala chinthu chakale, uchifumu wa m’chilengedwe chonse wa Yehova Mulungu udzafunga ponseponse kosatha pamene chiyanjo chaumulungu chosatha chidzakhala pa mtundu wa anthu woomboledwa wokhala pa dziko lapansi Laparadaiso. Kuti tikapeze mphotho imeneyi, tiyeni tonsefe titsimikize mtima kudya pagome la Yehova pokha, limene ladzala ndi chakudya chauzimu chabwino koposa!
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi tingapeŵe motani kusocheretsedwa ndi ziphunzitso za ziŵanda?
◻ Kodi nchifukwa ninji sitingathe kudya popanda vuto pagome la Yehova ndi pagome la ziŵanda lomwe?
◻ Kodi ndi chakudya chamtundu wotani chimene chikuperekedwa ndi ampatuko?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuchita chidwi ndi zinenezo za ampatuko kuli kowopsa?
◻ Kodi nziti zimene zili zipatso za ampatuko?
[Chithunzi patsamba 10]
Gome la Yehova ladzala ndi chakudya chauzimu chabwino koposa